KODI MA SHIATU RAAFIDA NDI ASILAMU OKHULUPILIRA?
Pomwe iwo anapanga shahaada ndipo amaikira umboni kuti palibe wopembedzedwa mwachoonadi kupatula Allah, ndikuti Muhammad ndi Mtumiki wake, komanso Qibla yawo ndi ku Makkah ndipo amaswali munsikiti?

Siyense yemwe wapanga shahaada asanduka Msilamu wokhulupilira. Ma munaafiq (achiphamaso) alinso ndi shahaada yomweyi, koma zikanakhala kuti shahada ndi swala zawo zidzawathandiza ku Aakhira, sibwenzi Allah Ta’la atawalonjeza kale kuti:

إِنَّ الْمُنَافِقِينَ فِي الدَّرْكِ الْأَسْفَلِ مِنَ النَّارِ وَلَنْ تَجِدَ لَهُمْ نَصِيرًا

“Ndithu achiphamaso adzakhala pansi penipeni pamoto; ndipo sudzampeza mthandizi woimira iwo” Surah Al-Nisaai 145

Tsopanotu ma Shia anachoka pa u munaafiq, ali penapake. Zili choncho chifukwa choti shahaada ya Tawheed ili ndi malamulo (macondition) ake komanso nsichi zake, ndiponso ili ndi zomwe zimapangitsa kuti shahaadayo iwonongeke. Choncho yemwe wapanga shahaada koma pambuyo pake wabweretsa zomwe zimaononga shahaadayo, kapena kuti akumasakaniza ibaada ndi shirk, basi shahaada imeneyo singazamuthandize kalikonse pantchito zake zabwino.

Mwapadera, dziwani kuti shahaada ya ma Shia anawonjezera gawo lotchula Ali, zomwe zikusemphana ndi shahaada yomwe anatisiyira Mtumiki salla Allah alaih wasallam.

Chimodzimodzi ma Shiatu Raafida; kufr yawo ndiyamphamvu kuposa ya Ayuda ndi Akhristu, monga mmene ma ulamaa akufotokozera; Sheikh Al-Qahtaanil Al-An’dalusi ananena mu shi’ri yawo, mwachidule kutanthauza kwake kuti:

“Musaganize (mwachikhulupiliro) kuti deen ya Rawaafid (ma Shia) ndikanthu, ndithu iwowo alibe malo mu deen poti ndima shaytwaan.”

Ma Rawaafid ndi oipisitsa padziko; amam’chemelera Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndikumawatukwana ma Sahaba ake, kuwada komanso kuwatulutsa Chisilamu.

Sheikhul Islam Ibn Taymiya Rahimahullah anatambasula zokhudza iwowa mu buku lawo la Minhaaji Al-Sunnat Al-Nabawiyya.

Ma Shiatu Raafida onse amawakudza manda ndi maliro (kukudza kwa ibaada). Imeneyo ndiye shirk yaikulu komanso ndikomwe ma shirk ena amachokera. Ma Rawaafidh ndi anthu oopsa kwambiri kwa Msilamu. Ndipo zimenezi kwa yemwe anawerengapo history ya anthu amenewa akudziwa zomwe ndikutanthauza. Pomwe omwe sakudziwa kalikonse za anthuwa, ndiaja omwe amanena kuti “bwanji mukuwatulutsa Chisilamu anthu oti anapanga shahaada?”

Sakuidziwanso shahaada ya Mashia kuti imadutsa motani. Ndi Msilamu wanji amene angaikire kumbuyo shahaada yomwe mkati mwake muli kutembelera ma Swahaba akuluakulu omwe anawalemekeza Mtumiki? Ndi Msilamu wanji yemwe angaikire kumbuyo gulu lomwe likutukwana komanso kutembelera mkazi wolemekezeka wa Mtumiki salla Allah alaih wasallam mai wa Okhulupilira onse? Ndi Msilamu wanji yemwe angalole gulu lina linyoze Aaisha radhia Allah Ta’la anha mkazi wa Mtumiki, mwana wa Mtsogoleri woyamba Mchisilamu pambuyo pa Mtumiki?

Akunyoza Hafsa mkazi wa Mtumiki, mwana wa Mtsogoleri wachiwiri pambuyo pa Mtumiki, akalowa bwanji kumoto mkazi wa Mtumiki inu nkukalowa ku Jannah? Akalowa bwanji kumoto atsogoleri a Chisilamu pambuyo pa Mtumiki (Abubakr, Umar, Uthman) inu atsogoleri a bid’ah komanso adani a banja la Mtumiki, ogalukira Sunnah za Mtumiki nkukalowa ku Jannah?

Pali zochitika zowononga zambiri zomwe zakhala zikuchitika mu mbiri ya Chisilamu zoyambitsidwa ndi ma Shia, anthu nkumaganiza kuti ndi Asilamu omwe akuchita, zoti sitingathe kuzitchula zonse poti ndi zitsanzo chabe. Zonsezo ndi maumboni oti amenewa ndi anthu oopsa ku Chisilamu kuposa adani a Chisilamu omwe ali owonekera aja.

Omwe amadziwa mbiri ya ma Raafida akuvomereza. Koma awo omwe sadziwa kanthu, ndiomwe amadana ndi kuwatchula ma Shiatu Raafida kuti ngoipa.

Tidziwe kuti chinthu cha chisanu ndi chimodzi (6) mu zinthu khumi (10) zomwe zimaononga Chisilamu, ndi:

البغض مما جاء به الرسول صلى الله عليه وسلم ولو عمل به كفر

Kukwiya ndizomwe anabweretsa Mtumiki salla Allah alaih wasallam, ngakhale atamazigwiritsa ntchito.

Zomwe anabweretsa Mtumiki salla Allah alaih wasallam zili mmagulu awiri: Qur’an ndi Sunnah. Choncho tikaonesetsa, anthu amenewa amanyoza Sunnah za Mtumiki nkumabweretsa sunnah zawo za mwaiwo zomwe ngakhale ma Swahaba sakuzidziwa. Allah Ta’la akunena kuti:

ذلِكَ بِأَنَّهُمْ كَرِهُوا مَا أَنْزَلَ اللَّهُ فَأَحْبَطَ أَعْمَالَهُم

“Zimenezo nchifukwa chakuti iwo azida zomwe Allah adavumbulutsa. Choncho waziononga zochita zawo” Surah Muhammad 9
Kukanira, kapena kudana ndizomwe anabweretsa Mtumiki kumaononga Chisilamu cha munthu, ngakhale atamagwira ntchitozo, Allah Ta’la amaziononga.

Allah Ta’la anatilamula kutsatira zomwe wabweretsa Mtumiki, ndipo Mtumiki anatilamula kuti titsatire ma khulafaa Raashideen (Abu Bakr, Umar, Uthmaan ndi Ali), koma ma Shia Raafida amakanira, ndipo sikukanira kokha koma kuwaponya ku moto ma Khalifa amenewa … pali Chisilamu pamenepo?

Note: Kumalawi kuno ma Shia tili nawo ponseponse koma ndiochepa omwe amatha kuwazindikira, chifukwa choti mphamvu zawo zikudzera mtimagulu tina tomwe timadzitcha kuti ndi Ahlu Sunnah, tomwe timazendewera muzochitika za ma shia, nkumasokeretsa nazo Ummah pang’onopang’ono. Nchifukwa chake sizikudabwitsa kuona ena akumawaikira kumbuyo mashia. Subhaanallah.