Kuchokera m’mawu omwe anthu amati ndi ochokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam,

عن أبي هريرة قال: قال رسول الله ﷺ : أول شهر رمضان رحمة، وأوسطه مغفرة، وآخره عتق من النار. منكر، روه الديلمي

Nkhani inachokera kwa Abi Hurairah radhia Allah anhu, anati: Mtumiki wa Allah ﷺ anati: “kumayambiliro kwa mwezi wa Ramadhan kuli Chifundo, pakati pake pali Chikhululuko, kumapeto kwake kuli Kuwomboledwa kumoto.” Addailami

Hadithiyi, inafala ndikukhanzikika pakati pathu, komanso ana athu amaiphunzira ku Madrasa, komatu ngakhale amatero kuti gawo loyamba ndi Rahmah lachiwiri Maghfirah, gawo lomaliza Itqu mina Nnaari, sizoona. Komanso amaphunzitsa kuti “Masiku 10 oyambilira … masiku 10 achiwiri … masiku 10 omaliza…” pomwe Hadith’yo sikutero.

Izi Mtumiki ﷺ sanayankhulepo, ndipo anachenjeza za kuopsa kwa kumunamizira iye, ponena kuti..

ومن كذب علي متعمدا فليتبوّأ مقعده من النار

“…Ndipo yemwe angandinamizire ine, akudzikhonzera malo kumoto”
Chifukwa cha mawu amenewa, tikamakhala tikuchenjezana za kum’namizira Mtumiki ﷺ, timafuna kuonesetsa kuti pasamapezeke bodza lamtundu uliwonse, kupatula zomwe zatidutsa chifukwa cha kusadziwa.

Hadith iyi inalipo ndithu tisanabadwe, ndipo tinaipeza ili mkamwamkamwa mwa ma Sheikh kuiphunzitsa, mpaka lero lino ambiri adakali nayo kumasulira kutsogolo kwa anthu, makamaka kumayambiliro kwa mwezi wa Ramadhan. Ndipo ngati Sheikh sakuilalikira, otsatira chapansi akumaona ngati mtsogoleriyo sanaphunzire mokwanira.

Hadithiyi ili ndi mawu abwino mkati mwake, achilimbikitso okoma komanso munthu amakondwa akamaimva nthawi zonse, ndipo anaigawa motere:

1. Gawo lakumayambiliro ndimasiku khumi, ali ndi Rahmah (Chisomo cha Allah).

2. Gawo lapakati ndimasiku khumi ndipo ali ndi Maghfirah (Chikhululuko).

3. Gawo lachitatu ndimasiku khumi ndipo ali ndi ‘Itiqu mina nnaari, (kuwomboledwa kumoto kumka kumtendere).

Mau onsewa ndiabwino ndithu mukafananitsa /mukatengera ma Hadith ena omwe ndi owonadi amene Mtumiki ﷺ anawayankhula ndikuvomerezedwa ndi ma ulamaa amene anapanga specialize phunziro la Hadith.

Tsopano kufooka komanso kudwala kwa Hadithiyi kuli apa:
Mtumiki ﷺ sanayankhule mawu amenewo, komanso sanaigawe Ramadhan motero. Ndipo ma Hadith okamba zaubwino ndikufunikira kwa kusala m’mwezi umenewu wa Ramadhan ndi ambiri zedi owonadi (a Saheeh).

Hadith iyi mundondomeko ya anthu ake oilandira mukupezeka anthu okwana awiri amene ndi:

Allie bin Ziyaad Jada’an: yemwe anali wosatha kusunga bwinobwino ma Hadith pamtima.

Yusuf bin Ziyaad Al-Buswariy: yemwe anali wodziwika ndi kumunamizira Mtumiki kawirikawiri muzonena zake.

Hadith imeneyi ndi ya dhwaeef (yofooka) munkar (yokanidwa), ndipo yalongosoledwa ndi Sheikh wamkulu pa nkhani ya kafukufuku wa ma Hadith, Sheikh Nasruddeen Al-Albaani, mmabuku ake “Silsilat Ahaadith Dhaeefah wal Mawudhu’ah Mujarrad ‘ani Ttakhreej” #5721 komanso “Silsilat Dhaeefah” #1569, ofuna kudziwa zambiri alowe mmenemo in shaa Allah.

