Nkhani ya ma Imam imavuta kuimvetsa chifukwa choti ma Imam anapezeka pambuyo pa ma Swahaba, ndiye ambiri omwe sakudziwa amaona ngati ma Imam anayi amenewa ndi amene amagawa Asilamu. Koma zoona zenizeni si choncho.

Chisilamuchi kuti chimveke bwinobwino kwa ife, timayenera kuchiphunzira kwa ma Sheikh, ma Ustaaz, ma Imam, ma Ulamaa, ma Mufti. Ndipo timatenga zomwe akutiphunzitsazo. Koma sizimapezeka kuti amene anaphunzira kwa Sheikh Muhammad apanga deen yawo, amene anaphunzira kwa Sheikh Mahmud apanga deen yawo, amene anaphunzira kwa Sheikh Abdullah apanga deen yawo, ayi ndithu.
Koma kuti onse amati tinaphunzira kwa sheikh wakuti wakuti ndipo anati zakuti zakuti. Ziphunzitso za aphunzitsi onsewa zimakhala zochokera kwa Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam. Ndipo amene amaphunzitsa zosemphana ndi Sunnah, ameneyo ndi osokoneza. Ndi amene amagawa Asilamu aja

Nchimodzimodzi , ma Imam 4 (Muhammad bun Idrisa Al Shafi, Malik bun Anas, Ahmad bun Hanbali, Abu Hanifah Al Nu’man bun Thabit), onsewa anali aziphunzitsi akuluakulu omwe anaphunzitsa Sunnah ya Mtumiki kwa anthu dziko lonse. ndipo ma Imam onse amene abwera pambuyo pawo amaphunzitsa deeniyi kuzera mu zomwe anali kuphunzitsa iwowa., kuchokera mu Sunnah za Mtumiki salla Allah alaih wasallam.
Madrasa a Imam aliyense amatengedwa ngati njira yodziwira momwe mtumiki ankapangira Deen. Nchifukwa chake madrasawa amatchedwa *Madh’hab*

Imam aliyense akhonza kutsatidwa. Ndipo ngati tingapeze zomwe imam wina akunena koma zosemphana ndi Sunnah, zimenezo tisadzitsatire, monga mmene ananenera imam Shafi kuti _mukaona zosemphana ndi Mtumiki mu madh’hab anga, musadzitenge, mutenge za mtumiki_, kusonyeza kuti iwo amaphunzitsa za Mtumiki, alibe kuyendera maganizo awo.
Ma Imam onse anayi ndi Ahlu  Sunnah (amaphunzitsa njiira ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam)
Nkhani ya ma Imam ndi yaitali pofuna kuti munthu yemwe sakudziwapo kanthu ayimvesetse, chifukwa ma imam amenewa amapangidwa attach chifukwa cha kusazindikira kuti ali ndi position yanji mu deen.
In sha Allah tidzitenga mutu umodzi umodzi, ndipo tiyesetsa malinga ndi mmene Allah atidalitsire ndi nthawi yake

Tingowalongosola pang’ono ma Imam amenewa kuti ndi ndani, nanga u Imam wawo unali nthawi yanji mu nyengo ya Chisilamuyi?

Ma imam alipo ambirimbiri osati anayi okhawa. Komanso aliko a magulu osiyanasiyana monga a chi Shia (alipo 12) komanso ena.
Omwe tidzikambirana ifewa ndi ma Imam athu, ma imam a SUNNAH.
Ma IMAM amenewa anagwirizana mu ziphunzitso zawo kumbali yaikulu ya Deen ya Chisilamu, koma anasemphana mu zochepa kwambiri zimene zimatha kupezeka solution yake mosavuta, poti zonsezo aliyense ankayendera ma umboni ochokera kwa Mtumiki kuzera mma swahaba. Choncho chifukwa cha timapoints tomwe anasemphanano ndi timene tinachitiksa kuti aliyense akhale ndi madh’hab ake malinga malongosoledwe ake. koma zonsezo zikubwelera ku Qur’an ndi Sunnah.
Tipeza mwachitsanzo nkhani ya kuika manja pamimba poswali, ma imam anakamba zosiyanasiyana, koma sizikutanthauza kuti ena amanama kapena samadziwa,,,zomwe zimachititsa kusemphanaku ndi malinga ndi mmene nkhani inafikira kuchokera kwa Mtumiki poti salla Allah alaih wasallam poti amatha kuchita chinthu chimodzi munjira zingapo. ndiye munthu amatha kusankha kuti atenga!! Eziti, koma zonsezo ndi zololedwa.

