Ndilandireni nonse, pamene tikuyamba program yachiwiri pambuyo pakumaliza pakumaliza program yoyamba yomwe inali Mgwirizano wa pakati pa Munthu ndi Majinn, ndipo mmenemo tafotokoza mmene ubalewu umachitikira, mavuto amene ubalewu umabweretsa kwa munthu, mmene tingadzitetezere kuti mavutowo asatipeze komanso njira ya machiritso ochokera mu Qur’an ngati mavutowo atatipeza. Pezani ma audio 51 a programuyi (Pa WhatsApp)

Tsopano monga tinalongosolera kale zifukwa zomwe zimapangitsa kuti mavuto amenewa adzipezeka pakati pathu, tinatchula chifukwa chimodzi chomwe ndi kuchuluka kwa ziphunzitso zosocheretsa, komanso kuchuluka kwa ma bid’ah mu society kaamba ka umbuli wa maphunziro a deen, zimene zimapangitsa kuti anthu adzikhulupilira zinthu zomwe Chisilamu sichinaphunzitse, chinaletsa, komanso kudalira njira za shirk pofuna kudziteteza kapena kuchira ku ufiti ndi ziwanda.
Choncho mu program yomwe tikuiyambayi tikufuna kulongosola zina mwa zikhulupiliro zimene zimatsogolera kuti Ummah udzionongeka mnjira imeneyo ndi njira zinanso. Iyitu ndi program yomwe ndaitcha Magulu a Osochera a Mchisilamu ndi Zikhulupiliro zawo.

Mu audio #0 yotsegulira programuyi, talongosolamo ma aayah ndi hadith zomwe zikuikira umboni kuti Chisilamu ndi chimodzi ndipo Allah Ta’la analetsa kugawanika timagulu mu deen, komanso analetsa kutsatira timagulu timene taganika mu deen, koma anatilamula kukhala mu gulu limodzi la Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndi ma Sahaba ake…limenelo ndiye gulu lolungama. Mtumiki salla Allah alaih wasallamanso chimodzimodzi analangidza ponena kuti ummah wake udzagawanika magul 73 ndipo limodzi lokha likalowa ku Jannah ena onsewo ku moto, atafunsidwa kuti gulu lopambanalo ndiye liti, anayankha kuti Jamaah, mu report lina anayankha kuti gulu lomwe ali Mtumiki ndi ma Sahaba ake. Kutyanthauza kuti ife Asilamu tidzifufuza gulu la Mtumiki wa Allah ndi ma Shaba ake anali, ndipo tikapezeka kuti talowa mu gulu lomwe lirinso ndi timagulu tinzake, tidziwe kuti tasochera, tikuyenera kubwelera.
Tabwelerani ku audio yotsegulira ku mumve ma aayah ndi ma Hadith amenewo.

Mosataya nthawi, tiyeni tiyambe ndi gulu lomwe linali loyambilira kupatuka mu Ahlu Sunnah wal Jamaah, linayamba liti, anayambitsa ndani, nanga zikhulupiliro zawo ndi zotani, nanga chinachititsa kuti apatuke ndi chani?
Ilitu ndi gulu lotchedwa Khawaarij

MA KHAWAARIJ

Munthu aliyense yemwe wapatuka mu utsogoleri wa Haqq womwe gulu la anthu lagwirizana, amatchedwa Khaarijiyya; ngakhale kutulukako kutakhala kwa nthawi ya ma Sahaba kuwatulukira ma Imaam anthawi imeneyo, kapena pambuyo pa ma Sahaba nthawi ya ma Tabieen komanso ma imaam a nthawi zonse mpaka munthawi yathu ino. Izi ndi monga mmene akukambira mu buku la الملل والنحل lolembedwa ndi الشهرستاني.
Sheikhul Islam Ibn Taimiya rahimahullah anati:

والخوارج هم أول من كفّر المسلمين، يكفرون بالذنوب ويكفرون مَن خالفهم في بدعتهم ويستحلون دمه وماله، وهذا حال أهل البدع، يبتدعون ويكفرون من خالفهم

“Ma Khawaarij ndi anthu oyambilira kuwapanga Asilamu kuti ndi okanira; iwo amakanira machimo komanso amawachita omwe samawatsatira mmabid’ah awo kuti ndi anthu okanira. Amaloleza kukhetsa mwazi wa omwe akusemphana nawo komanso kusakaza chuma chawo. Ichitu ndiye chikhalidwe cha anthu a bid’ah; amachita bid’ah ndikumawapanga omwe akutsutsana nawo kuti ndi anthu okanira.” Izi zikuchokera mu buku la Ibn Taymiya lotchedwa Majmoo’ Fatawa, vol.3/279

