Funso: 

Ena chifukwa cha kuopa kukhala osakwatira kapena osakwatiwa, mapeto ake amakwatira munjira yosakhala bwino kapenanso kukwatira mkazi/mwamuna yemwe amanena kuti “zimenezo (myambo ya Chisilamu) ine sindingakwanitse” koma iwe ukumukwatirabe poopa kuti ukhala osakwatira, malinga ndi momwe dziko likuyendera pakudana ndi malamulo ndi myambo ya Chisilamu. Kodi pamenwpa utani?

Kutamandidwa konse nkwa Allah Mbuye wa zooengedwa zonse, Mtendere ndi madalitso zipite kwa Mtumiki wake. 

Ngati munthu akukana banja pa zifukwa zovomerezeka ndi Sharee’ah, mbali ina yaikulu adziyezamira mwa Iye pomupempha, osamangokana ayi, Allah amapatsa zabwino zochuluka kuposa zomwe amadzifuna munthu.

Koma akamangokana nkumati ndikufuna wa deen olongosoka, pomwe mwini wake samampempha Allah; sakupanga istikhaarah, asayembekezere kuti Allah adzangomutumiza mwamuna wabwino kwa iwe. Akuyenera kumagwira ntchito zabwino uku akumupempha Allah kuti amutalikitse ku amuna osayenera ndikumpatsa mwamuna oyenera.

Kugonja pamenepo nkukhala osakwatiwa ndi vuto lalikulunso, chifukwa wadzitsegulira njira ya shytwaan. Shaytwaan amakonda yemwe wataya mtima mwa Allah. Munthu sanganene kuti ine ndidzingokhala ndizidzisunga osakwatiwa/osakwatiwa, osapanga chirichonse ndi mwamuna, ndizovuta.

Zimene timanena nthawi zonse kuti munthu afufuze banja labwino, mkazi kapena wabwino,,, timatero chifukwa sikuti ndi onse omwe ali oipa. Alipo abwino omwe akusakasaka anthu abwinonso. Koma Allah amawayesa imaan yawo powatalikitsa pakati pawo osawakumanitsa mwachangu, kuti akakwanitsa kukumana alemekeze banja lawo.

Ndiye munthu kukwatira/kukwatiwa oipa chifukwa choti sakuwapeza abwinowo, kukhala kusankha koipa pakugonjera zoipazo, komanso kuchepekedwa kwa imaan. Ina mwa ma mistake omwe amapanga munthu mu umoyo wake  ndi kufulumira pa zinthu.

خُلِقَ الْإِنسَانُ مِنْ عَجَلٍ

“Munthu walengedwa ndi chikhalidwe chokonda zinthu (zake zonse) mwachangu.” Qur’an 21:37

Mmene Allah ananena kuti “amuna abwino ndi a akazi abwino…,” zikupereka umboni woti abwinowo alipo ndipo munthu akuyenera kuyezamira mwa Allah pofunafuna banja, osangochita ngati akufunafuna malaya pamsika, zoti akapanda kuwapeza basi angotola aliwonse. Banja ndi moyo … kusankha kwako ndi chiyambi cha mbali yaikulu ya moyo wako kkmanso mathero ako, mwina ku Jannah kapena kumoto.

Choncho Mtumiki wathu anatilangiza kuti tikafuna kukwatira tizitsogoza kuzindikira komanso kutha kwa Allah, kwambiri kuposa eniakefe, chifukwa iye ndi amene amadziwa zabwino zathu, ndipo ndi yekhayo yemwe angatizembetse ku zoipa…ponena kuti “Allahumma inni astakheeruka bi’ilmika wa astaqdiruka biqudratika…”


Chiyambi chabwino pa banja chimapangitsa banja kukhala losangalala ndi lolungama munjira ya Chisilamu. Choncho ndibwino kuvutika pofunafuna mkazi/mwamuna wabwino mukanyengo kochepa kuti ukhale naye mwaubwino mpaka imfa pa dziko pano, mudzakumanenso ku Jannah in shaa Allah. Kusiyana ndi kupanga zachangu popeza banja mukanthawi kochepa, ukalipeza ndikukhala moyo wako wonse wozunzika, kapena kumangisintha amuna/akazi chifukwa cha kupezeka zolakwika mu zinthu zomwe simunaziganizire mmene munkafunana (Deen).


