Maloto amachitika pamene munthu wagona tulo ndipo mzimu wake umachoka mthupi ndikupita kwina  kumene atha kukakumana ndi mizimu ya anthu ena, omwalira kapena amoyo omwe ali mtulo ngati iyeyo.
Choncho Allah amangosiya connection pakati pa thupi ndi mzimu wake, ndipo Allah akafuna amatha kudula connection ija, mzimu uja nkusaubwezeretsanso, mpamene amati afera kutulo. Zimenezitu akuyankhula mwiniwake Allah Ta’la mu Surah Al Zumar Aayah 43 kuti
اللَّهُ يَتَوَفَّى الْأَنْفُسَ حِينَ مَوْتِهَا وَالَّتِي لَمْ تَمُتْ فِي مَنَامِهَا فَيُمْسِكُ الَّتِي قَضَى عَلَيْهَا الْمَوْتَ وَيُرْسِلُ الْأُخْرَى إِلَى أَجَلٍ مُسَمًّى
Mulungu ndiye amatenga mizimu pa nthawi ya imfa yake ndipo amatenga mizimu yomwe siidafe panthawi yogona tulo. Ndipo amaigwira mizimu imene wailamula kufa, (osaibwezera ku matupi awo). Koma inayo amaitumiza (kumatupi awo, yomwe nthawi yake siidakwane) kuti ikwaniritse nthawi yake imene idaikidwa.
 
Tsopano palinso nthawi zina zomwe munthu amatha kudzuka madzidzidzi chifukwa chodzidzimutsidwa pomugwira kapena phokoso; pamenepa chimachitika nchoti mzimu uja umakhala uli kutali ndiye umabwera mofulumira nthawi imodzi komanso mwa mphamvu. Nchifukwa chaketu pena munthu akadzuka modzidzimutsidwa amamva kuwawa pa mtima.
 
Mtumiki salla Allah alaih waallam anati:
الرُّؤْيَا ثَلاَثٌ فَبُشْرَى مِنَ اللَّهِ وَحَدِيثُ النَّفْسِ وَتَخْوِيفٌ مِنَ الشَّيْطَانِ فَإِذَا رَأَى أَحَدُكُمْ رُؤْيَا تُعْجِبُهُ فَلْيَقُصَّهَا إِنْ شَاءَ وَإِنْ رَأَى شَيْئًا يَكْرَهُهُ فَلاَ يَقُصَّهُ عَلَى أَحَدٍ وَلْيَقُمْ يُصَلِّي
Maloto ali mmagulu atatu:
a. Ochokera kwa Allah (nkhani yabwino)
b. Ochokera muzoganiza za munthu (zomwe munthu umaganizira kwambiri ndiye zimabwerezeka kutulo, maloto amenewa alibe ntchito).
c. Ochokera kwa shaytwan 
Ngati mmodzi wa inu walota zosangalatsa, akhonza kudzikamba ngati wafuna. Koma ngati walota zosasangalatsa, anasadzikambe kwa aliyense, ndipo adzuke ndikuswali.
 
Sitikuloledwa kutanthauzira maloto kupatula okhawo omwe ali ndi ‘ilm ya kutero, ndipo akudziwa matantahuziridwe omwe ndi ololedwa Mchisilamu. Ndipo tisamasulire mwachisawawa chifukwa tikhonza kusokeretsa nazo anthu, ndipo zingachititse kuti ena adzidalira maloto mmoyo mwawo. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali kulongosola maloto komanso anawaloleza ma Swahaba ena kutanthauzira.
Dziwani kuti otanthauzira maloto akhonza kulondola kapena kulakwitsa.
أن رجلًا أتى النبي صلى الله عليه وسلم فقص عليه رؤيا، فطلب أبو بكر ـ رضي الله عنه ـ أن يعبرها، فأذن له النبي صلى الله عليه وسلم، ثم قال أبو بكر ـ رضي الله عنه ـ بعد ذلك: بأبي أنت أصبت أم أخطأت؟ قال النبي صلى الله عليه وسلم: أصبت بعضًا وأخطأت بعضًا، قال: فوالله يا رسول الله؛ لتحدثني بالذي أخطأت، قال: لا تقسم.
Kuchokera kwa Ibn Abbas, Hadith yomwe inalandiridwa ndi Al Bukhari ndi Muslim, anati: munthu wina anafika kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndipo anamulongosolera maloto ake. Abubakr radhia Allah anhu anapempha Mtumiki kuti amasulire iyeyo ndipo Mtumiki analoleza. Abubakr anati pambuyo pake: Ndalondola kapena ndalakwitsa? Mtumiki anati: walondola zina ndipo walakwitsa zina. Anati: Wallahi inu Mtumiki, ndiuzeni zomwe ndalakwitsa. Anati: usalumbire.
 
Imaam Malik anati: asatanthauzire maloto aliyense kupatula yemwe akudziwa bwino. Ndipo ngati munthu walota zabwino, adzinene, koma ngati walota zosakhala zabwino, ayankhule zabwino zokha kapena akhale chete.
Kutanthauzira maloto molakwika kumakhala kunama, choncho yemwe sakudziwa kutanthauzira maloto asatanthauzire. Allah akunena kuti:
وَلا تَقْفُ مَا لَيْسَ لَكَ بِهِ عِلْمٌ
Ndipo usazitsate (pongoziyankhulayankhula kapena kuzichita) zomwe Sukuzidziwa; Al Israai 36