Zipembedzo zitatuzi zimagwirizana pa mfundo imodzi yofunikira: amayi ndi abambo onse analengedwa ndi Mulungu, Mlengi wa zonse. Komabe, kusagwirizana kumabwera pa kulengedwa kwa munthu woyamba, Adam ndi Hawaa.

Ku Chiyuda ndi ku Chikhristu, kulengedwa kwa Adam ndi Hawaa kunalongosoledwa mwatsatanetsatane mu Genesis 2:4-3:24. Anapitiriza kulongosola zomwe zinachitika pambuyo pa kulengedwa kwawo kuti: Mulungu adawaletsa onse awiri kudya zipatso za mtengo woletsedwa. Koma njoka idamunyengelera Hawaa kuti adyeko, ndipo Hawaa adamunyengelera Adam kuti adye naye. Pamene Mulungu anamudzudzula Adam pa zomwe adachita, iye adamuimba mlandu Hawaa: “Mkazi yemwe mwandiika naye malo ano wandipatsa chipatso choletsedwa kuti ndiye.” Pamenepo ndichifukwa chake Mulungu anati kwa Hawaa:

“Ndidzachulukitsa zopweteka kwa iwe pakubala, ndipo udzamva kuwawa pakubereka ana. Zolakalaka zako zidzakhala ndi mwamuna wako ndipo iye adzakulamulira iwe.”

Kwa Adam, Mulungu anati:

“Chifukwa choti iwe udamvera mkazi wako ndipo udadya kuchokera mumtengo … nthaka yonse iri yotembeleredwa chifukwa cha iwe, ndipo udzadya kuchokera muntchito zowawa masiku onse a moyo wako …”

Pomwe mu Chisilamu, kulengwedwa kwa munthu oyambilira kukupezeka malo angapo mu Qur’an, mwachitsanzo:

Qur’an 7:19-23: (Kenako Mulungu adanena kwa Adam) “E iwe Adam! Khala ndi mkazi wako mmunda wa Mtendere, (sangalalani ndi zomwe zili m’menemo) idyani paliponse pamene mwafuna. Koma mtengo uwu musawuyandikire kuopera kuti mungakhale mgulu la odzichitira okha zoipa.” Satana adayamba kuwanong’oneza (zoipa) kuti chioneke kwa iwo chimene chinabisika kwa iwo monga umaliseche wawo. Ndipo (Satana) adati: “Mbuye wanu sadakuletseni mtengo uwu, koma pachifukwa chakuti mungasanduke Angelo awiri, kapena kuti mungakhale amuyaya.” Iye adaalumbilira onse awiri kuti: “Ndithudi, ine ndine mmodzi mwa olangiza (ndikukufunirani zabwino).” Adawakopa mwachinyengo. Ndipo pamene adalawa zipatso za mtengowo umaliseche wawo udaoneka kwa iwo nayamba kudziphatika masamba (a mitengo) a m’mundamo. Ndipo Mbuye wawo adawaitana (mowadzudzula nati:) “Kodi sindinakuletseni mtengowu ndi kukuuzani kuti Satana ndi mdani wanu woonekeratu?” Iwo (Adam ndi mkazi wake) adati: (modzichepetsa), “Tadzichitira tokha zoipa, E Mbuye wathu! Ngati simutikhululukira ndi kuchita nafe chifundo ndiye kuti tikhala mwa otaika.”

Tikayang’anitsitsa mu kalongosoledwe kawiri komwe tamva pa nkhani ya kulenga, tikupezamo kusiyana kwakukulu; Qur’an yaika mlandu wofanana pa Adam ndi Hawaa chifukwa cha kulakwa kwawo. Palibe pomwe mungapeze Qur’an ikunena kuti Hawaa adamuyesa Adam pomudyetsa, kapena kuti iye adayambilira kudya asanadye Adam. Hawaa mu Qur’an sanatchulidwe monga wamayesero kapena wonyenga.

Komanso, amayi onse alibe mlandu woti apatsidwe nawo chilango cha zowawa za kubala, chifukwa malinga ndi Qur’an, Mulungu salanga munthu chifukwa cha zolakwa za wina. Adam ndi Hawaa adachita tchimo kenako adapempha Mulungu kuti awakhululukire, ndipo adawakhululukira. Plibenso tchimo lomwe linatsala ndikumayendelera ku mibadwo yonse mpaka lero lino.