Kugwiritsa Maphunziro Pakati Pa Achichepere”
Kuchokera mu “Al Kabeer wal Awsat” ya Al Tabarani, anati kuchokera kwa Abi Umaya Al Jumahi radhia Allah anhu:
“إن من أشراط الساعة – وفي رواية: ثلاثاً: إحداهن – أن يُلتمس العلم عند الأصاغر”. (صحيح الجامع:2207)، (الصحيحة: 695
“Ndithu mu zizindikiro za kutha kwa nthawi, kudzapezeka kugwiritsa ‘ilm pakati pa achichepere”
Achinyamata ambiri akulimbikira pofunafuna maphunziro komanso kuchita da’wah. Ndi chinthu chabwino kwambiri ndipo ndi chomwe ummah walero ukufuna. Komatu pamene pali vuto ndipoti achinyamatawa akumafulumira kuthyola chipatso chisanapse; kutulutsa ma fatwa, kuphunzitsa; koma zonsezo ambiri akumachita opanda ‘ilm yokwanira; akumachulutsa kugwiritsa ntchito maganizo awo.
Akafunsidwa zomwe sakudziwa akumaona zovuta kunena kuti “sindikudziwa”, akumaona kuti kudziwika kwa maphunziro awo kutsika. Izi nchifukwa choti mapeto a kuphunzira kwa masiku ano ndiko kupeza degree kapena certificate iriyonse. Opanda certificate pamaphunziro a Chisilamu ndiye kuti sanaphunzire poti alibe umboni wa komwe anaphunzira. Koma yemwe ali ndi certificate ndiye kuti waphunzira ndipo anamaliza kumbali ya deen, kotero kuti amatha kupatsidwa maina, maudindo komanso ulemelero waukulu pakati pa Asilamu chifukwa cha mapepala ake. 
Oikira ndemanga mu buku la Abdullah bun Al Mubaarak “Kitaabu Al Zuhdi”, Nuaim anati: Abdullah bun Mubarak anafunsidwa kuti: “kodi achichepere amenewa ndi ati?” anati: “awo omwe amayankhula malinga ndi kuganiza kwawo. Koma wachichepere yemwe akupanga report za munthu wachikulire (yemwe amatenga kuchokera mu Qur’an ndi Sunnah), ameneyo si wachichepere”.
Al Haafidh bun Haja anakambanso mu “Fat’hul Baari” 13/301, komanso “Muswannaf Qasim bun Asbagh” kuti:
“فساد الدين: إذا جاء العلم من قِبَل الصغير استعصى عليه الكبير، وصلاح الناس: إذا جاء العلم من قِبَل الكبير تابعه عليه الصغير” وذكر أبو عبيد: أن المراد بالصغر في هذا: صغر القدر لا السن، والله أعلم”
“Kuonongeka kwa Deen: ndi pamene maphunziro aadze kuchokera mwa achichepere kupita kwa achikulire. Kulongosoka kwa Deen: ndi pamene maphunziro aadze kuchokera mwa akuluakulu kupita kwa achichepere”.
Abu ‘Ubayd anati: “kutanthauza kwa kuchepa uku ndi kuchepa kwa kutha, kukwanitsa kupanga zinthu osati kuchepa kwa zaka za kubadwa..Allah ndamene adziwa zonse.”
Indetu, munthu amatha kukhala wamkulu zaka 40, koma palibe chomwe adziwa mu deen, ndiye wina akhonza kukhala wa zaka 20 koma akudziwa zambiri mu deen … ndiye zomwe akutanthauza kukula ndi kuchepa pa nkhani ya ‘ilm ya Deen.
Al Tabaraani rahimahullah, mu report lochokera kwa Ibn Mas’ud radhiaAllah anhu anati:
“لا يَزَالُ النَّاسُ صَالِحِينَ مُتَمَاسِكِينَ مَا أَتَاهُمُ الْعِلْمُ مِنْ أَصْحَابِ مُحَمَّدٍ صلى الله عليه وسلم، وَمِنْ أَكَابِرِهِمْ، فَإِذَا أَتَاهُمْ مِنْ أَصَاغِرِهِمْ هَلَكُوا”.
“Anthu adzakhala olongosoka, ochita zabwino komanso ogwiritsa zomwe zawafika mu ‘ilm kuchokera kwa ma Swahaba a Muhammad salla Allah alaih wasallam, kuchokera mwa akuluakulu awo. Koma (‘ilmuyo) ikadzayamba kuwafika kuchokera mwa achichepere mwa iwo, basi adzaonongeka.”
Kuchokera mu buku la “Kitaabul Jaami’i Bayaanul ‘Ilm” #2410, p1225, Maalik rahimahu-Allah anati:
“أَخْبَرَنِي رَجُلٌ: أَنَّهُ دَخَلَ عَلَى رَبِيعَةَ بْنِ عَبْدِ الرَّحْمَنِ، فَوَجَدَهُ يَبْكِي، فَقَالَ لَهُ: مَا يُبْكِيكَ؟ أَمُصِيبَةٌ دَخَلَتْ عَلَيْكَ؟ وَارْتَاعَ لِبُكَائِهِ، فَقَالَ: لا، وَلَكِنِ اسْتُفْتِيَ مَنْ لا عِلْمَ لَهُ وَظَهَرَ فِي الإِسْلامِ أَمْرٌ عَظِيمٌ، قَالَ رَبِيعَةُ: وَلَبَعْضُ مَنْ يُفْتِي هَا هُنَا أَحَقُّ بالحبس مِنَ السُّرَّاقِ “.
“Anandiuza munthu wina kuti analowa (mnyumba) mwa Rabieah bun Abdi Rrahmaan ndipo anampeza akulira. Anamufunsa: “Ukuliliranji? Chakugwera choipa?” Kenako anaoneka kuti ali ndi mantha ndipo  anati: “ayi, koma kuti wafunsaidwa (nkhani za deen) munthu opanda ‘ilm ndipo (malinga ndi kufotokoza kwake) zabweretsa zinthu zazikulu mu Chisilamu.” Rabieah anati: “ndithu anthu ena omwe akumapanga ma fatwa awo, akuyenera kumangidwa kuposa wakuba”