Kodi Istikhaarah ndi chani?
      Istikhaarah
Istikhaarah mu chiyankhulo cha Arabic
Kumeneku ndi kupempha kusankha kwabwino pa chinthu. Amanena kuti: “pempha chisankho kwa Allah ﷻ , akusankhira”.
Istikhaarah mu Deen
Kupempha kusankha, kapena kuti kupempha kuti akuchotsere kuvuta pa kasankhidwe, kumene kumachokera kwa Allah, kudzera popepmphera swalat kapena kupanga dua yomwe inaphunzitsidwa ndi Mtumiki ﷺ .
Lamulo lake
Ma Ulamaa anagwirizana kuti Istikhaarah  ndmi sunnah, ndipo umboni wake ndi Hadith yomwe anailandira Al Nukhari kuchokera kwa Jabir radhia Allah anhu: “Allahumma innii astahkeeruka bi’ilmika wa astaqdiruka biqudratika…”
Kodi munthu amafunika kupanga dua imeneyi nthawi yanji?
Ndithu munthu padziko lino zimamupeza zinthu zosiyansiyana zimene zimamusokoneza mmutu kuti apanga bwanji, kusowa chosankha chabwino. Choncho panthawi imeneyi amafunika kuthawira kwa Mlengi wa mitambo ndi nthaka komanso anthu, akweze manja ake ndikupanga dua, kumupempha kuti amupatse chabwino. Ndipo akuyenera kuoanga izi moupeza mtima osathamanga. Mwachitsanzo ngati munthu akufuna kugula phone, kapena akufuna kukwatira kaoena kugwira ntchito in yake, kapena akufuna kuyenda ulendo, amayenera kupanga Istikhaarah . Sheikhul Islam Ibn Taimiya anati: palibe amene angapange regret ngati atapanga istikhaara kwa Mlengi, komanso kupempha malangizo kuchokera kwa anthu, koma chinthuncho ndithu chidzachitika. Allah akunena mu Qur’an Surat Aali Imran 159 kuti “…ndipo chita upo ndi iwo pa chinthu ndipo ukatsikiza, yezamira kwa Allah”.
Qataadah anati: palibe gulu la anthu limene lingapange upo pa chinthu mudzina la Allah, koma Allah amawaongolera ku chomwe chili chabwino.
Imam AlNawawi ananena pa khomo la Al Istikhaarah komanso kukambirana, kuti: kupanga Istikhaarah  kwa Allah komanso kukambirana ndi anthu omwe ali ozindikira komanso odziwa kusova mavuto, zijmayenera kuchitika chifukwa munthu Sali okwanira mwa iye yekha. Munthu analengedwa ofooka, choncho amatha kukumana ndi zovuta ndikumasowa zochita.
Dua ya Swalat Al Istikhaarah
Kuchokera kwa Jaabir radhia Allah anhu anati: Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali kutiphinzitsa ife Istrikhaarah pa zinthu zones, monga mmene anali kutiphunzitsira Surat kuchokera mu Qur’an, ndipo ankati: “Mmodzi wa inu akafunisitsa chinthu (pakati pa zinthu ziwiri)”, aswali ma rakaat awiri osati a faradh, ndipo anene kuti:
Allahumma inni astahkiiruka bi’ilmika wa astaqdiruka biqudratika, wa as’aluka min fadhlikal adheem, fa innaka taqdiru walaa aqdiru, wa ta’lam walaa a’lam, wa anta ‘allaamul ghuyoob. Allahummah in kunta ta’lam anna hadhal amr (pamenepa atchule chinthucho/vutolo) khayrun lii fii deeni wa ma’aashi wa ‘aaqibati amri/’aajili amri wa aajilihi, faqdurhu lii wa yassir lii thumma baarik lii feehi. Allahummah wa in kunta ta’alam anna haadhal amra (pamenepa atchule chinthucho/vutolo) sharrun lii fii deeni wa ma’aashi wa ‘aaqibati amri/’aajili amri wa aajilihi, faswrifhu ‘annii waswrifni ‘anhu waqdur lii alkhayra haithu kaana thumma irdhwinii/raddhwini bih (pamenepa atchule chinthucho/vutolo)
