Nkhani inachokera kwa al-Bara’ ibn ‘Aazib yemwe anati: “tinapita ndi Mtumiki (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Iye) kumwambo woika mmanda mmodzi wa ma Ansar (mzika ya mumzinda wa Madina), ndipo titafika pa manda, tinapeza kuti sadaikidwe ku mphanga la manda.

Kenako Mtumiki (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Iye) anakhala pansi ndipo ife tinakhala momzungulira. Malingana ndi mmene tinakhalira chete, mukanaganiza kuti ngati mbalame zinatera mmitu mwathu. Ndipo Mtumiki (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Iye) anali kuseweretsa ndodo yake pokumba pa dothi. (kenako anayang’ana kumwamba, kenako pansi, kenako kumwamba katatu). Kenako anatiuza kuti: “Mumpemphe Mulungu kuti akutchinjirizeni ku chilango cha mmanda) anabwereza lamulo limeneli katatu. Kenako anati: “O Ambuye Mulungu, ndikudzintchinjiriza kwa inu kuchokera ku chilango cha mmanda” (katatu). Kenako anati: “Ndithu kapolo wokhulupilira akamasiyana ndi moyo uno ndikumapita ku umoyo uli nkudza, angelo amamutsikira ndi nkhope zawo zowala ngati dzuwa, amamveka iye nsalu (kafan) yochokera ku mtendere (jannah) ndipo amamukuta kuti asaole, mmankhwala ochokera kumwamba, kenako amakhala akumuyang’anira nthawi yonse.

Read in English Death of a Believer and a Non-believer

Kenako mngelo wa imfa amabwera ndikukhala kumutu kwake ndikunena kuti: “E, iwe mzimu wokhanzikika, lowa muchikhululuko ndi chisangalalo cha Mulungu” Pamenepo mzimu wa munthuyu umatuluka mosavuta ngati momwe dontho la madzi limatulukira mu chikho.  Kenako amawutenga ndikuwulowetsa mmalo otetedzedwa, ndipo fungo lokoma kuposa mafungo ena onse limatuluka kuchokera mu mzimuwo. Kenako mngelo wa imfa pamodzi ndi angelo ena amakwera nawo mzimuwo kumwamba, koma samadutsa gulu la angelo pokhapokha atalankhula kuti: “kodi mzimu umene uli wokongola komanso wa fungo lokomawu ndi wandani?” ndipo angelo aja amayankha nati: “ndi mzimu wa ujeni, mwana wa ujeni, amagwiritsa ntchito maina abwino amene munthuyo anali kugwiritsa ntchito pa dziko la pansi. Kenako amafika pa thambo lapansi (thambo loyamba), amapempha chilolezo kuti alowe ndipo amaloledwa, chomwecho mpakana ku thambo lomaliza lachisanu ndi chiwiri; kumeneko Mulungu Wapamwamba amanena kuti: “Lembani bukhu la kapolo wanga mu’illiyeen“Zowona ndithu kaundula wa anthu abwino ali mu ‘illiyeen. Nanga nchiyani chitakudziwitse iwe za ‘illiyeen? Ameneyu ndi kaundula wamkulu yemwe walembedwa mkati mwake ntchito za anthu ochita zabwino” Qur’an 83:18. Ndipo bukhu lake limalembedwa mu ‘illiyeen, kenako kumanenedwa kuti: “Mubwezereni ku dziko la pansi, poti ine ndinawalonjeza kuti kuchokera ku dothi ndinawalenga ndipo ku dothi lomwelo ndidzawabwenzera, kenako ndidzawatulutsanso kuchokera mu dothi lomwelo kachiwiri” Qur’an 20:55. Pamenepo, mzimu uja umabweretsedwa pa dziko lapansi [Mtumiki (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Iye)   anati “ndipo amamva mapazi a anthu amene anamuika mmandamo ali nkumusiya].

