Hijaama ndi liwu la Chiarabu lomwe likutanthauza muchiyankhulocho kuti “kuyamwa”, monga mmene timayankhulira kuti “mwana akuyamwa bere la mai ake”

حجم الطفل ثدي أمه أو مص الطفل ثدي أمه

Tsopano liwu loti

حجم

Likutanthauza size, ndipo likugwiritsidwa ntchito chifukwa choti tanthauzo lake lenileni ndilo kubwezeretsa size ya chinthu mmalo mwake, kapena kuphwetsa. Matanthauzo onsewa akutanthauzira ntchhito ya Hijaama yomwe ndi kuyamwa magazi omwe asonkhana mthupi, ndipo kuchotsedwa kwa magazi amenewa kumathandiza kupewa matenda osiyanasiyana mu Chifuniro cha Allah.
Hijaamah ndintchito, pomwe Mihjam ndi chida chomwe chimagwiritsidwa ntchito pa ntchito ya Hijaama, ndipo Hajaam ndimunthu yemwe amagwira ntchto yopanga hijaama.
Muchizungu Hijaama imatchedwa Cupping Therapy, potengera kuti zochotsera magazi zimakhala ngati timakapu choncho.
Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena mu Hadith yochokera kwa Anas Bun Maliki radhia Allah anhu:

… إن أمثل ما تداويتم به الحجامة

Ndithu njira yabwino yomwe mwagwiritsa ntchito pa treatment, ndi Hijaamah. Sahih Al-Bukhari #5696
Ananenanso mu Hadith yochokera kwa Abu Huraira kuti

… وإن كان في شيئ مما تداوون به خير فالحجامة

Choncho ngati pali chinthu chabwino chomwe mungagwiritsire ntchito pa treatment, ndiye Hijaamah
Sahih Abi Daud #2102 (Al-Albaani)
Ofuna kuwerenga zambiri apeze buku lotchedwa “Al Hijaamatu Nnabawiyyah” lolembedwa ndi Dr. Ahmad Abu Nnasr.