Zipembedzo zitatuzi zimasiyana kwambiri ndi pankhani ya kusudzulana. Chikhristu chimanyansidwa kwathunthu ndi kusudzulana, ndipo  Chipangano Chatsopano chimalimbikitsa za ukwati wopanda chisudzulo. Mmenemo akunena kuti, Yesu anati, Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wothetsa ukwati ndi mkazi wake, osati chifukwa cha dama, amamuchititsa chigololo akakwatiwanso, ndipo aliyense wokwatira mkazi wosiyidwayo nayenso wachita chigololo.(Mateyu 5:32). Zimenezitu sizomveka, chifukwa zikupereka maganizo a chikhalidwe cha ungwiro chomwe anthu sanachitepo. Zikuonetsa kuti ngati anthu awiri a pabanja awona kuti moyo wawo uli ndi mavuto omwe sangathe kukhonza, kusiyana banja sikungathandize. Komatu kukakamiza anthu awiri pa banja lomwe sangakhalire limodzi mwakufuna kwawo ndikoipa komanso kupha ufulu wawo waumunthu. Izi nchifukwa chake Akhristu amatengedwa kuti achita tchimo akathetsa banja ndipo amayenera kuimbidwa mlandu.

Pomwe Chiyuda chimalola kuthetsa ukwati ngakhale popanda chifukwa. Chipangano Chakale chinapereka ufulu kwa mwamuna ufulu wosudzula mkazi wake ngakhale atangokhala kuti sanamukonde:

“Mwamuna akatenga mkazi kuti akhale mkazi wake, ndiyeno ngati mkaziyo sanamusangalatse chifukwa wampeza ndi vuto linalake, azimulembera kalata yothetsera ukwati ndi kumpatsa mmanja mwake, nkumuchotsa panyumba pake. Pamenepo mkaziyo azituluka mnyumba ya mwamunayo ndi kukakhala mkazi wa mwamuna wina. Mwamuna wachiwiriyu akadana nayenso mkaziyo ndipo wamulembera kalata yothetsera ukwati nkuyiika mmanja mwake ndi kumchotsa panyumba pake, kapena ngati mwamuna wachiwiriyu amene anamtenga kukhala mkazi wake wamwalira, mwamuna woyamba amene anamchotsa uja sadzaloledwa kumtenganso kuti akhale mkazi wake pambuyo poti waipitsidwa. Kuchita zimenezo nkonyansa pamaso pa Yehova, chotero usachimwitse dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa monga cholowa.” (Deut 24: 1-4). 32

Mavesi amenewa adayambitsa mtsutso waukulu pakati pa ozindikira a Chiyuda chifukwa cha kusagwirizana kwawo pakutanthauzira mawu oti “kusasangalatsidwa”, “kuipa”, ndi ” kudana naye” omwe atchulidwa mmavesimo. Talmud inalongosola maganizo ake osiyana motere:

“Chiphunzitso cha Shammai chinati mwamuna sayenera kusudzula mkazi wake pokhapokha atamupeza ndi kugonana, pomwe chiphunzitso cha  Hillel chimati mwamuna akhoza kumusudzula mkazi ngakhale atangopezeka kuti sanaphike bwino chakudya.” Rabbi Akiba akunena kuti mwamuna amusiye mkazi wake ngakhale atangoona mkazi wina wokongola kuposa iye”(Gittin 90a-b).

Chipangano Chatsopano chinatenga chiphunzitso cha Shammai, pamene malamulo a Chiyuda anatengera maganizo a Hillel ndi R. Akiba. Koma popeza kuti chiphunzitso cha Hillel chinapambana, chinasanduka kukhala chikhalidwe cha Chiyuda kuti mwamuna ali ndi ufulu wosudzula mkazi wake popanda chifukwa. Chipangano Chakale sichinangopatsa mwamuna ufulu wosudzula mkazi wake “wosakondweretsa”, koma chimakutenganso kusudzula “mkazi woipa” kuti ndi lamulo lokakamizidwa:

“Mkazi woipa amachititsa manyazi, kukhumudwitsa, komanso kuvulaza mtima. 33 Kutaika kuli kwa mwamuna yemwe mkazi wake samusangalatsa. Mkazi ndi chiyambi cha tchimo, ndipo kudzera mwa iye tonsefe timafa. Musalole chitsime chodontha kuti chiyendelere; musalole mkazi woipa kuti ayankhule zomwe wafuna. Ngati sakuvomereza ulamuliro wanu, mumusudzule ndikumutumiza kwawo.” (Mlaliki 25:25)

Talmud inalongosola zinthu zingapo zomwe zimachititsa mwamuna kuti amusiye mkazi wake:

  • “ngati mkazi apezeka akudyera mumsewu,
  • ngati apezeka akumwera mumsewu,
  • ngati apezeka akuyamwitsa mwana mumsewu.

