Dowload PDF (direct link)

Listen/Download MP3

Twawaaf (Tawaf) ndi liwu la chinenero cha chiarab lomwe limatanthauza kuzungulira, ndipo malingana ndi malamulo a Hajj mchisilamu, liwuli limatanthauza kuzungulira nyumba yolemekezeka ya Ka’bah.

Tawaf  ili m’magulu atatu:

  1. Tawaf yapofika: Imeneyi ndi Tawaf yomwe anthu okapanga Hajj amapanga akangofika kumene ku Makkah.
  2. Tawaf ya gulu: Imeneyi ndi Tawaf yomwe iwo amapanga pambuyo pa kupereka nsembe popha zinyama.
  3. Tawaf ya pobwelera: Imeneyi ndi Tawaf yomwe anthu opanga Hajj amapanga panthawi yonyamuka ku Makka pobwelera kwawo.

Iwo akamapanga Tawaf (Kuzungulira Ka’bah), amakhala akudziyeretsa wokha pokalowa nyumba ya Ka’bah ndikuzungulira kasanu ndi kawiri (7) kuyambira pa mwala wakuda poyisiya Ka’bah chakumbali ya kumanzere. Ndipo pambuyo pa kuzungulira kulikonse, mwala wakuda umapsyopsyonedwa, kapena kugwiridwa kapena pongolozera mongav ngati ukuwulawira ngati kuli kotheka.

Akazi panthawi ya matenda awo akumwezi samaloledwa kupanga Tawaf. Ndipo amene ali oyeretsedwa ku matenda amenewa, akuyenera kupanga Tawaf. Uku kumayimira kulemekeza malo a Ibrahim omwe anatchulidwa mu Qur’an yolemekezeka motere:

“Ndipo (kumbukiraninso nkhani iye) pomwe tinayipanga nyumba (ya Ka’bah) kuti pakhale pamalo pobwelerapo anthu (poyendera anthu) ndikukhalanso malo a chitetezo. Ndikuti mupachite kukhala popemphelera swala pamalo pomwe Ibrahim adali kuyimilira pomanga nyumbayo . Ndipo tidamulamula Ibrahim ndi Ismail kuti iyeretseni nyumba yanga chifukwa cha oyizungulira (pochita Tawaf ) ndi amene akuchita m’bindikiro, ndichifukwa cha amene akuwerama ndi kulambira (kuswali m’menemo). (2:125).

Kenako Anthu amayima moyiyang’ana Ka’bah, poyima pakati pa iyo ndi pamalo pa Ibrahim pomwe amapemphera maraka’at awiri.

Kuyenda Ndawala Pakati Pa Saffa Ndi Marwah

Chinthu chinanso chomwe chimachitika popanga Hajj kapena Umrah ndiko kuyenda ndawala pakati pa mapiri awiri a Saffaa ndi Marwah.  Iye ayenera kukwera paphiri la Saffa  ndikuyima moyiyang’ana Ka’bah ndipo kenako ayenera kukweza manja ake pomuthokoza ndi kumuyamika Mulungu. Kenako amayenda pachipata chaching’ono  kufikira atakafika pa chigwa cha pakati pa Saffa ndi Marwah komwe amayendano mwandawala komanso mofulumira. Iye akafika paphiri la Marwa, amakwera phirilo ndikuchita chimodzimodzi monga momwe anachitira pa phiri la Safa. Ndipo kuyenda mwa ndawala pakati pa mapiri awiriwa kuyenera kumachitika kasanu ndi kawiri (7) kuyambira pa phiri la Safa kukamalizira pa phiri la Marwah.

Monga momwe tafotokozera kale kuti kuthamanga komwe kumachitika pakati pa phiri la Safa ndi Marwah chimakhala chikumbutso chomukumbulikira Hajar, mayi wake wa Ismail komanso mkazi wa Mneneri Ibrahim yemwe anali kuzungulira pamalowa pofunafuna madzi a mwana wake Ismail.

Ndizofunikira kwambiri kwa onse opanga Hajj akafika pa phiri la Safa kuwerenga mawu a Allah omwe akupezeka mu Qur’an yolemekezeka motere:

“Ndithudi Safaa ndi Marwah (mapiri awiri omwe omwe pakati pake pamachitika pemphero loyenda ndawala) ndi zizindikiro zolemekezera chipembedzo cha Mulungu. Choncho amene akukachita mapemphero kunyumbayo kapena kuchita Umrah, sikulakwa kwa iye kuzungulira pamenepo (pakati pa mapiri amenewo). Ndipo amene achite chabwino modzipeleka adzalipidwa. Ndithudi Mulungu ngothokoza, ngodziwa. (2:158)

Ndipo miyambo yonse ya Umrah imatsirizika pambuyo pa kumaliza kuyenda ndawala pakati pa Safaa ndi Marwah.

