KUCHOTSA CHIKAIKO PA KUSOKONEKERA KWA ANTHU ENA PA MATANTHAUZO A ENA MWA MA AAYAH A MU QUR’AN YOLEMEKEZEKA
Surah Ad Dhuha (Aayah #7)

وَوَجَدَكَ ضَالًّا فَهَدَى – الضحى 7

“Ndipo adakupeza uli wosazindikira (Qur’an) nakuongola (pokuzindikiritsa Qur’aniyo ndi malamulo a chipembedzo)” Surah Ad Dhuha Aayah #7

Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam asanapatsidwe uneneri wake ndi Allah anali kudandaula kwambiri poona anthu ake ali osokera ndiponso poona kuti iye sadali kudziwa momwe angawaongolere.

Pambuyo pake adali kumapita ku mapiri amene adali pafupi ndi mzinda wa Makka. Kumeneko adali kupemphera ndi kumalingalira ndi kupempha Allah kuti amusonyeze njira yachiongoko. (Ndemanga ya mu Qur’an Yotanthauzidwa M’chichewa ndi Shaikh Khalid Ibrahim Pitala – Sura Ad Dhuha).

Aayah yolemekezekayi tikayimvera pamwamba-mwamba chabe, tipeza kuti ikutiuza zoti Mtumiki ﷺ anali wosochera chibvumbulutso chisanamufike, kusochera komwe tikukudziwa kwa awo okanira. Pomwe mawu ena a Allah Ta’ala akunena kuti:

فَأَقِمْ وَجْهَكَ لِلدِّينِ حَنِيفًا فِطْرَتَ اللَّهِ الَّتِي فَطَرَ النَّاسَ عَلَيْهَا – الروم: ٣٠

“Choncho lunjika nkhope yako ku chipembedzo moyenera; (pewa kusokera kwa okana Allah. Dzikakamize ku) chilengedwe chimene Allah adalengera anthu. (Ichi n’chipembedzo cha Chisilamu chomwe n’choyenerana ndi chilengedwe cha munthu).” Surah Ar Rum Aayah #30

Akutanthtauza kuti Mtumiki ﷺ analengedwera Chipembedzo choyenera chimenechi. Izi zinali zodziwika mpaka pamene analandira Utumiki, ndipo zikutsimikizika malinga ndikuti chibvumbulutso choyambilira chinamufukira ali ku phiri la Hiraa akubindikira pamapemphero omwe anawayamba kalekale asanalandire utumikiwo.

Tsopano kutanthauza kwa mawu oti

وَوَجَدَكَ ضَالًّا فَهَدَى – الضحى 7

“wosazindikira (Qur’an) nakuongola”, akutanthauza kuti “unali wosazindikira zomwe ukuzidziwa panthawi ino kuchokera m’malamulo komanso zobisika za mu Deen zomwe sungazidziwe kuchokera m’chibadwidwe ngakhale munzeru, pokhapokha utaphunzira kuchokera mu Wahy (chibvumbulutso). Choncho Allah anakuwongola nakupatsa kuzindikira pazimenezo kudzera mu chibvumbulutso.

Choncho الضَلَالُ pamenepa, akutanthauza kuti “kukhala wosazindikira”.

Kuchokeranso mutanthauzo limeneli, timawerenga Mawu a Allah Ta’ala awa:

أَنْ تَضِلَّ إِحْدَاهُمَا فَتُذَكِّرَ إِحْدَاهُمَا الْأُخْرَى -البقرة: ٢٨٢

“… kuti ngati mmodzi mwa iwo (akazi awiriwo) angaiwale mmodzi wawo akumbutse winayo….” Surah Al Baqarah Aayah #282
Komanso

لَا يَضِلُّ رَبِّي وَلَا يَنْسَى – طه: ٥٢

“Mbuye wanga sasokera, ndipo saiwala.” Surah Taha Aayah #52
Komanso

تَاللَّهِ إِنَّكَ لَفِي ضَلَالِكَ الْقَدِيمِ – يوسف: ٩٥

“Tikulumbira Allah! Ndithu muli m’kusokera kwanu kwa kale (pokonda Yûsuf kuposa ife)” Surah Yusuf Aayah #95

Chimodzimodzinso mawu omwe mlakatuli wina anayankhula kuti:

وَتَظُنُّ سلْمىَ أَنَّنِي أَبْغِي بِهَا بَدَلًا أَرَاهَا فِي الضَلَالٍ تَهِيُم

“Salma akuganiza kuti ndimam’funa koma ine ndimamuona kuti ndiwosokera”
Zikuchokeranso pa mawu a Allah awa:

مَا كُنْتَ تَدْرِي مَا الْكِتَابُ وَلَا الْإِيمَانُ – الشورى: ٥٢

“…Siudali kudziwa kuti buku ndi chiyani, chikhulupiliro ndi chiyani…” Surah As Shuraa Aayah #52

“Imaan” akutanthauza malamulo a Deen ya Chisilamu. Ndipo M’mawu ake oti:

نَحْنُ نَقُصُّ عَلَيْكَ أَحْسَنَ الْقَصَصِ بِمَا أَوْحَيْنَا إِلَيْكَ هَذَا الْقُرْآنَ وَإِنْ كُنْتَ مِنْ قَبْلِهِ لَمِنَ الْغَافِلِينَ – يوسف: ٣

“… ndithu udali mmodzi mwa osadziwa zinthu, isanakufike.” Surah Yusuf Aayah #3

Komanso

وَعَلَّمَكَ مَا لَمْ تَكُنْ تَعْلَمُ – النساء: ١١٣

“… Ndipo wakuphunzitsa zomwe sudali kuzidziwa …” Surah Al Nisaai Aayah #113

Komanso

وَمَا كُنْتَ تَرْجُو أَنْ يُلْقَى إِلَيْكَ الْكِتَابُ إِلَّا رَحْمَةً مِنْ رَبِّكَ فَلَا تَكُونَنَّ ظَهِيرًا لِلْكَافِرِينَ – القصص: ٨٦

“Ndipo iwe sudali kulakalaka kuti ungapatsidwe buku (pamodzi ndi uneneri) koma izi zidachitika pa chifundo chochokera kwa Mbuye wako…” Surah Al Qasas Aayah #86
Ngakhale kuti ma ulamaa ena anati mawu oti

ضَالًّا

Akutanthauza kuchoka kwake kumene anachoka mu Makkah, ndipo ena anati kuchoka kwake komwe anapita ku Shami, komabe mawu omwe ali oyambilirawo ndiomwe ali owona (onena kuti الضَلَالُ mu Aayayi ikutanthauza kusazindikira).

Allah ndiye Mwini kuzindikira konse. Timpemphe Iye kuzindikira ndi kudzipereka kwa Iye.

دَفْعُ إِيهَامِ الاضْطِرَابِ عَنْ آيَاتِ الكِتَابِ صــ368-369