Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Yemwe ananena kuti: Watukuka ndi kudalitsika (Allah) Amene m’manja Mwake muli ufumu (wochita chilichonse pazolengedwa zonse); ndipo Iye ali ndi mphamvu yokwanira pachilichonse. Amene adalenga imfa ndi moyo kuti akuyeseni (mayeso) ndani mwa inu ali wochita zabwino (kwambiri). Ndipo Iye ndiWopambana m’mphamvu (salephera kanthu) ndiponso Wokhululukira (olakwa). Surah Al Israa 1-2.

Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Mtumiki wake wolemekezeka, yemwe ananena kuti: Ndili ndi chani ine padziko lapansi? Sindili kanthu padziko lapansi koma ngsti munthu wapaulendo yemwe wapumira ulendo wake pamthunzi, kenako wachoka kupitiriza ulendo wake nkuwusiya mtengowo.

M’bale wanga komanso mchemwali wanga wokondedwa, pali zinthu zina zomwe timangozichita chifukwa cha kuzolowera zomwe tinazipeza mchikhalidwe ndi mchikhulupiliro chakale, zomwe zimasemphana ndi malamulo a Chisilamu.
Anthu ambiri timasiyanitsa mapemphero/ibaadah pakati pa amuna ndi akazi, monga kuzinga nkhuku, kuswalira maliro, kusala masiku 6 a mwezi wa Shawwal, ndi zina zotero, zomwe tinlamulidwa kuti mwamuna ndi mkazi achite mofanana. Koma timawaletsa amuna kapena akazi kuchita ibaada inayake, malinga ndi zikhulupiliro komanso zizolowezi zathu. Ukutu nkulakwitsa kwakukulu mu Deen ya Allah.

Ndafunitsitsa kuti ndilongosole nkhani ya kuswalira jeneza munthu wamkazi, ndicholinga chofuna kuchotsa chikaiko chomwe anthu ena olalikira mma social media akuika mmitima ya Asilamu, makamaka Asilamu a chizimai, powauza kuti mkazi sakuyenera kuswalira maliro! Ndipo chomwe chautsa mapiri pachigwa ndinkhani yomwe inayamba kuzungulira pa WhatsApp mmasiku ochepa apitawa, pamene mai athu ena anatisiya (Allah awachitire chisoni ndikuwaika malo a Mtendere), ndipo azimai anapemphedwa kuti akaswalire nawo jeneza. Dongosolo loyenera linachitika ndithu motsatira malamulo, koma zitangochitika izi, ndipamene ndinazindikira kuti:

لا يجوز تأخير البيان عند الحاجة

Sitikuyenera kuchedweta kulongosola zinthu panthawi imene zikufunikira kuti anthu adziwe zoona zake zenizeni, chifukwa zinayankhulidwa zambiri, zosonyeza kuti ndithu Asilamu tidakali mum’dima pankhani ya maliro, ndipo tikuyenera kuthandizana kutuluka mumdima umenewu.

Amai ena anaona ngati maloza ndipo sanaswalire nawo, koma mmalo mwake anapita kwa Sheikh omwe amawaphunzitsa madrasa kuti akafunse za zimenezi. Tsoka ndiilo, a Sheikh atafunsidwa anayankha kuti zimenezo nzosatheka, ndipo ndibwino kwambiri osaswalira nawo maliro chifukwa amai wochita zimenezo amakhala m’gulu la anthu atsoka.

Sanapitilira powalangiza amai kuti mkazi ngakhale ataphunzira chotani, sangapange china chirichonse chomwe amuna amapanga mu Deen; mkazi kwake ndikuvomera basi, ndipo asaime pamodzi ndi amuna kumaswali. Malinga ndi kulongosola uku, mai aja anaona kuti ndithu ndimalodza azimai kuima kuswalira jeneza!

