Zinthu Zofunikira Kuti Yemwe Akufuna Kuphunzira Ayambilire Kuchita Kuti Adziteteze

Phunziro limeneli likuchokera pa mutu woti

“Ahlu Ssunnati wa ‘alaamaatihim”

Sheikh Rabieu bun Haadi Al Madkhali

Kufunafuna maphunziro mu deen ndi lamulo kwa wina aliyense, mwamuna, mkazi, mwana ngakhale mkulu. Palibe yemwe amasangalatsidwa kukhala mbuli pa zomwe anzake akudziwa. Tsopanotu kudziwa za deen sikutengera kuti ukusangalatsidwa kapena ayi, koma ndi faradh, chikakamizo kwa aliyense yemwe ali Msilamu kuphunzira. Palibe zoti ine sinnaphunzire ndili mwana ndiye panopa sindikwanitsa, ayi ndithu. Uphunzire mpaka pamene idzakufikire imfa, chifukwa maphunziro ali ngati nyanja, sungawamalize, alibe malire, choncho usadziikire malire kapena kudzitchula kuti ndamaliza maphunziro a deen.

Tsopano poti munthu amene ali munjira ya kusakasaka maphunziro a deen amakumana ndi zambiri zomugwetsera ku uchimo, komanso amatha kukumana ndi mtundu wa maphunziro omwe iyeyo sadziwa kuti ndi osochera, nkumangophunzira moyo wake wonse osadziwa kuti akuphunzira za kuseli; zokamuponya kumoto akadzigwiritsa ntchito, ma ulamaa anaika ndondomeko yothandiza yomwe munthu akuyenera kutsata kuti pena imuthandize akamafuna kuyamba kuphunzira deen, kupewa zovuta zomwe akanamakumana nazo pophunzira, izitu ndi zitetezo kwa iye.

Choyamba munthu asanayambe kufunafuna maphunziro mu deen, akuyenera kukhala ndi niyyah yoyera, asonkhanitse imaan mumtima mwake komanso kudzipereka ndi kuopa Allah.

Ayenera kuyamba ndi kuphunzira zinthu zomwe Allah Ta’ala wamulamula iye kuti akuyenera kukhala nazo nthawi zonse, monga Chikhulupiliro  Choyera (Al Aqeedah Al Khaaliswah); amudziwe Allah Tabaaraka wa Ta’la mmaina ake ndi mbiri zake, makamaka nkhani ya kukhanzikika kwake ndi ukulu wake (الاستواء والعلو) komanso zina ndi zina. Aphunzirenso kutanthauza kwa ma shahaada awiri omwe ndi

 (شهادة ألا إله إلا الله و شهادة أن محمدا رسول الله)

Shahaadatu allaa ilaaha illa Allah wa shahaadatu anna Muhammadan Rasulul Allah, kuti pasapezeke kusokonezeka pakati pawo. Ndipo adziwe malamulo ake a ma shahaada amenewa ndi zomwe zimaononga shahaada.

Kenako aphunzire Qur’an ndipo ngati angakwanitse kuloweza, atero poyambira ma surah ang’onoang’ono.

Aphunzire ma sunnah monga ma Hadith, ndipo ayambe afupiafupi nkumakwera, monga kuchokera mu Bulughul Maraam kapena ‘Umdatul Ahkaam.

Aloweze kuchokera mu Tawheed mabuku monga Al Usoolu Tthalaathah, kenako Kashfu Sshubuhaati, kenako Kitaabu Ttawheed…

Awerengenso za Tawheedil Asmaai wa Sswifaati kuchokera mu mabuku monga Al Waseet; kameneka ndi kabuku kakang’ono, ndipo ndikosavuta kuwerenga ndikuloweza mmasiku ochepa in sha Allah.

Choncho ngati angafune kupitiriza kufunafuna maphunziro, pamenepo khomo ndilotsekuka kwa iye ndipo ayamba kuphunzirano mabuku akuluakulu monga a Tafsir, ma Hadith otambasulidwa (mashrooha). Nahw (Malamulo a chilankhulo).

Koma ngati angafune kuti angophunzira zomwe zili zofunikira kwambiri pamoyo wake, aphunzire zofunikira pa swalaat, zoononga swalaat, ncholinga choti asagwere mu zoonongazo. Adziwenso Zakaat, kuti ngati ali ndi chuma adziwe mlingo wa zakaat komanso zonse zofunikira. Adziwenso Hajj ngati ali mwa omwe angakwanitse kupanga Hajj; adziwe mapangidwe a Hajj ndi zoononga Hajj komanso zina zonse.

Amenewo ndiye ma faraaidh ‘ain (zokakamizidwa mwa iye yekha), kenako adziwe ma faraaidh kifaayah (ma ibaada omwe amagwera kwa ena omwe sanachite nawo ibaadayo).

Zimenezi ndiye zomwe zili zofunikira kwambiri kwa twaalibil ‘ilm. Twaalibul ‘ilm sangakhale pachitetezo cha maphunziro ake ku kugwera mu shirk ngati sanadziwisitse khomo limeneli, akuyenera kudziteteza kwa oitanira ku shirk komanso mafitna omwe achuluka masiku ano, asanalowe mu kufunafuna maphunziro.

Wassalaam alaiku warahmatullah wabarakaatuh