KUKHANZIKIKA NDI KULUNGAMA
(Riyaadhu Sswaaliheen “Khomo 8”)
Allah Ta’la ananena kuti:
فَاسْتَقِمْ كَمَا أُمِرْتَ وَمَن تَابَ مَعَكَ وَلَا تَطْغَوْا إِنَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ
“Choncho (E iwe Mtumiki!) Pitiriza kulungama monga momwe akulamulira (iwe) pamodzi ndi omwe atembenukira (kwa Mulungu), ndipo musapyole malire. Ndithuw, Iye akuona zonse zimene muchita.” Surah Hud 112
Allah Ta’la ananenanso kuti:
إِنَّ الَّذِينَ قَالُوا رَبُّنَا اللَّهُ ثُمَّ اسْتَقَامُوا تَتَنَزَّلُ عَلَيْهِمُ الْمَلَائِكَةُ أَلَّا تَخَافُوا وَلَا تَحْزَنُوا وَأَبْشِرُوا بِالْجَنَّةِ الَّتِي كُنتُمْ تُوعَدُونَ نَحْنُ أَوْلِيَاؤُكُمْ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا وَفِي الْآخِرَةِ وَلَكُمْ فِيهَا مَا تَشْتَهِي أَنفُسُكُمْ وَلَكُمْ فِيهَا مَا تَدَّعُونَ نُزُلًا مِّنْ غَفُورٍ رَّحِيمٍ  نُزُلًا مِّنْ غَفُورٍ رَّحِيمٍ
“Ndithu amene anena (kuti): “Mbuye athu ndi Mulungu,” (povomereza umodzi wake), kenako nkupitiriza kulungama pa malamulo ake, Angelo amawatsikira iwo nthawi yakufa (uku akuti): “Musaope (pazomwe mukumane nazo). Ndipo musadandaule (pazomwe mwazisiya). Ndipo sangalalani ndi munda wamtendere umene mudalonjezedwa (kupyolera mmalirime a aneneri). (Angelo amanena kwa iwo): “Ife ndi athangati anu pamoyo wa padziko lapansi (pokulimbikitsani panjira yolungama), ndi tsiku lomaliza (pokupempherani chipulumutso kwa Mulungu); inu mukapeza kumeneko chilichonse chomwe mitima yanu ikafune (zokoma ndi zabwino); ndipo mukapeza mmenemo chilichonse chomwe mukachilakelake. (Limeneli ndi) phwando lochokera kwa (Mbuye) wokhululuka kwambiri, wachisoni.” Surah Fussilat 30-32
Allah Ta’la ananenanso kuti
إِنَّ الَّذِينَ قَالُوا رَبُّنَا اللَّهُ ثُمَّ اسْتَقَامُوا فَلَا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ
“Ndithu, amene anena (kuti): “Mbuye wathu ndi Mulungu”. Kenako ndikulungama, sadzakhala ndi mantha (tsiku lakufa kwawo ngakhale pambuyo pake), ndiponso sadzadandaula.” Surah Al-Ahqaf 13-14
Hadith #1/85:
وعن أبي عمرو، وقيل أبي عمرة سفيان بن عبدالله رضي الله عنه قال: قلت: يا رسول الله، قل لي في الإسلام قولًا، لا أسأل عنه أحدًا غيرك، قال: ((قل: آمنتُ بالله، ثم استقم))؛ رواه مسلم.
