الاعتقاد أننا سننادى بأسماء أمهاتنا يوم القيامة
Chikhulupiliro choti tikaitanidwa ndi maina a mayi athu tsiku la Qiyamah

Ma sheikh ena amalalikira ndikuphunzitsa anthu kuti tsiku la Qiyaamah akuti tizikaitanidwa ndi a maina amayi athu osati ndi maina abambo athu; akuti pokana kuyalutsa, poti amene amadziwa bambo amwana ndi mayi. Zimatheka mwana mkukulu ndi bambo wina koma bambo ake enieni asali amenewo. Ndiye pokana kuyalutsana kotereku tsiku la Qiyaamah akuti tizikaitanidwa ndi maina amayi athu. Koma kodi izi ndi zoona?

Mwachitsanzo  ngati dzina lako ndiwe Moosa ndipo mai ako dzina lawo ndi Maryam, akuti uzikaitanidwa kuti Moosa Ibn Maryam tabwera, osati Moosa Adam ngati mmene anthu amakudziwira pa dziko lapansi. Sitikagwiritsa ntchito ma surname athu apa dziko lapansi
Ndipo amapereka umboni kuchokera mu Hadith ina yomwe imanena kuti

(إن الناس يوم القيامة يدعون بأسماء أمهاتهم لا باَبائهم سترا من الله عليهم)
Ndithu anthu tsiku la Qiyaamah azikaitanidwa ndi maina amai awo osati maina abambo awo chifukwa Allah akawabisa kuchokera kuzoyaluka zawo.
Hadith imeneyi ndi yabodza ilibe chiyambi mChislamu ndipo uku ndikumunamizira Mtumiki zomwe sananene. Ibn Al Qayyim (رحمه الله) anena kuti hadith’yi ndi yabodza ndipo Ibn Hajar (رحمه الله) anati ndi Hadith yopeka. Sheikh Al Albaani (رحمه الله) anatiso ndi hadith ya bodza. Ndipo umboni oti hadith yi ndiyabodza muupeza mu (الضعيفة) (433)

Chifukwa chani ma sheikh amatiuza kuti tizikaitanidwa ndi maina amai athu ndi cholinga choti tisakayaluke? kodi mesa tsiku la Qiyaamah ndi tsiku lomwe aliyense ochimwa akayaluke? Ili ndi tsiku lija lomwe Allah (ﷻ) walichemerera kuti
(يوم تبلى السرائر)
Tsiku limene zobitsika zonse zidzaonekera poyera

Ndiye maina akabisa bwanji zoyaluka? Chomvetsa chisoni ma Sheikh ambiri akugwiritsa ntchito ma Hadith abodzawa powalalikira anthu ngakhale zitakhala kuti zikutsutsana ndi Qur’an yolemekezeka komanso chiphunzitso cha Mtumiki (ﷺ).

Tiyeni tsopano tiwone umboni wokwanira womwe ukusonyeza kuti tsiku la Qiyaamah mopanda chikayiko tikayitanidwa ndithu ndi maina abambo athu
Kuchokera mu Hadith ya saheeh yomwe ikupezeka mu Al Bukhari komanso Muslim, Mtumiki (ﷺ) ananena kuti

إن الغادر يرفع له لواء يوم القيامة يقال: هذه غدرة فلان ابن فلان
Munthu wachinyengo (ochimwa) adzikaimikiridwa chi banner chomwe zochimwa zake zidzikaonetsedwa ndipo kudzikanenedwa: izi ndizochimwa (chinyengo) za uje mwana wa uje. 
Hadith ya saheeh ngati mmene tanenera kale ikupezeka mu (البخاري)(6177) komanso (مسلم)(1735)

Ndipo Ibn Battaal (ابن بطال) (رحمه الله) ananena kuti hadith imeneyi ndi umboni wotsutsa chikhulupiliro chopotoka cha anthu omwe amakhulupilira kuti tsiku la Qiyaamah anthu adzikaitanidwa ndi maina amai awo. Izi mudzipeza mu
(فتح البارى) volume 10 page 579

Ndipo Ibn Qayyim (رحمه الله) ananena kuti:
الخلق يدعون يوم القيامة باَبائهم لا بأمهاتهم
Cholengedwa chikaitanidwa tsiku la Qiyaamah ndi dzina la bambo ake osati dzina la mai ake.
Izi ndiye zoona zomwe zili mu sunnah ya saheeh. Uumboni wa izi mu upeza mu book lotchedwa (تحفة المودود بأحكام المولود) page 191 ..

Tiyeni tiwalalikire zoona anthu tisawauze kuti akaitanidwa ndi mayina amai awo potengera Hadith yomwe ndi ya bodza ayi. Izi sizoyenera kwa ife alaliki tisokoneza anthu.

CHENJEZO LOFUNIKIRA
Palinso hadith ina yomwe anthu ena amagwiritsa ntchito polalikira anthu zakuitanidwa ndi maina awo komanso maina abambo awo pamodzi ndipo mudzitenga maina abwino. Hadith’yo imanena kuti:
(إنكم تدعون يوم القيامة بأسمائكم وأسماء اَبائكم فحسنوا أسماءكم)
Hadith imeneyi ndiya fooka (ضعيف أبي داود)(4948) komanso (ضغيف الجامع)(2036)