Ma Ulamaa (anthu ozindikira komanso amaphunzitsa za deen ya Chisilamu), ndi anthu olemekezeka pamaso pa Allah chifukwa choti iwo ndi Alowammalo a Aneneri, ndi atsogoleri oyenera kuwalemekeza kuposa mtsogoleri wa dziko chifukwa akutitsogolera ku moyo wosatha. Ndi oyenera kumawapemphera chikhululuko nthawi zonse. Yemwe angagwire ntchito yosamalira kapena kuthandiza ma Ulamaa, akugwira ntchito yotamandika kwambiri pamaso pa Allah komanso ya malipiro ochulukuka. Ma Ulamaa ali ndi maubwino ambiri omwe chifukwa chakusalabadira kwathu, timasemphana nawo maubwinowo mapeto ake timawada ma Ulamaa. Kodi simumadabwa kuti fitna zambiri zimagwera anthu omwe akuzindikira malamulo a deen?
Pofuna kulongosola maubwino a Sheikh, tikuyenera kudziwa kaye maubwino a maphunziro, chifukwa iwo ntchito yawo ndi kufalitsa maphunziro a deen; komanso chifukwa choti maphunziro ndi ofunikira kwambiri mmoyo wa Msilamu,,,Msilamu sangakhale Msilamu okwanira popanda maphunziro a Chisilamu, choncho sangapeze maphunziro a Chisilamu popanda Sheikh. Kuti Chisilamu chake chikhale cholongosoka, akuyenera kulemekeza Sheikh.
– Ma ulamaa kawirikawiri amakhala pafupi ndi Qur’an ndi Sunnah, ndipo ndi anthu oyambilira kuikira umboni muchoonadi kuti Allah ndi Mulungu Mmodzi yekha. Izi zikuchokera mu Surah Aali Imraan aayah 18:
شَهِدَ اللّهُ أَنَّهُ لاَ إِلَهَ إِلاَّ هُوَ وَالْمَلاَئِكَةُ وَأُوْلُواْ الْعِلْمِ قَآئِمَاً بِالْقِسْطِ لاَ إِلَهَ إِلاَّ هُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ
“Mulungu (mwini) akuikira umboni kuti: “Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye basi.” Ndipo akuikiranso umboni (zomwezi) Angelo ndi ENI NZERU (kuti Iye) ngokhazikitsa chilungamo. Palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya”
Apa tikuona kuti Allah anawayandikitsa ma Ulamaa (eni nzeru) pafupi kwambiri ndi Angelo pa khuikira umboni wa Tawheed, anawaika position #3, ndipo ndi ANTHU oyambilira kukhala olemekezeka padziko lonse. Kumeneku ndiko kulemekezeka kwakukulu komwe aliyense akuyenera kukupeza, osati kulemekezeka chifukwa choti ndiwe wa ndalama kapena oimba  kapena osewera mpira ndi kuchita zitsuzo. Zimenezo zilibe kanthu kalikonse ku aakhira.
– Ma ulamaa ndi anthu amene Allah Ta’la amayambilira kuwapatsa zabwino kuposa aliyense, monga mmene akunenera Mmtumiki salla Allah alaih wasallam:
مَنْ يُرِدْ اللَّهُ بِهِ خَيْراً يُفَقِّهْهُ فِي الدِّينِ
“Yemwe Allah wamfunira zabwino, amamuphunzitsa deen” Al Bukhari & Muslim
Umenewo ndi ubwino wa munthu yemwe wafuna kudziwa za deen; kuchokera mu chidwi chake Allah amamupatsa zabwino.
– Ma ulamaa ndi anthu omwe ali owopa Allah (ma ulamaa omwe maphunziro awo amawagwiritsa ntchito pa choonadi), monga mmene akunenera pa Sura Faatir aayah 28:
إِنَّمَا يَخْشَى اللَّهَ مِنْ عِبَادِهِ الْعُلَمَاء
“Ndithudi, omwe ali owopa Mulungu mwa akapolo ake ndi omwe ali ozindikira”
Iwo amakhala akuopa chilango cha Allah, choncho amakhala olemekeza malamulo ake.
