Anzathu ena ambiri akamapanga wudhu sachukucha mkamwa akuti kuwopa kuwononga swaum yawo.
Zimenezitu ndizolakwika pazifukwa zambiri:
1. Kuchukucha mkamwa sikuwononga swaum ngati ukupanga wudhu, ngakhale madzi atalowa kukhosi mwangozi swaum yako sinawonongeke.
2. Palibe umboni oti Mtumiki ﷺ kapena Swahaba aliyense kuti anadulirapo popanga wudhu mmalo motsuka mkamwa chifukwa choti akusala, palibe umboni umenewo Munthu akuyenera kutsuka mkamwa chifukwa Mtumiki ﷺ analamula kuti:
إذا توضأت فمضمض
Ukamapanga wudhu utsuke mkamwa
Imeneyi ndi Hadith ya Saheeh (yabwinobwino) ndipo ikupezeka mu Sahih Abi Daud 144.
Apa lamulo lomwe tikutenga mu Hadith imeneyi ndiloti ndi wajib (chikakamizo) kutsuka mkamwa, ndipo izi ndizomwe zinalongosoledwa mu buku lotchedwa Al Kalimaati Al Naafi’ah page 97
Ena mwa maumboni oti kutsuka mkamwa ndikololedwa ngakhale uli kusala (swawm)
Mtumiki ﷺ ananena kuti
وبالغ في الاستنشاق أي مع المضمضة إلا أن تكون صائما..
Muziwonjezera potsuka mphuno kufikitsa mkati pamodzi ndikutsuka mkamwa muzifikitsa mkati kwambiri kupatula nthawi yomwe mukusala”
Mu Hadith imeneyi mwina anthu ena  akhoza kuganiza molakwika kuti ikuletsa kutsuka mkamwa ndi kutsuka mphuno popanga wudhu nthawi yomwe munthu akusala.
Ife tikuti ayi sikuletsa kutsuka mkamwa komanso mphuno; koma chomwe chikuletsedwa mu Hadith imeneyi ndi mubaalaghah (kuwonjeza) ngati kufikitsa madzi kummero  nthawi yomwe akusala. Zimenezo ndi zomwe zikuletsedwa koma osati kutsuka mkamwako, kapena kutsuka mphunoko ayi.
Hadith imeneyi ndi ya Saheeh ndipo ikupezeka mu Sahih Abi Daud 143
Mwina pongofuna kulongosola momveka komanso kuphera mphongo bwino, tingobwera ndi  Hadith ina yomwe Umar radhia Allahu anhu panthawi yomwe anamufunsa Mtumiki ﷺ, iye anati:
قال عمر بن الخطاب للنبي (ﷺ) يا رسول الله قبلت وأنا صائم فقال النبي (ﷺ) أريت لو مضمضت من الماء و أنت صائم؟ قلت لا بأس به قال: فمه
Umar  ananena kwa Mtumiki (ﷺ) kuti: “Eh Mumiki wa Allah, ine ndamuphyophyona mkazi wanga nditasala”. Mtumiki anati: “Ukuwona bwanji ngati utatsuka mkamwa ukusala, pali vuto?” Umar anati: “Ndinati “ayi palibe vuto”. Mtumiki ﷺ anati: “Nchimodzimodzi kutsuka mkamwa komanso kuphyophyona sikuwononga swaum”.
Sahih Abi Daud 2385