Tikudziwa bwinolomwe kuti ena mwa majinn ndi ma shaytwaan (asatana), amenewa ndi ma jinn oipa, ndipo asatanawa amafa mmene amafera majinn ndi anthu. Onsewa akulowa mukuyankhula kwa Allah Ta’ala koti:

 كُلُّ مَنْ عَلَيْهَا فَانٍ – وَيَبْقَى وَجْهُ رَبِّكَ ذُو الْجَلَالِ وَالْإِكْرَامِ – فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

Zonse zili pamenepo (padziko) nzakutha. Ndipo idzatsala nkhope ya Mbuye wako Mwini ulemerero ndi  mtendere. (Inu zolengedwa zamitundu iwiri anthu ndi ziwanda) kodi ndi Mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti siWake?) Surah Al-Rahmaan 26-28

Kuchokera mu Sahih Al-Bukhari, Hadith inachokera kwa Ibn Abbaas radhia Allah anhu, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anaali kunena kuti:

أنَّ رَسولَ اللهِ صَلَّى اللَّهُ عليه وَسَلَّمَ، كانَ يقولُ: اللَّهُمَّ إنِّي أَعُوذُ بعِزَّتِكَ، لا إلَهَ إلَّا أَنْتَ الذي لا يَمُوتُ، وَالْجِنُّ وَالإِنْسُ يَمُوتُونَ.

Ee Allah, ndikudzitchinjiriza ndi Ulemelero wanu, palibe wopembedzedwa mu choonadi kupatula Inu Yemwe samwalira, pomwe majinn ndi anthu amamwalira

Ndipo zaka zomwe majinn amakhalira padziko pano, palibe yemwe akudziwa koma Allah Yekha. Koma zomwe tikudziwa ndizomwe Iye Mwini anatilongosolera kuti shaytwaan wamkulu Iblees adzakhala wamoyo mpaka Tsiku Lakutha kwa dziko. Mawu ake akupezeka motere:

قَالَ أَنْظِرْنِي إِلَى يَوْمِ يُبْعَثُونَ – قَالَ إِنَّكَ مِنَ الْمُنْظَرِينَ

(Satana) anati: “Ndipatseni nthawi mpaka tsiku limene adzaukitsidwa (akapolo anu ku imfa).” (Allah) adati: “Ndithudi iwe ndi mmodzi wa opatsidwa nthawi.” Surah Al-A’raaf 14-15

Ndipo majinn ena onsewo sitikudziwa zaka zawo zomwe amakhalaira moyo, koma kuti amakhala moyo wautali kusiyana ndi anthu.

Umboni wina wochokera muzochitika, wotsimikizira kuti majinn amafa, ndiwoti Khalid bun Al-Walid anapha shaytwaan (shytwaanatal ‘Izz, mtengo womwe anali kuwupembedza Arab), komanso Swahaabiyyu wina anapha jinn lomwe limaoneka mmaonekedwe a njoka.

Al-‘Aqeedatu fi Dhwauil Kitaabi wa Sunnah – 3- Aalamul Jinn wa Sshaytwaan, p.22