KODI NDIZOLOLEDWA KUMASULIRA KHUTBAH YA JUM’AH MUCHIYANKHULO CHINA ZITAKHALA KUTI ANTHU OMVETSERA SAKUVA CHIARABU?

Nkhaniyi anthu amasiyana zokamba zenizeni chifukwa choti nthawi ya Mtumiki kunalibe kumasulira, komanso panalibe chifukwa chomasulira khutbah poti Asilamu onse anali odziwa Arabic. Choncho palibe umboni wa kuletsa kapena kuloleza.

Gulu loyamba la ma Ulamaa linati ndizoletsedwa kumasulira khutbah ya pa minbar ya Jum’ah kapena Eid muziyankhulo zina ncholinga chofunisitsa kusunga chiyankhulo chomwe Allah anasankha kuti chigwiritsidwe ntchito, komanso potengera momwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndi ma Swahaba ake anali kuchitira, popanga khutbah mu chiarabu chokha mmadera omwe sanali achiarabu. KOMA zikatero ndiye kuti aliyense akukakamizidwa kuphunzira Chiarabu kuti azitha kumva khutba yonse popanda kumasulira.
Amenewo anathera pamenepo, ndipo awa amatanthauza kuti kupanga khutba yonse muchiyankhulo china…

Pomwe gulu lachiwiri linati ndizololedwa kumasulira, ngati omvera kapena ambiri mwaiwo sakudziwa Arabic, potengera kuti cholinga cha khutbah ndiko kuwalongosolera anthu kuti amvetsetse zomwe Allah awalamula kuti azitsatira, komanso machimo omwe anawaletsa, komanso kuwawongolera kumakhalidwe olemekezeka ndi kukhala ndi mbiri zabwino. Izi nzofunikira kuti anthu azimva zomwe khatweeb akunena makamaka munthawi zino zomwe Asilamu akusocheretsedwa.

Tsopano ngati kufikitsa ilm ya deen kwa anthu kuli koti sikungakhale kwaphindu kwa awo osadziwa Arabic chifukwa choti akuuzidwa muchiyankhulo chosamveka kwaiwo, pamenepo pakubwera kuloleza kumasulira ndipo palibe vuto lirilonse koma ubwino wokhawokha.
*Kuyankhula mu Arabic ndikumasulira.

Ngati pakati pa opanga khutba pali ena omwe amadziwa chiyankhulo chomwe amachimva anthucho, akuyenera kuphatikiza zoyankhula ziwirizo, choncho papezeka maslaha awiri: kupanga khutbah mu chiarabu, komanso kuwapanga anthu kuti amve ulaliki powamasulira. Zonsezo ndizabwino ndipo sizingakhale zoletsedwa pokhapokha ngati patabwera umboni wakuletsa.

UMBONI WA ZIMENEZI:
Alipo maumboni ambiri pazomwe tikunenazi, monga:
1. Kuchokera mu Sûrah Ibrahim Aayah 4:

وَمَا أَرْسَلْنَا مِن رَّسُولٍ إِلَّا بِلِسَانِ قَوْمِهِ لِيُبَيِّنَ لَهُمْ ۖ
“Ndipo sitidamtume Mtumiki aliyense koma ndi chiyankhulo cha anthu ake kuti awafotokozere.”

Mtumiki anatumizidwa kudziko lonse, kudzera ku Arabia komwe chiyankhulo chawo ndi Arabic… kwaomwe samamva Arabic sizikutanthauza kuti Mtumiki wawo si Iye, koma kuti akungoyenera kuchiphunzira, kapena kutanthauzira.

2. Kuchokera mu Hadith, Mtumiki salla Allah alaih wasallam analamula Zaid bun Thaabit kuti aphunzire chiyankhulo cha Chiyuda kuti aziwalembera komanso aziwalalikira ndi maumboni omveka mChiyankhulo chawo.

3. Pamene ma Swahaba anali kupita kukamenya nkhondo kumaiko a chikunja ku Persia ndi Rome, sanali kufikira kuwathira nkhondo koma anali kuyamba kuwalalikira, kuwaitanira ku Chisilamu, ndipo pakati pa woyankhula pamapezekapo mtanthawuziri… Pamene analanda maiko achikunja anawalalikira anthu mu chiarabu ndikuwatanthauzira, kenako anali kuwalimbikitsa kuti aphunzire chiArabu. Omwe anali osadziwa chiarabu mwaiwo, anali kuwaitanira muchiarabu ndikuwatanthauzira mChiyankhulo chawo.
Choncho, potengera mmene ma Sahaba anali kuchitira akapita maiko ena kumapanga Da’wah, njira imeneyi ndiyomwe ikuyenera kugwiritsidwa ntchito pamene tikuwalalikira anthu omwe sakudziwa Arabic, makamaka munyengo zathu zomalizazi komanso pamene Chisilamu chikuonekabe kuti nchachilendo pakati pa anthu.

Nanga anthu mmene akubwelera ku Chisilamu masiku ano, tiwayankhulire Arabic yosamasulira nkumati amvapo chani? ) Pomwe kale ma Swahaba anali kulalikira nkumatanthauzira mu chiyankho china. Ife lero tikuletsana chifukwa chani?

Tipanga bwanji Da’wah muchiyankhulo choti omwe tikufuna kuti asinthewo sakumva?

 

KHUTBA NDICHANI?
Tisatalikire kwambiri, amene munafika pa kalasi munaphunzira kachitabu kaja kotchedwa “Khitwaaba” kapenanso munawerenga mwapadera popanda kuponda pakalasi,, kuchokera mmenemo, mukudziwa kuti
الخطابة هي فن مشافهة الجمهور والتأثير عليهم واستمالتهم
Muwapanga bwanji anthu ta’theer komanso istimaal pomwe sakumva zomwe mukuyankhula?

Khutba ndiko kuwayankhula anthu… izi zimafunika kuona kuti kodi nkhani yomwe ndikiluyenera kuwauza, kuwaphunzitsa kapena kuwachenjeza kapena kuwasangalatsa nayo anthu pa Jum’ah ndiyotani? Tsopano kuti anthu akaimve, mukuyenera kupeza nthawi yoitanthauzira .. kaya pambuyo pa khutbayo kapena pambuyo pa Swalat.

Tawerengani mu bulu lotchedwa الخطبة والخطباء
Allah Ndiye Odziwa Zonse
#SheikhAbdulAzizBunBaaz