Tanthauzo
O Allah, ndikupempha mundipatse kusankha poti ndinu Odziwa zonse, ndipo ndikupempha mundipatse kutha poti ndinu Okutha, ndipo ndikupempha zabwino zanu zazikulu poti Inu ndi Okutha ndipo ine sinditha, mumadziwa ndipo ine sindidziwa, Inuyo ndi Odziwa zobitsika kwambiri. O Allah, ngati mukudziwa kuti (tchulani chinthucho) ndizabwino kwa ine mu Deen yanga, mu umoyo wanga komanso mathero anga, ndikhonzereni ndipo ndifewetsereni kenako mundidalitse nazo. O Allah, ngati mukudziwa kuti (tchulani chinthucho) ndi zoipa kwa ine komanso mu Deen yanga, mu umoyo wanga komanso mathero anga, zidusitseni zisandichitikire ndipo ndikhonzereni zabwino kulikonse komwe ziri ndipo kenako musangalale nane.
Hadith anailandira Al Bukhari 1166
Mapangidwe a Swalat ya Istikhaarah
 1. Pangani udhu wokwana
 2. Chitsimikizo .. mupange niyyah kuti mukuswaliyo ndi swalat ya Istikhaarah, musanaime pa swalat
 3. Muswali ma rakaat awiri … ndi sunnah kuwerenga Surat Al Kaafiroon pa rakaat yoyamba after Surat Al Fatihah, ndipo rakaat yachiwiri ndi sunnah kuwerenga Surat Al Ikhlaas pambuyo pa Surat Al Fatiha.
 4. Pambuyo pa salaam mukamaliza swalat yanu, nyamulani manja anu modzichepetsa kwa Allah Ta’ala komanso moganizira za ukulu wake ndi kutha kwake, mupange dua Istikhaarah.
 5. Kumayambilirop kwa duayo, muyamikeni Allah ndikumutamanda, ndikupempha mtendere ndi Madalitso zipite kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam tahmeed ndi thanaau kwa Allah (munene kuti Alhamdulillah Rabbil Aalameen, Allahumma salli wasallim alaa Muhammad salla Allah alaih wasallam). Komanso ndibwino kwambiri kupanga Swalaatul Ibrahimiyah imene imachitika pa Attahiyyaat: (Allahummah swalli ‘alaa Muhammad wa ‘alaa aali Muhammad kamaa swallaita ‘alaa Ibrahim wa ‘alaa aali Ibrahim. Wa baarika ‘alaa Muhammad wa ‘alaa aali Muhammad kamaa baarakta ‘alaa Ibrahim wa ‘alaa aali Ibrahim fil ‘aalameen innaka Hameedun Majeed)…kapemna mmene munganenere as you memorized.
 6. Kenakono werengani Dua Istikhaarah (Allahumma inni astahkeeruka bi’ilmika wa astaqdiruka biqudratika…mpaka kumapeto).
 7. Kenako mfunireni zabwino Mtumiki salla Allah alaih wasallam (salaat alaa Nnabi monga ya pa Tahiyyaatu ija.
 8. Mukatero mwamaliza kupanga swalaatul Istikhaarah … mwadzisiya mmanja mwa Allah kuti akusankhireni chabwino, poti Iyeyo ndamene akukudziwani inu kuposa eni akenu, komanso akudziwa zomwe ziri zoyenera inu.
Njira za mazpangidwe a Istikhaarah
Njira Yoyamba: Kupanga Istikhaarah kwa Mbuye wa zolengedwa zonse, yemwe ndi odziwa zomwe  zinachitika komanso zomwe zikuchitika komanso zomwe zidzachitike ndi momwe zidzachitikire.