Rabi Meir akunena kuti nthawi zimenezi mwamuna ayenera kumusiya mkaziyo” (Git 89a). Talmud inavomereza kuti mwamuna amusiye mkazi wosabereka (yemwe sanabereke mwana kwa zaka khumi): “Rabbi athu anatiphunzitsa kuti: Ngati mwamuna watenga mkazi ndi kukhala naye kwa zaka khumi ndipo sanabale mwana, adzayenera kumusiya banja “(Yeb. 64a).

Mmalamulo a Chiyuda, mkazi sangayambitse msudzulo. Koma ali ndi ufulu wakunena zoti asudzulidwe pa bwalo lamilandu la Chiyuda, ngati pali chifukwa champhamvu. Zifukwa zochepa kwambiri zimaperekedwa kuti mkazi atha kupempha kuti athetse banja, monga: Mwamuna amene ali ndi zilema kapena matenda a khungu, mwamuna wosakwaniritsa ntchito yake, ndi zina. Khoti likhoza kuthandizira zomwe mkaziyo akunena koma silingathetse banja. 34

Mwamuna yekha ndi amene angathe kuthetsa ukwati pakupereka kalata kwa mkazi wake. Bwalo likhoza kumukwapula, kumuika m’ndende komanso kumuchotsa muzochitika za mu tchalitchi mpaka atapereka kalata yoyenera ya chisudzulo kwa mkazi wake. Komabe, ngati mwamunayo wakakamira, akhonza kukana kupereka chisudzulo kwa mkazi wake ndikumakhala naye nthawi zonse. Choipa kwambiri nchoti akhoza kumusamukira popanda kumusudzula, ndikumusiya wosakwatiwa komanso wosasudzulidwa. Iye akhoza kukwatira mkazi wina kapena kukhala ndi mkazi aliyense wosakwatiwa ndikubala ana kuchokera mwa iye (ana awa amaonedwa kuti ndi ochokera munjira yolondola mmalamulo a Chiyuda). Mkazi yemwe wasiyidwa uja, sangathe kukwatiwanso ndi mwamuna wina popeza kuti adakali muchilamulo choti ndiwokwatiwa ndimwamuna wina (sanamusudzule), ndipo sangathe kukhala ndi mwamuna wina aliyense chifukwa akatero adzatengedwa kuti ndi wachigololo, ndipo ana ake obadwira mmenemo adzakhala wochokera munjira yolakwika mpaka mibadwo khumi yakutsogolo kwawo.

Mayi wotereyu amatchedwa agunah (mayi womangidwa). Ku United States lerolino kuli amayi a Chiyuda pakati pa 1,000 ndi 1,500 omwe ali ma agunah, ndipo mu Israeli, chiŵerengero chawo chikhoza kuposera pa 16,000. Amuna amatha kutenga ndalama zambirimbiri kuchokera kwa akazi awo omwe ali mumsasa kuti athetse banja la Chiyuda . 35

Chisilamu chili pakati pa Chikhristu ndi Chiyuda pa lamulo la chisudzulo; ukwati Mchisilamu ndi chiyanjano choyera chomwe sichiyenera kutswedwa kupatula pa chifukwa chomveka. Maŵanja akulangizidwa kuti azitsatira njira zoyenera zothetsera mavuto. Kusudzulana sikuyenera kuchitika kupatula ngati palibe njira ina yothetsera mavutowo. Mwachidule, Chisilamu chimavomereza kusudzulana, komabe sichimalimbikitsa kutero.

