Kodi Chisilamu chikutinji kumbali ya kuwonera ma filimu a deen?

Mchisilamu mulibe ma filimu, pazifukwa izi:

1. Chifukwa kupanga ma film kunachokera kwa ma kuffaar omwe njira yomwe amapangira makafirimu awo, ndiyoyenera malinga ndi iwowo; palibe njira yoyenera malinga ndi Chisilamu. Choncho zonse zoyenera kuchitika mu filimu zimakhala zochokera kuchikaafir.

Makafir amaona kuti ali ndikusowekera kwinakwake komwe kumapezeka mmafilimu; akapanga filimu zimakhala kuti basi deen yawo ikuyenda, ndipo amakhulupilira zonse zomwe zikuchitika mmene ndichiyembekezo chopeza zabwino kwa mulungu wawo. Iwo alibe shariah yonga yaife, Alhmadulillah kuti tinadalitsidwa ndizabwino; Aayah imodzi ya mu Qur’an imatikwanira ife kuposa zomwe angalongosole ma series a movie ambirimbiri.

Gulu la anthu silimapangitsa zinthu kukhala halal, kapena haraam … Ife Asilamu sitimangotenga zochita mu deen kuchokera kwa gulu la anthu…

2. Filimu ndi bodza, zopeka; sizimakhala zoona. Sitingapeze ‘filimu ya Chisilamu’ yopanda bodza mkati mwake, kapena kukhotetsa mbiri ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam komanso kupezekamo zosemphana ndi Aqeeda.

3. Kuti filimu isangalatse, imayenera kukhala ndi zinthu zokometsera zomwe zili zoletsedwa Mchisilamu, monga kupezekamo akazi omwe timaletsedwa kuwayang’anitsitsa, ndipo mmenemo amatha kupezeka osavala, komanso kusakanikirana ndi amuna pochitira limodzi zinthu. Izitu ngakhale filimu yaikulu yotchuka ija amaitcha kuti The Message/Uthenga, ya Mbiri ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam.

Zomwe zinalembedwa mmabuku ndizokwanira, chifukwa mmenemo amakhala akusimba za nthawi ya umbuli sharia isanabwere, tsopanbo ena akabwera nkudzapanga filimu ndikumadziyerekeza kuti ndi Abu Lahab, munthu woipa, zikhala kuti akuphunzitsa chani?

4. Mafilimu a Chisilamu omwe amapezekawa, ndiosayenera kupangidwa ndi kuwonera komwe chifukwa mmene ndanenera muja kuti zolinga zawo zimakhala zotengera kwa ma kuffaar omwe amapanga mafilimu awo. Tangoganizirani, Akhristu anapanga filimu ya Yesu, Asilamunso anapanga filimu ya Muhammad … Mkhristu wina anadziyerekeza mu filimuyo ngati Yesu ndipo ena anadziyerekeza ngati ophunzira ake. Chimodzimodzi Asilamu, anthu ambirimbiri anadziyerekeza ndi ma Swahaba.

Tsopano muone; Akhristu alero atakhutitsidwa ndi filimu ya Yesu, anamutenga munthu yemwe anadziyerekeza kuti ndi Yesu uja nkumamupachika mmanyumba mwawo, pamtanda, kumasema zithunzi zofanana naye, ndi chikhulupiliro choti uyu ndi Yesu ndithu!
Chimodzimodzi lero lino Msilamu akangoona chithu cha Anthony Quinn (Kaafir waku Mexico uja  yemwe anamuyerekeza ndi Hamza radhia Allahu anhu mu filimu ya Uthenga ya chingerezi) amakhulupilira kuti ndi Hamza!
Akamuona munthu yemwe anamuyerekeza ndi Yusuf alaih salaam mu filimu, amakhulupilira kuti ndiye Yusuf, mpaka ndithu anatenga chithunzi chake nkumamujambula malo ena ndi ena … tangoyesani kupita pa google mutaipe kuti Yusuf alaih salaam, musankhe images,, mumuona Mustafa Zamani waku Iran (Shia) ali pamenepo, ndipo zithunzi zake aliyense akaona amangoti ndi Yusuf weniweni, chifukwa cha filimu.

Tsiku lina pamene Mtumiki wa Allah, salla Allahu alaih wasallam anali kuyenda ndi ma Swahaba ake, anadutsa mtengo womwe ma mushrik anali kukolekamo zida zawo zankhondo, ndipo anati: Ee Mtumiki wa Allah, tipangireni ifenso malo okoleka monga mmene aliri awowo! Mtumiki anati: “Allahu Akbar, Allahu Akbar, izi ndi sunnah (zizolowezi), mwayankhula monga momwe anayankhulira anthu a Musa alaih ssalaam kuti “tipangireni ife mulungu monga mulungu wawoyo” Al-A’raaf 137″.

Inde, tikutha kuona kuti pali kusiyana kwakulu pakati pa pempho la anthu a Musa, omwe anali kupempha kuti awapangire mulungu wawo, ndi ophunzira a Mtumiki salla Allah alaih wasallam, omwe anapempha kuti awapangire chokolekamo zida zawo … komabe, pachifukwa choti anapempha kuti awapangire zotengera ku ma mushrik, Mtumiki anawaletsa kuti asakhale ndi chikhalidwe chomangotengera zochita za ma mushrik.

Kodi nanga n’chiyani chomwe chimawapangitsa ma mushrikiwa kupanga mafilimu?
Chifukwa choti alibe chakudya chauzimu, chomwe ndichakudya cha ife Asilamu ndipo chifukwa chokhala ndi chakudyachi, tilibe nthawi yomapanga ma filimu kapena kuwonera.
Pamenepa sikuti tiphatikize nkhaniyi mmaganizo ponena kuti ndiye kuti ndege, galimoto, phone, TV ndi zina zonse za tecknology, tizisiye chifukwa anazitulukira makaafir koyamba, ayi ndithu, zimenezo sizikulowa mu hadith yoti: “ndipo yemwe azifanizire ndigulu, ali mwa iwo”. Ngati ungatsegule TV pazinthu za halaal zoti palibe njira ina yomwe ungazipezere koma TV, monga kufuna kumva momwe dziko likuyendera kumbali ya utsogoleri, malangizo a zaumoyo, zamaphunziro ndi zina zotero, palibe vuto Mchisilamu ndipo ndizololezedwa … osati mmene amanenera ena kuti TV yonse ndi haraam. Komano TV yomweyo ikasanduka kukhala chirichonse kwaiwe Msilamu; kumangoonera zilizonse ndi za haraam zomwe, kukudutsa nthawi ya swalaat komanso kulolera kudula maubale, zimenezo ndi haraam – mu TV muli za haraam ndi halaa, zili ndi iwe kusankha za halal zokhazo … chimodzimodzi galimoto, phone, ndi zina zonsezo; magwiritsidwe ntchito ako ndamene akhale a halal kapena haram, koma chinthucho pachoka nchololezedwa.

Choncho Msilamu akhale wotanganidwa ndizomwe zingamuthandize mu Usilamu wake; apewe zomwe zingadetse Chisilamu chake komanso asakhale pa mpikisano ndi anthu polimbana ndiomwe akulamula zabwino ndi kuletsa zoipa, koma adziwerengere yekha isanamukwanire nthawi yosatheka kubwelera kudzadziwelengera.

 Fatawa Al-Mar’atul Muslimah p.613-614 Sheikh Al-Albaani

Edition: Ramadhan Isa