Abale olemekezeka M’chipembedzo, tikuwaphunzitsa zotani azimai athu? Kodi ndife okhonzeka kudzayankha funso limeneli pamaso pa Allah pambuyo poti tawasokeretsa anthu mazanamazana chifukwa chomusokeretsa mzimai mmodzi? Dziwani kuti mzimai ndi madrasa, ndi sukulu, ndipo mukam’khonza bwinobwino, mwakhonza gulu lonse, mukamusokeretsa, mwasokeretsa gulu lonse. Tipalingalire pamenepo. Tiphunzitse zomwe anatisiyira Mtumiki wanthu salla Allah alaih wasallam yemwe ananena kuti:

تركت فيكم أمرين فيما إن تمسكتم بهما لن تضلوا أبدا؛ الكتاب والسنة

Ndakusiyirani zinthu ziwiri, zomwe ngati mungazigwiritse osazisiya, simudzasochera mpaka kale; Qur’an ndi Sunnah. Komatu lero tazitaya zinthu ziwiri zija!

نسأل الله أن يعيدنا إلى صراط مستقيم

Timpemphe Allah atibwezeretse munjira yoongoka.

Tsopanotu, zomwe zikumvetsa chisoni ndizoti Asilamu ambiri lero lino tikutenga zinthu zopeka, ma bid’ah, ndikuwasandutsa kukhala zowona. Izi vuto silikuchokera mwa ochitawo kwenikweni, koma ma Sheikh, chifukwa iwo omwe ali ndikuzindikira ndamene amakhala chete kumawonelera Ummah ukusochera, osawaphunzitsa anthu choonadi, akuti kuopa kuti akawauza kuti zomwe akuchitazo nzolakwika, abweretsa fitna ndi mikangano pakati pa anthu! Inu, mukuopa kubweretsa fitna yoti munaibweretsa kalekale ndipo yamwa nzeru za anthu? Lero chitani zoti muwavuule anthuwo mu fitna yomwe munawagwetsera kale, fitna ya umbuli mu Deen. Ndipo izi muchite ndicholinga choti mupulumuke ku mawu oti:

حين سكت أهل الحق عن الباطل توهم أهل الباطل أنهم على حق

Pamene anthu ozindikira choonadi (mmalamulo a Deen) akhala chete pamene zopeka zikuchitika, ochita zopeka aja amaganiza kuti ali mu choonadi, ndipo zomwe akuchitazo zili mmalamulo a Deen. Mapeto ake malamulo a Deen omwe akutsutsana ndi zopeka zomwe anazizolowera anthuzo, zimasanduka kukhala zopeka kwaiwo. Nchifukwa chake lero lino tidakalimbanabe … pakati pa Ahlul Haqq (Anthu a Haqq) ndi Ahlul Baatwil (Anthu a Zopeka). Koma pasavute, palibe yemwe amafuna kukhala mugulu la anthu opeka, choncho solution yake ndikumangoyang’ana mu Qur’an ndi Sunnah basi.

Abale olemekezeka, Swalat ya Jeneza ndi faradh, lamulo lokakamizidwa kwa mwamuna ndi mkazi, ndipo mtundu wa faradh iyi ndi faradh kifaaya, ibaadah yomwe imatheka kukwaniritsa gawo la anthu, ndipo gawo lina la anthu likapanga kuchita ndiye kuti palibe chovuta. Koma ngati asapezeke ngakhale mmodzi ochita, ntchimo losachita ibaada imeneyo limagwera kwa onse.

Chiphunzitso cha Mtumiki salla Allah alaih wasallam pa zomwe tikuyenera kuchita pamwambo wa maliro ndi chiphunzitso chokhacho chomwe chili chopambana, komanso chosiyana kwambiri ndi ziphunzitso za zipembedzo zina kapena mitundu ina ya anthu; chifukwa choti muchiphunzitso cha Mtumiki salla Allah alaih wasallam mukupezekamo kuchitira zabwino maliro, kuwachitira zinthu zoyenera zomwe zikawathandize mmanda komanso tsiku lowuka, komanso kuwachitira zabwino abale a omwalirayo.

Chinansondichakuti m’mwambo wa maliro a Chisilamu mukupezeka kupembedza komwe anthu amoyo amapembedza Mbuye, Mlengi wawo.

