Munthu wina aliyense zimatengedwa zoyankhula zake kapena kusiyidwa, kupatula Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam, zoyankhula zake sitimayenera kudzisiya. Aalim wina aliyense ali ndi ilm yomwe ili ndi zoona komanso zabodza, zabwino komanso zolakwika. Choncho kwa amene akufuna kutenga ilm kuchokera kwa ma ulamaa, akuyenera kutenga zomwe zili zolondolazo, zoona komanso zabwino mu deen, ndipo adzitalikire zomwe zili zoipazo komanso zosemphana ndi shari’ah. Tili ndi ma Sheikh ambiri amene amakhala akukambidwa ndi mbiri zoipa, ma Sheikh amenewo amakambidwa chifukwa cha zolakwika zochepa zimene ali nazo, zomwe zimangofunika kuwawongolera,,,poyerekeza ndi migolomigolo ya ilm yomwe akusungira. Choncho zolakwika zimenezo zikamaoneka mwa ma sheikh ena, anthu amadzitenga ndikumuweruza nazo sheikhyo, mpaka kulengedzetsa kuti ameneyu ndi sheikh oipa osocheretsa komanso timutalikire, mmalo molangizana kuti tidzitalikire zomwe tadzizindikira kuti ndi zolakwikazo ndikutsatira zabwinozo. Sitikuyenera kumawanyoza ma sheikh ndi ma ulamaa otere, powatchula kuti osokoneza, osocheretsa; izi timasiya kuphunzitsa anthu zofunika kutenga, mapeto ake timakhala busy kuphunzitsa anthu za kuipa kwa Sheikh. Ndi zololedwa kutenga kwa ma ulamaa ilm yomwe ili yolondola komanso yothandiza mu deen’yo, osati kungoletseratu zokambidwa zawo zonse chifukwa cha kulakwika pa mas’ala amodzi awiri atatu. Tonsefe tikudziwa kuti ma Ulamaa ndi omwe akhalira mipando ya Atumiki pofalitsa uthenga komanso kugwira ntchito ya deen pa dziko lino la pansi. Kungosiyana kuti awa samalandira wahyi, komanso ali ndi zolakwika pa ntchito yawo, zomwe zimakhululukidwa komanso ife timayenera kudzitaya. Amenewa ndi anthu olemekezeka komanso ndi zolengedwa zomwe zili zabwino kwambiri pambuyo pa Atumiki. Ndi nyali zomwe zimaunikira anthu mumdima wa umbuli, komanso amawaongolera ku njira ya chiwongoko. Ma Ulamaa ndi anthu amene amaopa Allah kwambiri kusiyana ndi ena onse, chifukwa iwowo amakhala akudziwa ukulu wa Allah komanso tanthauzo la kupezeka kwawo pa dziko lino lapansi ndi udindo womwe anapatsidwa umene adzafunsidwe Tsiku la Qiyamah. Allah Ta’la akunea za anthu amenewa mu Surah Faatir Aayah 28: إِنَّمَا يَخْشَى اللَّهَ مِنْ عِبَادِهِ الْعُلَمَاءُ Ndithu odziwa ndi amene amamuopa Mulungu mwa akapolo ake Anthu awa ndi amene amasunga Shariah komanso asenza ilm ndipo sangafanane ndi wina aliyense, monga mmene akunenera mu Surah Al Zumar Aayah 9: قُلْ هَلْ يَسْتَوِي الَّذِينَ يَعْلَمُونَ وَالَّذِينَ لَا يَعْلَمُونَ Nena (kwa iwo, iwe Mtumiki): “Kodi amene akudziwa ndi amene sakudziwa, ngofanana?” Apatu akufuna kutiuza kuti sangafanane ndithu, Allah Ta’la amawakweza pamwamba anthu omwe ali ozindikira, monga mmene akunenera mu Surah Al Mujaadalah Aayah 11: يَرْفَعِ اللَّهُ الَّذِينَ آمَنُوا مِنْكُمْ وَالَّذِينَ أُوتُوا الْعِلْمَ دَرَجَاتٍ Mulungu awakwezera (ulemerero) mwa inu amene akhulupirira ndi amene apatsidwa