بسمِ الله الرحمن الرحيم

KUVALA HIJAB NDI ZOLINGA ZAKE MCHISILAMU

Uwu ndi uthenga kwazichemwali athu a Chisilamu.Alhamdulilah kuti Masiku ano Hijab ili paliponse limodzi ndi kutsogola kwa ma company opanga Zovala makamaka mikanjo yazimayi.kuli Mitundu Yochuluka ya Hijab,ndipo nde ikuvalidwadi.

Koma Hijab ndi Chani?? Cholinga chake ndi Chani? Ndi lamulo lanji lovala Hijab kwamkazi wa Chisilamu?? Nanga ndi kavalidwe kanjii ka Hijab komwe amalamulidwa mkazi wa Chisilamu?

Liwu lakuti Hijab limatathaunza pawiri pa sharia.

      Hijab muchiyankhulo cha Arabic imatanthaunza Kubisa

      Mamvekedwe a hijab mchisilamu; ndiKalikonse komwe kamabisa Thupi lamkazi, kuphatikiza khope ndi manja(Zikhatho). Ma Scholar adasephana maganizo  kodi Hijab imaphatikiza ndi khope ndi zikhatho zomwe?  Otsatira a lmam Ahmad ibn han-bal ndi otsatira a Imam Shafi *iwo amaona zakufunikira Kobisa mkazi khope yake(niqab) ndi zikhatho kwa Amuna achilendo* pomwe otsatira a Imam Malik ndi Abu Hanifah Iwo amati *sichikakamizo mkazi kubisa khope yake ndi zikhatho zake*, koma  zoyankhula za otsatira a Imam Abu hanifa ndi Otsatira a Imam Malik zimatsindikiza zakufunikira kobisa mkazi khope yake ndi zikhatho zake *akankhala kuti mkaziyo ndi okongola mooopsa* mopeleka mayesero,zili choncho ndi cholinga chotchinga mayesero ndi kufalikira  Kwazonyasa.

Choncho tikamatchula liwu la Hijab mukufotokoza kwathu, sitikutanthauza mpango okha,koma kuti chovala chobisa thupi lamkazi kuyambira kumutu mpaka pansi

MALAMULO AKAVALIDWE KA HIJAB

Kuti hijab yamkazi ikhale yokwanira payenera kupezeka izi

      Zimalamulidwa kuti ibise thupi lonse,kuphatikiza khope ndi zikhatho,ma Scholar ambiri achisilamu adapambanitsa kuti Hijab ikhale yopanda Zikongoletso.

      Isaonetse Thupi lamkazi kapena mbali ina yake, monga kuonetsa mbali yatsitsi,kapena siketi,dress ya Ng’amba.Atsikana ena amangoponya mpango mmutu osauvala bwino nalisiya tsitsi likuonekera,ndipo kuvala mpango bwinobwino koma kumusi nkuvala chang’amba,imeneyo si Hijab.

      Isankhale Yothina,kapena yofotokoza thupi  lamkazi monga ma Trouser ,  zomwe Atsikana ambiri akuchita masiku ano,Kuvala Hijab yothina yofotokoza kuti thupilo ndi lonenepa Kapena lowonda,Hijab ku Dinditsa mahip ndi ku Dinditsa Chidali (mabele) . Imeneyi Si hijab yomwe Chisilamu imalamulira  nde kuli ena muwaona avala hijab bwino bwino koma ndi yowewela Mmikono kumaonekera ndi malo ena,dziwani kuti Imeneyo si Hijab.

      lisamamveke Fungo lonukhira (Perfume). Hijab Cholinga chake ndi kusapeleka Chikoka kwa amuna ndi kutinso asaike chidwi chawo pamkazi,Choncho mkazi sali oyenera kuzipopera zonukhilitsa akamapita kunja kuti asakapeleke mayesero kumamucheukira amuna,koma sikutathauza kuti mkazi azikhala osazisamalira,kusamba ndi kokwanira,ndipo zonukhilitsa azizipopera akakhala pakhomo ndi mamuna wake.

Zoopsa ndi zoti Chifukwa chotayilira akazi achisilamu ziphuzitso za Chisilamu, mupeza kuti akazi ambiri ovala Hijab ndi omwenso ali patsogolo popeleka mayesero ndi mavalidwe awo amene akuwatcha kuti ndi Hijab wo,zomwe zikupangitsa kuti Hijab isakhaleso chotchingira mayesero koma kuti isanduke chobweretsa mayesero.

Tikaonetsetsa malamulo a hijabuwa akusowekera pakati pa akazi, mumpeza mtsikana wavala Zothina mwadala dala kuti Akope amuna,sasiyira pomwepo amajambulitsa Chindekha(Self) kaya ndi zimthuzi ,akatero mkumatumiza mma Social media,Facebook, kukhala ngati akuyitanira malonda. Dziwani mchitidwe otero ndi osephana ndi miyambo ya Hijab.

HIJAB NDI CHIKAKAMIZO KAPENA AYI?

