Kukhulupirika Pa Maphunziro a Chisilamu
الإخلاص في طلب العلم
Taonani kukhulupirika komwe kunali ndi ma Imaam amene Allah Subhaanah wa Ta’ala anawalandira ntchito zawo pa dziko la pansi ndi kumwamba:
Ndingokupatsani chitsanzo cha Imaam mmodzi, Imaam Al Shaafi’i rahimahu Allah, yemwe anayankhula mau omwe ndithu angabweretse kusintha mmitima ya ma Sheikh alero omwe ndi okhulupirika pa maphunziro awo omwe Allah awadalitsa nawo:
Anati: “Ndinakonda maphunziro angawa atafalitsidwa popanda kuwaika mudzina langa”. Sanali kukonda kuti zidzinenedwa kuti: Imaam Al Shafi’i anati zakuti zakuti… “Sizofunikira kwa ine kunena kuti: Al Shafi’i anati… koma zomwe ziri zofunikira kwa ine ndi zoti ofunafuna ‘ilm komanso Asilamu onse amvesetse maphunzirowo kuchokera mu Buku la Allah kapenanso mu Sunnah za Mtumiki salla Allah alaih wasallam”. Amenewatu ndiye anthu omwe aphunzira kukhulupirika kwa choonadi, kuphunzira zenizeni. Koma yemwe waphunzira Deen ndicholinga choti azilimbana ndi ambuli kapena azichita makani ndi ma Ulamaa, kapena ncholinga choti adzikopa anthu kuti adzimuchemelera pamaphunziro akewo, ameneyo ndithu ndi wakumoto, chifukwa choti anali kupanga shirk yaing’ono, RIYAA (Kudzionetsera pa ‘ibaadah), anaphunzira ncholinga choti atchuke, adziwike pakati pa anthu ndipo alandire ulemelero padziko lapansi. Ameneyo akakhala ku moto limodzi ndi ochita shirk ena.”
 
Dziwani kuti kuphunzira kopanda nako niyyah yabwino ndi koopsa, ndipo Hadith imodzi mma Hadith akuluakulu pa nkhani ya maphunziro (Maphunziro a Deen), imene imayenera kugwedeza mitima ya ma Sheikh, ndi imene ikukamba zoti anthu oyambilira omwe moto wa ku Jahannama tsiku la Qiyaamah udzawayakire kwambiri, ndi atatu: koma apa ndifotokoza za mmodzi mwa atatuwa:
ورجلٌ تعلم العلم وعلمه للناس فيؤتى به يوم القيامة
“…ndi munthu yemwe waphunzira maphunziro, ndikuphunzitsa anthu, tsiku la Qiyaama adzabweretsedwa ndikufunsidwa zomwe anachita ndi maphunziro ake omwe Allah anamudalitsa nawo. Adzanena kuti
يا رب تعلمت العلم وعلمته للناس، فتقول له الملائكة: كذبت
O Ambuye, ndinaphunzira  maphunziro ndipo ndinaphunzitsa anthu. Komatu Angelo adzanena kuti: wanama!
Tsiku loopsatu ili ma Sheikh komanso loyaluka.
يَوْمَ تُبْلَى السَّرَائِرُ
Tsiku limene zobisika zonse zidzaonekera poyera 86:9
Munthu unaphunzira bwinobwnio, unavutika zaka zambirimbiri osagona usana ndi usiku kuwerenga, utakhutira kuti waphunzira zochulukirapo unayamba kuwagawira anthu ena zomwe waphunzira, polalikira mmizikiti, kuphunzitsa mma madrasa, kuphunzitsa mma halqa mmizikiti, kaya ndi pa facebook whatsApp radio TV ndi malo osiyanasiyana omwe anthu amasonkhana. Unachita izi mmoyo wako wonse! Lero tsiku la Chiweruzo Angelo akukukanira kuti ayi, ukunama iwe? Akutanthauza kuti ukunama chani kodi?
فتقول له الملائكة: كذبت، بل تعلمت من أجل أن يقال عالم
Angelo akunena kuti: wanama, koma unali kuphunzitsa ncholinga choti anthuwo akunene kuti ndiwe ophunzira!
Kungoterotu sikudzapezekanso kukambirana kulikonse, chifukwa kulibe kuponderezedwa, aliyense adzalandira malipiro malinga ndi chitsimikizo chake komanso ntchito yakeyo…
الْيَوْمَ تُجْزَى كُلُّ نَفْسٍ بِمَا كَسَبَتْ لَا ظُلْمَ الْيَوْمَ إِنَّ اللَّهَ سَرِيعُ الْحِسَابِ
Mzimu uliwonse lero, ulipidwa zimene udachita; palibe chinyengo lero (pochepetsa mphoto kapena kuonjeza chilango). Ndithu, Mulungu ngwachangu (pa) chiwerengero chake, (sichichedwa).
…إِنَّمَا الأعْمَالُ بِالنِّيَّاتِ وَإِنَّمَا لِكُلِّ امْرِئٍ مَا نَوَى،
Ndithu ntchito zimayenda ndi zitsimikizo, ndilpo ndithu, munthu aliyense (adzapeza malinga ndi) zomwe anatsimikiza…
Ndiyetu basi kuchoka pamenepo adzakankhidwira ndi nkhope yake ku moto … عياذًا بالله رب العالمين
Hadith imeneyi, anaitulutsa Muslim mu Sahih Muslim vol.3 number 1513, pa كتاب الحدود، khomo lofotokoza za kudula mkono wa wakuba posatengera kulemekezeka kwa wakubayo kapena kunyozeka kwake, komanso khomo lomwe likufotokoza za kuletsa kukhululukira chilango cha Allah, number 1905.