– Ma ulamaa sali ofanana ndi anthu ena onse, Allah akunena mu Surah Al Zumar aayah 9:
قُلْ هَلْ يَسْتَوِي الَّذِينَ يَعْلَمُونَ وَالَّذِينَ لَا يَعْلَمُونَ إِنَّمَا يَتَذَكَّرُ أُوْلُوا الْأَلْبَابِ
“Nena kwa iwo iwe Mtumiki: Kodi amene akudziwa ndi amene sakudziwa, ngofanana?” Ndithu, ndi eni nzeru amene amalingalira.”
– Ma ulamaa ndi anthu omwe amasunga chitetezo cha Ummah mu deen, ndipo akasowa ma ulamaa, Ummah umasokonekera. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:
إِنَّ اللَّهَ لَا يَقْبِضُ الْعِلْمَ انْتِزَاعاً يَنْتَزِعُهُ مِنْ الْعِبَادِ وَلَكِنْ يَقْبِضُ الْعِلْمَ بِقَبْضِ الْعُلَمَاءِ، حَتَّى إِذَا لَمْ يُبْقِ عَالِماً اتَّخَذَ النَّاسُ رُءُوساً جُهَّالاً، فَسُئِلُوا فَأَفْتَوْا بِغَيْرِ عِلْمٍ، فَضَلُّوا وَأَضَلُّوا
“Ndithu Allah samachotsa maphunziro a ma ulamaa, kuchotsa kuchokera mwa iwo, koma amangowachotsa mizimu yawo,, mpaka samatsala ozindikira ndipo pamenepo anthu amawatyenga ambuli kukhala atsogoleri awo pa deen…akamawafunsa za deen amangopanga ma fatuwa owasocheretsa nkumadzisocheretsanso okha”
– Atsogoleri a deen ndi omwe akuyenera kutukulidwa ndi Allah, monga mmene akunenera pa Surah Al Mujaadalah aayah 11:
يَرْفَعِ اللَّهُ الَّذِينَ آمَنُوا مِنكُمْ وَالَّذِينَ أُوتُوا الْعِلْمَ دَرَجَاتٍ
“Allah amawanyamula mmastep apamwamba omwe akhulupilira mwa inu ndi omwe apatsidwa kuzindikira”
– Ma ulamaa ndi alowammalo a Aneneni, mmene akunenera Mtumiki salla Allah alaih wasallam:
وإن العلماء ورثة الأنبياء، إن الأنبياء لم يورثوا ديناراً ولا درهماً إنما ورثوا العلم، فمن أخذه أخذ بحظ وافر
“Ndithu ma ulamaa ndi alowammalo a Aneneri, ndipo Aneneri sanasiye ndalama koma anasiya ‘ilm…choncho yemwe angatenge ‘ilmuyo, ndiye kuti watenga gawo lokwanira la mtengo wapatali”
– Ozindikira deen (Aaalim) anatenga malo a Atumiki, ndipo kusiyana kokhako komwe kulipo pakati pa iye ndi Mtumiki ndi kwa Utumiki basi. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:
فَضْلُ الْعَالِمِ عَلَى الْعَابِدِ كَفَضْلِي عَلَى أَدْنَاكُمْ
“Kulemekezeka kwa ‘Aalim kwa opembedza olimbikira, kuli ngati kulemekezeka kwa ine pa apansi panu (pakuchita zabwino”
Pa ubwino a ma Sheikh ndi ambiri, ndipo zonse zomwe tingafotokoze apa zikutanthauza kuti ndikofunikira kumulemekeza Sheikh (yemwe waphunzira ndipo akugwiritsa ntchito maphunziro ake moyenera). Timukhamukire kuti tipeze maphunziro akewo, ndipo timulemekeze chifukwa kunyoza anthu oterowo ndi tsopka lalikulu komanso kudzitsekereza tokha ku zabwino.