الفتاوى الشرعية في القضايا العصرية
#ص٨٢-٨٥
Fatawa Al Shar’iyya fil Qadhaayal ‘Asriya
Page 82-85
“Kumuchita munthu kaafir yemwe ali osayenera kumuchita kaafir sizololedwa. Amene akuyenera kumuchita kaafir ndi amene ali oyenera kumuchita kaafir.
Amene ali osayenera kumuchita kaafir asachitidwe kaafir.
Munthu amene ali Msilamu, ndiye wachita chinthu cha ukafir, tisamutchule kuti ndi kaafir, mpaka atapezeka ndi mbiri zomwe zingamuchititse kukhala kaafir. Koma ngati mbirizo sizinapezeke, kumpanga kaafir ndi kulakwa ndipo ndi zosemphana ndi zomwe Allah wanena.”

Kupereka chigamulo (judgment) choti munthu wakuwakuti ndi kaafir kuchokera mu Chisilamu chake kumachokera kwa Allah Ta’la ndi Mtumiki wake, monga mmene zina zonse zimapangidwira halaal kapena haraam…palibe amene amalamula kuti chakuti ndi haraam kapena halaal posakhala kuchokera kwa Allah ndi Mtumiki wake.
Mau oti kafara kapena kaafirun omwe akupezeka mu Qur’an ndi mma Hadith potanthauza ntchito kapena zochita za munthu, sikuti mau onsewo amatanthauza kuti munthuyo wakanira kapena wapanga kufr yaikuli yomutulutsa mu njira ya Chisilamu.
Mwachitsanzo, Allah Ta’la akunena kuti
ومن لم يحكم بما أنزل الله فأولئك هم الكافرون
ndipo yemwe alamule posakhala kuchokera mu zomwe Allah wavumbulutsa (Qur’an) iwo ali okanira (makafir) Al Maaidah 44
Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti
سباب المسلم فسوق وقتاله كفر
Kumutukwana Msilamu ndi kutuluka mchilamulo cha Allah ndipo kumupha ndi kufr (kukanira)
Aayah ndi Hadithiyo sizikutanthauza kuti munthu ochita zimemezo ndi kaafir woti watuluka Chisilamu, koma kuti wachita tchimo lalikulu lofunika apange tawbah ndipo amukhululukira basi zithere pompo.
Choncho pamene kumugamula munthu kuti ndi kaafir kuli kochokera kwa Allah Ta’la ndi Mtumiki wake, ife sitikuloledwa kumugamula Msilamu kuti ndi kafir kupatula kuchokera mmaumboni a mu Qur’an ndi Sunnah, ndipo maumboniwo akhale loud ‘n clear pa kulongosola za kufr ya munthuyo, osati kungoyerekeza kapena kuganizira, kusonkhanitsa mau a ma ulamaa ena nkuwabweretsa pa munthuyo kuti zigwirizane timtulutse mu Imaan ndi Tawheed!
Kupanga choncho kumabweretsa malamulo oopsa pakati pa anthu mu deen.
Pachifukwachi Mtumiki salla Allah alaih wasallam anachenjeza za kumangompanga aliyense kuti ndi kaafir, pomwe zoona zake ndizoti sali kaafir…
أيما امرئ قال لأخيه: يا كافر، فقد باء بها أحدهما، إن كان كما قال وإلا رجعت عليه
Yemwe anganene kwa mzake kuti ndiwe Kaafir pomwe munthuyo sali choncho, ndiye kuti u kafiriwo ubwelera kwa oyankhulayo…
Komanso ena amati akaona Msilamu wapanga cholakwika, amakonda kuwalangiza Asilamu amzawo kuti: ameneyo ndi mdani wa Allah! – ameneyo ndi munthu oipisitsa mu deen timtalikire! popanda umboni wa zomwe akuyankhulazo.
Imeneyo si njira yokhonzera zolakwika mwa munthu ndinso mu deen. Koma kumeneko ndi kudzisonkhezera wekha nkhuni za kumoto.
Munthu amene angamuganizire mzake zoipa ndikumuponya mu kufr yatuluka mu deen kumachita munthuyo sali kafir, mau akewo am’bwelera oyankhulayo
Kufulumira kumpanga wina kuti ndi kaafir, kumabweretsa zoipa pakati pa anthu monga kukhetsa mwazi wa yemwe tampanga kuti wasiya deeniyo, kuladidwa chuma, kuletsedwa kulandira gawo la chuma chosiyidwa (Inheritance/Miraath), kuletsedwa nikaah ndi zina zambiri zomwe zimadza kamba ka kutuluka mu deen…
Tipewe kuganizirana u kafir wotulutsana Mchisilamu
Zonse izi ndi kwa okhulupilira  wamba,, opanda udindo pakati pa Asilamu.
