Kodi kumuona mkazi ndizololedwa usanapange naye nikkah?
Ndizololedwa kumuona mkazi yemwe wamufunsira ndipo mwatsimikiza kuti mukwatirana.
Malamulo a Chisilamu akunkera navutatuvabe poti anthufe tachulutsa kuyendera zomwe zimatisangalatsa osati zomwe Shariah imalola.
Choncho zomwe zikusemphana ndi shariah zasanduka kukhala zololezedwa pakati pathu, ndipo shariah yasanduka kukhala haraam.
Yemwe akugwiritsa sharia pano ali ngati yemwe wagwira mokulunga khala lamoto mmanja mwakwe. Inde, amaoneka ngati uncivilized, otsalira pakati pa anthu.
Mwachitsanzo tikanena kuti sizololedwa kukhala kapena kuyenda limodzi ndi mkazi pa awiriwiri, mkazi oti sim’bale wako kapena sunapange naye nikaah, zimakhala zovuta kuti titsatire poti timaona ngati sizingatheke kupanga nikaah anthu oti sanakumanepo (kugonana) komanso kuchiwandikira chiwerewere kumene.
Koma malamulo a Chisilamu ndi oti munthu sungakhale pa awiriwiri nkumacheza ndi mkazi wachilendo..
Pachifukwa ichi, zimakhalanso zovuta kumvesetsa tanthauzo la mau a Mtumiki salla Allah alaih wasallam onena kuti:
إذا خطب أحدكم المرأة فإن استطاع أن ينظر منها ما يدعون إلى نكاحها فليفعل
mmodzi wa inu akafunsira mkazi, ngati angakwanitse kuona zomwe zamuchititsa kuti amukwatire, akhonza kutero.
Pamenepa malinga ndi system yathuyathuyi mmene timachitira, timatenga mau oti …zomwe zampangitsa kuti amukwatire…  ndikuwatanthauzira mogwirizana ndi mmene timachitra zachisawawa: Timaona ngati akuti tikhonza kuyang’ana ngakhale maliseche ake; potitu munthu walero choyamba chomwe chimampangitsa kuganiza zofunsira banja, ndi chimenezo basi ndiye ndi zija ena amaloleza kugona ndi mkazi pambuyo poti angopanga khitbah (angofunsira) chongoti makolo mbali zonse akudziwa,  zimakhala ngati alandire license yopangira za haram.  Komanso ngakhale asanafunsire kumene, makolo asakudziwa,,,,,chifukwa choti akondana, basi amayamba kutengana koyenda, kujambulitsa limodzi, kudyera limodzi mma restaurant, kumwaza zithunzi mma status’mu atagwirana, akuti poti atsimikizirana kuti akwatirana….ka zinaa kamachitikanso ndithu.
Zimenezotu ku Chisilamu cha Qur’an ndi Sunnah kulibe. Koma zimaloledwa ndi ma Shia amene amatanthauzira Qur’an momwe akufunira komanso amakanira ma Hadith ma Swahaba. Iwo amaloleza kuti akhonza kumuyang’ana mkazi ngakhale maliseche … nanga munthu angasiyire pompo kuyang’ana ndi maso basi? kodi pamenepo chiletso cha Allah chija choti tisaiwandikire zinaa chiri kuti?
Ndipo musakhale pa awiri pamene ukumuonapo, upemphe kwa abale ake (mai ake, mlungo wake etc) komanso akhalepo
Ngati munthu sungakwanitse kumuyang’ana wekha, mwina chifukwa cha manyazi kapena kutangwanika, ukhonza kutumiza akazi omwe umawakhulupilira monga aliyense yemwe si wachilendo kwa iyeyo amene angakubweretsere zoona.
Anafika munthu kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndipo anamuuza zoti akufuna kukwatira mzimai wa ku Madina. Mtumiki anati:
wamuona? anati: ayi. Anamuuza kuti pita ukamuone chifukwa mmaso mwa ma Answaar (anthu a ku Madina) muli zabwino
Maonedwe Ake:
Mwamuna akhonza kumuona mkazi munjira izi:
Mkaziyo akhale ndi azibale ake monga makolo kapena aliyense wokwatirika kwa iye, ndipo amuyang’ane khope yake, manja, mikono, mapazi, ndi zomwe zimaonekera panja ndipo asapyole zimenezo, komanso mopanda chilakolako.
Allah Ta’la akunena kuti
ولا يبدين زينتهن إلا ما ظهر منها
Ndipo asaonetse zodzikongoletsa zawo kupatula zomwe zaonekera mwa izo
Waloledwa kuona koma osati kugwira. Choncho sakuloledwa kumugwira thupi lake ngakhale manja chifukwa ndi haram kwa iyeyo.
Akhonza kumuyang’ana kangapo ngati angafune. Komanso ndi zololedwa kumuona mwini wakeyo asakudziwa, bola osapyola malire a malo ololedwa kuona. Izi ndi malinga ndi ma Hadith komanso mmene ankachitira ma Sahaba.
Ref:
#Surah Al Moor/31
#Fat’hul Qadeer vol. 8/99
#Fat’hul Baari 9/181-2
#Noorun ‘alaa Ddarbi Sheikh bun Baaz
#Sheikh Muhammad Salih Al Munajjid
#Sheikh Abdullah bun Jibreen