Kodi ndi njira yanji yomwe ophunzira angalangizire Sheikh wake?
Zomwe zili zoyenera ndi opposite; Sheikh ndi yemwe akuyenera kulangiza ophunzira wake, chifukwa iyeyo ndi amene ali ozindikira zinthu komanso odziwa kuposa ophunzirayo. Ophunzira nthawi zonse amakhala akufunafuna maphunziro ndi malangizo kuchokera kwa Sheikh. Nthawi zina Sheikh akhonza kumaoneka kwa ophunzira kuti akulakwitsa pomwe sizili choncho, koma chifukwa cha kupelewera kuzindikira kwake ophunzirayo. Komabe ngati ophunzira wakaikira chinthu, mwina akuganiza kuti Sheikh alakwitsa, akuyenera kuwafunsa mwaulemu.
Ma Salaf Salih (mibado ya ma Ulama olungama omwe anapita), anali kulemekeza ma Sheikh awo ndikukhala ndi mwambo pa iwo. Izi ndi zomwe zili zokakamizidwa kwa ophunzira. Chimodzimodzi tikamamva mbiri za makolo athu omwe anali kuphunzira kalekale mma 1970-90s, timamva kuti anali kulemekeza ma Sheikh awo moti anali kuwagwilira ntchito za pakhomo, kumunda ndi zina zotero, ukutu sikuti kunali kulipira kapena nkhanza, koma kunali kudzala chikondi pakati pawo ndikuthokoza komanso kulemekeza maphunziro odhula omwe ankawapatsa.
Koma lero yemwe ali onyozeka kwambiri ndiye Sheikh!
Kuchokera mu report la Ibn Abdil Barri mu “Jaami’ul Ilm wa Fadhlihi”, Ali bun Abi Talib radhia Allah anhu anati: “Ena mwa ma right a ‘Aalim kwa ophunzira ndi: 
– Ukamupitira umpatse salaam
– Ukhale kutsogolo
– Usamulozere ndi chala kapena kumutsinzinira
– Usayankhule kuti: “Sheikh wakutiwakuti anayankhula zosemphana ndi zomwe mukunenazo”.
– Usagwire chovala chake, usafunse mafunso onyoza kapena kubweretsa mkwiyo kwa iwo…” p231
Koma ngati Sheikhyo ali wa bid’ah, kapena mwalangizidwa ndi ena kuti Sheikhyo ndi wosocheretsa, simukuyenera kutenga maphunziro ake. 
Ndipo akakhala kuti ndi Sheikh a Haqq koma kuti amalakwitsa nthawi zina, ukuyenera kuwalangiza kuzera mmafunso monga: “Kodi Sheikh, ndi lamlo lanji Mchisilamu munthu kupanga zakuti zakuti?” pamenepo ndiye kuti mwafunsa mwanzeru ndipo adziwa kuti mukufuna kuwaongolera zina zake mwaulemu, ndipo kuphunzira kwanu kukhala kodalitsika in sha Allah.
الأجوبة المفيدة عن أسئلة المناهج الجديدة س50 ص129-130