“Maina oletsedwa Kuwapatsa Ana Athu”
zitsanzo za maina abwino
Maina oyenera kuwapatsa ana athu MCHISILAMU akuyenera kukhala omwe ali abwino, KUPATULA awa:

1. Maina omwe ali ndi liwu la Ibaadah “Abdul-” kumayambiliro, nkulumikizidwa ndi maina osakhala a Allah. Monga maina awa: (ndi oletsedwa (Haram):
Abdul Rasul – Abdul Nabi – Abdul Shams – Abdul Uzza – Abdul Masih – Abdul Ka’bah – Abdul Muni’m ndi ena otero. Ndipo amene anapatsidwa kapena kupereka maina oterewa, akuyenera kusintha mwachangu ndikupanga tawbah chifukwa ndi SHIRK.

2. Ndizoletsedwa (Haram) kupereka dzina mmaina omwe ndi a Allah yekha, monga:
Al Khaaliq, Al Raziq, Al Rabb, Al Rahmaan, Al Rahim. ndi ena otero.

3. Ndizoletsedwa (Haram) kupereka dzina lomwe tanthauzo lake liri lokhunza Allah yekha, monga mbiri zake, ntchito zake, monga:
Malikul Muluku (Mfumu ya Mafumu..) – Al Qaahir (Opambana) ndi ena otero.

4. Ndizoletsedwa (Haram) kupereka kapena kudzitchula dzina mmaina a ma Kafir, kapena maina omwe amadziwika kuti amagwiritsa ntchito aKhristu ndi aYuda, ngakhale kuti eni ake enieniwo anali Olungama (Ophunzira a Yesu) monga:
Abdul Maseeh – Paul – Petro – George – John, Mathews – ndi ena otero.
Maina monga Paul, Petro, Simon, John, Mathews, akuchokera kwa ophunzira a Sayyidna Isa alaih Ssalam, omwe anali okhulupilira, malinga ndi mmene yasimbira Qur’an yolemekezeka. Koma munthawi zino malinga ndikuti maina amenewa amadziwika kuti ndi a chikristu, ndipo yemwe watchulidwa dzina mmaina oterewo amadziwika kuti si Msilamu ngakhale tisanamdziwe, maina amenewo sitikuyenera kudzitchulira.   

5. Ndizoletsedwa (Haram) kutenga maina a mafano kapena ma shaytan ndi zonse zomwe zimapembedzedwa posakhala Allah, monga: Iblis, Dasim, Tamreeh, Laqees, Hubal – Manaat ndi ena otero.

6. Ndizoletsedwa (Haram) kutenga maina a zinyama zonyozeka mmaonekedwe, monga:
Kalb (Galu) – Himaar (Donkey/Bulu)
zitsanzo za maina abwino

7. Ndizonyansa (Makrooh) mu Deen kutenga maina omwe amakhala ndi matanthauzo a negative; opatsa mantha, onyozetsa, komanso a chinthu choti mutachiona mungathawe. Maina monga:
Harb (Nkhondo) – Rasshaash (Machine gun) – Hayaam (matenda a bulu) – Mavuto – Masiye – Ebola ndi ena otero.

8. Ndizonyansa (Makrooh) mu Deen kutenga maina opatsa chilakolako (sexy names). Maina amenewa amakonda kupatsidwa kapena kudzipatsa atsikana, monga:
Virgin,  Romeo, Juliet ndi ena ambiri otero

9. Ndizonyansa (Makrooh) mu Deen kutenga mwadala maina a anthu ochita zoipa monga oimba, ovina, ma actor ndi ena otero. Ena amatenga dzina lawo labwinobwino nkuliphatikiza ndi la celebrity, monga “Usher Muhamad” – “2PAC Salim” –
“Beyonce Aminah” – Aaliyah Fatimah” – “Busta Issah” ndi ena otero. Ena amachotseratu dzina lawo labwino nkutenga maina ngati amenewa, ati chifukwa chomukonda munthuyo. Nyansi mu Deen.
Koma ngati anthuwo maina awo ali abwino monga Muhammad Ali, Iman Abdul Majid etc, nzololedwa kudzitchulira ndicholinga chotengera ubwino wa dzinalo, osati cholinga chomutengera actoryo ndi zochitika zake.