Hijab ndi yokakamizika kwamkazi kuyambira pomwe watha msinkhu akangoyamba *Msambo* Chifukwa munthu akatha msinkhu amayamba kulembeledwa Zintchito zake  zabwino ndi zoipa.Allah akuyankhula motere

وَقُل لِّلْمُؤْمِنَاتِ يَغْضُضْنَ مِنْ أَبْصَارِهِنَّ وَيَحْفَظْنَ فُرُوجَهُنَّ وَلَا يُبْدِينَ زِينَتَهُنَّ إِلَّا مَا ظَهَرَ مِنْهَا ۖ وَلْيَضْرِبْنَ بِخُمُرِهِنَّ عَلَىٰ جُيُوبِهِنَّ ۖ وَلَا يُبْدِينَ زِينَتَهُن.

“Nena kwa okhulupilira achikazi kuti aphimbe maso awo (posaona za Haram) ndikutinso  abise maliseche awo ( ku nyasi yachiwerewere) ndipo asamaonetse zikongoletso zawo kwa amuna (kupatula zokhazo zomwe zimaonekera zokha,monga zibangili Chifukwa sizikhala malo obisika) *Ndipo atsitse mipango yawo nabisa mipata yapachidali (uku atabisa mitu yawoyo) ndipo asaonetse zikongoletso zawo” . Qur’an 24;31 

Mu verse imeneyi Allah akuletsa akazi kuonetsa zikongoletso kwa Amuna kupatula kwa omwe adatchulidwa pansi pake pa verse imeneyi,mukafuna kuwadziwa Welenga Qur’an pa verse tatchulayi,Kenakonso Allah akuwalamulira Akazi zakutsitsa mipango yawo mokutira khosi mpaka kufika pansi pafupi ndi nchombo ndi cholinga chobisa zomwe zili pamenepozo, choncho mkazi ayenera kuonetsetsa kuti Chidali chake ndi mpata wapakati  pake (mabele) pabisidwa bwino bwino kuyambira kumutu.

PHINDU LOVALA HIJAB

      Kuyeretsa mitima ya amuna achisilamu ndi azikazi awo kumaganizo oipa asatana ndi zopusitsa zake.pamene mkazi akuvala mobisa thupi lake amuna sankhala ndi zikhumbokhumbo zoipa akamuona. Ngati momwe amuna ena amachitira amasangalatsidwa kuti mkazi wawo adzivala Zothina Zo Dinda paliponse kuti Anthu azilozerana kuti uyu ndi mkazi wa aujeni,namayakhula zambiri. Mavalidwe otero ndi oletsedwa kwa Asilamu.

      Kuonetsa kuzisunga kwamkazi ndi kumutalikitsa ku kuganizilidwa zoipa,choncho mkazi wa Chisilamu akavala hijab ayenera kuonetsa mwambo ndi kuchita zogwirizana ndi mavalidwewo,choncho ndi zamanyazi kumuona mtsikana ali mu hijab koma akuchita zosalongosoka,namasakanikirana ndi Amuna ,uwu ndi mchitidwe olakwika omwe atsikana achisilamu akuyenera kuwupewa .

      kumutetezera mkazi kwa anthu amene ali pa m’lolera opeza mpata owachita chipongwe akazi, ndi kumuteteza kwa Anthu ofooka iman ndi osadzigwira ku Zilakolako, mukudziwa kale nyengo yomwe Malawi ikudutsa,kuchuluka kwa mchitidwe onyasa ogwililira ndi zithu Zina zonyasa,ngakhale Timanena kuti mavalidwe amkazi sichifukwa chomugwililira koma kuti nthawi zina Kupewa kuposa kuchiza, ndipo kupewa kwake ndi kuvala mobisa thupi moyenera.

      kusunga ubale wam’banja pakati pa mamuna ndi mkazi, mamuna weniweni wa Chisilamu amakonda kuti Mkazi wake azibisa thupi lake choncho asasililidwe ndi amuna ena.

Ngakhale zili Choncho akazi apewe ma Fashion ahijab omwe agwa masiku ano, Chifukwa zambiri mwa izo sizofuna kumubisa mkazi koma kumuonetsera,choncho ma fashion ambiri amasiku ano akunkhala opeleka kwambiri fitnah (mayesero) mpaka mkazi  wa hijab akusililidwa ndi amuna,osati kusililidwa kwaubwino koma kwazilakolako zoipa,kuposaso mkazi Yemwe sadavale Hijab.

Aphuzitseni akazanu ndi azichemwali anu, ndi abale anu Hijab Yeniyeni yomwe Chisilamu chimafuna,kuti Timange community ya Asilamu yotalikirana ndi mayesero ndi zinthu zoipa,Tili kale kumapeto kwanthawi Kochuluka mayesero,Atsikana Achisilamu musakhale mayesero koma kuti mukhale Chitsanzo cha bwino cha Chisilamu ndi chitsanzo chabwino cha mudzi wanu ndi banja lanu kumbali yamavalidwe abwino.