Zinthu zokakamizidwa zoyenera kumuchitira munthu womwalira zilipo zinayi, ndipo muzinthu zinayi zimenezi, zitatu zimachitidwa ndi amuna komanso akazi, pomwe chinthu chimodzi chimachitika ndi amuna okha basi:

1. Kusambitsa (ghusl); ntchito iyi imachitika ndi anthu ochepa pomwe ena ali panja. Womwalira akakhala mwamuna, amasambitsa amuna ochepa, ndipo akakhala mkazi, amasambitsa akazi ochepa. Choncho, amuna komanso akazi akuyenera kusambitsa maliro.

2. Kuveka nsanda (kafn); ntchito iyinso imachitikanso ndi anthu ochepa, amaipitiriza omwe asambitsa aja, koma ndizololedwa kuti abwere ena kudzathandizira, ngati omwe asambitsa aja alibe kuzindikira kokwanira pa mavekedwe a nsanda. Choncho, amuna ndi akazi akuyenera kuveka nsanda.

3. Kuika mmanda (dafn); ntchito iyi imachitika ndi amuna okhaoka, ndipo ochepa, pomwe ena akudikira panja pa manda. Mkazi sakuloledwa kupita kumanda pamene maliro akukakwiliridwa, komanso sakuloledwa kuperekeza malirowo pamene akuchoka pakhomo. Choncho muntchito zinayizi, ntchito iyi yokha ndiyomwe mkazi sakuyenera kugwira nawo. Izi ndimalinga ndi malamulo a Chisilamu, osati malinga ndi chikhalidwe chomwe anthu anazolowera.

4.K Kuswalira Maliro/Jeneza (Swalaatul Janaazah); imeneyi  ndi ntchito yomwe imachitika ndi anthu omwe abwera pamwambo wa maliro (amuna ndi akazi omwe). Ndizololedwa kuswalira maliro anthu ochepa ndipo ena osaswalira, ngati pali zifukwa zokwanira kuwaletsa kuswaliko.

Nkhani yathu yagona pakuti: Malamulo a Chisilamu, Shariah, akuti bwanji pa swalaat janaaza ya azimai? Kodi mkazi ndiwololedwa kuswalira maliro?

Malinga ndimmene tamvera mu kufotokoza kwanga pa ntchito zinayi zoyenera kuchitika pa mwambo wamaliro, tamva kuti akazi ndiololedwa kuswalira maliro. Koma tsopano izi anthu ambiri akhonza kukhala ndi mafunso ofanana: zitheka bwanji? Chisilamu chake chiti chimenecho? Ku Malawi kuno mzimai uti yemwe anaswalirapo jeneza?

Koma ndithu mafunso onsewo yankho lake likupezeka malo amodzi; poti tikufuna kudziwa kuti Chisilamu chake chiti chomwe chikuloleza akazi kuswalira jeneza, funso ili likuikira umboni kuti swalaat iliyonse timaitenga kuchokera mu Qur’an ndi Sunnah za Mtumiki wathu wolemekezeka, salla Allah alaih wasallam.

Choncho tiyeni tiwone kuti Mtumiki anatiuza chani zokhudza swalaat zonse mopanda kupatula: Iye anati:

صلوا كما رأيتموني أصلي

Swalini monga mmene ine ndimaswalira
Swalaat zilipo zamitundu ingapo monga swalaat za fardh, za Sunnah, swalaat yopempha mvula, Eid, jeneza ndi zina zambiri. Zonsezi lamulo lake ndilofanana pakati pa amuna ndi akazi. Tilibe umboni wopatula kuti Hadith ija amatanthauza swalaat zisanu zokha ndi ma Sunnah ake, koma kuti amatanthauza swalaat zonse. Choncho, ife tisapatule.

Kuchokera mu chitabu cha Fatawa Nurun ‘alaa Ddarbi cha Sheikh wolemekezeka komanso wodalirika, Muhammad bun Saalih Uthaymin vol.6 pg. 96 Fatwa #3310, munafunsidwa funso lomweli motere:

Nthawi zina mu Mzikiti Wolemekezeka (Masjidul Haraam) mumalengezedwa kuti tiswalire maliro, kodi ndizololedwa kuti azimai apange nawo swalaat imeneyi (ya janaaza kapena swalaatul ghaaib) pamodzi ndi amuna?