Njira Yachiwiri: Kupempha malangizo kwa anthu omwe ali ozindikira, komanso odziwa kusova mavuto ndipo ndi osunga chilungamo ndi chinsinsi. Allah Ta’ala ananena kuti: “…ndipo chita upo ndi iwo pa chinthu…”, izi ankamuuza Mtumiki, ndipo Allah anati: “…choncho akhululukire ndi kuwapemphera Chikhululuko (Kwa Allah); ndipo chita nawo upo pazinthu. Ndipo ngati watsimikiza, yezamira wa Allah (basi, ndi kuchita chimene Watsimikiza kuchichita). Ndithudi, Mulungu amakonda oyedzamira kwa iye (odalira Iye)”. Surat Aal Imran 159.
Mtumiki ﷺ  anali ozindikira kambiri, amnali mtsogoleri wa anthu komanso mbendera ya Chiwongoko. Komatu iye anali kupempha malangizo kwa ma Sahaba ake mu zinthu zina zomwe zinkamusokoneza iye mmutu, chimodzimodzi ma Khalifah ake anali kupemphanso maganizo abwino kwa anthu omwe anali ozindikira.
“Kodi Mashoorah (kukambirana ndi ena pofuna kupeza ganizo lolondola) ndi Istiikhaara chimayenera kuyamba ndi chani?”.
Kumtundaku tamva kuti pali zinthu ziwiri zomwe munthu akhonza kuchita pofuna kuthandizika kupeza chinthu choyenera kuti achichite, ndip[o njira zake ndi ziwiri: kupanga Istikhaarah ndi kupanga mashoorah. Koma kodi zinthu ziwiri zimenezi zikuyenera kubwera motani? Chiyambe chani?
Pankhani imeneyi ma Ulamaa anakambapo zosiytanasiyana, koma zomwe zili zokhanzikika kuchokera mu kusiyanaku ndi zomwe ananena Sheikh Muhammad Salih Al Othaimin rahimahu Allah, mu Sharh Ryaadh AlSaliheen, kuti Istikhaarah imayenera kuyambilira, chifukwa Mtumiki Muhammad ﷺ  anati: “Mmodzi wa inu akafunisitsa kupanga chinthu, akuyenera kuswali ma rakaat awiri…”, ndipo ukabwereza mpaka katatu ndipo palibe chomwe chikusonya, yankhlua ndi athu tsopano (mashoora). Ndipo utenge zomwe akulangidzazo. Kupanga istishaar katatu kukuyenera kuchitika potengera kuti chinali chizolowezi cha Mtumiki ﷺ popanga dua ankapanga katatukatatu. Ndipo ma Ulamaa ena anati, munthu akuyenera kumaswalibe swalat Istikhaarah mobwerezabwereza mpaka zitaonekera kwa iyeyo kuti chabwino ndi chiti.
Malamulo a Istishaarah (Munthu yemwe akuyenera kupemphedwa malangizo)
Munthu akuyenera kufunsa maganizo pa chinthu motsatira ndondomeko monga mmene tanenera. Tsopano munthu yemwe tikumufunsa maganizoyo akhale otani?
 1. Akhale ozindikira komanso odziwa kusankha pakati pa zinthu ziwiri, odekha pobweretsa chiganizo komanso kuganizira bwinobwino.
 2. Akhale wabwino pa deen chifukwa munthu yemwe Sali olongosoka pa deen sangakhale wodalirika. Mu hadith yochokera kwa Anas bin Malik radhia Allah anhu, anati Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “Sangakhale okhulupilira (wa iman) ngati sali okhulupirika, ndipo sangakhale wa deen munthu yemwe sasunga chipangano” chifukwa iyeyo ngati Sali wabwino mu deen, ndiye kuti akhonza kupanga chinyengo – naudhu billah, choncho munthu akhonza kupempha malangizo kwa munthu oteroyo nkupatsidwa malangizo omupatsa mavuto.
