Mafunso omwe timafunsa pa za deen timafuna kudziwa kuti kodi deen yathu tiyendetse bwanji. Timafuna kudziwa kuti kodi ibaada tingachite bwanji, nanga chikhulupiliro chathu tingachisamale bwanji.

Kudzera mu kufuna kudziwa zinthu momwemo, ambiri tili ndi chizolowezi chofunsa zinthu zomwe sizingatithandize, monga kufuna kudziwa komwe kuli manda a aneneri akale, kufuna kudziwa chiyankhulo cha majinn ndi zina zotero. Zimenezo ndizofunika kungokhala nazo chete chifukwa kuzidziwa ngakhale osazidziwa palibe chomwe tingapindule, koma mwina tingathe kupeza nazo mavuto chifukwa tikapanda kupeza mayankho okomera mtima wathu, tikhala tikufufuza mayankho, mapeto ake tipeza mayankho olakwika.

Chimodzimodzi pali nthawi zina timafunisitsa kudziwa zinthu zoti sizingachitike, mwachitsanzo kufunsa kuti “kodi Qiyaamah itati idze lero lino, zingakhale bwanji?” kumachita kuti tikudziwa kuti singadze lero ndilero, koma pali ndondomeko ya kudza kwake.

Kwa ma Sheikh, munthu osazindikira akafunsa zoti sizingachitike, sizoyenera kumuyankha, ngakhale zili zokondedwa kutero. Komanso ena anaona kuti ndizoipa kuyankha chifukwa ma Salaf Saalih ena sanali kuyankhula pazinthu zosachitika.

Imaam Ahmad anati:

إياك أن تتكلم في مسألة ليس لك فيها  – إمام ابن الجوزي في مناقب الإمام أحمد 1/245

Usayankhule zomwe ulibe nazo mtsogoleri (umboni)

Koma ngati wofunsayo cholinga chake chili kufuna kudziwa hukmu yake, kapena kuti ngati chingachitike angapange bwanji, komanso ngati akuyembekezera kuti chikhonza kuchitika nthawi iriyonse, palibe vuto.

صفة المفتي والمستفتي – حكم الفتوى فيما لم يقع صـ185