Kodi ndichiphunzitso cha Mtumiki kusala kwa tsiku la 15 Sha’baan?

Hadith yomwe yabwera polimbikitsa swalaat ndi kusala komanso kuchita ibaada yosiyanasiyana pa 15 Sha’baan, siili mugulu la ma Hadith ofooka (a dhwaeef) koma ili mugulu la ma Hadith opeka komanso abodza (Mawudhuu ndi Baatwil). Ndipo Hadith ikakhala choncho sitikuloledwa kuitenga ngakhale kuigwiritsa ntchito pa ntchito zabwino kapena pa zilizonsezo.

Ma Ulamaa anapeza kuti ma report omwe aikira umboni pa ibaada imeneyi ndi owonongeka, abodza, monga momwe akunenera Ibn Al Jawziy mu chitabu chake chotchedwa “Al Mawdhu’aati (Zopeka)” vol. 2/440-445, komanso Ibn Taymiya, Abu Shaamah ndi ma Ulamaa ena odalirika mu Ahlu Sunnah wal Jamaah.

Chisangalalo cha Nisfu Sha’baan, kuswali usiku wake ndi kusala usana wakewo, ndi bid’ah (Ibaada yongopekedwa) ndipo mu Deen ya Chisilamu mulibemo.

Usiku wa 15 Sha’baan ulibe Hadith ya Swaheeh; ma Hadith onse omwe adza pankhaniyi ndiopeka. Usiku umenewu ulibe kupatulika kulikonse kowerengera Qur’an ngakhale swalaat yawekha kapena jamaah.

Mtumiki swalla Allahu ‘alaih wasallam sanapange ndipo sanaphunzitse, ngakhale ma Swahaba.

Zomwe anayankhula Ulamaa ena zoti usikuwu uli ndi kupatulika kwake, zinachokera mma report ofooka.
📚Fataawa Islaamiya vol.4/511
📚Majmu’u Fataawa wa Rasaail Sheikh Uthaymin Vol.2/23

Ena mwa masiku omwe ndi Sunnah kusala ndi masiku atatu a mwezi uliwonse (13,14,15). Ndipo ngati munthu unazolowera kusala masiku atatu amenewa, ukhonza kusala mpaka pa 15 Sha’baan potengera chizolowezi chako ndi niyya yoti umasala Sunnah ya masiku atatu mwezi uliwonse. Koma osalipatula tsikuli mmasiku onse.

Allah ndiye Mwini Kudziwa Konse