بسم الله الرحمن الرحيم
Bismillahi Rrahmaani Rraheem
يا أخت هارون ما كان أبوك امرأ سوء وما كانت أمك بغيا
Oh, iwe mlongo wa Haarun! Bambo wako sadali munthu woipa, ngakhalenso mayi wako sadali wachiwerewere Surah Mariam (19:28)
Nkhani yathu ikuchokera pa aayah imeneyi, pamene anthu ofunafuna zolakwika mu Qur’an amati akafika pamenepo amaima ndikumufunsa Msilamu kuti: *”nchifuiwa chani Qur’an imatchula kuti Mariam ndi mlongo wake wa Harun kumachita Mariam ndi Harun (m’bale wa Musa) pakati pawo panadutsa zaka zambirimbiri ndipo mibadwo yosiyanasiyana?”*
Choncho amaona kuti Qur’an ikulakwitsa.
Izitu si akhristu okha, koma ndithu nthawi zambiri ngakhale Asilamu ena, amakhala ndi mafunso ochuluka akamawerenga Qur’an, mafunso oti nthawi zina tikafunsidwa timasowa choyankha …
Mafunso ambiri onga ngati amenewa anafunsidwapo Mtumiki Muhammad ﷺ, ndipo mwachitsanzo pa funso la Mariam ndi Harun, tsiku lina Mtumiki ﷺ anatuma Swahabiy wina dzina lake Mugheerah bin Sha’abah kuti apite ku Yemen akafalitse uthenga. Koma atafika kumeneko mkristu wina anamufunsa kuti: “inu Asilam mu Qur’an timamva kuti:
يا أخت هارون ما كان أبوك امرأ سوء وما كانت أمك بغيا
“Oh, iwe mlongo wa Harun! Bambo wako sadali munthu woipa, ngakhalenso mayi wako sadali wachiwerewere”,
zitheka bwanji Maryam mwana wa Imran kuti akhale mlongo wa Haroon, kumapanga kuti Musa bin Umraan, m’bale wa Haroon pakati pawo ndi Maryam panadutsa zaka zambiri zedi?
Mugheerah bin Sha’abah sanakwanitse kuyankha mpaka anabwelera kwa Mtumiki  ﷺ kukamufunsa.
Mkristu ameneyu atafunsa funso limeneli anaganiza kuti wagonjetsa Asilamu komanso Chisilamu; wachipeza kukhala chipembezo chopelewera chomwe sichidziwa kulongosola mbiri za anthu akale odziwika.
Mugheerah bin Sha’abah atabwelera ku Madinah anamufunsa Mtumiki ﷺ za Aayah imeneyi kuti zitheka bwanji Maryam kukhala mlongo wa Harun pomwe pakati pawo panadutsa zaka zambirimbiri?
Mtumiki  ﷺ anayankha nati:
“kale anali kuwatchula ana awo ndi maina a Aneneri komanso anthu olungama…”
Alhamdulillah yankho linakwanira ndipo chikaiko chomwe anali nacho pa Chisilamu chinathera pompo.
Pofuna kuphera mphongo, tiwone Hadith yomwe ikupezeka mu Sahih Muslim (2135) komanso Al Tabari (23691):
Kuchokera mu Hadith ya Mugheerah bin Sha’abah radhia Allah anhu, anati: mmene ndinapita ku Najran (Yemen) anandifunsa anati “inu mumawerenga mu Qur’an yanu kuti ”Oh iwe mlongo wa Harun…” kumapanga kuti Musa ndi Isa pakati pawo panali zaka zochuluka kwambiri…”
Ndipo mu riwayah lina anati:
“inu mukudziwa bwino kuti pakati pa Isa ndi Musa panali kusiyana kwa zaka zambiri”
Ndipo nditabwerera kwa Mtumiki ﷺ ndinamufunsa za zomwe anali kundifunsazo, Mtumiki ﷺ anati: “kale iwo anali kuwaitanira ana awo ndi maina a Aneneri awo akale komanso anthu awo ochita zabwino”
Allah atipatse kuzindikira