Tiwadziwe ma Imaam a Madh’hab Anayi

1. Imaam Abu Hanifa AlNu’man bun Thabit
2. Imaam Maalik bun Anas
3. Imaam Muhammad bun Idris AlShaafi’iy
4. Imaam Ahmad bun Hanbal

Anthu amene amatsatira Qur’an ndi Sunnah za Mtumiki salla Allah alaih wasallam amatchedwa Ahlu Sunnah wal Jamaah
Kodi ma madh’hab ndi magulu a Chisilamu?
Madh’hab a Shafi’iyy, Maalikiyy, Hanafiyy komanso Hanbaliyy si magulu Mchisilamu. Koma ndi njira (Madh’hab) zomwe Ahlu Sunnah amatsatira pa maphunziro a deen.
Kwa ambiri, nkhani ya ma Imam imavuta kuimvetsa chifukwa choti ma Imaam amenewa anapezeka pambuyo pa ma Swahaba, ndiye ambiri omwe sakudziwa amaona ngati ma Imam anayi amenewa ndi amene amagawa Asilamu. Koma zoona zenizeni si choncho. Limeneli ndi gulu limodzi lomwe limatsatira Qur’an ndi Sunnah (Ahlu Sunnah wal Jamaah), ndipo ma Imaam amenewa anaphunzitsana wina ndi mzake.
Chisilamuchi kuti chimveke bwinobwino kwa ife, timayenera kuchiphunzira kwa ma Sheikh, ma Ustaaz, ma Imam, ma ulamaa, ma mufti. Ndipo timatenga zomwe akutiphunzitsazo. Ndipo sizimapezeka kuti amene anaphunzira kwa Sheikh apanga deen yawo, ayi ndithu.
Koma kuti onse amati tinaphunzira kwa sheikh wakutiwakuti ndipo anati zakutizakuti. Ziphunzitso za aphunzitsi onsewo zimakhala zochokera kwa Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam. Ndipo amene amaphunzitsa zosemphana ndi Sunnah, ameneyo ndi osokoneza. Ndi amene amagawa Asilamu aja.
Nchimodzimodzi , ma Imaam 4 (Muhammad bun Idrisa Al Shafi, Malik bun Anas, Ahmad bun Hanbali, Abu Hanifah Al Nu’man bun Thabit), onsewa anali aphunzitsi akuluakulu omwe anaphunzitsa Sunnah ya Mtumiki kwa anthu dziko lonse. ndipo ma Imaam onse amene abwera pambuyo pawo amaphunzitsa deeniyi kuzera mu zomwe anali kuphunzitsa iwowa, kuchokera mu Sunnah za Mtumiki salla Allah alaih wasallam.
Madrasa a Imam aliyense amatengedwa ngati njira yodziwira momwe mtumiki ankapangira Deen. Nchifukwa chake madrasawa amatchedwa Madh’hab.
Imam aliyense akhonza kutsatidwa. Ndipo ngati tingapeze zomwe Imaam wina akunena koma zosemphana ndi Sunnah, zimenezo tisadzitsatire, monga mmene ananenera eni akewo kuti mukaona zosemphana ndi Mtumiki mu madh’hab anga, musadzitenge, mutenge za mtumiki, kusonyeza kuti iwo amaphunzitsa za Mtumiki, alibe kuyendera maganizo awo.
Ma Imaam onse anayi ndi Ahlu Sunnah (amaphunzitsa njiira ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam).
Nkhani ya ma Imaam ndi yaitali pofuna kuti munthu yemwe sakudziwapo kanthu ayimvesetse, chifukwa ma Imaam amenewa amatodzedwa malinga ndi kusazindikira kwa ena kuti ali ndi potani mu deen.
Ma Imaam alipo ambirimbiri osati anayi okhawa. Komanso aliko a mmagulu osiyanasiyana monga a chi Shia (alipo 12) komanso ena. Koma omwe tidzikufotokozawa ndi ma Imaam athu a SUNNAH.
Ma Imaam amenewa anagwirizana mu ziphunzitso zawo kumbali yaikulu ya Deen ya Chisilamu, koma anasemphana mu zochepa kwambiri zimene zimatha kupezeka solution yake mosavuta, poti zonsezo aliyense ankayendera ma umboni ochokera kwa Mtumiki kuzera mma Swahaba. Choncho timfundo tomwe anasemphanato ndi timene tinachititsa kuti aliyense akhale ndi madh’hab malinga ndi malongosoledwe ake. koma zonsezo zikubwelera ku Qur’an ndi Sunnah.