10. Ndizonyansa (Makrooh) mu Deen kutenga dzina lomwe limatanthauza za machimo, monga:
Saariq (Robber/Rob) – Dhaalim/Mazloum (Mponderezi/Oponderezedwa)

11. Ndizonyansa (Makrooh) mu Deen kutenga maina a anthu omwe anali ochimwa monga:
Fir’aun (Pharaoh) – Haamaan – Qaarun – Abu Lahab – etc.

12. Ndizonyansa (Makrooh) mu Deen kutenga dzina lomwe laphatikizidwa ku ‘-Deen’ komanso “-Islam”, monga:
Muhyideen – Taqiyudeen – Nasrudeen – Kamaaludeen – Noordeen – Shamsdeen – Shihaabudeen – Jum’adeen –  Dhiyaaudeen – Saiful Islam – Shamsul Islam – Noorul Islam  – Hujjatul Islam ndi ena otero.
Ma Ulamaa ambiri ankakana kupatsidwa maina oterewa, ena mwa iwo ndi Imam Al Nawawi amene ankadana ndi kutchulidwa kuti Muhyideen (Odzutsa Deen). Sheikh Ibn Taimiyah ankadana ndi kutchulidwa kuti Taqiyudeen ndipo ananena kuti “…koma abale anga ndi amene andipatsa title imeneyo ndipo yatchuka pa ine…”. Komanso Sheikh Abu Abd Al Rahman  Muhammad Al Albaani ankakana kutchulidwa dzina loti Naasrudeen (Mpulumutsi was Deen).

13. Ndizonyansa (Makrooh) mu Deen kulumikiza ku -Allah liwu lina losakhala “Abdul-” kuti likhale “Abdullah”. Monga:
Hassaballah – Rahmatullah – Aayatullah – Kalimatullah (kupatula Isa ‘Yesu’ yekha) – Hujjatullah – Ruhullah (chifukwa Ruhullah ndi Jibril), (kupatulanso Isa) – ndi ena otero.
Chimodzimodzinso liwu loti “Rasul”.
Izi zikupezeka mu الفصل في الملل والأهواء والنحل “Alfaslu fi Al Milal wal Ahwaai wa Al Nihal vol.3/9”

14. Ndizonyansa (Makrooh) mu Deen kutenga maina a Angero, monga:
Jibril (Gabriel) – Israfeel – Mikail ndi ena otero.

15.  Ndizonyansa (Makrooh) mu Deen kutenga maina a ma Surah a mu Qur’an monga:
Taa Haa (Twaha) – Yaa Seen (Yasin) – Saad ndi ena otero, chifuklwa choti maina amenewa ndi a ma harf (zilembo) zomwe ma Surah ena anayambira, ndipo si maina a Mtumiki salla Allah alaih wasallam monga mmene ambiri amakhulupililira. Mupeza izi mu buku la تحفة المودود Tuhfatul Maudood, la Ibn Al Qayyim (ra).
zitsanzo za maina abwino

Maina omwe ali a makrooh (zonyansa kupanga mu deen), amakhala a makrooh kudzipatsa kapena kuwapatsa ana athu. Koma ngati munthu unalandira kalekale pamene operekawo sankazindikira ndipo ndi zovuta kuti usinthe pa zifukwa zomveka (monga kufalikira kwa dzinalo mma official  documents), palibe vuto kulisiya, komabe zomwe zili zabwino ndi kuyesetsa kupeza njira yosinthira.
Pomwe maina omwe ali haraam aja, akuyenera kusinthidwa pompano ndithu.
*********
Kulemekezeka kwa Maina mu Deen kuli mma Rank awa:
No.1- Abd Allah ndi Abdul Rahman
Chifukwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti: “Maina okondedwa kwa Allah ndi Abd Allah komanso Abdul Rahman” Sahih Muslim.

No. 2- Maina onse omwe amalumikizidwa ndi maina abwino a Allah, monga
Abdul Aziz –  Abdul Malik – Abdul Salam ndi ena onse.

No. 3- Maina a Atumiki ndi Athenga (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa iwo), ndipo lomwe liri labwino, lopambana komanso ndi mtsogoleri wa maina onse, ndi la Mtumiki wathu Muhammad salla Allah alaih wasallam komanso maina ake ena monga Ahmad.
Kenako maina a Atumiki omwe anakumana ndi zokhoma zochuluka kuposa ena onse komanso anapilira (أولو العزم Ulul Azmi), monga:
Ibrahim – Musa – Isa – Nuh (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa iwo)
Kenako maina a Atumiki ena onse.

