Pomaliza, tiyeni tiwone zomwe zimawonekera poyera kumaiko a Kumadzulo kuti ndi chizindikiro chachikulu cha kuponderezedwa kwa akazi; chophimba kapena chivundikiro cha mutu. Kodi ndi zoona kuti mu Chiyuda ndi Chikhristu mulibe lamulo la kuziphimba kwa amayi? Kuti tiyankh funsoli funsoli  momveka bwinobwino, tione kuchokera kwa Rabbi Dr. Menachem M. Brayer (Pulofesa wa Biblical Literature ku Yeshiva University), zomwe analemba m’buku lake, The Jewish Woman in Rabbinic Literature: “Chinali chizolowezi cha amayi a Chiyuda potuluka kupita kuchigulu cha anthu, kuphimba kumutu, ndipo nthawi zina ngakhale nkhope yonse kusiya diso limodzi lokha.” 76

Iye ananenanso mau ena ochokera kwa ma Rabbi akale kuti: “Sizoyenera kuti ana a Israel adziyenda panja mitu yosaphimba” ndipo “ali wotembeleredwa munthu amene amalolera kuti tsitsi la mkazi wake lidziwonedwa … mkazi amene amawonetsa tsitsi lake ndikudzikongoletsa, amabweretsa umphaŵi.” Lamulo la a Rabbi limaletsa kuchita mapemphero kapena kuwerenga mau olemekezeka pamaso pa mkazi wokwatiwa yemwe sanaphimbe mutu wake, chifukwa kusaphimba mmutu kwa mkazi ndi “umaliseche”. 77

Dr. Brayer ananenanso kuti “Mu nthawi ya Tannaitic, kusavala mmutu kwa mkazi wa Chiyuda kunali kutsutsana ndi kudzichepetsa kwake, ndipo ngati angapezeke kuti sanaphimbe mmutu, amalipiritsidwa 400 zuzim”. Dr. Brayer akufotokozanso kuti chophimba cha mkazi wa Chiyuda sichinali nthawi zonse ngati chizindikiro cha kudzichepetsa, koma nthawi zina chimayimira kusiyanitsa pakati pa ovala zapamwamba komanso otchuka, osati kudzichepetsa monga mwanthawi zonse. Chophimba chimabweretsa kulemekezeka kwa mkazi. Komanso chimaimira kuthekera kwa mkazi pokhala katundu wolemekezeka wa mwamuna wake. 78

Chophimbachi chimathandiza kulemekezeka kwa chikhalidwe cha mkazi. Akazi a makalasi apansi nthawi zambiri ankavala chophimba kuti apereke chithunzithunzi cha mtengo wapatali kwa ena. Mfundo yonena kuti chophimba chinali chizindikiro cha ulemu, ikukwanira kukhala yoona poti mahule sankaloledwa kuphimba tsitsi lawo, kuti adziwonedwa zodzikongoletsera zawo mosavuta. Komabe, iwo ankavala chovala china chake chamtengo wapatali kuti azioneka olemekezeka. 79

Akazi a Chiyuda ku Ulaya anapitiriza kuvala zophimba mpaka zaka za mma 19th century, pamene miyoyo yawo inasokonezeka kwambiri ndi chikhalidwe cha mdziko. Choncho akazi ambiri anayamba kukakamizika ndi chikhalidwecho nkuyamba kuyenda osaphimba. Azimayi ena a Chiyuda ataona kuti kwa iwo ndizovuta kuphimba kumutu, anabweretsa veil yawo ya mtundu wina yowoneka ngati – wig.. Lero lino, akazi a Chiyuda ambiri opembedza saphimba tsitsi lawo kupatula m’sunagoge. 80 Pomwe ena a iwo, monga magulu a Hasidic, amagwiritsabe ntchito wig.

Kodi nanga myambo ya Chikhristu ili pati pankhaniyi? Ndi zodziwika bwino lomwe kuti ma sister a chi Katolika akhala akuphimba mitu yawo kwa zaka zambiri, komatu sizomwezo; Paulo Woyera mu Chipangano Chatsopano analankhula mawu osangalatsa kwambiri pa chophimba:

“Koma ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu. Mwamuna aliyense amene akupemphera kapena kunenera atavala chinachake kumutu akuchititsa manyazi mutu wake, koma mkazi aliyense amene akupemphera kapena kunenera osavala kanthu kumutu akuchititsa manyazi mutu wake, popeza nchimodzimodzi ndi kumeta mpala. Ngati mkazi savala kanthu kumutu, amete mpala, koma ngati zili zochititsa manyazi kuti mkazi amete kwambiri tsitsi lake kapena amete mpala, azivala chakumutu. Mwamuna sayenera kuphimba kumutu kwake, popeza iye ndi chifaniziro ndi ulemerero wa Mulungu, koma mkazi ndi ulemerero wa mwamuna. Pakuti mwamuna sanachokere kwa mkazi, koma mkazi kwa mwamuna, ndiponso mwamuna sanalengedwere mkazi, koma mkazi analengedwera mwamuna. Ndiye chifukwa chake mkazi ayenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro kumutu kwake chifukwa cha Angelo.” (1 Akorinto 11:3-10).

