KULERA
Uku ndiko kutalikitsa nyengo ya pakati pa ana awiri, komanso kuika malire a chiwelengero cha ana omwe munthu akufuna kukhala nawo.
Msilamu kuchita zimenezi popanda chifukwa chovomerezeka, ndi kusemphana ndi malamulo a Chisilamu. Chifukwa munthu amaoangidwa kudzera mu kuberekana. Ngakhale Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam analamula kuti tikwatire mkazi wobereka (oti atibelekere ana ochuluka)
Ma ulamaa ananena kuti ndizofunika kukwatira mzimai amene tikumudziwa kuti ndi obereka.
Kuti tionesetse, tipeza kuti chifukwa chotengera njira za kulera ndi kuopa kuti sitikwanitsa kuwadyetsa kapena kuwalera. Komatu zifukwa zake zikakhala zimenezi ndiye kuti tikumudelera Allah kuti sangatipatse rizq lokwanira. Chifukwa mwiniwakeyo ananena kuti
analenga zonse ndipo ndi amene amadzidyetsa. Surat Hud aayah 6.
Komanso mu Surat Al Ankabut aayah 60 akunena kuti
palibe cholengedwa chomwe chimanyamula rizq  lake posakhala kuti Allah ndi amene amachidyetsa ndi inu momwe…
Ndipo Allah ananena kwa iwo amene amapha ana awo, potaya mimba ndi njira zina chifukwa cha kuopa umphawi, kuti:
“ifeyo ndi amene tidzawadyetsa” Surat Al Israai aayah 31.
Tsopano ngati chotengera kulera chili kutopa ndi kulera ana, kumeneku ndi kulakwitsa kwakukulu … kodi ndi angati amene akhalapo ndi ana ochepa koma alephera kuwalera? Nanga ndi angati omwe akhalapo ndi ana ambirimbiri koma kwa iwo kunafewetsedwa kuwalera? Si Mulungu Mmodzi yekhayo amene amawadyetsa ena ena nkuwamana? Ndiye ife tikufuna tidzisankhire, kupikisana ndi kusankha kwa Mulungu?
Kuvuta kapena kufewa kwa kulera kumabwera ndi Allah, malinga ndi mmene ife tikugwilira zintchito zathu. Munthu ngati angayezamire mwa Allah ndikumuopa zenizeni, amamufewetsera moyo wake, monga mmene akunenera pa Surat Al Talaaq aayah 4 kuti 
“ndipo yemwe aope Mulungu,  amufewetsera zochitika zake.”
Apa zaonekeratu kuti kuika malire (kulera)  kukusemphana ndi malamulo a Chisilamu.
Komatu pali nthawi zina zake zomwe ndi zololedwa kuchepetsa kubereka. Iyi ndi nthawi yomwe Allah ananena kuti musadzipatse mavuto,  musadziononge,  musaike moyo wanu pachionongeko. Nthawi imeneyi ndi imene mzimai amatha kukhala ofooka moti kukhala ndi pathupi kukhonza kumuonjezera kufookako kapenanso matenda ena. Pamenepa mkazi ndi ololedwa kugwiritsa ntchito njira zoletsera mimba mukanthawi kena kake,  ngati mwamunayo atalola.
Chisilamu sichikulimbikitsa kusiira pa njira kubereka.
Mu Majmoo’ Fataawa ya Sheikh Ibn Baaz,  analongosola kuti kuika malire obelekera (kulera) lisakhale lamulo loikidwa kuti anthu ayenera kubereka ana awiri okha,  monga mmene zikhalira masiku ano mmaiko ena mpaka kupereka chilango kwa anthu obereka ana opitilira awiri. Zimenezo ndi Haram komanso kupondereza ufulu wa munthu. Zololedwa ndi zoti munthu ndamene angaone yekha zifukwa zompangitsa kuti asapitilire kubereka, zikhonza kukhala zosavomerezeka ndi anthu (omwe anayambitsa njira za makonozi), koma zikhale zogwirizana ndi shariah (malamulo a Qur’an ndi Sunnah), monga ngati mkazi ali ndi matenda a mchibelekero kapena ali ndi matenda oti akhonza kupereka vuto ku mimba yake, komanso zikhale kuti zatsimikizidwa ndi ma dokotala, zikuloledwa kwa iyeyo kuima osabereka mpaka atadzachira matendawo ndipo ma dokotala adzanene kuti vutolo latha.
Ndipo ngati ali ndi ana ambiri ndiye akuopa kuti saakwanitsa kulera moyenera, akhonza kudikira chaka kapena zaka ziwiri osakhala ndi mimba, monga mmene Allah Ta’la akunenera mu Surat AlBaqarah  233:
“Ndipo azimai ayamwitse ana awo kwa zaka ziwiri zatunthu, kwa amene angafune kukwaniritsa kuyamwitsa”.