Ndasankha kukhala osakwatira/wa moyo wanga onse


Anthu anaika freedom of choice pa kukwatira ndikukhala pa banja lovomerezeka, chifukwa cha kunyengeka ndi mfundo za azungu omwe  akulimbana ndi malamulo a Deen ya Chislamu, omwe amatsutsa kalikonse ponena kuti Chisilamu chimapondereza ufulu wa munthu.Zimenezi zimapangitsa Asilamu omwe ali ofooka mu imaan ndi maphunziro akaganizira za kavuto kakang’ono mmabanja a anzawo, amangobwera ndi maganizo oti basi adzingokhala sadzakwatira mpaka kale. Ndiye kuli mabungwe ena omwe amalimbikitsa khalidwe limeneli powalimbikitsa omwe sanakwatire njira zochitira zinaa, zomwe zimamutalikitsira munthu khumbo la kukhala pabanja poti amati zomwe angamadzipeze m’banjamo akudzipeza munjira ina, “ndipo banja ndi mavuto okhaokha bola ndizingoyendera yomweyi”, amatero.


Tidziwe kuti kukwatira ndi imodzi mwa ibaada mChisilamu. Kukwatira ndi lamulo la Chisilamu ndipo phindu lake likubwelera ku society komanso mbali yaikulu kwa okwatira, komanso pomakhala ibaada, Allah Ta’ala amasangalala nawo anthuwo.


Kodi ibaada ya kukwatira ikuchokera pati?


Kukwatira ndi Sunnah mmasunnah osayenera kuwasiya.Sunnah ndi njira ya Mtumiki yochitira zinthu yomwe timayenera kutsatira. Tsopano pali Sunnah zomwe Mtumiki anali kuchita nthawi zina, ndipo nthawi zina sankachita; zimenezo zimatchedwa ghair muakkada (zosasindikizidwa) zoti ukhonza kuchita kapena osachita ngati pali chokuletsa kutero, posakhala kunyozera chabe. Pali Sunnah zomwe Mtumiki sankazisiya mmoyo mwake, komanso anazilamula kuti tidzichita; zimenezo ndi muakkada (zosindikizidwa) zomwe sitikuyenera kudzisiya popanda chifukwa cheninechi chovomerezeka. Imodzi mwa sunnah mauakkada zimenezi ndiko kukwatira. Iyitu ndi sunnah ya Aneneri onse.


Tsiku lina pamene anthu atatu anadza kwa Mtumiki kudzafunsa za ibaada, anali kutchula mmodzimmodzi ibaada yomwe amalimbikira, ndipo mmodzi wa iwo anati: Ine ndimaswali usiku wonse sindimagona. Wina anati: ine ndimasala chaka chonse ndipo sindimasula. Wina anati: ine ndiye ndimapewa azimai moti sindidzakwatira mpaka kale. Pamenepo Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “inu amene mwanena zakutizakuti, ndithu ine Wallahi ndimawopa Allah kuposa inu, koma ndimasala ndipo ndimamasula, ndimaswali usiku ndipo ndimagona, komanso ndimakwatira azimai. Choncho yemwe angasankhe njira zina posakhala za inezi, sali mwa ine.”