Read in English Death of a Believer and a Non-believer

Kenako angelo aukali amabwera nkumuopseza, ndipo amamukhanzika ndikumufunsa: “Mbuye wako ndi ndani? Amayankha kuti “Mbuye wanga ndi Mulungu”. Kenako amamufunsa: “Chipembezo chako ndi chani?” Amayankha kuti “Chipembezo changa ndi chi Islam”. Kenako amamfunsa: “Ndi munthu wanji amene adatumizidwa kwa inu? Amayankha kuti “Ndi Mtumiki wa Mulungu (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Iye)” Kenako amamufunsa nati: “Unapanga chani?” Amayankha: “Ndinawerenga Bukhu la Mulungu, kenako ndinalikhulupilira” [Mngelo amamuopseza] namfunsa kuti: “Mbuye wako ndi ndani?” Chipembezo chako ndi chani?” Mtumiki wako ndi ndani?” Amenewa amakhala mayeso omaliza kwa munthu okhulupilira pa dziko lino la pansi. Pamenepo ndi pamene Mulungu akuti: “Mulungu amawapatsa mphamvu anthu okhulupilira ndi mawu amphamvu pa dziko lapansi” Ndipo amayankha mafunso amenewa kuti: “Mbuye wanga ndi Mulungu, Chipembezo changa ndi Chisilamu, Mtumiki wanga ndi Muhammad (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Iye)”. Kenako oyitana amaitana kuchokera kumwamba: “Kapolo wanga wanena zoona, tsopano mutsegulireni Jannah, ndipo mumveke zovala za ku Jannah, ndipo mutsegulireni chitseko cha ku Jannah (mmanda mwake momwemo)”, kuti zabwino zake ndi fungo lake lim’bwelere. Ndipo manda ake amatambasuka kulekezera pamene pathere maso ake.

Kenako munthu amabwera kwa iye. Amakhala ndi nkhope yokongola, ndipo zovala zake zimakhala zokongola, komanso fungo lake limakhala labwino lokoma. Kenako amanena kwa munthuyo kuti: “Assalam Alaika – ndakubweretsera nkhani yabwino imene itakusangalatse {chisangalatso chochokera kwa Mulungu}. Tsiku iri ndi limene iwe udalonjedzedwa”. Kenako munthu uja amafunsa: ” Wa alaika Salaam – kodi ndiwe ndani? Chifukwatu nkhope yakoyo ndi ya munthu amene amabweretsa nkhani yabwino” Amayankha munthuyo: “Ineyo ndiye zintchito zako zabwino (zimene unali kugwira pa dzko la pansi) Ndikulumbira pamaso pa Mulungu, ndithu ine sindidamve china chirichonse chokhunzana ndi iwe, kupatula kuti iweyo unali munthu ofulumira pogwira nchito ya Mulungu ndipo unali ochedwa pomukanira, Tsopano Mulungu wakulipira zabwino”. Kenako munthu uja amati: “Ambuye Mulungu, bwenzani nthawi kuti ndibwelere pa dziko la pansi ku banja langa ndi chuma changa” amayankhidwa kuti:”Khala odekha ndi mtendere”

Read in English Death of a Believer and a Non-believer

Mtumiki (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Iye) anati: “Tsono kapolo osakhulupilira akamachoka padziko pano kupita ku umoyo uli nkudza, angelo amamutsikira iye nkhope zawo ziri zakuda, mmanja mwao muli nsalu yopangidwa ndi thonje la moto. Kenako mngelo wa imfa amabwera nkukhala mbali ya ku mutu kwake ndipo amanena: “E, iwe mzimu woipa tuluka ndipo lowa mu ukali wa Mulungu ndi chilango chake”. Motero mngelo amauchotsa mzimuwo mthupi la munthuyo mofulumira, mopanda chifundo, ngati mmene amachotsera malovu akagwera pa nsalu. Potuluka mzimuwu, umang’amba misempha ndipo umatembeleredwa ndi  angelo onse a pakati pa kumwamba ndi pansi pano, angelo onse a kumwamba, komanso makomo a ku Jannah amatsekedwa. Palibe khomo la ku janna limene limakhala lopanda anthu pokhapokha okhawo opemphera kuti mizimu yoipa ija isapeze danga. Kenako mngelo uja amautenga mzimu uja ndipo posakhalitsa amausiya munsalu yachisaka. Kenako mumatutuluka chifungo choipisitsa kwambiri padziko lonse.