Ndiye pali gulu lina lotchedwa a Al Wa’eediya mkati mwa ma Khawarij omwe amkhulupilira kuti yemwe wachita tchimo lalikulu ndi kafir ndipo akalowa kumoto خالدين فيها أبدا osatulukanso. Izi zikuchokera الملل والنحل vol.1/129
Pambuyo pa kumwalira kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam, kunaoneka timagulu, tima movement tomwe nthawi ya Mtumiki kunalibe. Magulu ena anali oyambitsidwa ndi ma munaafiq amene anasiya Chisilamu, awa ndi anthu amene Abubakar radhia SAllah anhu anawathira nkhondo, chimodzimodzinso nthawi ya Uthman radhia Allah anhu, ma fitnah ndi zochitika zina zinasatidzana mu ulamuliro wa Chisilamu cholinga chosokoneza chitetezo cha Chisilamu.

Tsopano munthawi ya Ali Radhia Allah anhu, kunaonjezerekanso timagulu tina ndi zikhulupiliro zosiyanasiyana, monga Shi’ah ndi Khawaarij. Awiri onsewa anali ndi gawo pa utsogoleri wa Ali radhia Allah anhu: Ndipo omwe anali kuima mu swaff imodzi ndikukhala olimba pakumukonda Ali komanso kutsimikiza za ukhalifa wake pambuyo pa Mtrumiki salla Allah alaih wasallam posakhala wina aliyense, amatchedwa Shi’iyah, ndipo omwe amakanira za ukhalifa wake ndikutuluka mu ulamuliro wake, komanso osasangalatsidwa ndi kuyendera malamulo ake, ameneyo amatchedwa Khaarijiyyah.
Ataonekera ma Khawaarij poyera, Ali radhia Allah anhu anawathira nkhondo…
Kodi nanga ma Khawaarij ndi ndani? Nanga zikhulupiliro zawo ndi zotani?

Ma Khawaarij ndi Ndani?
Khawaarij ndi gulu lomwe linaukira Ali radhia Allah anhu pambuyo pa kuvomereza chigamulo (Attahkeem) chomwe chinachitika pankhondo ya Asswiffeen, pakati pa iye ndi Mu’aawiyah bun Abi Sufyaan radhia Allah anhuma.

Ma Khawaarij ali ndi maina awo ena amene anadziwika nawo malinganso ndi kugawanika kwawo komwe kunachitika. Maina monga Hurooriyyah, Al Shuraat, Al Maariqah, Al Muhakkamah. Maina amenewa amasangalatsidwa nawo ndithu kupatula dzina loti Al Maariqah, chifukwa cha kudana nazo zoti iwowo ndi owukira deen monga mmene thungo imachokera nkufikira mwa munthu wobaidwa. monga mmene Mtumiki salla Allah alaih wasallam anawasimbira mu hadith yolemekezeka:

“Mu Ummah umenewu kudzabwera anthu omwe azidzanyozetsa swalat zanu pa swalat zawo, azidzawerenga Qur’an koma simadzapyola kukhosi kwawo (samadzaigwiritsa ntchito), azidzasiya deen monga mmene nthungo imasiyira choponyera pokalowa mwa munthu ndikumayang’ana kuti kodi nthungoyo yatulutsa magazi? Sahih Al Bukhari.

Pomwe Imaam bun Hazm Al Dhwaahiri akuona kuti dzina la Khaariji limapita kwa aliyense yemwe akuchita zofanana ndi omwe anatuluka mu ulamuliro wa Ameeril Mu’mineen Ali radhia Allah anhu ndikutsatira zikhulupiliro zawo. Iye akunena kuti: “Yemwe wagwirizana ndi ma Khawaarij pokanira chigamulo komanso kuwapanga ochimwa machimo aakulu kuti ndi makafir ndikuwapanga kuti akalowa kumoto mpaka kale, komanso kuti utsogoleri ndiwololedwa kupatula kwa ma Quraish, ameneyo ndi Khaarijiy…

Chiyambi cha Ma Khawaarij
Ma ulamaa ena anati kuyambika kwa Khawaarij kunali nthawi ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam, kuchokera pamene Dhul Khuwaiswirah ochokera mwa ma Bani Tamim. anatsutsa Mtumiki salla Allah alaih wasallam poyankhula ndi mau ake, monga mmene zalongosoleredwa mu Sahih Al Bukhari, mu Hadith ya Abi Saeed Al Khudari, anati:

لما نحن عند رسول الله صلى الله عليه وسلم وهو يقسم قسما أتاه ذو الخُوَيصِرة وهو رجل من بني تميم فقال: يا رسول الله اعْدل، فقال: (ويحك ومن يعدل إذا لم أعْدِلْ ،وخسرت إن لم أكن أكن أَعْدِلُ) فقال عمر: يا رسول الله اذَن لي فيه فأضربَ عنقه، فقال: (دعْه فإن له أصحابا يحقر أحدُهم صلاته مع صلاتهم وصيامه مع صيامهم يقرءون القرآن لا يجاوز تراقيَهم يمرقونمن الدين كما يمقر السهم من الرّميّة) – البخاري 3610

Hadith yomwe inachokera kwa Saeed Al Khudri, anati: Pamene tinali ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam panthawi imene anali kugawa zinthu, kunafika Dhul Khuwaisira wochokera ku Bani Tamimn ndipo anati: “E Mtumiki, chitani chilungamo” Mtumiki anati: “Zodandaulitsa kwa iwe! kodi ndindaninso wina yemwe angachite chilungamo ngati ndingapande kuchita ine? ndidzakhala oluza ndikapanda kuchita chilungamo”. Umar radhiallah anhu anati: “E Mtumiki, ndiloleni ndingomudula mutu wakeyo ameneyu” Mtumiki anati: “Musiyeni, poti iye ali ndi anzake omwe omwe azidzapemphera ndikusala, moti ukhonza kudzaona ngati kusala kwako nkopanda ntchito poyerekeza kusala kwa iwowo. Azidzawerenga Qur’an koma samadzaigwiritsa ntchito) ndipo adzachisiya Chisilamu monga mmene thungo imalowera mthupi lamunthu obayidwa…”

Al Aajiriy rahimahullah anati:

والخوارج هم الشراة الأنجاس الأرجاس، ومن كان على مذهبهم من سائر الخوارج، يتوارثون هذا المذهب قديما وحديثا، ويخرجون على الأئمة والأمراء، ويستحلون قتل المسلمين.
فأول فرنٍ طلع منهم على عهد رسول الله صلى الله عليه وسلم هو رجل طعن على رسول الله وهو يُقَسّم الغنائم بالجعرانة، فقال: اعدل يا محمد، فما أراك تعدلُ …

Ma Khawaarij ndi anthu oipisitsa, onyansa, ndipo otsatira madh’hab a gulu limeneli la ma Khawaarij akhala akusiyirana madh’hab amenewa kuyambira kalekale mpaka panopa, ndipo awa ndi anthu amene amatuluka mu utsogoleri wa ma imaam ndi atsogoleri ena, komanso kupha Asilamu amakupanga kukhala halal. Munthu oyambilira kuonekera mwa ma Khawaarij nthawi ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali (Dhul Khuwaisira) munthu yemwe anamunyoza Mtumiki panthawi imene anali kugawa ziweto ku Ju’raanah, ndipo anati: Iwe Muhammad, ndikukuona sukuchita chilungamo…mpaka kumapeto kwa hadith. Izi zikupezeka mu bukhu ltchedwa Al Shari’ah, page 21.

Vuto la mkulu ameneyu linali loti anasankha kukhulupilira maganizo ake ndikutsutsana ndi maganizo a Mtumiki salla Alaih wasallam. Akanafatsa ndikuganizira, akanadziwa kuti kuti iyeyo alibe maganizo oposa a Mtumiki, komanso alibe mau amphamvu kuposa a Mtumiki. Ndipo otsatira a munthu ameneyu, ndi amene analimbana ndi Ali bun Abi Taalib radhia Allah anhu.

Mwa ma ulamaa omwe anatsimikiza kuti yemwe anayambitsa Khawaarij anali Khuwaiswirah, ndi Abu Muhammad bun Hazm ndi Al Shahristani.

Ndipo ma ulamaa ena ananena kuti kuyambika kwa Khawaarij kunali nthawi ya Uthman radhia Allah anhu pazochitika za fitnah zomwe zinathera kuphedwa kwa Uthmaan. Ndipo Ibn Kathir anawatchula anthu amenewo kuti ndi ma Khawaarij.

Iyi ndi audio yoyamba, mukhonza kupeza ma audio onse 25 (Pa WhatsApp)