No. 4- Maina a Akapolo a Allah omwe ankachulukitsa kuchita zabwino, motsogozedwa ndi ma Sahaba Olemekezeka a Mtumiki. Ndi zokondedwa (mustahabb) kutenga maina a anthu amenewa, potengera ubwino wawo komanso kuti adzitikumbutsa zintchito zabwino nthawi zonse kuti ma step athu a zabwino akhale apamwamba.
Koma nzachisoni munthu kutenga dzina la munthu yemwe anali wabwino, koma zochita zake zimakhala zosemphana ndi mwini dzinalo komanso za kumoto.

No. 5- Dzina lirilonse labwino lomwe liri ndi tanthauzo lokongola komanso lotamandika.
*********
Ndi zofunikira kwambiri tisanapereke dzina kwa mwana, kuonesetsa kuti dzina limenelo lidzakhala lake mmoyo wake wonse, osapereka dzina mwa temporary kuti adzasintha _akadzavinidwa_ …chifukwa inu simudziwa kuti mwanayo adzafika kumeneko. Komanso osapereka dzina loti lidzampatse mpanikizo iyeyo kapena makolo ake, kapena yemwe anampatsa dzinalo, akadzakula, posapeza nalo ufulu malinga ndi zimene likukamba.
zitsanzo za maina abwino

Zofunika Kuonesetsa Tisanapereke Maina
Tidzionesetsa kuti dzinalo lisadzakhale losemphana ndi ena mwa mastage a mu umoyo wake, ndikutanthauza kuti likhale loyenera nyengo zake zonse kuyambira ku ukanda wake, ku umwana wake, ku unyamata wake, ku ukulu wake, ku ubambo wake, ku ukalamba wake, mpaka pamene adzamwalire, lidzakhale dzina labwino…osati achina Mcherewatha – Chiwangulinda – Cheweje – Anguyekwaswere – Mtunduwatha.. maina amenewa ndi oipa komanso ndi oyendera kanyengo kena kake.
*********
Anthu ena amati ngati mu ndandanda wa maina ako simukupezeka dzina la chiMalawi, monga “Ramadhan Nu’man Abu Bakr Isa”, ndiye kuti siukulikonda dziko lako komanso mtundu wako monga Chewa, Yao etc, komanso sungadziwike kuti ndiwe ochokera kuti. Koma akuti lipezekepo lina lake kumapetoko, monga “Ramadhan Nu’man Ab Bakr Isa Likwanya”..eyaa, pamenepo ndine mMalawi weniweni wachiyao!
Ine ndikuti: Allah ananena yekha kuti anatisiyanitsa ziyankhulo ndi mitundu kuti tidzidizwana, osati maina. Choncho tisatenge dzina loipa chifukwa chotsatira komwe tikuchokera. Chisilamu chakwanira kukhala address yako.
*********
Oyenera Kupereka Dzina
Ndi udindo wa BAMBO chifukwa dzina lawo ndi limene mwanayo adzatenge ngati lachiwiri. Komabe ndi zabwino kuti bambo akambirane ndi mai pofufuza dzina loyenera la mwanayo ndipo akhonza kutenga maganizo a mayiwo ngati dzinalo liri labwino komanso pofuna kuwasangalatsa.
*********
Mwana akuyenera kutenga dzina la bambo ake kukhala lachiwiri, ngakhale bambowo atamwalira, kapena banja latha, komanso ngakhale atakhala kuti sanamuonepo mwanayo chibadwire komanso sanamulere.
*********
Chenjezo
Ena amafunisitsa kupereka dzina Lori pali wins amene anapatsidwapo kuyambira kale. Imeneyi ndi ngozi, chifukwa ambiri amatenga maina ku ziyankhulo dzina powamva kukongola. Ndipo amadzazindikira atakula kuti anatenga dzina losemphana ndi tawheed.
Tidzipereka maina omwe tikuwadziwa tanthauzo lake.
**********
Ndi zoletsedwa (Haram) mwana kutchulidwa ndi dzina losakhala la bambo ake omubala, KUPATULA ngati mwanayo anabadwira panja pa nikaah (zinaa), pamenepo ndiye kuti atenge dzina la MAI AKE, ndipo sali ololedwa kutenga la bambo ake.
*********
Allah ndi Yemwe Adziwa Kwambiri komanso salakwitsa. Ndipempha Chikhululuko ngati mu zokambazi muli kusokoneza kapena kusokeretsa kwa mtundu uliwonse komwe sindinakuzindikire.

zitsanzo za maina abwino