Kulemekeza makolo ndi umodzi mwa maudindo amene anaikidwa ndi zipembedzo zosiyanasiyana pa dziko lapansi kukhala ofunikira kwa munthu wina aliyense. Chislam chinalumikiza kulemekeza makolo pambuyo pa kupembedza Allah Mmodzi yekha popanda kuphatikiza ndi milungu ina. Kusonyeza kuti kulemekeza makolo ndi imodzi mwa Ibaadah yofunikira pamaso pa Allah.

Mu Qur’an yolemekezeka, Allah (sw) anati:
وَقَضَى رَبُّكَ أَلاَّ تَعْبُدُواْ إِلاَّ إِيَّاهُ وَبِالْوَالِدَيْنِ إِحْسَاناً إِمَّا يَبْلُغَنَّ عِندَكَ الْكِبَرَ أَحَدُهُمَا أَوْ كِلاَهُمَا فَلاَ تَقُل لَّهُمَا أُفٍّ وَلاَ تَنْهَرْهُمَا وَقُل لَّهُمَا قَوْلاً كَرِيماً… الإسراء 23
“Waqadhwaa Rabbuka allaa ta’budoo illaa iyyaahu, wabil walidayn ihsaanan. Immaa yablughannal kibara ahaduhumaa aw kilaahumaa falaa taqul lahumaa uffin walaa tanharhumaa waqul lahumaa qawlan kareeman” Qur’an 17:23
“Ndipo walamula Mbuye wako kuti musapembedze wina koma iye yekha yekha ndikuti muchitire zabwino makolo anu. Ngati mmodzi wa iwo afika msinkhu waukalamba uli naye, kapena onse awiri, usawanenelere mawu a mnyozo ndiponso usawakalipire koma yankhula nawo ndi mau aulemu.”

Pali ma Hadith ambiri omwe Mtumiki (saw) ananena posonyeza kufunikira kwa kuchitira zabwino makolo:
Mu’awiyah bin Haidah anamufunsa Mtumiki (saw) kuti:
يا رسول الله، من أبر؟ قال “أمك” قلت من أبر؟ قال “أمك” قلت من أبر؟  قلت من أبر؟ قال “أمك” قلت من أبر؟ قال “أباك ثم الأقرب فالأقرب
Ya RasoolAllah, man ubarr? Qaala “Ummaka” qultu man ubarr? Qaala “Ummaka” qultu man ubarr? Qaala “Ummaka” qultu man ubarr? Qalla “Abaak thuma al-aqrab fal aqrab”
“O Mtumiki (saw), kodi ndingamchitire zabwino ndani? Mtumiki anati “Mayi ako” ndinati kodi ndingamchitire zabwino ndani? Mtumiki anati “Mayi ako” ndinati kodi ndingamchitire zabwino ndani? Mtumiki anati “Mayi ako” ndinati kodi ndingamchitire zabwino ndani? Mtumiki anati “Bambo ako, kenako oyandikana nawo”.

Ndizofunikira kwambiri kuwapemphera makolo ma Duah. Qur’an yolemekeza ikupereka duah iyi:
وَقُل رَّبِّ ارْحَمْهُمَا كَمَا رَبَّيَانِي صَغِيراً … الإسراء24
Waqul Rabbi rhamhumaa kamaa rabbayaani swagheera” Qur’an 17:25
“Ndipo nena: Mbuye wanga achitireni chisoni makolo anga monga momwe ankandilerera ku ubwana”
Ndizofunikiranso kwambiri munthu kusanzikana bwino ndi makolo ake pochoka, chifukwa iyeyo ndi gawo limodzi la makolo akewo ndipo ngati angachoke makolo ake atakhumudwa, mwayi wa paulendo kapena komwe akupita kuja umakhala wochepa.

Munthu wina anapita kwa Mtumiki (saw) kuti akagwirizane za msamuko, koma anawasiya makolo ake akulira chifukwa cha kusamuka kwa mwana wawo. Mtumiki (saw) anamuuza kuti abwelere kwa makolo ake ndipo akawasangalatse moti akawasiye akusangalala monga mmene anawasiyira akulira.

Kutukwana makolo ndi tchimo lalikulu mmachimo akuluakulu omwe Munthu amagweramo. Allah (sw) analetsa mchitidwe woterewu. Iye anati:
فَلاَ تَقُل لَّهُمَا أُفٍّ وَلاَ تَنْهَرْهُمَا وَقُل لَّهُمَا قَوْلاً كَرِيماً… الإسراء 23
“…falaa taqul lahumaa uffin walaa tanharhumaa waqul lahuma qawlan kareeman” Qur’an 17:23
“Ndipo usawanenelere mawu a mnyozo ndiponso usawakalipire koma yankhula nawo ndi mau aulemu”

Mu Hadith ya Abdullah bun Amru, Mtumiki (saw) analangizanso pa nkhani yomweyi kuti:
“Limodzi mwa machimo akulakulu, munthu kutukwana makolo ake”

Anthu anafunsa kuti “angatukwane bwanji makolo ake” ndipo Iye (saw) anati:
“Akatukwana munthu ndi kumutukwanira bambo ndi mayi ake 
Kutukwana makolo ndi tchimo lalikulu moti limafanana ndi chilango cha tchimo la kumuphatikiza Allah ndi milungu ina (shirk).
Imraan bun Hasin anati: Mtumiki (saw) anati:
“Mukuti bwanji za chiwerewere, kumwa mowa ndi kuba?”
ndipo anthu anati: “Allah ndi Mtumiki wake ndi omwe akudziwa. Mtumiki (saw) anati:
“Zimenezi ndi machitidwe oipa; ndipo mmenemo muli zilango, kodi ndikuuzeni za machimo akuluakulu? Kumuphatikiza Allah ndi china chake (shirk) komanso kunyoza makolo .”