Kuchoka kwa ‘ilm komanso kufalikira kwa Umbuli
Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam analongosola kuti kuchoka kwa maphunziro ndi kuonekera kwa umbuli komanso kufalikira pakati pa anthu ndi chizindikiro cha kutha kwa nthawi.
Al Bukhari ndi Muslim (Allah awachitire chisoni) anatulutsa report kuchokera kwa Abi Huraira radhia Allah anhu kuti Mtumiki wa Allah salla Allah alaih wasallam anati:
“لا تقوم الساعة… حتى يُقبض العلم…” الحديث.”
“Sidzafika nthawi (yomaliza) … mpaka ‘ilm idzachotsedwe”
Al Bukhari ndi Muslim Allah awachitire chisoni, anatulutsanso report kuchokera kwa Abu Huraira kuti Mtumiki wa Allah salla Allah alaih wasallam anati:
“إن من أشراط الساعة أن يتقارب الزمان، وينقص العلم…” الحديث.”
“Ndithu mu zizindikiro za kutha kwa nthawi, nyengo idzakhala yowandikana, ndipo kuzindikira (‘ilm) kudzachepa”
Mu report lina,
“أن يُرفع العلم ويثبت الجهل. أو قال: يظهر الجهل”.
“‘ilm idzachoka ndikukhanzikika umbuli” kapenanso “ndipo udzaonekera umbuli” 
Tsopanoktu maphunziro omwe akutanthauza apa si maphunziro wamba, koma ochokera mu Qur’an ndi Sunnah komanso maphunziro ena omwe amachokera mmenemo. Amenewo ndi maphunziro omwe anasiyidwa ndi Atumiki a Allah onse – Mtendere wa Allah ukhale pa iwo onse – makamaka Mtumiki wa Allah salla Allah alaih wasallam yemwe anasiyira Ummah uno Qur’an ndi  Sunnah. Ndiye pamene nyengo zomwe Atumiki anali zikunka nadzitalikirana ndi nyengo yathu, nawonso maphunziro awo a Atumikiwo akumanka naacheperachepera chifukwa choti akumanka naatalikira limodzi ndi nyengoyo … mapeto ake umbuli ndi umene ukudzadza paliponse.
Pali Hadith yomwe ikupezeka mu Sunan Al Nasaai kuchokera kwa ‘Amru bun Taghlib radhia Allah anhu, Mtumiki wa Allah salla Allah alaih wasallam anati:
“إن من أشراط الساعة: أن يفشو المال ويكثر، وتفشو التجارة، ويظهر الجهل، ويبيع الرجل البيع، فيقول: لا. حتى أستأمر تاجر بني فلان، ويلتمس في الحي العظيم الكاتب لا يوجد”.
“Ndithu mwa zizindikiro za kutha kwa nthawi, chuma chidzafalikira ndikuchuluka, malonda adzafalikira, umbuli udzaonekera ndipo munthu azidzagulitsa malonda ake ponena kuti: ayi (sindikugulitsa) mpaka nditapempha lamulo kuchokera kwa wamalonda (businessman) ochokera m’banja lakutilakuti, ndipo anthu adzakhala akufunafuna olemba mabuku koma sadzapezeka”
Kuchokera mu Al Bukhari ndi Muslim, Hadith ikuchokera kwa Abdullah bun Mas’ud ndi Abu Musa Al Ash’ariy radhia Allah anhuma, anati: Mtumiki wa Allah salla Allah alaih wasallam anati: 
“إِنَّ بَيْنَ يَدَيِ السَّاعَةِ أَيَّامًا يَنْزِلُ فِيهَا الْجَهْلُ، وَيُرْفَعُ الْعِلْمُ، وَيَكْثُرُ فِيهَا الْهَرْجُ “. وَالْهَرْجُ الْقَتْلُ”. (أخرجه الشيخان وأحمد والترمذي).