Imam Abu Hanifah Al Nu’man bun Thabit
Anabadwa mchaka cha 80 AH (699AC) ndipo anamwalira 150 AH (767 AC)
Madh’hab: Hanafiyy

Imam Malik bun Anas
Anabadwa mchaka cha 93 AH (715 AC) ndipo anamwalira 179 AH (769 AC)
Madh’hab: Malikiyy

Imam muhammad bun Idrisa Al Shafi’i
Anabadwa mchaka cha 150 AH (766 AC) ndipo anamwalira mchaka cha 204 AH (820 AC)
Madh’hab: Al Shafi’iyy

Imam Ahmad bun Hanbal
A
nabadwa mchaka cha 164 AH (780 AC) ndipo anamwalira 241 AH (855 AC)
Madh’hab: Al Hanbaliyy

Imam Abu Hanifah ndi imam oyambilira mwa onsewo, ndipo anali Taabi’iy (yemwe anadza pambuyo pa ma Swahaba), anakumana ndi ma Swahaba a Mtumiki ambirimbiri ndithu. Koma sanakumane ndi ma imam ena atatu omwe anadza pambuyo pakewo.

Imam Al Shafi’i yemwe ndi wachitatu 3, anakumana ndi ma Imam anzake onsewo kupatula Abu Hanifah yemwe ndi wakale. (mupanga masamu kuzera mu ndandanda wawo mumtundamo).

Imam Al Shafi’i anaphunzira kwa Imam Malik ndipo anali mphunzitsi wa Imam Ahmad bun Hanbali

Kodi nanga ma Imam amenewa kwawo nkuti? Ndi aku Makkah kapena Madina kapena ku Egypt
Imam Abu Hanifa anabadwira ku Kufa ku Iraq ndipo anamwalilira ku Baghdad ku Iraq komweko
Imam Malik bun Anas anabadwira ku Madina awaahku udiraipoanmalilira ku Madinah komweko
Imam Al Shafi’i anabadwira ku Gaza, Palestine ndipo anamwalilira ku Fustat ku Egypt
Imam Hanbal anabadwira ku Baghdad ku iraq ndipo anamwalilira ku Baghdad komweko

Kodi Njira zinayi zimenezi ndi zabwino kutsatira? nanga zinayamba kupezeka liti mu Chisilamumu?
Madh’hab anayi amenewa (Ahmadiyya/Hanbaliyya – Shafi’iyya – Malikiyya – Hanafiyya), ndi madh’hab odziwika, amene anayamba kudziwika mma 2nd century pambuyo pa msamuko, monga madh’hab a Hanafiyya ndi Malikiyya, pomwe Shafi’iyya ndi Hanbaliyya anayamba kufala pambuyo pake mu 3rd century, ndipo ma Imam ake ndi abwino ndithu komanso ali mu chiwongoko ndi choonadi. Anthu amenew ndi ma Imam a chiwongoko komanso ma Ulamaa abwino. Koma sizikutanthauza kuti samalakwitsa, chifukwa iwowo si atumiki kapena angelo, koma ndi anthu ngati ife tomwe kungosiyana kuti anaphunzira ndikulimbikira kwambiri pa ilm ya Deen. Choncho, wina aliyense ali ndi zofooka zake malinga ndi mmene anapezera maphunziro ake kuchokera mu Sunnah. Sizikutahthauza kuti anamaliza chilichonse mu Sunnah za Mtumiki salla Allah alaih wasallam popanda chosiya, koma anayesetsa moti mpaka anthu amawatsatira chifukwa cha chilungamo chawo, ndipo ena mwa otsatira ndi amene analemba mabuku a zokamba zawo komanso ma fatwa awo. Koma chifukwa choti sizimalephera kulakwitsa, ma Imam amenewa pali zina ndi zina zomwe sanadzipeze mma Sunnah a Mtumiki ndipo anayenera kupanga ijtihaad nkubweretsa zoyenera malinga ndi mmene zina ziliri.