Komatu akhala kuti yemwe akuchitiridwa zimenezoyo ndi mtsogoleri wa Asilamu, sheikh wodziwika ndi ubwino pakati pa Asilamu, yemwe amaitanira ku tawheed, yemwe ali ndi udindo wotsogolera anthu pa swalaat ngati imam, yemwe amaphunzitsa Asilamu ndikumatulutsa ma sheikh ndi zina zotero… Ndi zoopsa kwambiri kungobwera poyerayera kumpanga kaafir munthu oteroyo, pa zifukwa zoti akhonza kukhonzedwa ndikupanga tawbah.
Akamati kuti uyu ndi sheikh wamkulu sizikutanthauza kuti samalakwitsa, sitikutanthauza kuti iyeyo ndi Mtumiki amalandira wahy, maphunziro akewo sakumuyeretsa kukhala 100% ochita zabwino. Ngakhale Mtumiki salla Allah alaih wasallam, anati
كل بني آدم خطاء وخير الخطائين التوابون
Munthu aliyense amachimwa, ndipo mwa ochimwa omwe ali abwino ndi awo omwe amapanga tawbah
Choncho kumutulutsa Sheikh kapena imaam mu tawheed, ndi kumpanga kukhala mushrik..kumutulutsa mu chikhulupiliro ndi kumpanga kukhala kaafir, tamuponya Sheikh mu gulu la akhristu ndi ayuda a masiku ano, chifukwa chongoganizira malinga ndi nzeru zathu.
kodi nanga ifeyo ndi oyera 100% tilibe machimo?
Ayi ndithu, ndi Allah yekha amene ali oyera ndipo ife tikuyenera kumatenga malamulo omugamulira munthu kuchokera kwa Iye ndi Mtumiki wake.
Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:
…إلا أن تروا كفرت بواحا عندكم فيه من الله برهانا
musampange wina kuti ndi kafir
pokhapokha mutaona mwa iyeyo ukafiriwo mwa clear, komanso mukhale ndi umboni wochokera kwa Allah Ta’la
ukafir sumakwanira mwa Msilamu potengera zochita za machimo monga fisq, dhulm, kumwa mowa, kuyenda juga, ndi kuchita za haraam
ukafir sungakwanire mwa Msilamu ngati sunaonekere poyera
ukafir sukwanira mwa Msilamu popanda umboni wa direct, komanso wa Sahih wopanda zigamba, wongoganizira kapena kutengera ma example chabe
ukafir sukwanira mwa Msilamu potengera mau a sheikh wina wake ngakhale atalemekezeka chotani,  ngakhale atakhala ophunzira chotani, ngakhale atakhala okhulupilira motani…  Ngati mau akewo sakuchokera mmaumboni a mu Qur’an ndi Sunnah, akunama ameneyo.
Allah Ta’la akunena mu Surat Al A’raaf 33 kuti
قُلْ إِنَّمَا حَرَّمَ رَبِّيَ الْفَوَاحِشَ مَا ظَهَرَ مِنْهَا وَمَا بَطَنَ وَالْإِثْمَ وَالْبَغْيَ بِغَيْرِ الْحَقِّ وَأَن تُشْرِكُوا بِاللَّهِ مَا لَمْ يُنَزِّلْ بِهِ سُلْطَانًا وَأَن تَقُولُوا عَلَى اللَّهِ مَا لَا تَعْلَمُونَ
“Nena kwa iwo: ndithu Mbuye wanga waletsa zinthu za uve zoonekera ndi zobitsika, ndi tchimo, ndi kuwukira atsogoleri popanda choonadi, ndi kuphatikiza Mulungu ndi chomwe sadachitsitsire umboni wakuti chiphatikizidwe ndi Iye, ndiponso waletsa kumunenera Mulungu zimene simukudziwa”
Kumuchita munthu kaafir yemwe ali osayenera kumuchita kaafir sizololedwa. Amene akuyenera kumuchita kaafir ndi amene ali oyenera kumuchita kaafir.
Amene ali osayenera kumuchita kaafir asachitidwe kaafir.
Munthu amene ali Msilamu, ndiye wachita chinthu cha ukafir, tisamutchule kuti ndi kaafir, mpaka atapezeka ndi mbiri zomwe zingamuchititse kukhala kaafir. Koma ngati mbirizo sizinapezeke, kumpanga kaafir ndi kulakwa ndipo ndi zosemphana ndi zomwe Allah wanena.