“Ndithu pamene nthawi idzawandikire kutha, kudzabwera masiku omwe umbuli udzatsika (udzafika mwa anthu) ndipo ‘ilm idzanyamuka (idzachoka), ndipo kuphana kudzachuluka” Al Bukhari, Muslim, Ahmad, Al Tirmidhi
Kuchokera mu Al Bukhari ndi Muslim, Hadith yochokera kwa Ana bun Malik radhia Allah anhu, anati: Mtumiki wa Allah salla Allah alaih
wasallam anati:
“إِنَّ بَيْنَ يَدَيِ السَّاعَةِ لأَيَّامًا، َيُرْفَعُ الْعِلْمُ، و يَنْزِلُ فِيهَا الْجَهْلُ – وعند أحمد بلفظ: “ويفشو فيها الجهل-“.
“Ndithu kumapeto kwa nthawi, maphunziro adzachoka ndipo umbuli udzatsika” mmau a Ahmad: “ndipo umbuli udzafalikira”
Komanso kuchokera kwa Al Bukhari ndi Muslim, Anas Bun Malik radhia Allah anhu anati: Ndinamva Mtumiki wa Allah salla Allah alaih wasallam akunena kuti: 
“إن من أشراط الساعة أن يرفع العلم، ويظهر الجهل. ويفشو الزنا، ويُشرب الخمر، ويذهب الرجال، وتبقي النساء، حتى يكون لخمسين امرأة قيم واحد”.
“Ndithu muzizindikiro za kutha kwa nthawi, ‘ilm idzachoka ndipo umbuli udzaonekera, chiwerewere chidzafalikira ndipo mowa udzamwedwa (kwambiri), amuna adzatha (adzachepa) ndipo adzatsala (adzachuluka) azimai, mpaka adzapezeka azimai 50 kuyang’aniridwa ndi mwamuna mmodzi”.
Tikumbutsane, kuti kutanthauza kwa umbuli mma Hadithimu, akutanthauza umbuli pa za deen. Izi zikutsimikiza malinga ndi mmene zabwelera ndi Al Tabarani kuti:
“يأتى على الناس زمان لا يُدْري فيه ما صلاة؟ ما صيام؟ ما صدقة؟”.
“Idzafika nthamwi pa anthu, yomwe samazadziwa kuti swalaat ndi chani, swiyaam ndi chani, nanga swadaqa ndi chani”
Izitu ndi zoona ndipo zikuchitika lero liro. Kupezeka kuti tsiku ndi tsiku ma Sheikh akuphunzitsa kuti swalaat ndiye key ya ku Jannah, zinaphunzitsidwa izi kalekale zaka zoposa 1400 zapitazo, koma lero anthu adakafunsabe kuti “kodi pa swalat tingaime chotani? kodi nzololedwa kuphatikiza Al Jum’ah ndi Al Dhuhr? kodi akamati swalat yakudutsa imakudutsira pati? mafunso ambiri pa swalat osonyeza kuti swalat sitikudziwa. Chimodzimodzi swiyaam, panopa tati zii sitikufuna kudziwa za swiyaam, koma ikadzangoyambika, 30 days imeneyo idzakhala yofunsa za swiyaam, kusonyeza kuti mpaka pano sitikudziwa kuti kodi munthu kuti usale mwezi wa Ramadhan ukuyenera kupanga chani, kodi nanga zoonongetsa kusala kwako ndi ziti, nanga uyo ndi ololedwa kusala? uyo ndi oletsedwa kusala? Chimodzimodzinso swadaqah, kale zinali zomveka kuti swadaqa ndichani, koma lero sitikuidziwa … sitikudziwa kuti ndindani oyenera kupereka swadaqa, ndindani oyenera kulandira? ndi nthawi yanji? kodi nanga choperekedwa ngati swadaqah ndi chani? Zambiri zomwe lero lino sitikuzidziwa, koma zonsezo zinalongosoledwa kalekale ndi ma Sheikh omwe anamwalira … anapitatu ndi i’lm yawo ija.
