Imaan – الإيمان
Imaan (chikhulupiliro) yeniyeni sichinthu chophweka kuchipeza. Imaan yomwe sivuta kuipeza ndi imene imapezeka kudzera mu nkhani zopeka. Munthu akhonza kukhala ndi imaan pa zinthu zabodza ndikumalimbikira ibaadah yake, koma kuchokera mu kukhulupilira zabodza.

Bodza likakhanzikika limasanduka choonadi…
Kalekale Mtumiki salla Allah alaih wasallam asanalandire utumiki, anthu anali kupembedza mafano ndipo anali ndi imaan yoopsa. Anali kukhulupilira kuti mafano ndi amene amawayandikitsa iwowo kwa Allah, motero kuti akamawapempha zofuna zawo, amakawafikitsira mapemphowo kwa Allah. Komatu Allah ankawapatsa anthuwa zofuna zawo malinga ndi mmene Iye Mwini wakhonzera…ndipo anthuwa ankakhulupiliradi kuti zikudzera mu ibaadah yomwe akupereka ku mafano ija. IMAAN الإيمان.

Mtumiki atabwera ndi Noor nkuwaletsa anthu aja kupembedza komanso kukhala ndi imaan pa mafano, anthu anafuna kupha Mtumiki wa Allah chifukwa chowaletsa kukhulupilira zabodza.
Lero lino tilinso ndi zinthu zomwe tinawapeza akuluakulu anthu akudzikhulupilira, zina ziri mmabuku ndithu. Koma chifukwa choti zinakhanzikika mmitu mwathumu ndipo imaan yathu ikudalira zimenezo, ma Sheikh omwe ndi alowammalo a Atumiki akutiunikira koma ife tikubwelera nthawi ya umbuli yomwe ija Chisilamu chisanabweretse shariah zake. IMAAN الإيمان.

Si Asilamu okha, ngakhalenso akhristu amakhulupilira zabodza mpaka amachiritsidwa nazo ku matenda…chifukwa cha imaan yawo yomwe imawapeza akamva kapena kuona zozizwitsa kuchokera kwa “maprophet” awo omwe ndi abodza…motero mpaka munthu yemwe anali ndi bala losapola kwa zaka zitatu nkudzachiritsidwa ndi a pulofeti, kumuuza kuti apulofeti amenewotu ndi abodza, sangakhulupilire. IMAAN

Zonsezo zikuchitika mchipembedzo chathuchi,  Allah atiwongole.
Nchifukwa chaketu Msilamu weniweni ndi amene amapempha kwa Allah kuti “ihdina sswiraatwal mustaqeem”  اهدنا الصراط المستقيم ka 17 kapena ka 29 patsiku lirilonse.

Asilamu omwe mwaphunzira ndikuzindikira kuti anthufe timakhulupilira zabodza (ngakhale kuti zimatikweza imaan),  tiwunikireni tidzikhulupilira zoona, ndipo amene imaan yake ingapande kutsika pambuyo poti wadziwa kusiyanitsa pakati pa zabodza ndi zoona kusintha; ameneyo ndiye Mu’min weniweni.

اهْدِنَا الصِّرَاطَ الْمُسْتَقِيمَ
صَدَقَ اللَّهُ العُظِيم

Allah atiwongolere kunjira yoongoka