Sheikh athu anayankha kuti:
Inde, mzimai ali ngati mwamuna pa swalaat ya maliro, monga swalaat zina zonse; pamene nthawi yoti swalaat ichitike yakwana, akhonza kuswali nawo, ndipo apeza thawaab chimodzimodzi mmene apezere mwamuna, chifukwa maumboni a swalaat imeneyi sanapatule kalikonse.

Ndipo malinga ndi olemba mbiri ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam (Seerah), Asilamu anaswalira janaza ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam magulumagulu: amuna pawokha, kenako azimai pawokha. Choncho palibe vuto, ndipo zoyenera kuchitika ndizoti pamene janaza yafika ndipo mzimai alipo komanso ali wokhonzeka, tipange dongosolo loti aswalire nawo janazayo, tisachitire umbombo thawaab za swalaat ya Jeneza.

Anthu ena chikaiko pankhani ya mzimai kuswalira jeneza, chimawafika pa maimidwe a pa swalaat, poti tinazolowera kuti swalatiyi imachitika pabwalo, kodi azimai aime nawo ndipo aziwonana ndi amuna?

Malo oswalira jeneza tiwasankha malinga ndi mmene tsikulo liliri, koma sikuti zinaikidwa kuti swalaatiyi izichitikira pabwalo basi. Malo awa tikhonza kuswalira jeneza:

1. Munzikiti; ndipo kutero kukhonza kupereka mpata wokwanira kwa azimai omwe akufuna kuima nawo. Umboni wakuswalira jeneza munzikiti ukuchokera mu Hadith:

عن عبادة بن عبد الله بن الزبير أن عائشة أمرت أن يمر بجنازة سعد بن أبي وقاص في المسجد فتصلى عليه فأنكر الناس ذلك عليها فقالت ما أسرع ما نسي الناس ما صلى رسول الله صلى الله عليه وسلم على سهيل بن البيضاء إلا في المسجد.

Ubbaada bun Abdillah bun Azzubair radhia Allah anhu, yemwe akunena kuti Aaisha radhia Allah anha, analamula kuti jeneza ya Sa’d bun Abi Waqqaas ilowetsedwe mu Mzikiti kuti nayenso aswalire nawo. Pamene (analowetsa mumzikiti ndikupemphelera,) anthu anamva zomwe zinachitikazi (zoti azimai aima nawo pa swalaat Janaza), anayamba kuyankhula zambiri zotsutsana ndi mchitidwewo, mpaka anali kunena kuti imeneyo ndi bid’ah (zopeka), ndipo kuti jeneza sikuyenera kulowetsedwa munzikiti. Pamene Aaisha radhia Allah anha anamva zoyankhulazi, anati: “Bwanji anthu akuiwala mofulumira kuti Mtumiki salla Allah alaih wasallam anaswalira jeneza ya Suhayl bun Al-Baydhwaa munzikiti?” Muslim, باب الصلاة على الجنازة في المسجد, Hadith no. 973

Kodi nkhani iyi yomwe inachitika ndi Mai wathu Aaisha, sikufanana ndi zomwe zikuchitika masiku anozi? Tinene kuti ma Sheikh omwe akuletsa Azimai kuswalira Jeneza Hadith imeneyi sanayione?

Ikupezeka mu Sahih Muslim, باب الصلاة على الجنازة في المسجد, Hadith no. 973. Ndipo maphunziro alipo angapo mmenemo: Azimai aziswalira Jeneza, komanso munzikiti ndiamodzi mwa malo oswalira jeneza.

2. M’nyumba: Ndizololedwanso kuswalira jeneza mnyumba, makamaka azimai. Ndipo izi ndizosavuta, panthawi imene azimai amaliza kukhonza maliro a mzimai mzawo, asanatulutsidwe mnyumbamo azimai aswalire, kenako akaswalire amuna. Chimodzimodzinso ngati wamwalirayo ndi mwamuna, azimai akhonza kuswalira paokha mnyumba … pamenepa nditambasula bwinobwino kutsogoloku, in shaa Allah.