Zomwe tikuyenera kusamala
 1. Tikuyenera kumapanga istikhaara pa chitnhu chilichonse, chingachepe bwanji
 2. Tikamapanga tidzikhala ndi chitsimikizo choti Allah ﷻ apereka zabwino ndipo tisakaikire, chifuikwa kukaikira kulikonse kumasintha qadar komanso kumamanitsa zomwetikufuna kuti Allah atipatse. Tikhale ndi mtima umodzi pamene tipanga dua, tiganizire komanso kudzimva tokha zomwe tikupemphazo.
 3. Simukuyenera kupanga dua Al Istikhaarah pambuyo pa swala ya Faradh (Fajr, Dhuhr, Asr, Maghrib Isha) koma mupange salat ya sunnah pambali, yomwe ndi salat Al Istikhaarah.
 4. Ndizololedwa ngati mutafuna kupanga Istikhaarah pambuyo pa sunnah ya nafl kapena salaat AlDhuha kapena nafl iliyonse, koma mukhale kuti mwapanga niyyah ya musanalowe mu swalayo. Koma ngati mungalowe mu swalayo popanda kupanga niyya ya Istikhaarah, simukuloledwa kuswali ngati istikhaara chifukwa choti niyyah ndi ya swala ina.
 5. Ngati zakufikani zoti mukuyenera kuswali salat Al Istikhaarah koma muli munthawi yoletsedwa kuswali, pilirani mpaka nthawi imeneyo idutse. Koma ngati chinthu chomwe chikukupangitsani kuti mupange istikhaaracho mukuona kuti chidutsa mukapanda kuswali nthawi imeneyo, swalini ndipo mupange Istikhaarah.
 6. Ngati china chake chakuletsani kupanga salaat Istikhaarah , monga ngati haidh (mzimai), dikirani mpaka chiletsocho chichoke. Kopma ngati mukuona kuti vutolo ndilokhanzikika nthawi yaitali, mukhonza kupanga dua Al Istikhaarah popanda salat.
 7. Ngati simunaloweze dua Al Istikhaarah, mukhonza kuwerenga poonera pa pepala, koma zomwe zili bwino kwambiri ndi kuloweza.
 8. Ndi zololedwa kupanga dua Al Istikhaarah musanapange salaam pambuyo pa Attahiyyaat…komanso ndi zololezedwa kuipanga pambuyo pa salaam kumapeto kwa salaat.
 9. Mukapamga Istikhaarah, pitirizani zomwe mumachita ndipo musayembekezere maloto  kutulo.
 10. Ngati sizinaoneke zoti musankhe, mubwerezenso Istikhaarah.
 11. Musaonjezere pa dua imeneyi china chake, kapena kuonjezerapo ma dua ena ndi ena. Chifukwa imeneyo ndi yomwe Mtumiki ankaphunzitsa. Choncho musaonjezere kapena kupungula.
 12. Musalole kuti maganizo anu akulamuleni kusankha popanda kudutsa mu njira ziwirizi (Istikhaarah, Istishaarah),chifukwa mukhonza kusankha chinthu chomwe mu8kuganiza kuti nchabwino pomwe ndi choipa, ndipo izi mudzazizindikra zinthu zitavuta. Zinthu monga kukwatira mkazi wina wake kapena kugula galimoto ina yake yomwe mukuifuna ndi zina zotero. Koma mukuyenera osagwiritsa ntchito maganizo anu chifukwa imeneyo sikhala Istikhaarah ya kwa Allah.
 13. Musaiwale kupempha malangizo kwa amene ali ozindikira komanso odziwa kusova mavuto, ndipo pangani Istikhaarah ndi Istishaarah pamodzi.