Inde, Allah Ta’la akamachotsa mizimu ya ophunzira, amachotsa ndi ‘ilm yawo yomwe … ndiye ngati otsalawo ali mbuli, umbuli umafalikira padziko. Ndi izi lero tikuwatenga ambuli anzathu ngati ma ozindikira, nkumawaveka umufti anthu osayenera kukhala ma mufti. Kalikonse komwe angalalikire iwo kumakatenga kuti ndi fatwa. Inu simukudabwa kuti mawu oti FATWA komanso MUFTI kale lonseli anali kuti? Zikutanthauza kuti kalelo kunalibe ma mufti? ayi ndithu, koma kuti Mufti anali special munthu oyenera kukhala Mufit. Zolankhula zimakhala zosiyana pakati pa Fatwa ndi zina. Anthu sankangotchulana chisawawa kuti MUFTI, zomwe angayankhule ma tullaab (anyamata omwe adakaphunzira sukulu) sizinkatchedwa kuti Fatwa. Komatu lero, chifukwa cha umbuli wa kusadziwa tanthauzo la Fatwa, tanthauzo la Mufti, tikungodzipachika u Mufti ku maina athu, amvekere Mufti wakuti wakuti … munthu mmutumo Qur’an ma Zuj 15 sanakwane, ma Hadith ngakhale 10 ochokera mu Mahadith 40 sanaloweze. Akangolalikira kuti qaala Rasulullah salla Allah alaih wasallam, bunial Islam ‘alaa khamsin ,,, timvekere atipatsa fatwa lero! Zonsezo ndi umbuli womwe wadza munthawi yomaliza ino.
Ibn Maaja komanso Al Haakim anatulutsa Hadith yochokera kwa Hudhaifa bun Al Yamaan radhia Allah anhu, anati: Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:
“يدرس الإسلام كما يدرس وشي الثوب، حتى لا يُدْرى ما صيام ولا صلاة ولا نسك ولا صدقة، وليسري على كتاب الله عز وجل في ليلة لا يبقى في الأرض منه آية، وتبقى طوائف من الناس، الشيخ الكبير العجوز يقولون: أدركنا آباءنا على هذه الكلمة “لا إله إلا الله” فنحن نقولها، فقال له صلةُ: ما تغني عنهم لا إله إلا الله وهم لا يدرون ما صلاة ولا صياماً ولا صدقة ولا نسكاً؟ فأعرض عنه حذيفة، ثم ردها عليه ثلاثاً، كل ذلك يعرض عنه حذيفة، ثم أقبل عليه في الثالثة فقال: يا صلة، تنجيهم من النار، تنجيهم من النار، ثلاثة”.”
“Chisilamu chidzatha mmene zokongoletsera pa nsalu zimathera, mpaka anthu sazadziwa kuti kodi swawm ndi chani, nanga swalaat ndi chani, hajj ndi chani, nanga swadaqa ndi chani. Buku la Allah (Qur’an) lidzachotsedwa mu usiku ndipo padziko sipadzapezeka  aayah ngakhale imodzi. Koma adzatsala anthu ena okalamba, achichepere achimuna ndi achikazi, ndipo adzanena kuti: “tinawapeza makolo atu akunena mau awa: “Laa ilaah illa Allah, ndipo ife tikutsatira mmene ankanenera iwowo.” Swilatu anati: “Kodi nanga nzabwino zanji zomwe adadzipeze mu kuyankhula kwawo Laa ilaah illa Allah pomwe sadziwa swalaat ndi swiyaam, sadziwa hajj  ngakhale swadaqa?” Pamenepo Hudhaifa anamutembenukira Swilatu, ndipo iye anabwereza funsoli katatu koma Hudhaifa anali kumutembenukirabe. Kachitatuko Hudhaifa anayankha naye mobwereza katatu kuti: “Iwe Swilatu, mau amenewo ndamene adzawapulumutse ku moto!”