nzeru. Komanso potitsimikizira kuti anthu amenewa ndi olemekezeka pamaso pa Allah, anawaika level #3 yoikira umboni pa umodzi wa Allah, monga mmene akunenera mu Surah Aali Imraan Aayah 18: شَهِدَ اللَّهُ أَنَّهُ لَا إِلَهَ إِلَّا هُوَ وَالْمَلَائِكَةُ وَأُولُو الْعِلْمِ قَائِمًا بِالْقِسْطِ لَا إِلَهَ إِلَّا هُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ Mulungu (mwini) akuikira umboni kuti: “Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye basi.” Ndipo akuikiranso umboni (zomwezi) angelo ndi ENI NZERU (kuti Iye) ngokhazikitsa chilungamo. Palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya. Choncho izi zikukwanira kwa ife, komanso ndi waajib kumulemekeza yemwe Allah Ta’la wamuika pafupi ndi Iye Mwini poikira umboni za Tawheed yake komanso kuona kwa Umulungu wake. Komatu ngakhale zili chonchi, kuli anthu ena amene anapatsidwa mayesero a kufooka kwa iman koopsa, komanso kuipa lirime komwe eni akewo sazindikira ngakhale atauzidwa motani. Amangoona kuti ali pa chilungamo basi. Ndiye amakhala pa chintchito chomangofufuza njira zonyozera ma sheikh, ma ulamaa komanso atsogoleri a Deen; amalolera kuononga nthawi yawo, chuma chawo komanso ulemu wawo, nkudzigulitsa zonsezi ndi kunyoza ma ulamaa, cholinga chowasitsa nyota komanso kuti zoyankhula/zolemba zawo zisagwire ntchito yowongola Ummah. Kumachita iwo anagwira ntchito imeneyi ndi ikhlaas popanda kuyang’ana zofuna za anthu, analumbira pamaso pa Allah kuti adzateteza deen yake mpaka imfa idzawapeze, kuti mpaka Asilamu adzagwiritse njira ya Haqq, ndikuwachenjeza omwe ali otailira mu njira ya Haqq. Apa ndikamati ma Ulamaa, ma Sheikh, ndikutanthauza aliyense amene waphunzira deen ndikumagwira ntchito yofalitsa, kuyambira ma ulamaa akalekale kufikira alero lino amene akupanga graduate komanso amene akupitiriza maphunziro awo mma school osiyanasiyana, akuyenera kulemekezedwa komanso alemekezane pakati pawo. Mlembi wa buku lina la Aqeeda, Al Tahaawi rahimahu Allah, akunena mu vol.2 page 740 kuti: “…ndipo ma ulamaa omwe anapita mbuyomu kuyambira ma Sahaha. ma Taabieen komanso ma Imaam ena onse a pa Chilungamo (pa chi Arab amatchedwa ma Salaf Ssaalih), ndi anthu abwino kwambiri komanso ndi ozindikira Chiphunzitso cha Chisilamu cholondola – sakuyenera kutchulidwa anthu amenewa posakhala mwa ubwino, ndipo amene angawatchule anthu amenewa mowanyoza, ndithu sali munjira (ya Mtumiki)”. Nchifukwa chakenso ma Ulamaa a nthawi imeneyo anali kuchenjeza kawirikawiri za kunyoza ma ulamaa komanso kuwayankhulira zosakhala bwino. Al Haafidh bn ‘Asaakir rahimahu Allah akunena mu book lake lotchedwa Tabyeenu Kadhbi Al Muftareen page 28: “Ndipo dziwa iwe m’bale wanga – Allah atidalitse ndi Chisangalalo chake komanso atipange kukhala amodzi mwa omuopa Iye kumuopa kwenikweni – (dziwa) kuti nyama ya ma ulamaa ndi poison; kawirikawiri Allah amamuyalutsa amene akuwanyoza ma ulamaa…” Nkhani inachokera Imam Ahmad bn Hanbali rahimahu