 14. Istikhaarah sungampangire munthu wina. Koma nzotheka kwambiri mai kumupemphera mwana wake kuti Allah amusankhire chabwino, nthawi iliyonse komanso pa salat iliyonse, – posakhala Istikhaarah  mmalo awiri awa:
Malo Oyamba: Pa Sajdah
Malo Achiwiri: Pambuyo pa Tashahhud komanso salaat ala Rasul ﷺ monga mmene timapangira pambuyo pa Attahiyyat.
 1. Ngati mwakaikira kuti mwapanga niyya ya Istikhaarah ndipo mwapanga swalat kenako mwazindikira muli pa swalat, pasngani niyya ya nafl basi, ndipo pambhuyo pake pangani swla ya Isstikhaarah ndi niyya ya Istikhaarah.
 2. Ngati uli ndi zinthu zingapo zofuna Istikhaarah, ndi zololedwa kupanga istikhaara imodzi pa zonsezo? … zomwe zili bwino kwambiri komanso zoifunikira ndiye kupanga istikhaara imodzi pa choice chilichonse. Kom ngati munga phatikize palibe4 vuto.
 3. Sizaololedwa kupanga Istikhaarah pa chinthu cha mahrooh, ndipo pa chinthu cha haram ndiye kwambiri,nzoletsedwa. Istikhaarah idzibwera pa zinthu za halal.
 4. Sizololedwa kupanga Istikhaarah pogwiritsa ntchito Musabbahah (tasbeeh) kapena Qur’an, monga mmene amachitira ma Shia – Allah awaongole, koma Ist5ikhaarah imayernera kuchitika munjirta yomwe ili yovomerezeka yomwe anaphunzitsa Mtumiki Muhammad ﷺ, Swalat+Dua.
Phindu la Istikhaarah
Kuchokera mu Hadith ya Sa’d bun Abi Waqqaas, Mtumiki salla Allah alaih wasallamanati: “Mwana wa Adam amakhala osangalala mmoyo wake pamene wapanga Istikhaarah kwa Allah, ndipo mwana wa Adam amakhala osangalala ngati akukhutitsidwa ndi zomwe wapatsidwa ndi Allah. Mwana wa Adam amazkhala odandaula pamene akusiya kupanga Istikhaarah  kwa Allah ﷻ , ndipo mwana wa Adam amakhala akudandaula pamene akulandira mkwiyo wa Allah. ﷻ .”
Ibn al Qayyim ananena kuti: Chikhonzero cha Allah chimakwanira pa zinthu ziwiri: Istikhaarah yochokera pansi pa mtima, komansiKusangalatsidwa ndi chikhonzerocho.
Umar bun AlKhattab: sindikudandaula kuti mmene ndiliri ndi mmene ndikukondera kapena mmene sindikukondera, chifukwa choti sindikudziwa kuti chabwino nchiti pa zomwe ndikukonda kapena kuchida
Choncho m’bale wanga, usakhale okhumudwa ndi mavutho  kapena mayesero amene akugwera, chifukwa kutheka kuti kudzera mu mavuto amenewo ndi momwe mtendere wako udzachokere, komanso kutheka chinthu chomwe ungachikonde nkukhala gwero la mavuto ako kutsogolo. Allah Ta’la akunena mu Surat AlBaqara 216 kuti: Komatu Mwina mungachide chinthu pomwe Icho chili Chabwino kwainu. Mwinanso mungakonde Chinthu pomwe icho chili choipa Kwainu. Koma Mulungu ndiyemwe Akudziwa. Ndipo inu simudziwa.
Sheikhul Islam ibn Taymiya  anati: Yemwe wapempha Istikhaarah  kwa Mlengi ndikupempha malangizo kwa anthu oyenera, ndikutsimikizika zoyenera kuchitazo, sangadzadandaule.
Ndipemphe Allah atipatse zabwino mu zomwe tikumupempha komanso atipange kukhala anthu owongoka
Mtendere ndi Madalitso za Allah zipite kwa Mtumiki wake Omaliza Muhammad salla Allah alaih wasallam
Wassalam Alaikum warahmatullah wabarakaatuh