Tiyeni tiwone kaye mbali ya kuvomerezayi: Chisilamu chimavomereza kuti onse awiri atha kuthetsa ubale wawo wabanja, choncho, chinapereka kwa mwamuna ufulu wa Talaq (chisudzulo). Koma mosiyana ndi Chiyuda, Chisilamu chinapereka ufulu kwa mkazi, woti akhonza kuthetsa banja kudzera munjira yotchedwa Khul’a. 36

Ngati mwamuna wathetsa ukwati mwa kusudzula mkazi wake, sangathe kulandira mphatso iliyonse ya ukwati yomwe anapereka. Qur’an ikuletsa momveka kuti amuna osudzula asabwezeredwe mphatso zawo za ukwati ngakhale zitakhala za mtengo wapatali kapena zopindulitsa.

Qur’an 4:20: “Ndipo ngati mufuna kusintha mkazi wina mmalo mwa wina (pokwatira wina kusiya wakale) pomwe mmodzi waiwo (woyambayo) mudampatsa milumilu yachuma, musatenge (kulanda) chilichonse. Kodi mungachitenge mwachinyengo ndi utchimo woonekera?”

Koma ngati mkazi wasankha kuti banja lithe, ndiye kuti adzayenera kubweza  mphatso kwa mwamuna wake. Kubweza mphatso zaukwati panthawiyi kuli ngati malipiro abwino kwa mwamuna yemwe akufuna kumusunga mkaziyo pamene mwini wake wasankha kumusiya. Qur’an yalangiza amuna a Chisilamu kuti asatenge mphatso zomwe adawapatsa akazi awo pa ukwati, kupatula ngati mkaziyo ndamene wafuna kuti banja lithe:

Qur’an 2:229: “Ndipo sizili zololedwa kwa inu kuti mutenge (kulanda) chilichonse chimene mudawapatsa (akazi anu) pokhapokha (onse awiri) ngati akuopa kuti satha kusunga malire a Mulungu (malamulo a Mulungu). Ngati muopa kuti sasunga malire a Mulungu, ndiye kuti pamenepo pakhala popanda tchimo kwa iwo (mwamuna woyamba ndi mkaziyu) kulandira (kapena kupereka) chodziombolera mkazi. Awa ndiwo malire a Mulungu; choncho musawalumphe. Ndipo amene alumphe malire a Mulungu (powaswa), iwowo ndiwo anthu ochitazoipa.” 37

Mkazi wina adadza kwa Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam pofunafuna kuthetsa ukwati wake, adamuwuza Mtumiki kuti adalibe vuto ndi khalidwe la mwamuna wake, koma vuto linali loti sanamufune iye mpaka kufika polephera kukhala naye. Mtumiki adamufunsa kuti: “Ungamupatse munda wake (mphatso yaukwati yomwe adakupatsa)?” Iye adati: “Inde”. Mtumiki adamulangiza mwamuna kuti atenge munda wake ndikuvomereza kuti ukwati uthe (Al-Bukhari).

Nthawi zina mkazi wa Chisilamu akhoza kukhala wokonzeka kusunga banja lake, koma amapezeka kuti akuyenera kupempha talaaq pachifukwa chomveka, monga nkhanza za mwamuna, kudana popanda chifukwa, mwamuna wosakwaniritsa maudindo ake, ndi zina zotero. Zikakhala choncho, bwalo la milandu la Chisilamu limayenera kuthetsa ukwatiwo.

Mwachidule, Chisilamu chinapereka kwa mayi wa Chisilamu maufulu ochitira zinthu zina mosiyana ndi mwamuna, monga kuti akhoza kuthetsa ukwati kudzera mu Khula ‘ ndipo akhoza kumusumira kuti amusudzule. Mkazi wa Chisilamu sangamangidwe ndi mwamuna. Amenewa ndiwo maufulu amene ankapusitsa akazi a Chiyuda omwe anali munthawi yoyambilira ya Chisilamu mzaka za mma 7th century pakufunafuna kupeza ngongole za chisudzulo kuchokera kwa amuna awo a Chiyuda mmakhoti a Chisilamu, ndipo kenako ma Rabbi adalengeza kuti ngongole izi sizigwira ntchito. Pofuna kuthetsa chizolowezi ichi, ma Rabbi anapereka maufulu ndi maudindo atsopano kwa akazi a Chiyuda pofuna kuyesa kufowoketsa malamulo a makhoti a Chisilamu. Akazi a Chiyuda omwe ankakhala mmayiko a Chikhristu sanali kupatsidwa mwayi wofanana nawo, poti lamulo la Chiroma pa kutsudzula, lomwe linali kutsatidwa kumeneko, silinali lopatsa chikoka kuposa lamulo la Chiyuda. 38