Koma kwa amene anatsimikiza zopanga Hajj yokha (Ifrad) kapena kulumikiza Hajj ndi Umrah (Qiran) ayenera kukhala muzovala zawo za Ihram mpaka atamaliza miyambo yonse ya Hajj.

Koma kwa awo amene anatsimikiza za kupanga Umrah payokha popimira ndikudzayilumikiza ndi miyambo ya Hajj (Tamatu’u) pa tsiku la chisanu ndi chitatu (8) la mwezi wa Dhul-hijjah, akhoza kusiya zovala zawo za Ihram koma ayenera kuzinga chinyama chomwe chimaperekedwa kwa osauka.  Ngati sanapeze choti ndikuzinga, ayenera kusala masiku atatu ali ku Hajj komweko ndipo ayeneranso kudzasala masiku asanu ndi awiri akadzabwelera kwawo. Ndipo mtundu wa Hajj wa Tamattu’u ndi opambana kwambiri poyerekeza ndi Ifrad komanso Qiran chifukwa choti mtundu wa Hajj umenewu ndi osavuta komanso Mtumiki salla Allah alaih wasallam anawuyamikira.

Kuchoka Ku Makkah Kupita Ku Minah

Patsiku lachisanu ndi chitatu (8) la mwezi wa Dhul-Hijjah, onse opanga Hajj ayenera kuchoka ku Makka ndi kupita ku Mina. Apa ndi pomwe munthu amene anatsimikiza za Hajj ya Tamatu’u amavalanso zovala zake za Ihram ndi kuzilumikiza ndi onse opanga Hajj. Masana onse ayenera kupezeka pa Mina, malo omwe ali pa mtunda wa Makilomita asanu ndi anayi kuchokera ku Makka. Kumeneko iwo amapemphera mapemphero awo a Dhuhr, Asr, Maghrib komanso Isha ndipo pamapeto pake amagona tsiku limelo pamalo amenewa.

Kuyima Paphiri La Arafah

Patsiku la chisanu ndi chinayi la mwezi wa Dhul-Hijjah, Asilamu opanga Hajj amapemphera pemphero lawo lam’mawa (Fajr) pa Mina, kenako amadikilira kutuluka kwa dzuwa. Kenako iwo amanyamuka kupita ku phiri la Arafah akulankhula mokweza mawu onena kuti Allah Akbar omwe amatanthauza kuti Mulungu ndi wamkulu. Kumeneko, iwo amapemphera pemphero la Dhuhr molumikiza ndi pemphero la Asr panthawi ya pemphero la Dhuhr.

Kuyima pa phiri la Arafah ndi umodzi mwa miyambo yotamandika komanso yofunikira kwambiri yomwe imachitika nthawi ya Hajj. Munthu osiya kupanga mwambo umenewu sanganene kuti wapanga Hajj. Ngati anthu ena utawadutsa mwambowu chifukwa cha zovuta zina mwina chifukwa cha kuchulukana kwa anthu, ayenera kupanga madzulo angakhale m’pakana kum’banda kucha wa tsiku lachikhumi (10) lamwezi wa Dhul-Hijja.

Pokamba za ubwino wa kuyima pa phiri la Arafah, Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti:

“Palibe Hajj kwa munthu ngati sanayime pa phiri la Arafah”.

 

Kugona Usiku Pa Muzdalfah

Pambuyo pa kuyima paphiri la Arafa, Asilamu onse amanyamuka tsiku lomwelo kupita ku Muzdahlfah komwe amakafikako chakumadzulo dzuwa lisanalowe. Muzdalfah ndi malo omwe amapezeka pakati pa Arafah ndi Mina. Mbendera zomwe zimasonyeza malire a malo olemekezeka, zimabzalidwa. Mapemphero a Maghrib komanso Isha amapempheredwa mophatikiza.

Iwo amakhala pa Muzdalfah m’pakana usiku kufikira nthawi ya pemphero la m’mawa wa pa 10 Dhul-Hijjah. Munthawi yonse yomwe iwo amakhala ali pa Muzdalfah, amakhala akumuyamika Mulungu, kuwerenga bukhu lolemekezeka la Qur’an pamalo a chizindikiro omwe Allah anawatchula m’bukhu lake lolemekezeka la Qur’an  motere:

“Ndipo mukabwelera kuchoka ku Arafah, Tamandani Mulungu pamalo otchedwa Mash’ar Haram (Muzdalfah). Ndipo mukumbukireni monga momwe adakutsogolerani. Ndithudi kale mudali mwaosochera. (2:198)”

Pambuyo pa kupemphera pemphero lakum’bandakucha (Fajr) pa 10 Dhul-Hijjah,  onse amachoka pa Muzdalfah ndi kupita ku Mina uku atatenga timiyala ting’onoting’ono tomwe amakatigwiritsira ntchito pogenda zipilala za Aqaba zomwe ziri pa Mina. Munthu amene sangathe kotero chifukwa cha matenda kapena kukalamba, ayenera kupeza munthu oti akachite mwambo umenewu m’malo mwa iye.