Kenako angelo aja amakwera nawo mzimu uja kumwamba, ndipo samadutsa gulu la angelo pokhapokha amanena kuti: “kodi mzimu woipa umenewu ndi wa ndani?” ndipo amati: ” ndi wa ujeni mwana wa ujeni” amagwiritsa ntchito maina amene anali kudana nao pa dziko la pansi. Kenako amafika pa mtambo wadziko la pansi (mtambo woyamba) ndipo amapempha chilolezo koma samaloledwa kulowa. Kenako Mtumiki wa Mulungu (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa iye) adawerenga “Ndithudi amene akukanira zivumbulutso zathu nadzitukumula nazo, samatsekulidwa kwa iwo makomo a ku mwamba, ndipo samalowa ku munda wa mtendere mpaka ngamira idzalowe pa chibowo cha singano…” Qur’an 7:40

Read in English Death of a Believer and a Non-believer

Kenako Mulungu wa pamwamba amanena kuti: “Lembani bukhu la kapolo wangayo mu Sijjeen2 pansi pa nthaka”. Kenako kumanenedwa kuti: “Mubwezereni ku dziko la pansi, poti ine ndinawalonjeza kuti kuchokera ku dothi ndinawalenga ndipo ku dothi lomwelo ndidzawabwezera, kenako ndidzawatulutsanso kuchokera mu pdothi lomwelo kachiwiri” Qur’an 20:55. Kenako mzimu wake umachotsedwa kumwamba mwa nkhanza ndipo umabwenzedwanso kuthupi lake. Mtumiki (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Iye)   adawerenga kuti: “amene akum’phatikiza Mulungu ndi mafano ali ngati wogwa kuchokera ku mwamba, kenako mbalame nkumuwankha, kapena mphepo kukamtaya malo akutali”. Qur’an 22:31. [Mtumiki (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Iye)   anati “ndipo amamva mapazi a anthu amene anamuika mmandamo ali nkumusiya. Kenako angelo awiri aukali ndipo oopsa amabwera nkumamuopseza, ndipo amamukhanzika ndikumufunsa momuopseza kwambiri motero amachita mantha: “Mbuye wako ndi ndani?” amayankha kuti: “Huh? Huh? (kutanthauza kudandaula komanso mantha chifukwa cha kusowa choyankha) sindikudziwa” kenako amamfunsanso: “Chipembezo chako ndi chani?’ ndipo amayankha: ” Huh?, Huh?, sindikudziwa” kenako amamfunsa: “ndi munthu uti amene anatumizidwa kwa inu?” ndipo amayankha: ” Huh?, Huh?, sindikudziwa (ndinamva anthu akunena…!)”. Mtumiki (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Iye) adati “kenako kumanenedwa kwa iye: “siukudziwa, ndipo siukudziwa kulankhula!”

