Pachiyankhulo chabe, mawuwa amatanthauza kubindikira, pamene pa Shariah mawuwa amatanthauza kubindikira munzikiti ndikachitidwe kake, komanso ndichitsimikizo chake, ndicholinga chofuna kudziyandikitsa kwa Allah.
Lamulo la I’tikaaf
Lamulo la I’tikaaf ndi Sunnah, ndipo imayenera kuchitika mu khumi lomaliza la mwezi wa Ramadhan kwa amene angakwanitse kuchita I’tikaafuyo. Lamulo lake limasintha kukhala Waajib ngati munthu waipanga yekha kukhala Waajib; mwachitsanzo wapanga lonjezo kuti abindikira mumziki masiku atatu kupanga ibaadah. Apa lamulo limasintha; imakhala Waajib chifukwa kukwaniritsa lonjezo nkokakamizidwa.
Umboni wa I’tikaaf ukuchokera mu Qur’an yolemekezeka, pamene Allah akunena kuti:

وَلَا تُبَاشِرُوهُنَّ وَأَنْتُمْ عَاكِفُونَ فِي الْمَسَاجِدِ تِلْكَ حُدُودُ اللَّهِ فَلَا تَقْرَبُوهَا
Musawakhudze akazi anu pomwe inu mukubindikira mmizikiti amenewo ndiye malamulo a Mulungu choncho musawayandikire
Ndipo kuchokera mu Sunnah, Mayi wa anthu okhulupilira, Aisha radhia Allah anha, analongosola kuti
كان صلى الله عليه وسلم يعتكف في العشر الأواخر من رمضان…
Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali akubindikira mumzikiti mukhumi lomaliza
Ma ulamaa anagwirizana kuti I’tikaaf ndi chisankho chamunthu, akuyenera kupanga nthawi yomwe waonera kuti akwanitsa kutero chifukwa I’tikaaf imawonjezera mwamunthu kuyera komanso ndinjira yabwino yomwe munthu amadziyandikitsira kwa Allah.
Zoyenereza kuti I’tikaaf itheke
I’tikaaf kuti itheke pamafunika ma zinthu izi kuti zikwaniritsidwe:
• Niyyah (chitsimikizo): Paja ntchito iriyonse yabwino imawerengedwa malingana ndi chitsimikizo chake, monga momwe Hadith ya Saheeh ikufotokozera.
Twahara: I’tikaaf siyomerezeka kwa munthu yemwe ali ndi janabah, haidh komanso nifaas. Koma mkazi yemwe ali pa istihaadhwa amaloledwa kuchita I’tikaaf chifukwa wa istihaadhwa ndiwoyeretsedwa.
Munsikiti: I’tikaaf  ikuyenera kuchitikira munsikiti ngati mmene Allah wanenera mu Qur’an Yolemekezeka kuti
وَلَا تُبَاشِرُوهُنَّ وَأَنْتُمْ عَاكِفُونَ فِي الْمَسَاجِدِ
Ndipo musawandikire akazi anu pamene inu muchita I’tikaaf kumzikiti.
Ikanakhala kuti I’tikaaf ndiyovomerezeka kuchitira malo ena ake osakhala munsikiti, ndiye kuti kutchula kwansikiti mu aayah iyi sikukanakhala ndiphindu lirilonse.
Imaam Abu Hanifah anapanga kusala kukhala ntchito yoyenereza ngati munthu akupanga I’tikaaf yalonjezo posakhala ya mu Ramadhan, mwachitsanzo munthu unalonjeza kwa Allah kuti mukazandipatsa mwana ndizapanga I’tikaaf munsikiti kwamasiku atatu, ndiye zakwaniritsidwa, ndi waajib akwaniritse lonjezolo komanso asale kudya masiku omwe akachite I’tikaaf yalonjezoyo.
Imaam Maliki anakupangaso kusala kukhala ntchito yoyenereza I’tikaaf ya lonjezo komanso ya Sunnah.
