Pali anthu ena anazolowera kulumbira m’Dzina la Allah, mwachitsanzo kunena kuti “Wallahi…”, ndipo amachitenga kukhala chizolowezi chawo pakuyankhula kulikonse, zofunikira ngakhale zosafunikira.

Chizolowezi choterechi ndicholakwika kwambiri. Ndizosaloledwa kuchulukitsa kulumbira chifukwa kumeneko ndikusewera ndi Dzina la Allah ndi kulichotsa ulemu wake.

Tikam’peza munthu wolumbiralumbira pazilizonse, tidziwe kuti amakhala wonama kwambiri ndipo tisamutsatire zoyankhula zake ndipo timulangize kusiya mchitidwe umenewo, chifukwa Allah Ta’ala ananena kuti:

وَلَا تُطِعْ كُلَّ حَلَّافٍ مَهِينٍ

Ndipo usamumvere aliyense wochulukitsa kulumbira ndiponso woyaluka Surah Al Qalam #10

Mu Hadith ina, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati ndithu mwa anthu atatu omwe Allah sakawayankhula Tsiku la Qiyaamah komanso sakawayeretsa machimo awo ndipo adzapeza chilango chowawa: Munthu yemwe samagula katundu popanda kulumbira, ndipo samagulitsa popanda kulumbira. Al-Tabaraani – Al-Mu’jamul Kabeer 6/346

Komanso mu Tafsir ya aayah yonena kuti:

وَاحْفَظُوا أَيْمَانَكُمْ

Ndipo sungani malumbilo anu, (musaswe chomwe mudalumbirira) Surah AlMaaidah #89

Akutanthauza kuti musalumbire kupatula pomwe zafunikira kuti mulumbire, pofuna kudzipulumutsa kudzera muchoona chomwe mukuyankhula.

Choncho tisaike kulumbira muchiyankhulo chathu kukhala ngati fashion, chifukwa malumbirowa tidzakafunsidwa nawo ndipo tidzalangidwa akadzapezeka kuti analibe chifukwa.

>Zaadul Mustaqna’  Al-Fawzaani 2/292<