Ubwino wa Isa alaih salaam ukuwonekera kuchokera mu ntchito yomwe anapatsidwa. Anali Mneneri omalidza asanabwere Mneneri Muhammad salla Allah alaih wasallam, komanso anali Mtumiki omaliza kwa ana a Israel. Allah analipatula banja la Isa alaih salaam ndi madalitso, potchula dzina lake ka 25 ndipo dzina la mai ake latchulidwa ka 31.

 Zakariya alaih salaam anali muyang’aniri wa Mariam alaih salaam, mwana wa Imran alaih Salaam. Iyea anammangira Mariam kachipinda mnyumba yopemphelera. Mneneri Zakaria anali kumuyang’anira Mariam pomuphunzitsa ndikumulangiza nthawi zonse, choncho anakula ndi moyo wopembedza Allah nthawi zonse.

Tsiku lina pamene Mariam anali kupemphera, Mngelo anamufikira mmaonekedwe a munthu. Iye anali ndi mantha poganiza kuti munthuyo anadza ndi mavuto. Anapempha kwa Allah kuti amutchinjirize kuchokera ku zovuta zomwe angabweretse munthuyo ngati anali oopa Mulungu. Kom Mngelo anamuuza kuti iye anatumizidwa ndi Allah kuti adzampatse mwana woyera wopanda machimo. Pamenepo Mariam anadekha anafunsa kuti akhala bwanji ndi mwana pomwe sanakhunzidwe ndi mwamuna aliyense. Mngelo anamuuza kuti zimenezo ndizosavuta kwa Allah, Allah adzamupanga iye kukhala chizindikiro  cha mphamvu zake kwa anthu.

Ulendo wa Mngelo uja udamupatsa mantha Marima kwa Masiku angapo, iye anali kuganiza kuti zingatheke bwanji kukhala ndi mwana pomwe alibe mwamuna?

Patadutsa myezi ingapo ali ndi mimba, anayamba kumva ululu ndipo anachoka mosadziwa komwe anali kupita. Koma sanathe kupita patali chifukwa cha ululu wa mimba, ndipo anakhala pansi pa mtengo wa tende, pamene mwana anabadwira.

Mariam anali oda nkhawa ndi mwana wake poganiza kuti angakhale bwanji ndi mwana opanda bambo. Iye analira kuti bola akanangofa zimenezo zisanachitike. Pompo anamva mau kuchokera kwa Mngelo, omulimbitsa mtima kuti asadandaule, Allah waika kamtsinje pansi pake, ndipo anamuuza kuti agwedeze mtengowo ndipo ugwetsa zipatso zakupsa. Anamuuza kuti adye ndikumwa madzi a mumtsinje uja kuti abwezeretse mphamvu zake. Zimenezo ndi mphamvu za Allah.

Mariam alaih salaam anamwa madzi kuchokera mumsinje muja ndikudya zipatso. Tsopan mtima wake unakhanzikika ndi zozizwitsa za Allah. Patadutsa kanthawi anadzuka ndikumapita kunyumba, koma anaganizanso zomwe angakawauze anthu. Pamenepo, chozizwitsa china chinachitika; mwana yemwe anangobadwa posachedwa, anayamba kuyankhula. Anamuuza kuti akakumana ndi munthu aliyense amuuze kuti walumbira kwa Allah kuti asale ndipo sayankhula ndi aliyense.

Anthu anapsa mitima pomuona ali ndi mwana mmanja mwake. Anamukalipira kuti wachita chinthu choipa, koma iye anangokhala chete; anaika chala pakamwa kusonyeza kuti sangayankhule. Kenako anamulozera mwana wake. Pamenepo anthu anakwiya ndikumufunsa kuti angayankhule bwanji ndi mwana wakhanda. Koma anali odabwa pamene mwana anayamba kuyankhula. Iye anayankhula modekha nati: “Ndine kapolo wa Allah, ndipo wandipatsa buku ndikundipanga kukhala  Mneneri. Allah wandipanga kukhala olemekeza mai yemwe wandibereka. Mtendere ukhale pa ine kuyambira tsiku lomwe ndabadwa, tsiku lomwe ndidzamwalire komanso tsiku lomwe ndidzawukitsidwe.”

Anthu anangoimaima nkumangomuyang’ana mwana modabwa. Ngakhale panali ena omwe amakhulupilira kuti kuyankhula kwa mwana kuja chinali chinyengo chabe, ambiri anazindikira kuti mwana uja anali opatulika ndipo zachitika mwachifuniro cha Allah. Kenako Mariam anakhala momasuka popanda kunyozedwa.

Yusuf yemwe ankagwira ntchito ya matabwa, anali odabwa ndi nkhani ya Mariam alaih salaam. Atamufunsa kuti mtengo ungamere popanda mbewu,  anayankha kuti inde ndizotheka, poti munthu oyambilira kulengedwa anabadwa popanda mbewu. Kenako anamufunsanso kuti ndizotheka kukhala ndi mwana popanda mwamuna? Iye anayankha kuti inde, Allah analenga Adam popanda mwamuna ngakhale mkazi.

Zizindikiro za utumiki zinankera patsogolo pamene Isa anali kukula. Amatha kuwauza anzake zomwe angadye madzulo, zomwe asunga komanso malo omwe asunga.

Pamene anali ndi zaka 12, anapita ndi mai ake ku Jerusalem, ndipo atafika anawasiya mai ake ndikulowa mnyumba yopemphelera mmene azibusa anali kulalikira ku khamu la anthu. Iye sadawaope kukhala pamodzi ndi akuluakulu. Patadutsa kanthawi anaimilira ndikufunsa mafunso kwa abusa, ndipo abusa anasokonezeka ndi mafunsowo moti analephera kuyankha. Anayesetsa kumukhanzika pansi ndikumuletsa kuyankhula koma sanalole, iye anapitiriza kufunsa ndikupereka maganizo ake. Izi zinamutangwanitsa Isa alaih salaam mpaka anaiwala kuti wasiya mai ake panja. Iwo anabwelera kunyumba poganiza kuti mwina Isa wabwelera kale pamodzi ndi anthu ena. Koma atafika kunyumba anapeza kuti mwana kulibe, choncho anabweleranso kukamufufuza. Anamufufuza nthawi yaitali ndipo pomaliza anampeza ali ndi anthu akupanga debate. Iye adakwiya naye, koma anawauza mai ake kuti sanazindikire kuti nthawi yatha pamene anatangwanika ndi kutsutsana ndi azibusa.