Zomwe zimachitika masiku ano zobisa mahr nkudzaitanitsa nthawi yomwe nikaah ikuchitika, si chiphunzitso cha Chisilamu, komanso mboni ziwiri kufunsa mahr tsiku la nikaah sichiphunzitso cha Chisilamu.

Mahr imayenera kukhala ikudziwika kwa waliyy (muyang’aniri wa mkazi) pomafika tsiku la nikaah, ndipo (waliyy) ayenera kulandira mahr mmalo mwa mkaziyo ndikukamupatsa mwamuna pambuyo pa mwambo wa nikaah.

Zomapita kukafunsa mahr kwa azimayi tsiku la nikaah ndi zina mwa zomwe zili zolakwika, ndipo zobweretsa chisokonezo mu Chipembedzo, komanso ndi njira yopangitsa kusakanikirana kwa azibambo ndi azimayi, zomwe ndi uchimo ku Chipembedzo cha Allah (Chisilamu), Chipembedzo chokhacho chomwe ndi cha Allah, pomwe zipembedzo zinazi ndi zabodza ndipo zopeka, anthu ake amangodzipangira zawozawo zomwe afuna panthawiyo, zopanda ndondomeko ya umulungu wa Mlengi wawo.

Mkwatibwi asapezeke pagulu la amun a kuti alandire mahri kapena certificate. Ngati amuna ndi azimai akhala mosiyana, pasapezeke amuna ena kulowa kwa azimai ncholinga chokatenga mahr yomwe mkazi waitanitsa. Mkazi asafunsidwe kuti “mahri zingati?” kapena “mahri yake ndi chani?” kuti kenako ayankhule potchula mahr. Monga mmene tanenera kale, maitanitsidwe a mahri oterowo ndiosemphana ndi chiphunzitso cha Chisilamu.

Mwambo wa nikaah ya Chipembezo choonadi cha Allah opembezedwa mu choonadi, uyenera kukhala osiyana ndi mwambo wa ukwati wa zipembedzo zabodza ndi zopeka.

Nikaah yeniyeni ya malamulo a Chisilamu imachitika mosapitilira mphindi zisanu 5 ngati khutba itachitika, ndipo ngati khutba palibe, pa mphindi imodzi yokha nikaah imakhala yatha. Pa nikaah sipamakhala mwambo wina uliwonse kuposa kukwatitsa; kusiyana ndi walima (chikondwelero cha nikaah), ndipo ndi zofunika kusiyatsa pakati pa nikaah ndi walima.

Ma sheikh akuyenera kuphunzitsa anthu ndondomeko yofewa ya nikaah malinga ndi chiphunzitso cha Sunnah. Ndipo asalekelere mchitidwe wa nikaah woononga komanso wodzetsa mantha mmitima ya Asilamu omwe sanakwatire. Achinyamata ambiri amakhala akuopa kupanga nikaah chifukwa cha kusokonezeka ndi zochitika za mmanikaah ena, zomwe zimawaopseza kuti sangakwanitse malinga ndi kuchepekedwa kwa mthumba. Masheikh aphunzitse zoona zenizeni zoti Nikaah yolondola simafuna ndalama zoti mpaka kulepheretsa mwambo. Achite nikaah ndipo walimah adzachite tsiku lina akadzakhonzeka bwinobwino.