Kuchotsedwa Kwa Kuwerenga Pambuyo Pa Imaam Mu Swalaat/Rakaat Zokweza Mawu

Swifatu Swalaat Nabiy salla Allah alaih wasallam (Sheikh Al Albaani) pge 98

Kodi Kuwerenga Surah Al Fatiha kunalolezedwa nthawi yanji nanga kunaletsedwa nthawi yanji?

Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali ataloleza kwa otsatira kuwerenga Surat Al Fatihah pambuyo pa Imaam pa swalaat zokweza mawu, ndipo izi zinachitika pa swalaat ya Al Fajr pamene anali kuwerenga (iye Mtumiki) ndipo anabanika. Atamaliza swalaat anati (kwa ma Swahaba):

“لعلكم تقرؤون خلف إمامكم” قلنا: نعم هذًّا يا رسول الله! قال: “لا تفعلوا؛ إلا بفاتحة الكتاب، فإنه لا صلاة لمن لم يقرأ بها”

“Ndiganiza kuti mumawerenga pambuyo pa imam wanu”. Ndipo ife (ma Swahaba) tinati: inde (timawerenga) mofulumira inu Mtumiki! Adati: “Musamapange; kupatula (kuti aliyense wainu aziwerenga) Surah yotsegulira Buku (Surah Al Fatiha), chifukwa ndithu palibe swalaat kwa yemwe sadaiwerenge (Al Fatihah)” Sahih Al Bukhari, Sunan Abu Daud, Imaam Ahmad, Sunan Al Tirmidhi, Al Dariqutni.

Kenako anawaletsa kuwerenga Surat Al Fatiha yonse pa rakaat zokweza mawu. Ndipo izi zinachitika pamene anamaliza swalat yokweza mawu powerenga Qur’an (ma report amanena kuti swalaat yake inali ya Al Subhi), iye (Mtumiki salla Allah alaih wasallam) anati:

“هل قرأ معي منكم أحد آنفا؟” فقال رجل: نعم، أنا يا رسول الله فقال: إني أقول “مالي أنازع؟!”

“Kodi alipo mwainu amene amawerenga nane posachedwapa?” munthu wina anati: inde, ine (ndimawerenga) Mtumiki wa Allah! (Mtumiki) anati: “Ndithu ine ndikuti: n’chifukwa chani ndikupikisana (nanu powerenga)” (Apa Mtumiki amatanthauza kuti kuwerenga pamene iyenso akuwerenga kunali ngati kulimbirana zomwe akuwerengazo), malinga ndi kuyankhula kwa Al Khattwaani.

Kuwerenga Pambuyo pa Imaam

Ndipo Abu Hurayra radhia Allah anhu anati: ndipo anthu anasiya kuwerenga pamodzi ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam panthawi yokweza mawu, pamene anamva mawu amenewa kuchokera kwa Mtumiki, choncho anayamba kumawerenga mwaokha mobisa mawu pa rakaat zomwe imam sakweza mawu. (Izi kuchokera kwa Malik, Al Humaydiy, Al Bukhari, Abu Daud, Ahmad ndi Al Muhamili (6/139/1), Al Tirmidhi, Abu Hatim Al Raazi, Ibn Hibbaan ndi Ibn Al Qayyim)

Mtumiki salla Allah alaih wasallam anakupanga kukhala chete pamene imam akuwerenga, kokwanira kukhala kumtsatira imam, ndipo anati:

إنما جعل الإمام ليؤتم به، فإذا كبر فكبروا، وإذا قرأ فانصتوا

“Ndithu imam anaikidwa kuti adzitsatidwa; pamene wachita takbeer, inu chitani takbeer, pamene wawerenga, inu khalani chete” Kuchokera kwa Ibn Abi Shaybah (1/97/1), Abu Daud, Muslim, Abu ‘Awaana, Al Rawbaani mu Musnad yake (24/119/1) zomwe zikupezekanso mu Al Irwaai (Sheikh Al Albaani) p332 ndi 394.
ndipo anakupanga kumvetsera kukhala mmalo mwa kuwerenga poyankhula kuti:

من كان له إمام فقراءة الإمام له قراءة

“Yemwe akutsogozedwa ndi imam, kuwerenga kwa imaamuyo kukukwanira kwa iye” Ibn Abi Shaybah 1/97/1, Al Darqutni, Ibn Maajah, Al Tahaawi, Ahmad, Ibn Taymiyah Ibn Abdil Haadi (Al Furoo’ 47/2), Irwaail Ghaleel 500

Omwe angafune kupitiriza pamenepa, akhonza kulowa mu

صفة صلاة النبي للشيخ محمد ناصر الألباني، صـ100

Kuwerenga Pambuyo pa Imaam