Tiyeni tsopano tione momwe Chisilamu sichimalimbikitsira kusudzulana. Mwamuna wa Chisilamu sayenera kusudzula mkazi wake chifukwa chakuti sanamukonde. Qur’an yalangiza amuna a Chisilamu kuti azikhala okoma mtima kwa akazi awo ngakhale atapanda kuwakonda:

Qur’an 4:19: ” Ndipo khalani nawo mwaubwino. Ngati mutawada (musalekane nawo), mwina mungade chinthu chomwe Mulungu waika zabwino zambiri mkati mwake.”

Mtumiki salla Allah alaih wasallam analangizanso chimodzimodzi kuti: “Mwamuna wokhulupilira sayenera kumuda mkazi wokhulupilira. Ngati sakonda chimodzi mwa makhalidwe ake, adzasangalatsidwa ndi china” (Muslim).

Mtumiki  adatsindikanso kuti Asilamu abwino ndi omwe ali abwino kwa akazi awo:

“Okhulupilira omwe amasonyeza chikhulupiliro changwiro kwambiri ndi omwe ali ndi khalidwe labwino kwambiri, komanso omwe ali abwino mwa inu ndi omwe ali abwino kwa akazi awo” (Tirmidthi).

Komabe, Chisilamu ndi Chipembedzo chenicheni ndipo chimadziwa kuti nthawi zina ukwati umatha. Zikatero, malangizo ochita chifundo kapena kudziletsa sangakhale njira yothetsera vuto. Kodi nanga pamenepo tingachite chani kuti titeteze ukwati? Qur’an inapereka malangizo othandiza kwa wokwatira (mwamuna kapena mkazi) pamene mkazi kapena mwamuna walakwira mzake. Kwa mwamuna yemwe chikhalidwe cha mkazi wake chikuopseza chitetezo cha banja lake, Qur’an inapereka malangizo anayi monga momwe ziliri m’mavesi otsatirawa:

Qur’an 4:34: Ndipo akazi omwe mukuopa mnyozo wawo, (1) achenjezeni; (2) ndipo kenako achokereni pamphasa. (Apo ayi), (3) akwapuleni; (kukwapula kosavulaza) koma ngati akukumverani, musawafunire njira yowavutitsira. Ndithu Mulungu ndi yemwe ali wapamwamba, wamkulu (kuposa inu nonse). Ndipo (inu aweruzi) (4) ngati muopa mkangano pakati pawo (pamwamuna ndi mkazi wake), tumizani nkhoswe yakuchimuna ndi nkhoswe yakuchikazi. Ngati iwo atafuna kuyanjanitsa, Mulungu awapatsa mphamvu zoyanjanitsira pakati pawo (okanganawo).”

Malangizo atatu oyambilirawo ayenera kuyesedwa koyamba, ngati alephera, akuyenera kuthandizirapo mawanja ena omwe ali okhunzidwa pa ukwati wa awiriwo. Tiyenera kuzindikiranso, kuti mamvetsedwe a mavesi awiriwo, sakulamula kumenya mkazi mwankhanza, koma kumenya kwake kofuna kumuphunzitsa kuti asinthe khalidwe, osati kumuvulaza kapena kumumvetsa kuwawa kulikonse. Ndipo ngati zitheke, mwamuna saloledwa mwa njira iliyonse kupitilira kukwiyira mkazi. Ngati sizitheka, mwamunayo saloledwa kugwiritsanso ntchito njira imeneyo, koma tsopano pakufunika ayesere njira yomaliza yomwe ndi kupeza thandizo la ena, malinga ndi mmene mavesi akunenera.

Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam adalangiza amuna a Chisilamu kuti sayenera kuchita izi pokhapokha pazoipa zomwe mkazi wachita moonekera, monga chiwerewere. Komabe ngakhale pamulandu wachiwerewere ndi ina yoteroyo, chilango chake chiyenera kukhala chaching’ono ndipo ngati mkazi sakusintha, mwamuna saloledwa kumukwiyitsa:

“Ngati apezeka ndi chiwerewere chotseguka, muwasiye okha pamabedi awo ndikupereka chilango chochepa. Ngati akukumverani, musawakhumudwitse munjira iliyonse” (Tirmidthi)

Komanso, Mtumiki salla Allah alaih wasallam adaletsa kumenya kulikonse kosayenera. Amayi ena anadandaula kwa iye kuti amuna awo adawakwapula, atamva izi, Mtumiki adati:

“Amene amachita zimenezo (kumenya akazi awo) si abwino mwa inu” (Abu Dawood).

Pamenepa tikuyenera kukumbukira kuti Mtumiki salla Allah alaih wasallam adanenanso kuti:

“Wopambana mwa inu ndiye yemwe ali wabwino ku banja lake, ndipo ine ndine wabwino kwambiri pakati panu ku banja langa” (Tirmidthi).

Mtumiki adalangiza mkazi wina, dzina lake Fatimah bint Qais, kuti asakwatiwe ndi mwamuna wina yemwe anali kudziwika ndi kumenya akazi: “Ndinapita kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndipo ndinati: Abul Jahm ndi Muawiah akufuna kuti andikwatire.”Mtumiki (mwa uphungu) adati: “Kukamba za Muawiah, ndi wosawuka; ndipo Abul Jahm ali ndi chizolowezi chomenya akazi” (Muslim).

Tiyenera kuzindikira kuti Talmud imalimbikitsa kumenya mkazi ngati njira yopelekera mwambo. 39 Mwamuna sanapatsidwe malire pa zolakwa za mkazi zikuluzikulu, monga kupezeka ndi chiwerewere. Iye amaloledwa kumenya mkazi wake ngakhale atakana kugwira ntchito ya pakhomo. Komanso, sikuti angololedwa kupereka chilango chopanda malire kokha, koma analoledwanso ngakhale kumusiya ndi njala kapena kumuvulaza kumene. 40 Kwa mkazi yemwe mwamuna wake ali ndi khalidwe loipa lochititsa kutha kwa banja, Qur’an yapereka malangizo awa:

Qur’an 4:128: “Ndipo ngati mkazi ataona kuti ndi mwamuna wake akukanganakangana ndi kupatulana, palibe kulakwa pa iwo kuyanjana pakati pawo mwachimvano. Ndipo chimvano ndichabwino. (Munthu aliyense amaumirira chimene afuna). Chifukwa chakuti mitima ya anthu imaumirira umbombo. Koma ngati muchita zabwino ndi kuopa Mulungu, ndithudi, Mulungu ngodziwa nkhani zanu zonse zomwe muchita.”

Pamenepo, mkazi akulangizidwa kufunafuna chiyanjano ndi mwamuna wake (ngakhale popanda thandizo la banja lakwawo). Tidziwe kuti Qur’an sinalangize mkazi kuti atenge njira yosamuka malo ogona kapena kumenya; pofuna kumuteteza mkazi kuti asapwetekedwe ndi mwamuna wake yemwe ali ndi khalidwe loipa kale akamafuna kubwezera. Ndipo kumenyana kumene kungachitike pamenepo kudzabweretsa mavuto oopsa m’banja kuposa zabwino zomwe akuyembekezera kudzipeza. Ma ulamaa ena anati bwalo la milandu (khothi) likhonza kugwiritsa ntchito njira ziwirizi pa mwamunayo mmalo mwa mkazi … kutanthauza kuti: khoti limulangize mwamuna wopandukayo, kenako limuletse bedi la mkazi wake, ndipo pomalizira pake alandire chilango cha kumenenyedwa. 41

Pomaliza, Chisilamu chimapereka malangizo apamwamba kwa anthu okwatira, kuti ateteze mawanja awo pamene vuto lagwa. Ngati mmodzi wa iwo akubweretsa chiopsezo pakati pawo, winayo akulangizidwa ndi Qur’an kuti achite zotheka komanso munjira yabwino kuti apulumutse ubale wawo woyerawo. Koma ngati njira zonse zalephereka, Chisilamu chimalola kuti anthu awiriwo apatukane mwamtendere ndi mwachikondi.

Amayi