Allah anati: “Nyama ya ma ulamaa ndi ya poison; yemwe fungo lake lingamufikire amadwala, ndipo yemwe angadyeyo amafa”. Al Mu’eed fi Adab Al Mufeed wal Mustafeed pge71 Apatu ma Imam amenewa akutanthauza kuti kudya nyama ya ma ulamaa (kuwaipitsa ndi kuwanyoza), kumampititsa munthu mchionongeko. Abu Sinaan Al Asadi rahimahu Allah anayankhula mu Tarteebul Midraak 2/14 kuti: “Munthu ofuna kuphunzira mas’alah a mu deen akayamba ndi kuphunzira kujeda anthu komanso kuwayankhulira zoipa asanaphunzire mas’alawo, adzasangalala bwanji?”. Ndi zomwe tikudziona masiku anaozi, munthu sanayambe nkuphunzira deen komwe, kuyamba kupanga judge ma ulamaa, oteroyo angaphunzire bwanji? ndu Aalim wanji wabwino kwa iye amene angamphunzitse ndikupindula?? Imam Ahmad bun Al Adhra’i rahimahu Allah ananena mu _Al Raddul Waafir_ Pge.197: *”Kujeda ma Ulamaa, makamaka akuluakulu, ndi tchimo lalikulu”*. CHILANGO KWA OMWE AKUNYOZA MA ULAMAA 1. Oterowo akuvala dzina la u faasiq (otuluka mmalamulo a Mulungu), pambuyo poti anali wa imaan. Allah Ta’la akunena mu Surah Al Hujuraat Aayah 11: ا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا يَسْخَرْ قَوْمٌ مِنْ قَوْمٍ عَسَى أَنْ يَكُونُوا خَيْرًا مِنْهُمْ وَلَا نِسَاءٌ مِنْ نِسَاءٍ عَسَى أَنْ يَكُنَّ خَيْرًا مِنْهُنَّ وَلَا تَلْمِزُوا أَنْفُسَكُمْ وَلَا تَنَابَزُوا بِالْأَلْقَابِ بِئْسَ الِاسْمُ الْفُسُوقُ بَعْدَ الْإِيمَانِ وَمَنْ لَمْ يَتُبْ فَأُولَئِكَ هُمُ الظَّالِمُونَ E, inu amene mwakhulupirira! Amuna asanyoze amuna anzawo; mwina (onyozedwa) nkukhala abwino (kwa Mulungu) kuposa iwo (onyoza). Nawonso akazi asanyoze akazi anzawo; mwina onyozedwa nkukhala abwino (kwa Mulungu) kuposa iwo (onyoza). Ndipo musatukwanizane pokumbana mitundu kapena kuitanana ndi maina oipa. Taonani kuipa komuyitanira munthu ndi dzina loti fasiki (wotuluka m’malamulo a Mulungu) atakhulupirira kale; ndipo amene salapa (ku zimenezi), iwo ndiwo (ochimwa) odzichitira okha chinyengo. 2. Amenewo amakhala kuti atsatira sunnah yoipa, choncho amatsenza zoipa zawo komanso zoipa za omwe awatsatira mpaka tsiku la Qiyaamah. Chifukwa oitanira ku zabwino ali ngati yemwe wachita, ndipo oitanira ku zoipa chimodzimodzi yemwe wachita. Allah Ta’la akunena mu Surah Yaaseen Aayah12: وَنَكْتُبُ مَا قَدَّمُوا وَآثَارَهُمْ …ndipo tikulemba zimene atsogoza (m’dziko lapansi m’zochita zawo) ndi zomwe amasiya pambuyo (atafa, zonkerankera mtsogolo)… 3. Amenewo ndi zolengedwa zoipa: Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena mu hadith yomwe inachokera kwa Imam Ahmad, kuchokera kwa Abd Rrahmaan bun Ghanm radhia Allah anhu: “abwino mwa akapolo a Mulungu ndi amene amati akaonedwa, amachititsa kumkumbukira Mulungu. Ndipo oipa mwa akapolo a Mulungu ndi amene amayenda ndi miseche, amalekanitsa pakati pa okondana….”. Anthu oipa choterewa amakhala nthawi zonse akufufuza ma mistake a anthu olemekezeka komanso odalitsidwa. Akapeza mistake imodzi, imakhala ntchito yofuna kuwaipitsira ntchito zawo zodalitsika pamaso pa Allah. Kutaya nthawi. 