Hadithiyi  ili mu (صحيح الجامع:8077)، (صحيح ابن ماجه:3273)، (السلسلة الصحيحة:87)
Mtumiki wa Allah salla Allah alaih wasallam anadzudzula munthu yemwe ali mbuli pa deen, yemwe sadziwa za Chipembedzo chake koma amadziwa za dziko lapansi, amadziwa za pa dunia zokha. Ndipo analongosola kuti ndithu Allah Ta’ala amakwiya naye. Pali Hadith yomwe anaitulutsa Ibn Hibbaan kuti Mtumiki wa Allah salla Allah alaih wasallam anati:
“إِنَّ اللَّهَ يُبْغِضُ كُلَّ جَعْظَرِيٍّ جَوَّاظٍ صَخَّابٍ فِي الأَسْوَاقِ، جِيفَةٍ بِاللَّيْلِ، حِمَارٍ بِالنَّهَارِ، عَالِمٍ بأمر الدُّنْيَا، جَاهِلٍ بأمر الآخِرَةِ”.
“Ndithu Allah amakwiya ndi munthu odzikweza, olimba mchilengedwe chake, owumira osapereka, olongolola mumsika, okonda kugona usiku ngati mtembo, pomwe masana wonsewu akutangwanika ndi za dziko, amakhala ngati bulu masana (potangwanika ndi za mdziko) amakhala odziwa za dziko koma mbuli pa za deen”
Mukayang’anisitsa mmene tiliri anthufe lero lino; mupeza kuti ambiri mwa ife akutangwanika ndi za dziko, kudzitsata mosafuna kudutsidwa kanthu, mpaka kusanduka a zikachitika mumvera kwa ife. Koma kumbali ya za ku Aakhira, zomwe zingadzawathandize ku Aakhira, ndi ambuli otheratu moti amachita kudzilengedzetsa kuti ife za deenizi ndiye ndi ambuli, monyadira kukhala ngati kuti iwo adzapatulidwa kuti poti anali ambuli. Zonsezitu ndi zotsatira za kutangwanika ndi moyo, malonda, masewera, kudya, fashion … ndikudana ndi مجالس العلم والعلماء, kudana ndi maphunziro a deen komanso ma Sheikh. Masheikh lero lino amayang’anidwa ndi diso lachipongwe, kusekedwa kuti ndi anthu otsalira. Maphunziro awo samawelengedwa ngati kanthu.
Mmacommunitymu apezeke munthu oti anapanga graduate ku Shari’ah, ndiye apezeke munthu yemwe anapanga graduate ku Business Administration; onsewo ali pa line yofunsira ntchito; atengedwa wa Business Administration, poganiza kuti wa Sharia sadziwa Business Administration, kuona ngati mChisilamu mulibe kuphunzira za business. Sadziwa kuti yemwe waphunzira Shariah amaphunziranso Business Administration momwemo, ndipo imakhala yakathithi …pomwe yemwe waphunzira Business Administration ku school yoti si ya Chisilamu, sanaphunzire Sharia, sanaphunzire kalikonse ka Chisilamu. Ndiye society ikufuna yemwe alibe maphunziro aku Akhira kusiya wa deen  poona ngati palibe chomwe akudziwa.
Mphunzitsi wa madrasa akutengedwa ngati alibe ntchito pomulipira ndalama yongokwanira kugulu tomato pamsika, vuto lake ndi lomweli kuti olemba ntchito nawo alowedwa umbuli woganiza kuti mphunzitsi wa deen ndi opanda ntchito tisamuonongere ndalama.
Tsopano tikamati “Kuchoka ‘ilm kapena kuchotsedwa kwa ‘ilm”, sikuti ‘ilm ikumachoka mmitu ya anthu nkusanduka opanda nzeru. ayi. Koma kuchoka kwa ‘ilm apa tikutanthauza kumwalira kwa omwe asenza ‘ilm ndipo akuigwiritsa ntchito. 