Kuchokera kwa Abi Amru, kapena Abi Amrah Sufyaan bun Abdullah (Allah asangalale naye), anati: Ndinati: Ee Mtumiki wa Allah, tandiuzeni liwu mChisilamu lomwe sindingamufunse wina kupatula inu. Anati: “Nena kuti: Ndakhulupilira Allah, kenako ulungame” – Muslim
Hadith #2/86:
وعن أبي هريرة رضي الله عنه ‏:‏ قال‏:‏ قال رسول الله ﷺ قاربوا وسددوا، واعلموا أنه لن ينجو أحد منكم بعمله‏”‏ قالوا‏:‏ ولا أنت يا رسول الله ‏؟‏ قال‏:‏ ‏”‏ولا أنا إلا أن يتغمدنى الله برحمة منه وفضل‏”‏ ‏رواه مسلم‏. ‏
Kuchokera kwa Abi Hurairah (Allah asangalale naye), anati: Mtumiki wa Allah (salla Allah alaih wasallam) eanati: “Khalani oyandikira kwa Allah (potsatira njira yoongoka mopanda kulumpha malire) ndipo khalani okhanzikika ndi olungama. Ndipo dziwani kuti palibe mwa inu amene adzapulumuke chifukwa cha ntchito zake”. Wina anati: Ngakhalenso inuyo Mtumiki? Anati: “Ngakhale ineyo, kupatula ngati Allah atandiphimba ndi chifundo komanso chisoni chake” – Muslim
*********
٩- باب التفكير في عظيم مخلوقات الله تعالى وفناء الدنيا وأهوال الآخرة وسائر أمورهما وتقصير النفس وتهذيبها وحملها على الاستقامة
KUCHETELERA UKULU WA KULENGA KWA ALLAH, KUTHA KWA MOYO WA PADZIKO, ZOOPSA ZA TSIKU LOMALIZA, KUFOOKA KWA MZIMU WA MUNTHU NDI KUWUKHONZA KUTI UKHALE WOLUNGAMA
(Riyaadhu Sswaaliheen “Khomo 8”)
Allah Ta’la ananena kuti:
قُلْ إِنَّمَا أَعِظُكُم بِوَاحِدَةٍ أَن تَقُومُوا لِلَّهِ مَثْنَى وَفُرَادَى ثُمَّ تَتَفَكَّرُوا مَا بِصَاحِبِكُم مِّن جِنَّةٍ إِنْ هُوَ إِلَّا نَذِيرٌ لَّكُم بَيْنَ يَدَيْ عَذَابٍ شَدِيدٍ
Nena: “Ndithu ndikukulangizani chinthu chimodzi, kuti muimirire chifukwa cha Mulungu; awiriawiri ndi mmodzimmodzi, ndipo kenako mulingalire; (muona kuti uyu Muhammad salla Allah alaih wasallam chilichonse chomwe akunena nchoona. Ndiponso muona kuti) mnzanuyu alibe misala. Iye sichina, koma ndimchenjezi wanu chisanadze chilango chaukali.” – Surah Sabai 46
Allah Ta’la ananenanso kuti:
الَّذِينَ يَذْكُرُونَ اللَّهَ قِيَامًا وَقُعُودًا وَعَلَى جُنُوبِهِمْ وَيَتَفَكَّرُونَ فِي خَلْقِ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ رَبَّنَا مَا خَلَقْتَ هَذَا بَاطِلًا سُبْحَانَكَ
“Omwe amakumbukira Mulungu, ali chiimire ali chikhalire, ndi ali chigonere chamnthiti mwawo; amalingalira kalengedwe ka thambo ndi nthaka (m’mene Mulungu adazilengera, uku akuti): “Mbuye wathu! simunalenge izi mwachabe, ulemerero ngwanu. Tichinjirizeni kuchilango chamoto.” Aali Imraan 109-191
Allah Ta’la ananenanso kuti:
أَفَلَا يَنْظُرُونَ إِلَى الْإِبِلِ كَيْفَ خُلِقَتْ وَإِلَى السَّمَاءِ كَيْفَ رُفِعَتْ  وَإِلَى الْجِبَالِ كَيْفَ نُصِبَتْ  وَإِلَى الْأَرْضِ كَيْفَ سُطِحَتْ  فَذَكِّرْ إِنَّمَا أَنْتَ مُذَكِّرٌ
“(Kodi akunyozera kulingalira zisonyezo za Mulungu), sakulingalira kungamira idalengedwa motani? Ndi thambo (limene akuliona nthawi zonse) m’mene lidatukulidwira (kutali popanda mzati)? Ndi mapiri momwe adakhazikitsidwira (molimba)? Ndi nthaka momwe idayalidwira. Basi, kumbutsa (anthu) ndithu, iwe ndiwe mkumbutsi.” Surah Al GHaashiyah 18
Allah Ta’la ananenanso kuti:
َأفَلَمْ يَسِيرُوا فِي الْأَرْضِ فَيَنظُرُوا
“Kodi sadayendeyende padziko nkuona…?” Surah Al Hajj 46
Ma aayah ndi ambiri pa mutu umenewu. Ndipo imodzi mwa ma Hadith ake ndi hadith 66 pa Mutu wa Kuchetelera (باب المراقبة) mu buku la Riyaadhu Ssaliheen, yonena kuti “Munthu wanzeru ndi amene amadziwelengera yekha (ndikupewa ntchito zoipa). Ndipo amagwira ntchito zabwino zomwe zidzamuthandize pambuyo pa imfa…”