4. Anthu amenewa amakhala source ya nkhondo yolimbana ndi Allah; Hadith imene anailandira Al Bukhari, Allah Rabbul Aalameen akunena mu Hadith Al Qudsi: “yemwe angadane ndi waliyyu wanga, wadziputira nkhondo”. 5. Anthu amenewo akupereka mwayi wa kuyankhidwa kwa dua ya Aalim woponderezedwa: Ngati dua ya munthu aliyense oponderezedwa ilibe chotchinga pakati pake ndi Allah .. mukuona bwanji dua ya Aalim, waliyyu wa Allah? Allah akunena mu Hadith al Qudsi: “akandifunsa ndimpatsa, ndipo akathawira kwa ine kuchokera kuzoipa, ndimteteza” anailandira Al Bukhari Imaam Al Hafidh ibn Abbas Al Hassan bn Sufyaan anadzayankhula kwa munthu wina amene anamuyankhulira zosakhala bwino: “Ee, iwe, ndakupilira nthawi yaitali pano ndili ndi zaka 90; choncho muope Allah powalemekeza ma Sheikh, chifukwa kutheka kuyankhidwa dua yawo yokupangira iwe” Siyari A’laamu Al Nubalaa vol.14 pge159 6. Allah amamulanga malinga ndi ntchito yakeyo: Malinga ndi kuti aliyense adzalandira malipiro oyenera ntchito zake, onse omwe amanyoza ma ulamaa akuyenera kusamala chifukwa chilango cha ntchito imeneyi ndi chowawa. Umakhala kuti ukulimbana ndi omwe akuitanira kuchiwongoko pokhotetsa da’wah yawo kuti isanduke chisocheretso. 7. Amapatsidwa mavuto a imfa ya mtima: Al Haafidh ibn Asaakir rahimahu Allah anati: ndipo yemwe atulutse mau onyoza opanga criticize ma ulamaa, Allah amupatsa imfa ya mtima: فَلْيَحْذَرِ الَّذِينَ يُخَالِفُونَ عَنْ أَمْرِهِ أَنْ تُصِيبَهُمْ فِتْنَةٌ أَوْ يُصِيبَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ Achenjere amene akunyozera lamulo lake kuti mliri ungawapeze, kapena kuwapeza chilango chowawa.Surah Al Nour Aayah 63 Ananena Mukhallad: Mzathu wina anatilongosolera kuti anakambapo tsiku lina ndi Al Hassan bn Dakwaan zoipa za munthu wina, ndipo bin Dakwaan anati: mmh! usakambe zoipa za ma ulamaa, Allah awuphetsa mtima wako. 8. Yemwe anganyoze ma ulamaa pa nkhani za deen komanso pa zolankhula zawo za malamulo a Allah, ndithu ali pa chiopsezo chachikulu, ngati angamachite zimenezo akudziwa. Allah Ta’la akunena mu Surah Al Tawbah Aayah 65-66 kuti: قُلْ أَبِاللَّهِ وَآيَاتِهِ وَرَسُولِهِ كُنْتُمْ تَسْتَهْزِئُونَ * لَا تَعْتَذِرُوا قَدْ كَفَرْتُمْ بَعْدَ إِيمَانِكُمْ Nena: “Mumachitira Mulungu ndi aya zake ndi Mtumiki wake zachipongwe?” Musapereke madandaulo (abodza) ndithu mwaonetsera ukafiri wanu poyera, pambuyo pakukhulupirira kwanu (kwabodza). Ngati gulu lina mwa inu tilikhululukira (litalapa), gulu lina tililanga chifukwa cha kupitiriza kulakwa kwawo.” 