Pomwe Imam Al Shafi’ ndi Imaam Hanbali sanapange kusala kukhala ntchito yoyenereza kuti I’tikaf ya lonjezo itheke.
• Ndizovomerezeka kwa mayi kuchita I’tikaaf pambuyo poti watenga chilolezo kuchokera kwa mwamuna wake ngati ali okwatiwa, ndipo kwa makolo ake kapena kwa aliyense yemwe akumuyang’anira iyeyo ngati ali osakwatiwa; chifukwa mkazi otha nsinkhu bwino satuluka mnyumba popanda chilolezo.
I’tikaaf ya mkazi imaloledwa kuchitikira munsikiti komanso malo apadera opemphelera nymba mwake.
Ma ulamaa onse anagwirizana kuti I’tikaaf ya mzimayi munsikiti itha kuchitikira kunsikiti malingana ndi ma Hadith ena odziwika bwino:
كان النبي صلى الله عليه و سلم يعتكف العشر الأواخر من رمضان حتى توفاه اللع تعالى  ثم اعتكف أزواجه بعده 
Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali kuchita I’tikaaf mmasiku 10 omalizira mpaka anatengedwa ndi Allah, ndipo nawo akazi ake anapanga I’tikaaf pambuyo pake.
Choncho apa titha kuona kuti mkazi nayenso akuyenera kuchitira I’tikaaf yake munsikiti, si condition kukhala mzikiti wawukulu ayi kapena omwe umasonkhana anthu ambiri kapena zokakamizika kuti ukhale nsikiti wa Jum’ah, poti mkazi kupita kunsikiti sikwabwino kwenikweni, choncho ngati akachitira misikiti yomwe kumasonkhana anthu ambiri akuyenera apangiridwe malo obisika womwe azikhalako amayiwo pa ibaadah yawo, oti amuna asafikepo mpaka amalize ibaadah yawo yonse.
Imaam Abu Hanifah anati ndi makrooh mkazi kuchitira I’tikaaf kunsikiti chifukwa iwo siwoyenera kupita kunsikiti mwachisawawa. Mkazi kuzibisa ndikoyenera kwa iye kwambiri, anati akuyenera kuchitira mnyumba mwake pamalo ake omwe amapemphelerapo.
Zomwe Zimaononga I’tikaaf 
Zoononga I’tikaaf ndi monga kukhalira pamodzi mkazi ndi mamuna wake, ndipo kuchita zonse zomwe zingabweretse chilakolako kuti, mpaka akhalire limodzi zimaletsedwa. Koma kugwirana, kukumbatirana popanda chilakolako kulibe vuto. Kutulukatulukanso munsikiti popanda chifukwa chomveka kumawononga I’tikaaf, koma ndizovomerezeka kupita kunyumba kwake kukadya, kukasamba, kukadzilemekeza ndi zina zofunikira pamoyo, koma osati kukapanga business kapena kukacheza ndi mai akunyumba monga banja. Kudyera limodzi komanso kumwa sikuwononga bola akamaliza abwelerenso.
Ndizovomerezekanso mkazi kupita kukamuona mwamuna wake kumalo omwe akuchitira I’tikaafuyo.
Imaam Al Shafi’ ndi Imaam Maliki anati ngati munthu atuluke kupita kunsikiti wina ndicholinga chokapemphera mwina Jum’ah, ndiye kuti I’tikaaf yakeyo yawonongeka chifukwa iwo anati I’tikaaf iyenera kuchitikira pansikiti womwe Jum’ah imapempheredwa pompo.
I’tikaaf ilibe nthawi yeniyeni, kotero munthu utha kuchita malingana ndi chitsimikizo chako, mwachitsanzo munthu atha kuchita I’tikaaf kwamasiku atatu basi nkumabwerako, palibe vuto. Ndipo nyengo yaifupi kwambiri pa I’tikaaf ndi usana ndi usiku.