Kuti tiwonetsetsenso kumbali ina kuchokera mmawu omwe akupezeka mu Hadith ya dhaeefuyo, akusemphana ndi mawu omwe akupezeka mma Hadith a Saheeh monga:

فعن جابر رضي االله عنه قال: “قال رسول االله صلى االله عليه وسلم: إن لله في كل يوم وليلة عتقاء من النار في شهر رمضان، وإن لكل مسلم دعوة يدعو بها فتستجاب له.

Nkhani inachokera kwa Jabir radhia Allah anhu, anati: Mtumiki wa Allah ﷺ anati: “Ndithu Allah muutsiku ndi usana uliwonse m’mwezi wa Ramadhan amawombola kumoto (akapolo ake), ndipo dua ya Msilamu aliyense yomwe angaapange, Allah amamuyankha.”

Mu Hadith imeneyi, zikutsimikizika kuti kuwomboledwa kumoto ndi Chifundo cha Allah, inde, palinso zambiri zomwe Allah amatichitira kudzera mu Chifundo chake, ndipo zonsezo sizimakhala mmasiku owerengeka, koma onse. Chimodzimodzi Chikhululuko chili mmasiku wonse.

Kodi Mukumuikira Allah Malire a Kupereka kwake?

يَا أَيُّهَا النَّاسُ أَنْتُمُ الْفُقَرَاءُ إِلَى اللَّهِ وَاللَّهُ هُوَ الْغَنِيُّ الْحَمِيدُ

“E, inu anthu! Inu ndiosaukira (chinthu chilichonse) kwa Allah; koma Allah Ngwachikwanekwane (sasaukira chilichonse kwa inu); Wotamandidwa (ndi zolengedwa zonse).”

Kunena kuti Chifundo cha Allah chili m’masiku khumi okha, Chikhululuko cha Allah chili m’masiku khumi okha, Allah amawombola akapolo kumoto mmasiku khumi wokha, zinapereka ulesi kwa anthu, ulesi wakupempha kwa Allah Chifundo kuyambira pa 11, ulesi wakupempha Chikhululuko kumayambiliro ndi kumapeto kwa Ramadhan, ulesi wakupempha chipulumutso kumoto kumayambiliro ndi pakati pa mwezi wa Ramadhan! Ati chifukwa choti anamva Hadith ikunena kuti Rahmah (Chifundo cha Allah) chili kumayambiliro, ndipo kwinako kulibe Chifundo cha Allah … anamva kuti Maghfirah (Chikhululuko cha Allah) chimapezeka pakati, ndipo kwinako kulibe kukhululukidwa, choncho palibe chifukwa chopemphera chikhululuko pa 1 mpaka pa 9, pa 21 mpaka pa 30!

Tipemphe Allah atipatse kuzindikira pakufufuza kalikonse komwe tamva kuchokera mkamwa mwa anthu kapena mmabuku kuti ndi Hadith, tisanafalitse bodza lompekera Mtumiki salla Allah alaih wasallam, poti bodza lompekera iye silingafanane ndi bodza lopekerana pakati pathu.

اللهم تقبل صيامنا واغفر لنا وارحمنا يا أرحم الراحمين. رَبَّنَا تَقَبَّلْ مِنَّا إِنَّكَ أَنْتَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ. وَتُبْ عَلَيْنَآ إِنَّكَ أَنتَ التَّوَّابُ الرَّحِيمُ. اللَّهُمَّ إِنّا نعُوذُ بِكَ مِنَ الْبَرَصِ، وَالْجُنُونِ، وَالْجُذَامِ، وَمِنْ سَيِّئِ الأَسْقَامِ
اللَّهُمَّ صلِّ وسلِّم على عبدِك ورسولِك نبيَّنا محمد، وعلى آله والصحابةِ أجمعين، وعن التابعين ومن تبعهم بإحسانٍ إلى يومِ الدين وسلِّم تسليما كثيرا