Kuyambikidwa konse nkwa Allah Mwini zolengedwa zonse, Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Mtumiki wake wolemekezeka.
Kodi tikhonzekere motani mwezi wa Ramadhan?

Pamene tili pa chitseko cha mwezi wa Ramadhan, aliyense mwa ife akuyenera kuti akudziwa komwe akupita chitsekochi chikangotsegulidwa. Aliyense akuyenera kulingalira kuti kodi wakonzeka zenizeni pa ulendowu?

Ambiri tili ndi chizolowezi cholakwika pa makhonzekeredwe a mwezi wa Ramadhan, kotero kuti timakhonzekera poganizira budget ya mpunga ndi mbatata za futari, ena kusonkhanitsa ma series kuti aziwonera, ena panopa akufufuza ma program mma TV channels, oyenera kuti azitaitsa nthawi yawo mmwezi umenewu.

M’bale wanga dziwa kuti mwezi wa Ramadhan siuli ngati ndodo yamatsenga yomwe imasanduka nthawi imodzi kukhala njoka! Mwezi wa Ramadhan siungasinthe ulesi womwe wakhala nawo chaka chonsechi, nthawi imodzi kukhala wa imaan yamphamvu, popanda kudzikhonzekeretsa mwini wako!

Mwezi umene ukubwerawu ndiwa business, kodi wakhonzeka kupanga business yosaluza ndi Allah?

Inu ndi ine timakhala tikuilira Jannah. Tsiku lirilonse tikukamba za Jannah. Komatu sitingakaipeze Jannah imeneyi mwachisawawa mosavuta, popanda kuikirapo mtima wonse.

Tikhonzekere kugwira ntchito zabwino zomwe zingakatilowetse ku Jannah chifukwa cha mwezi wa Ramadhan. Mtumiki wa Allah Muhammad salla Allah alaih wasalam anati:

Mngelo Jibril anandiuza kuti: Yemwe waupeza mwezi wa Ramadhan ndikupezeka kuti sanakhululukiridwe machimo ake, akalowa kumoto.

Pali zinthu 10 zimene ndikufuna kuti tigawane, zomwe ndikukhonzekera kokwanira kwa mwezi wa Ramadhan.

Tawbah Yeniyeni: Uku ndi kulapa kwenikweni, kulapa komwe munthu umakhululukidwa machimo ako onse nkukhala ngati wangobadwa kumene.

Kulapa ndikokakamizidwa nthawi zonse, koma chifukwa choti tikulowa mmwezi wowaukulu wolemekezeka, ndizofunikira kwambiri kulapa machismo kuti ntchito zabwino zomwe tizizipanga tikalowa mmwezi umenewu zikhale zopanda machimo aliwonse.
وَتُوبُوا إِلَى اللَّهِ جَمِيعًا أَيُّهَ الْمُؤْمِنُونَ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ
Lapani, bwelerani kwa Allah nonse inu okhulupilira, kuti mukhale osangalala.

Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam anatitsimikizira kufunika ndi ubwino wa kulapa, ponena kuti:
يا أيها الذين آمنوا توبوا إلى الله فإني أتوب في اليوم إليه مائة مرة
Inu amene mwakhulupilira, lapani kwa Allah poti ine ndimalapa kwa Iye ka 100 patsiku

Kupanga ma Dua: Ma Salaf kapena kuti anthu okhulupilira omwe analipo ife tisanabwere, kuyambira ma Swahaba a Mtumiki, anali kupempha kwa Allah myezi 6 usanafike mwezi wa Ramadhan, kuti awafikitse mmweziwu, ndipo pambuyo pa mweziwu anali kupempha myezi 5 kuti awalandire ntchito zomwe agwira mmwezi wa Ramadhan. Choncho, Msilamu akuyenera kumupempha Mbuye wake kuti amufikitse mwezi umenewu ali wabwino mu umoyo wake komanso mchipembedzo chake, komanso amupemphe kuti amuthandize kutsata malamulo ake ndi kuti amulandire ntchito zake zabwino.

Kusangalala chifukwa cha kuwufika mwezi umenewu tili wathanzi: Nzachidziwikire kuti kuwufika mwezi wa Ramadhan uli wathanzi komanso wakutha kusala ndi kupanga ibaada yonse, ndimadalitso aakulu kwa Msilamu aliyense, chifukwa Ramadhan ndinyengo yopeza zabwino mosavutikira, kalikonse kabwino komwe ungapange kamaonjezereka ka 10. Zitseko za ku Jannah zimatsekulidwa ndipo za kumoto zimatsekedwa. Mwezi wa Qur’an, wa makhululuko, wa chifundo cha Allah. Iye akunena kuti:
قُلْ بِفَضْلِ اللَّهِ وَبِرَحْمَتِهِ فَبِذَلِكَ فَلْيَفْرَحُوا هُوَ خَيْرٌ مِمَّا يَجْمَعُونَ
Nena: “Chifukwa cha ubwino wa Allah ndi chifundo Chake, (mwapeza zimenezi), choncho asangalalire zimenezi.” Izi ndizabwino kwambiri kuposa zimene akusonkhanitsa (m’zinthu za dziko lapansi).

Kubweza ngongole zomwe tinali nazo mu Ramadhan yomwe yapita: Sizoyenera kuti munthu yemwe anasiya masiku mmwezi wa Ramadhan ya chaka chatha, alowenso mu Ramadhan ina ngongole ija asanabweze. Imeneyo imakhala ngongole yaikulu ndipo osazitenga bwino umagwera nazo mmachimo. Choncho nzofunika kwambiri kubweza masiku aja tisanalowe mu Ramadhan yomwe ili nkudzayi.