Imaam Abu Hanifah Al Nu’man bun Thabit
Anabadwa mchaka cha 80 AH (699AC) ndipo anamwalira 150 AH (767 AC)
Madh’hab: Hanafiyy
Imaam Malik bun Anas
Anabadwa mchaka cha 93 AH (715 AC) ndipo anamwalira 179 AH (769 AC)
Madh’hab: Maalikiyy
Imaam muhammad bun Idrisa Al Shafi’i
Anabadwa mchaka cha 150 AH (766 AC) ndipo anamwalira mchaka cha 204 AH (820 AC)
Madh’hab: Al Shafi’iyy
Imaam Ahmad bun Hanbal
Anabadwa mchaka cha 164 AH (780 AC) ndipo anamwalira 241 AH (855 AC)
Madh’hab: Al Hanbaliyy
Imam Abu Hanifah ndi Imaam oyambilira mwa onsewo, ndipo anali Taabi’iy (yemwe anadza pambuyo pa ma Swahaba)
Anakumana ndi ma Swahaba a Mtumiki ambirimbiri ndithu. Koma sanakumane ndi ma Imaam ena atatu omwe anadza pambuyo pakewo.
Imam Al Shafi’i yemwe ndi wachitatu, anakumana ndi ma Imaam anzake onsewo kupatula Abu Hanifah yemwe ndi wakale.
Imaam Al Shafi’i anaphunzira kwa Imaam Malik ndipo anali mphunzitsi wa Imaam Ahmad bun Hanbal.
Uwunso ndi umboni woti ma Imaam amenewa ndi amodzi ndithu, anaphunzitsana, komanso ziphunzitso zawo onsewo ndi zochokera kwa Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam.
Kodi nanga ma Imaam amenewa kwawo nkuti?
Ndi aku Makkah kapena Madina kapena ku Egypt, ku Iraqi kapena ku India?
Imaam Abu Hanifa anabadwira ku Kufaa ku Iraq ndipo anamwalilira ku Baghdad ku Iraq komweko
Imaam Maalik bun Anas anabadwira ku Madina anamwalilira ku Madinah komweko
Imaam Al Shafi’i anabadwira ku Gaza, Palestine ndipo anamwalilira ku Fustat ku Egypt
Imaam Hanbal anabadwira ku Baghdad ku iraq ndipo anamwalilira ku Baghdad komweko
Kodi njira zinayi zimenezi ndi zabwino kutsatira? nanga zinayamba kupezeka liti mu Chisilamumu?
Madh’hab anayi amenewa (Hanbaliyya – Shafi’iyya – Malikiyya – Hanafiyya), ndi madh’hab odziwika, amene anayamba kudziwika mma 2nd century pambuyo pa msamuko, monga madh’hab a Hanafiyya ndi Malikiyya, pomwe Shafi’iyya ndi Hanbaliyya anayamba kufala pambuyo pake mu 3rd century, ndipo ma Imaam ake ndi abwino ndithu komanso ali mu chiwongoko ndi choonadi.
Anthu amenewa ndi ma Imaam a chiwongoko komanso ma Ulamaa abwino.
Koma sizikutanthauza kuti samalakwitsa, chifukwa iwowo si Atumiki kapena Angelo, koma ndi anthu ngati ife tomwe kungosiyana kuti anaphunzira ndikulimbikira kwambiri pa ‘ilm ya Deen. Choncho, wina aliyense ali ndi zofooka zake malinga ndi mmene anapezera maphunziro ake kuchokera mu Sunnah.
Sizikutahthauza kuti anamaliza chilichonse mu Sunnah za Mtumiki salla Allah alaih wasallam popanda chosiya, koma anayesetsa moti anthu amawatsatira chifukwa cha chilungamo chawo, ndipo ena mwa otsatira ndi amene analemba mabuku a zokamba zawo komanso ma fatwa awo. Koma ma Imaam amenewa pali zina ndi zina zomwe sanadzipeze mma Sunnah a Mtumiki ndipo anayesetsa kupanga ijtihaad nkubweretsa zoyenera malinga ndi mmene zina ziliri.
Kodi Mtumiki anali wa Madh’hab anji
Ena chifukwa cha umbuli, mmalo momapempha Allah kuti awapatse maphunziro komanso awawongolere ku Aqeedah yabwino, amakhala busy kunyoza ma Imaam amenewa, poganiza (mwaumbuli momwemo) kuti amenewa ndi atsogoleri a magulu.
Amakonda kufunsa funso limeneli. Koma kwa munthu ozindikira sangafunse chifukwa kukhala ngati kumuchepetsa Mtumiki. Mtumiki salla Allah alaih wasallam sanali wa madh’hab a ma imam amenewa, chifukwa ma imam onsewa ndi otsatira Mtumiki choncho Mtumiki sangakhalenso otsatira madh’hab ena ake pa anayiwa. Iye ndi mphunzitsi wamkulu pomwe awa ndi aphunzitsi ang’onoang’ono
Kodi ndikoyenera kutsatira Imaam mmodzi yekha?
Mutu uwu ndi wautali, koma in sha Allah ndiyesetsa kukamba mwachidule, ndikhulupilira titolapo kanthu.
Zili waajib kwa Msilamu kuphunzira tanthauzo la mau oti Laa ilaaha illa Allah Muhammadun Rasul Allah.
