Kudya dothi ndi chizolowezi chosafunikira chomwe chimachitika ndi azimai ngakhalenso ana ena.
Nthawi zina chimakhala chikhalidwe chotengera, pomwe nthawi zina zikhonza kubwera kuchokera mu condition inayake yamthupi, monga kusowa kwa michere ina makamaka iron. Zimenezi zimatha kumpangitsa munthu kulakalaka dothi.. pambuyo pake zimapitilira kukhala chizolowezi.
Komano nthawi zambiri timaona azimai oyembekezera akudya dothi, funso lomwe labwera apa ndilofuna kudziwa kuti Chisilamu chikutijnji pakuda dotihi?
Sipanadze aayah kapena hadith yokamba za kudya dothi, nchifukwa chake ma ulamaa anakamba zosiyanasiyana; ena anati haram, ena makrooh, ndipo ena anati nzololedwa kudya ngati palibe vuto lomwe lingadze kamba ka kudya dothilo.

Chakudya chirichonse nchololedwa, kupatula zomwe shariah inaletsa. Koma pazomwe Sharia sidaletsezo ngati pali choti ukadya chikuyambira mavuto mthupi, ndibwino kuchipewa, chifukwa Allah analetsa kuika moyo pachiopsezo, kapena kudziononga. Choncho chakudya chimenecho ndi haram.

Zilinso choncho malinga ndi ndemanga yomwe anaikira Sheikh Ibrahim Al-Murawidhi pakuyankhula kwa Imaam Al-Nawawi mu Rowdat Twalibeen 3/291, pamene ankalongosola za chakudya: “zokamba zimanena kuti kudya dothi ndi haram, koma zilibe umboni uliwonse, choncho sibwino kuti tiweruze ponena kuti ndi haram, kupatula ngati mmenemo muli zobweretsa mavuto”.

Mukulongosola kwa ena, anati zonse zomwe zingabweretse mavuto ndi za haram, monga timyala, dothi ndi mchenga (Asnal Matwaalib 1/659), pamenepo mpamene Al-Murawidhi anati tikuyenera kuchichita chinthu haram ngati zaonekera ziopsezo mwa icho.

Al-Sabki anati: “palibe hadith yomwe yaletsa kudya dothi, koma poti limapereka mavuto ngati lachulukitsidwa, choncho zikhala haraam”
Ibn Qudaama mu Al Mughni 9/429 anati: “Imaam Ahmad anati: ndimadana ndi kudya dothi, koma ngakhale palibe hadith yolondola, dothilo limapereka mavuto kuthupi”, ndipo zinanenedwa kuti ndi zonyansa kudya, choncho kupewa kudya ndibwino kwambiri.

Mathero
Ndibwino kufunsa kuchipatala kuti tidziwe, ngati kudya dothi kungabweretse mavuto mthupi, tisadye. Koma ngati sikungabweretse mavuto, palibe vuto kudya.
Kusiyana kwa ma ulamaa pankhaniyi ndi chifukwa cha ma experiment, osati maumboni, poti palibe umboni uliwonse wochokera mu Hadith. Choncho pitali kuchipatala akuyezeni ngati muli oyenera kudya dothi.
Wallahu a’lam