Paulo Woyera analembera zokhunza akazi ophimba kuti chophimba chimayimira chizindikiro cha ulamuliro wa munthu yemwe ndi chithunzi ndi ulemelero wa Mulungu, pa mkazi yemwe analengedwa kuchokera kwa munthu.

Pa mitu ya zolemba za Tertullian Woyera yotchedwa ‘On The Veiling Of Virgins’ (Kudziphimba kwa Anamwali), analemba kuti, “Atsungwana inu, mumavalira zophimba zanu mmisewu, kotero muyenera kuvalanso mu tchalitchi; mumavala pamene muli pakati pa alendo, choncho muzivalanso pakati pa abale anu …” 81

Mmalamulo a Canon mu mpingo wa Katolika lero lino, muli lamulo lomwe limafuna amayi kuti aziphimba mitu yawo mu tchalitchi. 82 Mipingo ina ya Chikhristu, monga Amish ndi Amennoni, mwachitsanzo, amawaphimba akazi awo mpaka lerolino. Malinga ndi atsogoleri awo a Tchalitchi, chifukwa cha chophimbachi ndi chakuti: “Chophimba kumutu ndi chizindikiro cha kugonjera kwa mkazi kwa mwamuna wake ndi Mulungu”, chomwe chikufanana ndi lingaliro lomwe linalembedwa ndi Paulo Woyera mu Chipangano Chatsopano. 83

Kuchokera mmaumboni onsewa, zikuwonekeratu kuti Chisilamu sichinapeke chophimba (hijaab), koma kuti chinalimbikitsa ndikuchipanga kukhala lamulo. Qur’an imalamula amuna ndi akazi okhulupilira kuti adzolike maso awo ndikusamalira kudzichepetsa kwawo, kenako chikuwalimbikitsa amayi okhulupilira kuti afikitse zophimba mmutu mukhozi mpaka pachifuwa:

Qur’an 24:30-31: “Auze Asilamu achimuna kuti adzolitse maso awo (asayang’ane zoletsedwa), ndipo asunge umaliseche wawo. Ichi nchoyera kwambiri kwa iwo. Ndithu, Mulungu akudziwa nkhani za zonse zomwe achita. Ndipo auze Asilamu achikazi kuti adzolitse maso awo, ndikusunga umaliseche wawo, ndipo asaonetse (poyera) zomwe amadzikongoletsa nazo kupatula zimene zaonekera poyera (popanda cholinga chotero). Ndipo afunde kumutu mipango yawo mpaka mzifuwa zawo…”.

Qur’an yawonetsa poyera kuti hijab ndiyofunikira chifukwa imamusungira ulemu mkazi, komano nchifukwa chani kusungira ulemu mkazi kuli kofunikira? Qur’an yalongosolanso momveraka bwino:

Qur’an 33:59: ” E, iwe Mneneri! Uza akazi ako, ndi ana ako aakazi, ndi akazi a Asilamu, kuti adziphimbe ndi nsalu zawo (akamatuluka mnyumba), kutero kuchititsa kuti adziwike, asazunzidwe (ndi anthu achipongwe). Ndipo Mulungu Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni.”.

Chimenecho ndicho cholinga chake; kudzichepetsa pamaso pa Mulungu ndikudzipatsa ulemu, zimateteza akazi kuti asachitidwe chipongwe. Choncho, cholinga chachikulu cha hijab Mchisilamu ndiko kudziteteza. Tidziwe kuti, hijab ya Chisilamu ndiyosiyana ndi hijab ya Chikhristu chifukwa choti ya Chisilamu cholinga chake si kusonyeza umwini wa mwamuna pa mkazi wake, kapena kusonyeza kugonjera kwa mkazi kwa mwamuna wake. Komanso, hijab ya Chisilamu ndiyosiyana ndi ya Chiyuda chifukwa ya Chisilamu sikusonyeza ulemelero pa zovala za mtengo wapatali kapena kutchuka pakati pa amayi.

Cholinga cha hijab ya Chisilamu ndicho kudzilemekeza, kugonjera Mulungu komanso kudziteteza kwa amuna. Chikhulupiliro cha Chisilamu ndichoti nthawi zonse ndibwino kukhala otetezeka kuti zoipa zisakugwere. Qur’an ili yokhunzidwa kwambiri pa kuteteza matupi a amayi ndi chikhalidwe chawo, kotero kuti amuna omwe anganamizire mkazi mopanda chilungamo ayenera kulangidwa koopsa:

Qur’an 24: 4: “Ndipo amene akunamizira akazi odziteteza (powanamizira kuti achita chiwerewere), ndipo osabwera nazo mboni zinayi, akwapuleni zikoti 80; ndiponso musauvomereze umboni wawo mpaka kalekale. Iwo ngotuluka mchilamulo cha Mulungu.”