Kodi Mtumiki anali wa Madh’hab anji
Ena ponyoza ma Imam amenewa, amakonda kufunsa funso limeneli. Koma kwa munthu oganiza sangafunse chifukwa kukhala ngati kumuchepetsa Mtumiki. Mtumiki salla Allah alaih wasallam sanali wa madh’hab a ma imam amenewa, chifukwa ma imam onsewa ndi otsatira Mtumiki choncho Mtumiki sangakhalenso otsatira madh’hab ena ake pa anayiwa. Iye ndi mphunzitsi wamkulu pomwe awa ndi aphunzitsi ang’onoang’ono

Kodi ndikoyenera kutsatira Imam mmodzi yekha?
Mutu uwu ndi wautali, koma in sha Allah ndiyesetsa kukamba mwachidule, ndikhulupilira titolapo kanthu.

Zili waajib kwa Msilamu kuphunzira tanthauzo la mau oti Laa ilaaha illa Allah Muhammadun Rasul Allah
Laa ilaaha illa Allah kutanthauza kuti palibe OMUPEMBEDZA mu choonadi koma Allah yekha…
Muhammadun Rasul Allah kutanthauza kuti palibe OMUTSATIRA ku choonadi posakhala Mtumiki Muhammad

Choncho yemwe angabwere nkumati titsatire Imam mmodzi yekha ndikusiya ma Imam ena onsewo, kapena kuuza Ummah kuti udzitsatira zokamba za Aalim mmodzi yekha mwa omwe analipo kale kapena omwe alipo panopa, ameneyo ndi osokoneza, komanso osocheretsa mu Deen.

Ife ndife Asilamu, ndipo timapembedza Allah yekha komanso timatsatira Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam. Choncho titsatire Imam aliyense yemwe akuphunzitsa chiphunzitso cha Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndipo tisatsatire yemwe akuphunzitsa zosemphana naye.

Choncho kuitanira kapena kuwalalikira anthu kuti adzitsatira Imam Shafi’i yekha, kapena Imam Hanafi yekha etc, ndi kusokeretsa Umma ndipo izi ndi zina mwa zisocheretso zomwe zinakhanzikika  mu Ummah uno.

Ma Imam anayi amenewa ndi ma Imam a Qur’an ndi Sunnah, amene anantithandiza kutiwongolera komanso kutiphunzitsa zomwe timachita pakali panopa mu deeniyi kuchokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam.
Zinanenedwa kwa Imam Al Shafi’i kuti E iwe Abu Abdillah, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati zakutizakuti, nanga iwe ukutipo bwanji? Imam Al Shafi’i anakwiya koopsa ndipo anati: Subhaana Allah, ukundiona ngati ndachokera mutchalitchi (ndine m’busa)? ukutha kundiona ndi chi belt (cha umbusa)? ukundifunsa kuti Mtumiki anati…nanga iwe ukutipo bwanji? Ine ndingayanhkulepo chani pamene Mtumiki swalla Allah alaih wasallam wayankhula?. Ndi zoonanso kuti Imam Al Shafi’i anati: “ngati nkhani ili yoona, imeneyo ndi njira yanga”, komanso mmodzi wa iwo (ma Imam anayi) ananena kuit: “Ndi zoletsedwa kwa munthu kuyankhula zomwe ife tayankhula mpaka atadziwa bwino bwino komwe ife tadzitenga”.

