Kodi n’chifukwa chani ma Sheikh amalalikira pamaliro ndi kumanda pomwe imfayo payokha ndi mlaliki?

Tibwelere kaye mbuyo pang’ono, makamaka pa mawu oti:

كَفَى بِالمَوْتِ وَاعِظًا

“Yakwanira imfa kukhala mlaliki”

Mawu amenewa ambiri amanena kuti ndi Hadith ya Mtumiki swalla Allaahu alaih wasallam, kudutsira kwa ‘Ammaar bun Yaasir radhia Allahu anhu. Koma imeneyi ndi Hadith ya dhwaeef sanad (yofooka chain), ndipo ena amati ndimawu a Imaam Al-Shaafi’i rahimahu Allaah. Koma mawuwa, sakuyenera kutengedwa kuti ndi Hadith ya Mtumiki nkumaikira umboni ngati Hadith ndithu. Inde, uthengawo ndiwabwino ndipo ndilangizo lamphamvu.  Koma tingochotsapo zoti anayankhula Mtumiki swalla Allaahu alaih wasallam.

KULALIKIRA PA MALIRO (BEFORE SWALAATUL JANAAZA)

Malinga ndi kafukufuku wanga pankhaniyi, kudzera mu kuwunika Sunnah komanso bid’ah, sindinapezepo choletsa chirichonse pa kulalikira pamaliro swalaat janaazah isanachitike. Ndipo tikayionetsetsa bid’ah, ndapeza kuti sizoona kuti tizinena zoti kulakirako kuli m’gulu la bid’ah, chifukwa kuwalalikira anthu komanso kuwakumbutsa zinthu ndizomwe tinalamulidwa m’Chisilamu, monga mmene Allah akunenera mu Surah Al-Nahl (125):

ادْعُ إِلَى سَبِيلِ رَبِّكَ بِالحِكْمَةِ وَالمَوْعِظَةِ الحَسَنَةِ

“Itanira (anthu) ku njira ya Mbuye wako mwanzeru ndi ulaliki wabwino…”

Komanso mu Surah Al Nisaai (63) akunena kuti:

وَعِظْهُمْ وَقُلْ لَهُمْ فِي أَنْفُسِهِمْ قَوْلًا بَلِيْغًا

“…ndipo alangize ndi kuwauza mawu ogwira mtima”.

Sanaike nthawi special yowalalikira anthu, kapena kuletsa nthawi ina yake kuti musalalikire. Mtumiki swalla Allahu alaih wasallam anali kuwalalikira anthu mmalo omwe anali kukumanirana monga momwe tikudziwira kwa amene timawaerenga mbiri ya Mtumiki (Seerah). Komanso Mtumiki anawalalikira ma Swahaba pa manda. Izitu Mtumiki anali kusankha nthawi yomwe waona kuti mitima ya anthu ili tayaali kumvera ndi kutenga ulaliki, choncho ulalikiwo umakhala wotengedwa ndi mitima yonse. Izi zikuikiridwa umboni ndi Hadith yochokera kwa Ibn Mas’ud radhia Allahu anhu, yonena kuti Mtumiki anali kuwonetsetsa nthawi, malo komanso anthu oyenera kuwalalikira ndi kuwaphunzitsa, ndipo anali kuwonetsetsa kuti kutalika kwa ulaliki kuyenere ndi malo omwe akulalikirawo. Osati pamaliro kulalikira mpaka 1 hour, akatero asinthane olalikira angapo: a Sheikh, akuchipani, akuntchio, amfumu, eni mbumba … anthu mpaka kupsa ndi dzuwa! Imeneyitu si hikma yomwe Allah anatiuza ija, kumagwiritsa ntchito nzeru pofuna kuwalalikira anthu.

Koma chifukwa cha kusowa hikma kwa ambiri, n’chifukwa chake zikaiko zinalowa mmitima ya ambiri kuti malo akutiakuti sioyenera kulalikira.

Nthawi yomwe anthu akudikira kuti ku manda kuthe kukumbidwa, kapena pamene akudikira kuti okhonza maliro m’nyumba muja amalize kusambitsa ndi kuveka, mmalo moti anthu angokhala ndi kumalongolola za AfCON kapena za Tonse Alliance, bwanji abwere Sheikh awakumbutse anthu za imfa kwa 10 minutes?

Kumandansotu chimodzimodzi, pamene ena akukwilira dzenje, ena akumvera ulaliki patali ndi malo omwe ikugwiridwa ntchito yokwilira ija, akamalandirana makasu, ena azipita kukmvera, ndipo sionse omwe amagwira ntchitoyo. Izitu ngakhale Mtumiki n’zimene anali kuchita nthawi zina, monga momwe tikumvera mu Hadith ya Barraa bun ‘Aazib yaitali ija, mukhonza kuipeza apa: https://malawiummah.com/imfa pamene Mtumiki anakhala pansi podikira kuti mtembo uyikidwe mmanda, ndipo anayamba kuyankhula kwa anthu momwe imfa ya okhulupilira ndi osakhulupilira imakhalira. Hadithi ikupezeka mu Sahih Al Bukhaari.

Koma, tisaupange ulaliki wa pamaliro kukhala chimodzi mwa zinthu zomwe zikupezeka mu ndondomeko ya mwambo wa maliro. Ndizotheka osalalikira ngati taona kuti sitikuyenera kutero, ndizothekanso kulalikira ngati taona kuti n’zoyenera kutero. Koma tisafike powonjezera zomwe zingapangitse kuti kulalikira kukhale waajib.

Pomaliza, mawu oti

كَفَى بِالمَوْتِ وَاعِظًا

“Yakwanira imfa kukhala mlaliki” sakukwanira kuima paokha ndikugwira ntchito yolalikira, popanda kuwatenga anthu omwe ali ndi ‘ilm mu Deen n’kutulutsa zomwe mawuwa afumbata. Choncho mu imfa muli zambiri zofunika kutambasulidwa, zomwe olalikira amatambasula kuti anthu atengepo phunziro.

Zomwe ndalongosolazi ndimomwe ndikudziwira, koma simathero a kuzindikira, choncho ngati pali mistake, ndidziwitseni kuti ndikhonze. Allah atiwonjezere kuzindikira.