3. Panja pa Mzikiti: Ndizabwino kwambiri kukhonza malo oti swalaat ya Janaaza izichitikira, panja pa mzikiti, poti ichi chinali chizolowezi nthawi ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Umboni:

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال نعى لنا رسول الله صلى الله عليه وسلم النجاشي صاحب الحبشة يوم الذي مات فيه فقال: “استغفروا لأخيكم” وصف بهم بالمصلى فكبر عليه أربعا

Hadith ikuchokera kwa Abi Hurairah radhia Allah anhu, anati: Pamene Mtumiki salla Allah alaih wasallam analengeza za imfa ya Mfumu (Najaashi) yaku Ethiopia patsiku lomwe anamwalira, anati: “M’pemphereni m’bale wanu chikhululuko”, ndipo anawaika mmizere pamalo oswalira, kenako anamupemphelera ma takbeera anayi. Sahih Al-Bukhari no. 1327

Mu Hadith ina,

عن عبد الله بن عمر رضي الله عنهما أن اليهود جاءوا إلى النبي صلى الله عليه وسلم برجل منهم وامرأة زنيا فأمر بهما فرُجما قريبا من موضع الجنائز عند المسجد

Yochokera kwa Abdullah bun Umar radhai Allah anhuma, yemwe anati Ayuda anabweretsa kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam mwamuna ndi mkazi womwe anachita zinaa, Mtumiki analamula kuti agendewdwere pamalo pamene anali kuswalirapo Janaazah.

Ndalonjeza kuti ndilongosola bwino mfundo ya kuswalira maliro mnyumba. Imaam Al-Nawawi rahimahu Allah analongosola mu chitabu chake chotchedwa Sharhul Muhaddhab, vol.5/172 kuti:

Tsopano azimai, ngati pali amuna, aswali limodzi potsatira imam mmodzi … Imaam Al-Shaf’i rahimahu Allah: ndizokondedwa (mustahabb) azimai kuswalira maliro aliyense payekhapayekha… Sharh Al-Muhaddhab vol.5/172

Nawo Sheikh Ibn Uthaymin rahimahu Allah atafunsidwa kuti kodi mkazi ndiololedwa kusonkhanitsa abale ake achizimai mnyumba ndikuwaswalitsa swalaat ya jeneza ya m’bale wawo yemwe wamwalira pakhomopo? Iwo anayankha kuti:
Inde, palibe choletsa kuti mzimai aswalire jeneza, munzikiti pamodzi ndi anthu ena, ngakhalenso mnyumba. Chifukwa choti mzimai sakuletsedwa kuswalira maliro, koma akuletsedwa kupita kumanda. Majmu’ Fatawa vol.17/157

Atafunsidwanso za lamulo la mzimai kuswalira jeneza munzikiti kapena kunyumba, iwo anayankha kuti: Swalat ya jeneza kwa mkazi ndibwino kuswalira mnyumba, zimenezo ndiye zomwe zili zabwino. Koma ngati angatuluke kukaswali pamodzi ndi anthu kumzikiti, palibe vuto. Koma chifukwa choti zimenezi sizili common, sizili zofalikira pakati pathu, ngati angachikhanzikitse kuti azimai asamaswalire maliro, palibe vuto ngakhale asaswalire, monga mmene chizolowezi chathu chiliri. Koma chizolowezi chimenecho asachipange kukhala phata la deen, nkuyamba kulalikira kuti mkazi ndiwoletsedwa kuswalira jeneza moti akangoswalira amapeza tsoka. Ayi, kumeneko ndikuwnjezera malmulo mu Deen. Ngati wafuna kuswalira aswalire, ngati anafune, asiye. Pajatu ndi faradh kifaayah… Majmu’ Fatawa vol.17/114

Muzokamba zonsezi, titenge zoti mkazi ndiwololedwa kuswalira maliro, chimodzimodzi momwe aliri mwamuna. Swalaat iriyonse mkazi aswali.

Pomaliza ndikupempha Allah atipatse kuzindikira mu deen komanso kukhala ndi chidwi chofunafuna maphunziro a Chisilamu.