Nsembe

Pambuyo pa kugenda zipilala zimenezi, iwo amayamba kupeleka nsembe zawo pozinga zinyama. Mazanamazana a nkhosa, mbuzi, komanso ngamila zimakhala zitasungidwa kale ndicholinga choti ziperekedwe nsembe. Ndipo mwala waukulu omwe uli cha kumadzulo kwa chigwa cha Mina unakhazikitsidwa ngati malo chifukwa cha mwambo umenewu.

Patsiku limeneli lomwe limakhala pa 10 mwezi wa Dhul-Hijjah, Asilamu dziko lonse lapansi amapeleka nsembe zawo popha zinyama zosiyanasiyana ndiponso amasangalalira limodzi chisangalalo cha kupeleka nsembe. Ndipo munthu amene anatsimikiza za Hajj ya Tamattu’u samapeleka nsembe pokhapokha ngati atapanga ndawala pa Safaa ndi Marwah.

Tawaful-Ifadah (Tawaf Yagulu)

Onse opanga Hajj ayenera kupanga Tawaf yapagulu komwe kuli kuzungulira limodzi pagulu pa 10 Dhul-Hijjah pambuyo pa kumeta tsitsi ndi kuwenga zikhadabo. Ndipo Tawaf imeneyi ikhoza kuchitika m’masiku atatu otsatira pambuyo pa tsiku lopeleka nsembe.

Pambuyo pa Tawaf imeneyi, iwo akhoza kusiya zovala zawo za Ihram ndikupitiliza kuyamika komanso kumuyeretsa Allah.

Tiyenera kudziwa kuti Munthu amene anatsimikiza za kupanga Hajj ya Tamattu’u, sangapange Ihlal (kumuyeretsa Allah ndi kumukuza) ngati sanayende nawo ndawala pa Safaa ndi Marwah kachiwiri. Iye ayenera kudziwa kuti ndawala yoyamba yomwe iye amayenda imakhala ya Hajj.

Pambuyo pa kumuyeretsa komanso kumukuza ndi kumutamanda Mulungu, onse ayenera kubwelera ku Mina ndi cholinga choti akamalize masiku atatu otsatira pambuyo pa tsiku lopeleka nsembe ndipo m’masiku amenewa iwo ayenera kupitiliza kugenda timiyala ting’onotig’ono kuyambira masana mpakana kulowa kwa dzuwa.

Tawaful-Wadaa

Gawo lotsiriza la mwambo wa Hajj ndi Tawaful –Wadaa (Kuzungulira kolawira). Malingana ndi Hadith’ yomwe anayilandira Ibn Abbas, Mtumiki salla Allah alaih wasallam analamula kuti anthu opanga Hajj omwe sinzika za M’makka ayenera kuzungulira komwe kumasonyeza kulawirana asananyamuke ku Makkah kubwelera kwawo.

Kukayendera Manda A Mtumiki salla Allah alaih wasallam

Mwambo otsirizira kwambiri pa miyambo ya Hajj ndiko malinga ndi malamulo ndi oti onse opanga Hajj ayenera kupita ku Madina kukayendera manda a Mtumiki wathu Muhammad salla Allah alaih wasallam. Panthawi yomwe iwo akulowa munzinda wa Mumzikiti wa Mtumiki ku Madina, ayenera kutchula china chilichonse chomwe iwo akuchidziwa mu zabwino za ubwino komanso kufunikira kwa Mtumiki wathu Mhammad salla Allah alaih wasallam komanso ayenera kupempha chiwongoko kwa iye pa umoyo wake wauzimu.

Pambuyo pa kulowa mumzikiti wa Mtumiki salla Allah alaih wasallam, iwo ayenera kupemphera Maraka’at awiri kenako ndi kupita ku manda a Mtumiki komwe amakanena mawu awa:

Mtendere ukhale pa inu, Mtumiki wa Allah, Ndikuchitira umboni kuti palibe wina oyenera kupembedzedwa mwachowonadi kupatula Allah, ndikuti inu ndi kapolo komanso Mtumiki wa Allah.

Komanso ndikofunikira kwambiri kwa iwo kutembenukira chakum’mawa ndi cholinga chofuna kupeleka ulemu kwa Abubakar komanso manda a Mlowa m’malo wa Mtumiki pambyo pa Abubakar yemwe ndi Umar radhia Allah anhu.

Ubwino ndi Kufunikira Kwa Hajj