Apa Mtumiki amatanthauza kuti kusiya kukwatira chifukwa chodziyandikitsa kwa Allah, ndizolakwika ndipo sichiphunzitso chake. Ndiye omwe amati ine sindidzakwatira koma ndizingozisunga, akuzinamiza; chifukwa 1. Akusemphana ndi sunnah ya Allah yomwe iye anapezekera, 2. Chimenecho sichiphunzitso cha Mtumiki. Ndiye munthu akuti akudziyandikitsa kwa Allah pochita zomwe zili zosayenera ndi Allah, amulandira ndani? akudzitalikitsa ndithu.Mau oti “…sali mwa ine” sakumutulutsa munthu Chisilamu.


Ma hadith olamula kukwatira alipo ambiri, koma tingoona kaye mbali zina, chifukwa ambiri akangomva kuti Mtumiki analamula zakuti, amayankhula kuti “aaa imeneyo ndi sunnah, sunnah ngakhale osachita”. Kuyankhula komanso kuganiza uku ndikolakwika komanso kunyoza malamulo a Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndikuwachepetsa. Omwe amadziwa kufunikira kwa Sunnah koma samakwanitsa kupanga mwakusafuna, amadandaula kwambiri mmoyo mwawo, pomwe mbuli imasangalala ikamva ena akunena kuti “olo osachita supeza nsambi”.


Kodi kusiya ibaada yomwe analamula Mtumiki ndi tchimo?


Ndi tchimo kusiya ibaada yomwe analamula Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Chisilamu malamulo ake akuchokera mu Qur’an ndi Sunnah. Allah Ta’ala watilamula kambirimbiri kutsatira Mtumiki salla Allah alaih wasallam, monga:


وَمَا آتَاكُمُ الرَّسُولُ فَخُذُوهُ وَمَا نَهَاكُمْ عَنْهُ فَانتَهُوا وَاتَّقُوا اللَّهَ إِنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعِقَابِ

“Ndipo chimene wakupatsani Mtumiki, chilandireni; ndipo chimene wakuletsani chisiyeni. Muopeni Mulungu (potsatira malamulo ake). Ndithu, Mulungu ngwaukali polanga”. Qur’an 59:8


Ili ndi lamulo la Allah, akutilamula kutsatira zomwe watilamula Mtumiki ndikusiya zomwe watiletsa. Ndipo tiwope chilango cha Allah potsatira lamulo lake loti tidzitenga zomwe Mtumiki watilamula. Kukwaira ndi Ibaada yolamulidwa.


Munthu asazisankhire kuti ine sindikwatira … kungofuna chabe. Ngakhale patapezeka zifukwa, athane ndi zifukwazo mpaka akwatire. Osazisankhira zochita zina pambuyo poti walamulidwa zoti uchite:


وَمَا كَانَ لِمُؤْمِنٍ وَلَا مُؤْمِنَةٍ إِذَا قَضَى اللَّهُ وَرَسُولُهُ أَمْراً أَن يَكُونَ لَهُمُ الْخِيَرَةُ مِنْ أَمْرِهِمْ وَمَن يَعْصِ اللَّهَ وَرَسُولَهُ فَقَدْ ضَلَّ ضَلَالاً مُّبِيناً

“Ndipo sikoyenera kwa wokhulupirira wachimuna ndi wokhulupirira wachikazi, Mulungu ndi Mtumiki wake akalamula chinthu, iwo kukhala ndi chifuniro pazinthu zawo. Ndipo amene akunyoza Mulungu ndi Mtumiki wake, ndithu, wasokera; kusokera koonekera.” Qur’an 33:36


Kuzisankhira zochita ndikusiya zomwe tinalamulidwa ndiko kunyoza Allah ndi Mtumiki wake omwe anatilamula zoyenera kuchita. Asiyeni awo omwe amayendera maufulu awo ozikhonzerawo, azizisankhira zomwe akufuna poti mwina malamulo mchipembezo chawo amawalola kudzisankhira zochita. Koma inu musatengere, poti muli ndi malamulo a moyo wanu – Qur’an yolemekezeka yomwe inalongosoledwa ndi Sunnah.