9. Apatsidwa mathero oipa (na’udhu billah): Al Qaadhi Al Faqeeh Al Shaafi’iy Muhammad bn Abdillah Al Zubaidi, anabadwa mchaka cha 710 AH, maa shaa Allah mkuluyu anaphunzira ndithu, anapanga sharh buku lotchedwa Al Tanbeeh ma volume 24; anali wophunzira moti ankatulutsa ma fatwa ndithu, ma student ake anachuluka ku Yemen ndipo anatchuka kwambiri. Koma pambuyo pa kutchuka kumeneku…; Al Jamaal Al Misriy akulongosola kuti anamuona panthawi imene ankamwalira, lirime lake linatuluka panja ndikusanduka lakuda…atafufuza, anapeza kuti mkuluyu anali munthu wabwino komanso olimbikira, koma kodi zomwe zinachititsa kuti pa imfa yake atuluke lirime ndikukhala lakuda ndi chani? atafufuza anapeza kuti mbali ina kuseliku anali kulimbana ndikunyoza Imaam wamkulu, Imam Sheikh Muhyi Deen Al Nawawi, moti anamuipitsira mbiri yake mpaka ophunzira omwe amatuluka mwa iye anali odana ndi Imam Al Nawawi, nawonso anali kuphunzitsa zodana ndi Imam Al Nawawi. Izi zikupezeka mu Al Durar Al Kaaminah vo.4 page 106, komanso mu I’laamu bihurmati Ahli Al Ilm wal Islaam pge. 322. Apatu tikuphunzira kuti ma sheikh sibwino kunyozana ma sheikh nokhanokha. Mwaphunzira, lemekezani maphunziro a ma sheikh ena amene anapita inu musanabadwe, iwo anatenga zawo, nanu pangani zanu zoti mutenge, muwasiye anthu ali muchiwongoko, koma musachite zoti mutenge matembelero chifukwa cha kunyoza ena. Mtumiki salla Allah alaih wasallam analetsa kutukwana tambala chifukwa amadzutsa ku Swalaat, ngati analetsa kunyoza nkhuku, what more Aalim yemwe ndi warathat Anbiyaa, oitanira ku njira ya Allah komanso zolengedwa zolemekezeka pambuyo pa Atumiki? Abu Al Dardaa radhia Allah anhu ananena kuti: Kodi ife tinali ndani kupanda mau a ma fuqahaa (ma ulamaa)? Al Hassan Al Basri rahimahu Allah anali kuyankhula mu Jaami’u Bayaan Al ‘Ilm_ p236 kuti: Dunia yonseyi ndi mdima wokhawokha, kupatula pamene pasokhana ma ulamaa. Komanso anati: Ndithu anthu, kuti akhale anthu, amadalira akuluakulu awo (ma sheikh), kodi akapita ma sheikhwo, akhala chotani? Dziwani kuti kupereka mavuto kwa ma Ulamaa ndi chimodzimodzi kupereka mavuto ku Qur’an ndi Sunnah. Pomaliza, tiyeni tikhale olimbana ndi kusakasaka ilm nthawi zonse, chifukwa onse amene anadzipereka kufalitsa ilm, samatenga ilm kwa Shytwaan koma kwa Allah ndi Mtumiki. Choncho ife ngati tili ndi matenda opatsidwa ndi shytwaan ndiye tikufuna kulowelera pakati pa ma ulamaa ndi ophunzira awo cholinga tisokoneze, tidziwe kuti tikuiputa nkhondo imene sitingawine, mapeto ake ndi kudzenje la moto komwe chipulumutso chake tidzachisiye pa dziko lino ndipo sizidzatheka kuti tidzabwelere kudzachitenga kuti tikapulumuke. Kunyoza ma Sheikh ndi ntchimo lalikulu, ndipo zimakubwelera wekha onyozawe .. Msilamu adzitalikitse. Chenjezo kwa onyoza ma Ulamaa Khalidwe lonyoza Sheikh wina aliyense mu umoyo wa munthu lisamachitike. Chifukwa zimapereka ulesi kwa amene akufuna kuphunzira kuchokera kwa ma Sheikh amene tikuwanyozawo. Ngati mukuzidziwa zoipa za masheikh ena, zisiyeni zisawakhunze ena, ndipo tibweretsereni zabwino zawo zokhazo. Allah Ta’la anatiletsa kunyoza anthu omwe amapanga shirk, tikanyoza anthu oterowo timapeza nsambi, komatu ndi anthu oti sangatithandize chilichonse…inu ndiye mukunyoza ma ulamaa … zomvetsa chisoni. Basi Allah atiwonetse njira yoongoka إهدنا الصراط المستقيم يا رب