Laa ilaaha illa Allah kutanthauza kuti palibe OMUPEMBEDZA mu choonadi koma Allah yekha.
Muhammadun Rasul Allah kutanthauza kuti palibe OMUTSATIRA ku choonadi posakhala Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam
Choncho yemwe angabwere nkumati titsatire Imaam mmodzi yekha ndikusiya ma Imaam ena onsewo, kapena kuuza Ummah kuti udzitsatira zokamba za Aalim mmodzi yekha mwa omwe analipo kale kapena omwe alipo panopa, ameneyo ndi osokoneza, komanso osocheretsa mu Deen.
Ife ndife Asilamu, ndipo timapembedza Allah yekha komanso timatsatira Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam. Choncho titsatire Imaam aliyense yemwe akuphunzitsa chiphunzitso cha Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndipo tisatsatire yemwe akuphunzitsa zosemphana naye.
Kuitanira kapena kuwalalikira anthu kuti adzitsatira Imaam Shafi’i yekha, kapena Imaam Hanafi yekha etc, ndi kusokeretsa Ummah ndipo izi ndi zina mwa zisocheretso zomwe zinakhanzikika  mu Ummah uno.
Nchifukwa chaketu timamva ena akunena kuti awa ndi a gulu la Hanafi, awa ndi a Shafi … Ena amanena kuti
aah ine za ma imaamuzi sindimatsatira zimagawanitsa ummah, ndimapanga za Mtumiki basi. Izitu zimanenedwa malinga ndi kusokonezana komwe kumachitika pa nkhani ya ma Imaam amenewa. Ozindikirawo samafuna kutiwunikira osadziwafe.
Ma Imaam anayi amenewa ndi ma Imaam a Qur’an ndi Sunnah, amene anatithandiza kutiwongolera komanso kutiphunzitsa zomwe timachita pakali panopa mu deeniyi kuchokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam.
Zinanenedwa kwa Imaam Al Shafi’i kuti E iwe Abu Abdillah, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati zakutizakuti, nanga iwe ukutipo bwanji?
Imaam Al Shafi’i anakwiya koopsa ndipo anati: Subhaana Allah, ukundiona ngati ndachokera mutchalitchi (ndine m’busa)? ukutha kundiona ndi chi belt (cha ubusa)? ukundifunsa kuti Mtumiki anati…nanga iwe ukutipo bwanji? Ine ndingayankhulepo chani pamene Mtumiki swalla Allah alaih wasallam wayankhula?
Ndi zoonanso kuti Imaam Al Shafi’i anati: “ngati nkhani ili yoona, imeneyo ndi njira yanga”, komanso mmodzi wa iwo (ma Imaam anayi) ananena kuit: “Ndi zoletsedwa kwa munthu kuyankhula zomwe ife tayankhula mpaka atadziwa bwino bwino komwe ife tadzitenga”
Apatu kuthanthauza kuti eni akewo anatisambira mmanja ponena kuti iwo samangokamba za mmitu mwawo, koma amakamba zokhazo zomwe zikugwirizana ndi chiphunzitso cha Mtumiki.
Choncho yemwe akunena kuti ine ndimatsatira Imaam Shafi’i pa swala timaika manja chotere, akuyenera asanatenge zimenezo afufuze kaye kuti Imaam Shafi anadzitenga kuti. Osati kungoti Imaam Shafi anati chonchi, ayi.
Deeniyi nkhokwe zake ndi ziwiri (Qur’an ndi Sunnah) koma madengu ngambirimbiri.
Tikuyenera kuwatsatira ma Imaam amenewa mopanda kupyola muyeso chifukwa ena anagawa pakati pa Asilamu kuzera mma Imaam amenewa, nchifukwa chake ena amanena kuti sindingatsatire Imaam aliyense chifukwa zimagawanitsa Chisilamu, kukhala ngati deeniyi angaimve potenga direct kuchokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam.
Ena anafika level yomasalana mmaikomu, chifukwa chowadziwa kwambiri madh’hab molakwika.
Amafunsa kuti;
Kodi nkololedwa wa Hanafi kukwatira wa Shafi’i?, chifukwa choti a madh’hab a Hanafi amanena kuti yemwe wanena kuti: ine ndi Mu’min in sha Allah, ndiye kuti wakaikira imaan yake, choncho yemwe wakaikira iman yake ndiye kuti ndi kaafir Pomwe a Shafi amanena kuti ndi zololedwa munthu kunena kuti ndine Mu’min in sha Allah, podziwa kuti Allah ndamene amalowetsa Imaan yako mumtima.
Pachifukwa ichi, anthu ena otsatira Hanafi amanena kuti sangakwatire mkazi wa Madh’hab a Shafi chifukwa ndi ma Kafir – Subhana Allah – mpaka kutulutsana Chisilamu!!?
Imaam Al Shafi’i komanso Imaam Abu Hanifah ndi otalikitsidwa ku zonse zomwe amakhulupilira anthu oterowo.