Tikuyenera kusakasaka komwe tingamapeze maphunziro/ilm ya deen, kuti tizitha kugwiritsa ntchito mwezi wa Ramadhan mozindikira zomwe tikupanga, komanso kudzera mmaphunzirowo tidziwa zambiri za mwezi wa Ramadhan.

Tisiye ndi kudzitalikitsa ku ntchito zomwe zingatitangwanitse ku ibaada ya mmwezi wa Ramadhan.

Tikhanzikike pakhomo ndi azikazi athu, azimuna athu ndi ana athu kuti tizitha kuwauza komanso kuwaongolera malamulo a kusala mwezi wa Ramadhan. Komanso kuti tiziwapanga monitor ana athu omwe tikuwapangitsa practice kusala. Koma ngati tili ndi ntychito zina za panja pa nyumba monga ku office kaya ma business, tionetsetse kuti zisamatiiwalitse udindo wathu kunyumba.

Tifunefune mabuku a Chisilamu oti tiziwerenga panyumba, kapena tiwagawireko ma imam athu pamzikiti kuti aziwawerengera anthu munzikiti mmwezi umenewu.

Kuchulukitsa kusala mmwezi wa Sha’ban, ngati munali kupanga zimenezi, ndiye kuti mwakwaniritsa sunnah ya Mtumiki pokhonzekera Ramadhan.

Kuwerenga Qur’an: tidzizolowezetse kuwerenga Qur’an, komanso tiwazolowezetse ana athu kuwerenga Qur’an, chifukwa imeneyi ndi ntchito yotamandika kwambiri mmwezi wa Ramadhan.

M’bale wanga, dziwa kuti Qur’an ndimphatso yaikulu yomwe ambiri sanaizindikirebe. Ndimphatso yaikulu munthawi iliyonse, ndipo m’mwezi wa Ramadhan ili ndi malipiro ochuluka zedi ukayiwerenga mwakathithi.

M’bale wanga, dziwa kuti chilichonse chomwe chikukhudzana ndi Qur’an, Allah anachipanga kukhala chapamwamba chifukwa cha kulemekezeka kwa Qur’an, yomwe ndi Buku lapamwamba kuposa mabuku ena onse.

M’ngelo Jibril anabweretsa Qur’an kwa Mtumiki, choncho Allah anam’panga kukhala wabwino wolemekezeka mwa Angelo onse.

Qur’an inabvumbulutsidwa kwa Mneneri Muhammad, choncho Allah anam’panga Muhammad kukhala Mneneri wolemekezeka kwa onse.

Qur’an inabvumbulutsidwa kwa Asilamu, choncho Allah anawapanga Asilamu kukhala anthu olemekezeka mwa anthu onse.

Qur’an inabvumbulutsidwa Mmwezi wa Ramadhan, choncho Allah anaupanga mwezi wa Ramadhan kukhala wabwino kuposa myezi yonse.

Qur’an inavumbulutsidwa mu usiku wa Lailatul Qadr, choncho Allah anaupanga usiku wa Lailatul Qadr kukhala wolemekezeka kuposa mausiku wonse.

Yemwe angakhale connected ndi Qur’an, akhala wolemekezeka kuposa wina aliyense, chifukwa Allah analemekeza chilichonse chokhudzana ndi Qur’an.

Wallahi, ngati ungaipange Qur’an kukhala gawo la tsiku lako, dziwa kuti chirichonse cha iwe chikhala chopambana. Musaidelere Qur’an, poti ndiimene ingakunyamuleni kukuikani pamwamba pa ena.

M’bale wanga, tiye tikhonzekere polemba timetable ya mawerengedwe a Qur’an mmwezi umenewu, ndipo tiyesetse kuimaliza kangapo, poti thawaab za Allah kwa akapolo ake ochita zabwino nzosatha.

Mtumiki salla Allah alaih wasallam anatitsimikizira kuti munthu wowerenga chilembo chimodzi cha mu Qur’an amalandira malipiro okwana ten, komatu apa samatanthauza liwu limodzi, koma chilembo chimodzi, monga mu liwu loti – Alif laam meem -, alif ali ndi thawaab ten, laam ali ndi thawaab ten ndipo meem ali ndi thawaab ten. Chimodzimodzi kungowerenga kuti Bismillah Rrahmaan Rraheem, chifukwa choti zilembozo zilipo 19, ndiye kuti upeza thawaab 190. Kodi ndima Bismillah Rrahmaan Rraheem angati omwe mungawerenge mu Qur’an yonse? Nanga mukamawerenga Qur’an yonse, mupeza thawaab zingati? Tiyeni tisadzimane thawaab.

Ndikupempha Allah atikhululukire machimo athu ndi kuti atipange kukhala anthu oyera mitima tikamalowa mwei wa Ramadhan.

In shaa Allah tikhala tikukumbutsana zosiyanasiyana zokhudza mwezi uwu wa Ramadhan nthawi ngati zomwezi. Ndipo kwa amene angafune kudziwa zoonjezera, komanso kuwerenga mabuku okhudza mwezi wa Ramadhan, atipeza ku office yathu ya Islamic Information Bureau tikangopitilira Kips restaurant msewu wa Liwonde.
وصل اللهم على حببينا المصطفى و على آله وصحبه و زد وبارك عليهم
والسلام عليكم ورحمة الله وبركاته