Tayesani kufananitsa chilango ichi ndi chilango cha kugwililira m’Baibo:

“Mwamuna akapeza ndi kugwira mtsikana, namwali wosalonjezedwa kukwatiwa, nkugona naye ndipo onsewo agwidwa, mwamunayo azipereka masekeli 50 asiliva kwa bambo a mtsikanayo, ndipo akhale mkazi wake chifukwa chakuti wamunyazitsa. Sadzaloledwa kumusiya ukwati masiku onse a moyo wake. “Pasapezeke mwamuna aliyense wotenga mkazi wa bambo ake kuopera kuti angavule bambo akewo.” (Deut. 22: 28-30)

Tidzifunse pamenepa kuti kodi mwa awiriwa; msungwana wogwiliridwa ndi mwamuna wogwililira, ndi ndani yemwe akulangwidwa? Mwamuna yemwe wangolamulidwa kupereka chindapusa, kapena msungwana yemwe wakakamizidwa kukwatiwa ndi mwamuna yemwe wamugwilirira ndikukhala naye mpaka atamwalira? Funso linanso ndiloti: ndi chiyani chomwe chimateteza kwambiri amayi pakati pa Qur’an ndi Baibulo? Anthu ena, makamaka Kumadzulo, akhonza kunyoza mfundo ya kudzichepetsa kuti atetezedwe. Iwo yankho la kutsutsa kwawo amati kumuteteza mkazi komwe kuli kwabwino ndiko kudzera mmaphunziro, chikhalidwe chotukuka ndi kudziletsa. Pamenepo titha kunena kuti chabwino, koma sizikukwanira kukhala chitetezo cha zomwe akudzitetezazo. Ngati ‘chitukuko’ chili chitetezo chokwanira, nanga bwanji amayi aku North America samayerekeza kuyenda okha mumsewu wamdima – ngakhalenso mmalo opanda magalimoto? Ngati maphunziro chabe ali njira yopambana yothetsera mavutowa, nchifukwa chani yunivesite yolemekezeka ngati ya Queen’s ili ndi dongosolo la ‘kuperekeza kunyumba’ ophunzira achikazi? Ngati kudziletsa chabe kuli njira yothetsera vutoli, ndichifukwa chiyani milandu yochitira chipongwe amayi mmalo antchito imalengezedwa tsiku ndi tsiku mma TV ndi mma wailesi? Zitsanzo za omwe aimbidwa mlandu wa zakugonana zaka zochepa zapitazi, ndi monga: Akuluakulu a asilikali, Akuluakulu a malo a ntchito, ophunzitsa ku university, nduna za boma, akuluakulu a makhoti akuluakulu, ngakhalenso pulezindent wa United States! Sindinakhulupilire maso angawa pamene ndimawerenga kafukufuku ameneyu mu chikalata cholembedewa ndi Mphunzitsi wamkulu mu Ofesi yaku Queen’s University:

Ku Canada, amayi amachitiridwa chipongwe ndi chiwerewere pa mphindi 6 zilizonse, mayi mmodzi mwa atatu aliwonse ku Canada amakhala akugwiliridwa , ndipo mmodzi mwa anayi aliwonse amakhala pachiwopsezo cha kugwiliridwa kapena kuyesera kugwiliridwa. Mmodzi mwa 8 aliwonse amatha kugwiliridwa panthawi yomwe ali ku university. Kafukufuku wapeza kuti 60% ya amuna a mma university ku Canada, amachita za chiwerewere mowumiriza atsikana akapanda kugwidwa.

China chake ndithu chikulakwika pakati pathu moyo womwe tikukhalawu; Kusintha kwakukulu pa chikhalidwe cha anthu kukufunika kwambiri; kuvala modzilemekeza, kuyankhula komanso chikhalidwe pakati pa amuna ndi akazi chikhale chabwino. Kupanda kutero, zotsatira zidzipezeka kuti chikhalidwe choipa chikunkera mtsogolo tsiku ndi tsiku, koma mwatsoka azimayi okha ndi amene amakhala akulipira ndi kulangidwa. Ndi zoonadi kuti tonsefe tikuvutika, koma pali kusiyana, malinga ndi kuyankhula kwa Khalil Gibran “… munthu yemwe amalandira zibakera sali ngati yemwe akuwerenga zibakerazo.” 84

Choncho, anthu monga a ku France omwe amathamangitsa amayi achichepere mmasukulu chifukwa chovala mwaulemu, akudzivulaza okha.  Ichi ndi chimodzi mwazovuta zamdziko lathuli masiku ano, pamene tikuona kuti mpango wakumutu womwewu umalemekezedwa ndipo umatengedwa kuti ndi chizindikiro cha ‘chiyero’ ukavalidwa ndi a Katolika ndicholinga chofuna kukwaniritsa umwini wa mwamuna, pomwe kuvalidwa ndi Msilamu umasonyeza ‘kupondereza’ osati kuteteza ndi kulemekeza.

Mathero