Njira zomwe angatsatire kuti zaka ziwirizi akhale osabereka ndi izi:
– Kutayira madzi panja: njira iyi ndiyololedwa kwa amene agwirizana kuti agwiritse ntchito,  ngakhale ili yopanda guarantee ndifukwa kutheka kukomedwa nkuiwala…mapeto ake mimba kupezeka.
– Kupewa kukumana pamene mkazi ali mu ovulation period (nthawi imene mimba imatha kubwera mosavuta ngati Allah wafuna).
Kudzipangitsa kuti usiye kubereka popanda vuto lirilonse lomwe lingakuononge, ndikulakwa kwakukulu.
Ndipo vuto lisakhale kusowa chakudya,  ena smachotsa mimba yotha myezi 4 chifukwa choopa kuti amudyetsa chani. Sikuti chakudyacho Allah angakumaneni mpaka moyo wanu wonse,, iye akunena mu Surat Al Israai 31:
“ndipo musaphe ana anu chifukwa choopa njala,  ndithu ife ndamene timawadyetsa ndi inu nomwe… kuwaphako ndi tchimo lalikulu zedi”.
Qur’an inatiuza kale kale njira zabwino koma sitinadzizoloweze pakati pathu,  pa chifukwa ichi zikupezeka kuti njira ziwiri zimenezi nzachilendo ndipo tikukopeka ndi njira zobweretsa anthu omwe zolinga zawo ndi kulimbana ndi kuchepetsa chiwelengero cha anthu, chapansipansipo akupanga target Chisilamu.
Kuti tifunse chifukwa choyambilira chomwe chinabweretsa njira za kulera zomwe tikutengera masiku ano, tipeza kuti akuti chifukwa choti anthu tachulukana ndipo malo palibe, komanso munthu amavutika kudyetsa ana akamuchulukira. Zifukwa zake ndi zimenezo. Kodi mesa dzikoli tinalipeza? Tikamatero tikufuna kutanthauza kuti Allah anatilengera dziko laling’ono?
Pamenepo atibweretsera njira zoipa kwambiri komanso zoononga chilengedwe cha munthu monga izi:
1. Vasectomy. Yomwe amagwiritsa ntchito mwamuna podula msempha woyenda umuna wake kotero kuti asadzaberekenso.
2. Condom. Amagwiritsa ntchito mwamuna kapena mkazi popewa kuti umuna usagwere mkati.
3. Diaphragm/Cap. Mkazi amaika chokhala ngat condom kukhomo kwake. Subhanallah
4. Loop/Coil/IUD. Mkazi amaika mkati mwa chiberekero kuti mimba isameremo.
5. Pill. Mkazi amamwa zomwe zimachepetsa kukhwima kwa mazira.
6. Injection. Mkazi amabaidwa mankhwala oletsa mimba such as DepoProvera
7. Inplant. Kuchepetsa kupangidwa ndikutulutsidwa kwa mazira okhwima.
8. Tubal ligation. Mkazi amadulitsa njira yoyendamo mazira motero kuti sazaberekanso mpaka moyo wake onse. Ndi zina zotero.
Njira zonsezo mukadzionesetsa mupeza kuti zikupereka mavuto … zodabwitsa nzoti chiyambile maplan awowa sizikuthandiza, Mmalo mwake anthu akuononga miyoyo yawo. Tidziwe kuti njira za kulera zimenezo ndizimene anazikhazikitsa anthu omwewa opembedza satanawa, tikumbukirenso kuti satana wamkulu analonjedza kwa Allah nthawi yomwe analengedwa munthu,  kuti adzamusokoneza njira yotsatira Allah, Allah Ndiye anamuuza kuti “kupatula akapolo anga abwino” Ndiye zina mwa njira za shaytan zosokonezera akapolo a Allah ndi zimenezi,  koma ife sitikuzindikira chifukwa cha kukomedwa ndi modern world. Chisilamu ndi chokwanira ichi chinabweretsa njira zonse za umoyo wa munthu, koma tikudzibisala nkulandira za azungu ofuna kuchepetsa chiwelengero chathu. Akumabwera ndi mabungwe awo omwe kwawoko kulibe. Akumabwera mmsiko osauka nkumatinamiza kuti kusaukaku nchifukwa cha kuchulukana, landirani achina BLM mutenge njira za kulera za makono … Pomwe omwewo ndamene akutsogolera kuti maiko adzisauka.
Ndithu tikanakhala kuti timatsatira njira za Chisilamu muzochitika zathu zonse, bwenzi tisakuona vuto lirilonse.