Kenako oyitana amaiyana kuchokera ku mwamba: “Kapolo wanga wakamba zabodza, choncho mutambasulireni ng’anjo ya moto, ndipo mtsegulireni khomo la ku moto (mmanda mwake momwemo). Pamenepo mmphweya wotentha wakumoto ndi chimphepo chake chimam’bwelera mmanda muja, ndipo manda aja amabwelera, kukhala othina kwambiri, motero kuti thupi lake limakhala lopanikidzika zedi. Kenako munthu amabwera kwa iye, nkhope yake ndi zovala zake zonyansa, komanso wafpungo loipa kwambiri. Kenako amamuyankhula munthu uja nati: “Nkhani yoipa kwa iwe ‘limeneli ndiye tsiku lomwe unali kulonjezedwa lija'” Qur’an 70:44. Kenako amayankha nati: “Iwenso nkhani yoipa kwa iwe, kodi ndiwe ndani? chifukwa nkhope yakoyo ndi ya amene amabweretsa zoipa.” Ndipo amamuyankha nati: ” Ine ndine ntchito zako zoipa zija (zomwe unali kugwira pa dziko la pansi), ndikulumbira pamaso pa Mulungu, ndithu ine sindidadziwe china chirichonse chokhunzana ndi iwe, kupatula kuti iweyo unali munthu ofulumira pokanira Mulungu ndipo unali ochedwa potsatira malamulo ake, Tsopano Mulungu wakulipira zoipa”. Kenako amamtumizira osaona, osalankhula komanso ongokhala chete, atagwira mmanja mwake hamala (hamala imeneyi itamenya phiri, phirilo lingamwazikane lonse) ndipo amammenyera hamala imeneyi mpakana asanduke dothi. Ndipo Mulungu amam’bweretsanso mmene analiri koyamba, ndipo amamenyedwanso, mpakana amalira modandaula kumvetsa chisoni. Kulira kwake kumamvedwa ndi cholengedwa chirichonse kupatula munthu ndi ma jinn, ndipo khomo la ku moto, limatsekulidwa kwa iye (mmanda momwemo). Ndipo amanena kuti: “Ambuye Mulungu, musabweretsa nthawi”

Hadith imeneyi inachokera kwa Ahmed bin Hambal, Abu Dawud, Ibn Majah, At-Tayalisi ndi Hakim amene ananena kuti ndiyolandiridwa ndi Bukhari ndi Muslim. Inalembedwa ndi Imam Ahmed ndipo amene analemba mau amene akupezeka pakati pa mabracketswo ndi ochokera kwa ena mwa opelekera nkhani za Ahmed.

Zofunika kuzidziwa mu nkhaniyi

1) ‘Illiyeen: kuchokera ku mawu oti ‘uluww amene akutanthauza kukula. Amenewa ndi malo akupezeka kumwamba ku mitambo isanu ndi umodzi kumene mizimu ya anthu okhulupilira imasonkhana (Ibn ‘Abbas). Komanso liwu limeneli limatenga tanthauzo la ‘malo aakulu komanso otambasuka’ (Ibn Kathir)

2) Sijjin: kuchokera ku mau oti sijn, kutanthauza kuti kuchepa/kuthina/ndende. Amenewa ndi malo otsika kwambiri (onyozeka) kumene mizimu ya anthu osakhulupilira imasonkhana (Ibn Abbas) komanso mawu amenewa amatenga tanthauzo loti ‘malo otsika komanso ochepa’ (Ibn Kathir)

Tikawerenga hadith ya muntundayo, tiganiza ngati mavuto a mmanda amakhala kwa anthu osakhulupilira okha kapena amene amaphatikiza Mulungu ndi zina mmapemphero, mu umulungu wake, mukulenga kwake ndi mmaina ake. Komatu si choncho ayi! Hadith imeneyi ikutiuza zambiri. Tatiyeni tiyiwerenge mosamala: Ibn ‘Abbas (Mulungu asangalale naye) ananena kuti tsiku lina Mtumiki wa Mulungu (Mtendere ndi Madalitso zipite kwa Iye) anadutsa pa manda ndipo ananena kuti: “Anthu awiri amene ali mmanda umu, sakuzunzidwa ndi machimo ena koma ochepa, komansotu ndi machimo aakulu; mmodzi wa iwo anali akunyamula nkhani uku ndi uko (miseche) pomwe winayu sanali kudzisamalira akamakodza (Bukhari ndi Muslim)

Allah ndi amene adziwa zonse

Death of a Believer and a Non-believer

Otanthauzira Mchichewa: Ramadhan N.A Isa. Kutanthauzira koyamba – 2010. Kutanthauzira kwachiwiri – 2016. Kuchokera M’bukhu la Sahih Al Bukhariy