Apatu kuthanthauza kuti eni akewo anatisambira mmanja ponena kuti iwo samangokamba za mmitu mwawo, koma amakamba zokhazo zomwe zikugwirizana ndi chiphunzitso cha Mtumiki. Choncho yemwe akunena kuti ine ndimatsatira Imam Shafi’i pa swala timaika manja chotere, akuyenera asanatenge zimenezo afufuze kaye kuti Imam Shafi anadzitenga kuti. Osati kungoti Imam Shafi anati chonchi, ayi.

Tikuyenera kuwatsatira ma Imam amenewa mopanda kupyola muyeso chifukwa ena anagawa pakati pa Asilamu kuzera mu ma Imam amenewa ndipo ena amanena kuti sindingatsatire imam aliyense chifukwa zimagawanitsa Chisilamu, kukhala ngati deeniyi angaimve potenga direct kuchokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam.

Ena anafika level yomasalana mmaikomu, chifukwa chowadziwa kwambiri madh’hab, molakwika. Amanena kuti; Kodi nkololedwa wa Hanafi kukwatira wa Shafi’i?, chifukwa choti a madh’hab a Hanafi amanena kuti yemwe wanena kuti: ine ndi Mu’min in sha Allah, ndiye kuti wakaikira imaan yake, choncho yemwe wakaikira iman yake ndiye kuti ndi kaafir. Pomwe a Shafi amanena kuti ndi zololedwa munthu kunena kuti ndine Mu’min in sha Allah, podziwa kuti Allah ndamene amalowetsa Iman yako mumtima.
Pachifukwa ichi, anthu ena otsatira Hanafi amanena kuti sangakwatire mkazi wa Madh’hab a Shafi chifukwa ndi ma Kafir – Subhana Allah – mpaka kutulutsana Chisilamu!!? Imam Al Shafi’i komanso Imam Abu Hanifah ndi otalikitsidwa ku zonse zomwe amakhulupilira anthu oterowo.

Msilamu aliyense okhulupilira akuyenera kutsatira Qur’an ndi Sunnah. Anthu omwe akuwongolera ku choonadi amatha kulondola kapena kulakwitsa, koma Qur’an ndi Sunnah sizimalakwitsa, choncho potsatira ma Imam tidzionesetsa kuti zomwe tikutsatirazo zikuchokera mu Qur’an kapena Sunnah.
Choncho ngati tingamatsatire Imam, ngati walakwitsa tisamutukwane, kapena kunyoza chiphunzitso chakecho, koma mmalo mwake tiyeni tifufuze zoona zake chifukwa nawonso anachita kufufuza ndi mmene anadzipezera.
Palibe munthu yemwe angatsatidwe nkumatenga chilichonse mu ziphunzitso zake popanda kupatula, posakhala Mtumiki salla Allah alaih wasallam.

Tsopano zomwe maumboni ake sitingawapeze mu Sunnah kapena mu Qur’an, tikuyenera kukutsatira yemwe tatsimikiza kuti ali ndi kuzindikira kom,anso ndi owopa Allah ndipo ali ndi ilm yodalirika, monga ma imam anayi amenewa.
Choncho ophunzira sakuletsedwa kuyezamira ku mas’ala omwe sizikupezeka mu Qur’an ndi Sunnah directly, koma akupezeka ndi ma imam akuluakulu mwa iwo. Al Mazni rahimahu Allah anali mmodzi wa ophunzira a Imam Al Shafi’i rahimahu Allah, ndipo ankayanhkula kuti: zikanakhala zololedwa kwa munthu kutengera munthu, ine sindikanatengera wina kupatula Al Shafi’i, chonsechotu Al Mazni anali ophunzira wa Imam Shafi’i koma sanakakamire madh’hab amodzi a mphuzitsi wake okha.