Basharul Haafi rahimahu Allah anati:
“Yemwe amakonda kuti azifunsidwa (za deen), sali oyenera kufunsidwa”
قال بشر الحافي رحمه الله تعالى: مَن أحبَّ أن
يُسْأَلَ، فَليسَ بِأَهْلٍ لِأَنْ يُسْألَ.
Mau awa ndi akuya zedi. Allah atipatse kumvesetsa
Phunziro:
Kuitanira kuti uzifunsidwa za deen ponena kuti “ngati mukufuna kudziwa za deen muzindifunsa ine…” ndiko kukonda kufunsidwa. Kuyankhula koteroko kumasonyeza kuti ukudzionetsera kuti ndiwe wozindikira kwambiri kuposa ena, ndipo anthu sakuyenera kufunsa kwa ena koma iwe wekha.
Zotsatira zake ndizoti anthu amayamba kukuona kuti iwe ndiwe wozindikira kwambiri kuposa aliyense pakati pawo; palibe wina yemwe ali ndi ‘ilm kuposa iweyo poti wadzilengezetsa.
Ndiye zimapezeka kuti munthu woteroyo akafunsidwa zinthu zoti sakudziwa, amachita manyazi kunena kuti sakudziwa, mapeto ake amangoyankha zakezake nkumasocheretsa anthu, poti anthuwo sangamutsutsenso. Komanso sangapite kwa ma Sheikh ena kuti akaonjezere maphunziro poti anthu akumudziwa kuti ndi ozindikira kuposa onse.
Zofunika kwa omwe Allah awadalitsa ndi maphunziro pa deen, akadziwidwa kuti akuzindikirapo zinthu, asadzikweze pamwamba ena ena onse… adzichepetse… akafunsidwa aziyankha zomwe akudziwa, ndipo kumapetoko azinena kuti ‘Allah ndiye mwini kudziwa konse’ kapena mau ena ofanana ndi amenewa… kupatula ngati waiwala. Ngati sakudziwa anene kuti sakudziwa, ngati angakwanitae kufufuza, anene kuti ‘ndidikireni ndifufuze’.
Izi sichikakamizo, koma ndinjira imodzi ya kudzichepetsera pamaso pa Wodziwa Zonse (Allah) komanso zimapangitsa kuti Allah akudalitse ndi maphunziro oonjezera.