Izitu zikuchoke mu Hadith ya Mtumiki wa Allah salla Allah alaih wasallam yomwe anaitulutsa Al Bukhari ndi Muslim, ku chokera kwa Abdulllah bun Amru bun Al ‘Aas radhai Allah anhu, anati: Ndinamumva Mtumiki wa Allah salla Allah alaih wasallam akunena kuti: 
“إن الله لا يقبض العلم انتزاعاً ينتزعه من العباد، ولكن يقبض العلم بقبض العلماء، حتى إذا لم يُبْقِ عالماً اتخذ الناس رؤوساً جهّالاً، فسُئِلوا فأفتَوْا بغير علم فضلُّوا وأضلُّوا”
“Ndithu Allah samachotsa ‘ilm (kuzindikira za Deen), kuchotsa kwenikweni kuchokera mwa akapolo ake (pambuyo poti awapatsa kuzindikirako), koma amachotsa ‘ilm pochotsa mizimu ya ma Ulamaa (‘ilm ya ma Sheikh odalirika imapitira limodzi ndi imfa pamene Allah atenga mizimu yawo). Ndipo pamene ophunzira atha onse, (amatsala ambuli okhaokha ndipo anthu amawatenga ambuli kukhala owatsogolera (pa za Deen); akafunsidwa amangoyankha zammutu nkumawasocheretsa anthu komanso kudzisocheretsa okha.”
Kodi izi sizkuchitika? Ndi miyandamiyanda ya ma Sheikh ingati yomwe yatisiya ndipo apita ndi ‘ilm yawo ija? Lero ndiye kwadza njira zambirimbiri zopezera ‘ilm koma tsoka ndi ilo oyenera kutiphunzitsa moyenera anapita ndi luntha lawo limene ankaligwiritsa ntchito pophunzitsa, osati pa facebook, osati pa whatsapp, osati pa TV, osati pa radio; koma munzikiti, kunyumba kwawo, pakhonde kapenanso pa madrasa ochita kupalasira njinga kuti akafike. Lero tili ndi miyandamiyanda ya ma Sheikh omwe apanga replace, alowammalo mwa miyandamiyanda ya ma Sheikh aja, koma apanga replace dzina lokha. ‘ilm mulibemo, ngati ilimo akumabisa kwa anthu posamalira mchere, angachotsedwe ntchito. Pomwe ma Sheikh athu akale ankaphunzitsa kuti anthu aidziwe deen osati kuti alemere. Ankaphunzitsa opanda certificate ya pepala koma zinthu nkumamveka, koma lero ma Sheikh a ma cerificate ali mbwee paliponse, ‘ilm yawo ikumatuluka akalonjezedwa ndalama … 
 
أبكي لعلمائي قد سلفوا
ليت الايامَ معكم تعود يوما             لأخبرها ماذا فعل بي البعد
بكيت على الفراق بدمع عيني    فلم يغن البكاء ولا النحيب
Al Tabarani kuchokera mu Hadith yomwe inachokera kwa Abi Umama Al Baahiliy, anati Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:
“خذوا العلم قبل أن ينفد ثلاثاً، قالوا: يا رسول الله وكيف ينفد وفينا كتاب الله، فغضب، ثم قال: ثكلتكم أمهاتكم، ألم تكن التوراة والإنجيل في بني إسرائيل ثم لم يُغنِ عنهم شيئاً؟ إن ذهاب العلم ذهاب حملته ” – ثلاثاً.
“Tengani ‘ilm isanathe!” anati: “Mtumiki, itha bwanji kumachita mwa ife muli Buku la Allah (Qur’an)?. Mtumiki anakwiya ndikuwafaunsa kuti: Kodi mwa ana a Israel munalibe Tora ndi Injeel (Gospel/Bible) koma kenako mabuku amenewo sanawathandize kalikonse? Dziwani kuti kuchoka kwa ‘ilm ndi kuchoka kwa onyamula ‘ilmuwo” mau awa anabwereza katatu.
