Pambuyo pa chigumula, anthu a Nuh alaih salaam anachulukana padziko.

Mneneri Nuh alaih salaam anali ndi ana komanso zidzulu zambiri, choncho chiwelengero cha anthu padziko chinakula. Ambiri mwa iwo anakhanzikika ku Yemen. Zimakambidwa kuti omwe anakhanzikika kumeneko anali ochokera mwa Iram, mmodzi wa zidzukulu za Mneneri Nuh alaih salaam. Amenewa ankatchedwa anthu a ‘Aad. Anthu a ‘Aad anali akuluakulu, amphamvu komanso olimbikira ntchito. Anali ndi luso lomanga nyumba zitalizitali zokongola.

Anthu a ‘Aad analemera ndikumanga nsanja zikuluzikulu pa phiri lirilonse ndipo anali onyadira ndi mmene analiri. Koyamba, onse anali Asilamu abwino ndipo anali kupembedza Allah subhanah wa ta’ala. Koma patadutsa nthawi, satana anawasocheretsa.

Anthu a ‘Aad anapanga mafano kuchokera ku miyala ndikumawapembedza. Ananyalanyaza machenjezo a Allah ndipo mmalo mwake ankapembedza mafano amenewa mpaka anagwera mnjira zoipa.

Pamenepo Allah anaganiza zotumiza Mneneri wina padziko. Panthawiyi, Allah anasankha Hud alaih Salaam kuchokera mwa iwo kuti adzawachenjeze monga mlangizi wokhulupirika.

“Allah wanditumiza kwa inu,” anawauza anthu ake, “Iye ndi amene anakuphunzitsani chirichonse, anakupatsani dziko ili, anakupatsani ana anu ndi zinyama, choncho mukuyenera kusiya kupembedza milungu yabodza. Mulungu woona alipo mmodzi basi. Mukuyenera kumvera malamulo ake.” Anawauza.

Koma anthu a ‘Aad adamkalipira Mneneri: “ndiwe ndani kuti utilangize ife? Tikumvere iwe chifukwa chani?” ndipo ananyalanyaza zoyankhula za Mneneri.

“Ndasankhidwa kuti ndifalitse uthenga wa Allah” anawauza modekha. “Mverani zomwe ndikuyankhula, koma mukapanda kutero, ndikuopa kuti Allah akulangani.”

Anthu aja sanamvere, ndipo anati: “siwe kanthu koma wabodza! Chifukwa chani ife timvere mau a munthu wabodza?”

“Ine si wabodza” Mneneri Hud anawauza. Ndipo anthu a ‘Aad anati: “Ngati suli wabodza, titsimikizire kuti zomwe ukuyankhulazo ndi zoona! Muuze Allah atitumizire chilango!”

Hud alaih salaam anali odandaula ndi kukhumudwa atamva izi.

“Sine wabodza, ndine Mneneri wa Allah” anawauza moona, koma palibe yemwe anamukhulupilira ndipo anamchokera.

Mneneri anayesetsa kulalikira mafuko osiyanasiyana:

“Kodi mukuganiza kuti nyumba zomwe mwamangazi zikhala muyaya?” anawafunsa. “Kumbukirani kuti ndi Allah yemwe anakupatsani chuma; Iye ndi Mbuye wanga komanso Mbuye wanu, ndipo Iye yekha mukuyenera kumukhulupilira. Ndinakuchenjezani mbuyomu; koma mukapanda kumvera Allah, adzabweretsa  anthu ena mmalo mwanu. Allah ndi Odziwa ndipo Wakumva chirichonse.”

Koma akuluakulu a fuko anamukananso ndikumutcha opusa ndi wabodza.

Mtumiki anayesetsabe kuwatsimikizira kuti akhulupilire,

“O anthu anga, “sine opusa” anawaza. “Ine ndi Mtumiki wochokera kwa Mbuye wa zolengedwa zonse. Ndikukufotokozerani zomwe Iye akufuna komanso kukulangizani”

Sanamumvere Mneneri ndipo anamutembenukira ndikupitiriza kupembedza mafano. Omwe anamvera mau a Mneneri anali ochepa kwambiri.

Hud adazindikira kuti Allah awalanga anthu a ‘Aad posachedwa, poti Allah amalanga anthu osakhulupilira mosayang’ana kulemera kwawo, kuvuta kapena kulemekezeka kwawo.

Pambuyo pamasiku ochepa, chilala chinadza dziko lonse; mitambo sinatsitse mvula ndipo dzuwa linanyeketsa mchenga wa mchipululu.

Anthu a ‘Aad anapita kukamufunsa Hud: “bwanji chilala chimenechi?” Mneneri anayankha: “Allah wakukwiyirani. Mukamukhulupilira, akuchotserani mavuto ndiukukutsitsirani mvula”

“Ndiwe opusa!” Anamuseka Mneneri monyoza.

Chilala chinaonjezereka; mitengo inabiliwira ndipo mimera inafa. Koma anthu anapitiriza kupembedza mafano.

Myezi yambiri inadutsa popanda kulandira ngakhale dontho la mvula. Anthu a ‘Aad anakana kuvomereza kuti Allah ndi Mulungu wawo ndipo anapempha mafano kuti awatsitsire mvula. Koma chilala chinapitilira kwa zaka zitatu.

Tsiku lina pamene Mneneri anali kupemphera, Allah Subhaanahu wa Ta’ala anamuuza kuti asonkhanitse anthu omwe anamukhulupilira ndikutuluka mu mzinda wa ‘Aad.

Mosakhalaitsa, thambo lalikulu lakuda linaoneka kumwamba. Koma osakhulupilira aja sanadziwe kuti Allah ndamene wanatumiza thambolo kudzawachenjeza; iwo  anali kuganiza kuti thambo limenelo liwatsitsira mvula, choncho anapitiriza kupembedza mafano aja.

Nthawo yomweyo nyengo inasintha kuyamba kuzizira komanso mphepo yamkuntho yomwe inagwedeza chirichonse; mitengo, mimera ngakhalenso anthu. Mphepo inakuntha usana ndi usiku. Ndipo anthu a ‘Aad anazindikira kuti ichi ndi chilango chochokera kwa Allah ndipo anayamba kuthawa. Anabisala mmanyumba koma mphepo ija inali yamphamvu kotero inaononga nyumba zawo. Ena anabisala pansi pa nyumba zikuluzikulu koma mphepo yamphamvu inaononga nyumba zonse ndipo anafera momwemo.

Mphepo inakuntha kwa masiku 7 ndi mausiku 8 mpaka mzinda wonse unasanduka bwinja. Anthu onse anaonongedwa kupatula Hud ndi anthu ake poti anamvera chenjezo la Allah Subhaanahu wa Ta’ala. Anasamukira ku Hadhramawt komwe anakhala mwamtendere, kupembedza Allah Mmodzi yekha Woonadi.