Malamulo Ochititsa kuti Munthu Asale
– Chisilamu:
Yemwe sali Msilamu sanalamulidwe kusala
– Nzeru:
Wamisala sanalamulidwe kusala
– Kutha Msinkhu:
Mwana wamng’ono sanalamulidwe, koma ngati angakwanitse kusala alamulidwe kutero kuti azizolowera
– Kutha kusala:
Sanalamulidwe omwe sangakwanitse, monga nkhalamba zina. Odwala sanalamulidwe.
– Kukhanzikika:
Wapaulendo sanalamulidwe
Malamulo Ochititsa Kuti Kusala Kukhale Kovomerezeka
– Chisilamu
– Kusiya kwa haidh ndi nifaas
– Kukhala ndi nzeru
– Kukhala ndi chitsimikizo usiku
Ma sunnah a kusala
– Kudya chakudwa cha kum’bandakucha (Suhoor )
– Kuchedwetsa dakwi (kudya kumapeto kwa nthawi)
– Kufulumizitsa kumasula
– Kuchulukitsa kupanga ibaada yosiyanasiyana monga kuwerenga Qur’an, kupanga ma dhikr, kupemphera usiku, kuswali ma sunan rawaatib (ma sunna akumayambiliro ndi pambuyo pa swalat), kupereka swadaqa, kudzipereka pa kuchita zabwino.
– Kusamala lirime popewa kuchulutsa zoyankhula, komanso kupewa kuyankhula zoipa monga bodza, miseche, kutukwana ndi zoipa zina.
– Kumasula ndi tende kapena madzi
– Kupanga dua pakumasula, chifukwa dua yomwe imanenedwa pakumasula simakanidwa ndi zina zotero
Haraam (zoletsedwa) pa Swawm
– Kunama
– Miseche
– Kunyozana
– Kuchita zosokoneza
– Kupereka mavuto kwa ena
ndi zina zotero
Makrooh (zonyansa) pa Swawm
– Kusungira malovu ndikumeza
– Kupyola pochukucha mkamwa ndi mphuno (mpaka madzi kugwera mmimba) ndi zina zotero
Zomwe zimaononga swawm
– Kudya ndi kumwa masana
– Kugonana masana
– Haidh ndi nifaas
– Kutuluka Chisilamu
– Zinthu zomwe zimadalira kudya ndi kumwa
– Kulowa chinthu mmimba kudzera mkamwa kapena mphuno
– Kutsanza mwadala
– Hijaama (cupping)
– Kukaikira pa niyya
Zomwe siziononga swawm
– Kusazindikira za malamulo a swawm
– Kudya kapena kumwa chifukwa cha kuiwala
– Kuchitika chinthu pmosafuna monga Ihtilaam
– Kukakamizidwa (kuwopsezedwa) kuchita chinthu chomasulitsa
Ololedwa kumasula
– Odwala
– Wapaulendo
– Wa haidh ndi nifaas
– Nkhalamba yaimuna ndi yaikazi
– Oyembekezera komanso oyamwitsa ngati awopera moyo wawo kapena moyo wa mwana
– Kumasula ndicholinga chokonzekera jihaad
– Kumasula ndicholinga chofuna kupulumutsa munthu
Your Comments