Tatiyeni tibwelere kaye pang’ono ku Hadith yomwe taikamba ija yoti “…ndipo pamene ophunzira atha onse, (amatsala ambuli okhaokha ndipo anthu amawatenga ambuli kukhala owatsogolera (pa za Deen ; akafunsidwa amangoyankha zammutu nkumawasocheretsa anthu komanso kudzisocheretsa okha.” mau awa akutanthauza zazikulu ndithu zomwe zikufunika kukhala nazo tcheru. Akutanthauza kuti yemwe akuyankhula (kutulutsa fatwa) pa zomwe sakudziwa, ndithu akuchita tchimo. Koma ngati Muftiyo ali mwa anthu anzeru, odziwa za deen, kuchokera mma Ulamaa odalirika mdziko komanso yemwe ali ndi zomuyenereza kukhala mufti, komanso wapereka moyo wake ku maphunziro amene amufikitsa mpaka kumapeza zoonadi za zomwe akuyankhulazo; oteroyo amakhala kuti wapanga ijtihaad pa zomwe zikufunika kulongosoledwazo ndipo akalongosola ndi maumboni okwanira koma kupezeka kuti walakwitsa, ameneyo samalembedwa machimo. Izi zikuchokera pa mau a Allah Ta’ala mu Surah Al Ahzaab aayah 5:
 وَلَيْسَ عَلَيْكُمْ جُنَاحٌ فِيمَا أَخْطَأْتُمْ بِهِ وَلَكِنْ مَا تَعَمَّدَتْ قُلُوبُكُمْ
“Palibe uchimo kwa inu pa zimene mwazichita molakwitsa (mosazindikira). Koma (pali uchimo) pazimene mitima yanu yachita mwadala.”
Komanso Mtumiki wa Allah salla Allah alaih wasallam ananena kuti:
“إذا حكم الحاكم فاجتهد فأصاب، فله أجران، وإذا حكم فاجتهد فأخطأ فله أجر واحدٌ”.
“Ngati mtsogoleri (woweruza) waweruza molingana ndi kulimbikira kwake (pa kufunafuna choonadi) ndiye wagamula zoona, amapeza malipiro awiri. Koma ngati walimbikira (kufunamfuna choonadi pakugamula kwake) ndipo wagamula koma walakwitsa, amapeza malipiro amodzi.
Hadithiyi anaitulutsa Al Bukhari ndi Muslim kuchokera kwa Amru bun Al ‘Aas radhia Allah anhu
Koma tsopano akapereka fatwa munthu oti sioyenera kupereka fatwa nkudzalakwitsa, kapena kuti ndi oyenera kupereka fatwa koma sanalimbikire kufunafuna choonadi pa funso limene wafunsidwa kapena pachinthu chimene akufuna kupelekera fatwacho, kenako nkudzalakwitsa, ameneyo amakhala kuti wachimwa chifukwa choti wasokeretsa anthu munjira ya Allah. 
Allah Ta’ala akunena mu Surah Al Nahl aayah 25:
لِيَحْمِلُواْ أَوْزَارَهُمْ كَامِلَةً يَوْمَ الْقِيَامَةِ وَمِنْ أَوْزَارِ الَّذِينَ يُضِلُّونَهُم بِغَيْرِ عِلْمٍ أَلاَ سَاء مَا يَزِرُونَ 
(Motero akuwasokeretsa anthu) kuti adzasenze mitolo yawo (yamachimo) yokwanira pa tsiku la Qiyama, ndiponso gawo lamitolo ya omwe akuwasokeretsa popanda kuzindikira (osokerawo). Dziwani kuti ndi yoipa kwabasi mitolo yomwe azikaisenza!
Izi zikupezeka mu  الفتيا ومناهج الإفتاء: صـ 134 – 136
Gawo Lachiwiri